Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr22 November tsamba 1-11
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Timitu
  • NOVEMBER 7-13
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwbr22 November tsamba 1-11

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

NOVEMBER 7-13

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 5-6

“Tili Ndi Ambiri Kuposa Amene Ali Ndi Iwowo”

it-1 716 ¶4

Elisa

Anapulumutsa Isiraeli kwa Siriya. Pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Yehoramu ya Isiraeli, Siriya anakonza zokaukira Isiraeli modzidzimutsa. Kwa maulendo angapo, Elisa analepheretsa zimene Benihadadi II ankafuna kuchita. Elisa ankauza Mfumu Yehoramu chilichonse chimene Asiriya ankafuna kuchita. Poyamba Benihadadi ankaganiza kuti winawake pa gulu lawolo ali ku mbali ya mfumu ya Isiraeli. Koma atazindikira munthu weniweni amene ankachita zimenezi, anatumiza asilikali ake ku Dotana omwe anazungulira mzindawo ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo n’cholinga choti akagwire Elisa. Mtumiki wa Elisa anachita mantha kwambiri koma Elisayo anapemphera kwa Mulungu kuti amutsegule maso mtumikiyo “moti anaona kuti dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.” Ndiyeno asilikali a mfumu ya Siriyawo atayamba kuyandikira, Elisa anapemphera kuti pachitike chodabwitsa china ponena kuti: “Chonde chititsani khungu mtundu uwu.” Kenako Elisa anauza asilikali a Siriyawo kuti, “Nditsatireni,” koma sanafunike kuchita kuwagwira padzanja zomwe zikusonyeza kuti anachita khungu m’maganizo osati m’maso. Iwo sanam’zindikire Elisa yemwe anabwera kuti adzamtenge komanso sanazindikire kuti akupita nawo kuti.—2Mf 6:8-19.

w13 8/15 30 ¶2

Elisa Anaona Magaleta Oyaka Moto—Kodi Inunso Mukuwaona?

Elisa sanachite mantha pamene anazunguliridwa ndi adani ku Dotana. Iye sanaope chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ifenso tiyenera kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Choncho tizipempha mzimu woyera wa Mulungu kuti tikhale ndi chikhulupiriro ndiponso makhalidwe ena amene mzimuwu umatulutsa.—Luka 11:13; Agal. 5:22, 23.

it-1 343 ¶1

Khungu

Zimaoneka kuti khungu limene asilikali a Siriya anachita chifukwa cha mawu amene Elisa analankhula linali la m’maganizo. Zikanakhala kuti asilikali onse anachita khungu la m’maso ndiye kuti akanafunika kuchita kugwiridwa pamkono kuti ayende. Koma nkhaniyi imangofotokoza kuti Elisa anawauza kuti: “Njira yake si imeneyi ndipo mzinda wake si umenewu. Nditsatireni.” Pa zimene zinachitikazi, munthu wina dzina lake William James ananena m’buku lake lonena za kaganizidwe ka anthu (Principles of Psychology, 1981, Vol. 1, tsa. 59) kuti: “Vuto lina lochititsa chidwi lokhudza matenda a m’maganizo ndi kuchita khungu la m’maganizo. Munthu akachita khungu limeneli sikuti amalephera kuona zinthu ayi koma amalephera kuzizindikira. Vuto limeneli tingati limabwera pamene ubongo ukulephera kutanthauzira zimene maso akuona. Ndipo zimachitika chifukwa chakuti malo amene pamafikira zithunzi zimene maso aona sakulumikizana ndi malo ena mu ubongomo.” Zikuoneka kuti linali khungu limeneli limene Yehova anachotsera asilikali a Siriya atafika ku Samariya. (2Mf 6:18-20) N’kutheka kuti nawonso amuna a ku Sodomu anachita khungu la m’maganizo chifukwa nkhani yake imati m’malo modandaula kuti asiya kuona, iwo ankapitiriza kufufuza khomo la nyumba ya Loti.—Ge 19:11.

Mfundo Zothandiza

w05 8/1 9 ¶2

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Wachiwiri

5:15, 16—N’chifukwa chiyani Elisa anakana mphatso ya Namani? Elisa anakana mphatsoyo pozindikira kuti iye anachiritsa Namani mozizwitsa mwa mphamvu za Yehova, osati zake ayi. Iye sanaone ngati chinthu choyenerera kudyererapo pa ntchito imene Mulungu anam’patsa. Olambira oona masiku ano samafuna kudyererapo pa ntchito yotumikira Yehova. Iwo amamvera mawu a Yesu akuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:8.

NOVEMBER 14-20

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 7-8

“Yehova Anachita Zimene Anthu Sankayembekezera”

it-1 716-717

Elisa

Komabe, patapita nthawi, Benihadadi II analowa mumzinda wa Samariya, osati kungopita mwachangu kukamenya nkhondo n’kubwerera, koma anapita mwamphamvu ndipo anazungulira mzindawo kuti aulande. Zinthu zinafika povuta kwambiri moti mpaka mfumu inalandira nkhani yoti mayi wina wadya mwana wake. Mfumu Yehoramu mwana wa Ahabu, “munthu wopha anthu uja,” analumbira kuti apha Elisa. Koma lumbiro lakeli silinachitike. Yehoramu ndi msilikali wake womuthandiza atafika kunyumba ya Elisa, Yehoramuyo ananena kuti sakukhulupiriranso kuti Yehova angawathandize. Elisa anatsimikizira mfumuyo kuti tsiku lotsatira kukhala chakudya chambiri. Koma wothandizira mfumu uja anakayikira kuti zimenezi sizingatheke ndipo Elisa anamuuza kuti: “Uona zimenezi ndi maso ako, koma sudya nawo.” Yehova anachititsa kuti mumsasa wa Asiriya mumveke phokoso limene linachititsa Asiriyawo kuti aganize kuti magulu ogwirizana a asilikali akubwera kuti adzamenyane nawo moti anayamba kuthawa, kusiya msasa wawo komanso chakudya chili momwemo. Mfumu itamva kuti Asiriya athawa, inaika womuthandizira uja kuti aziyang’anira pageti la mzinda wa Samariya, ndiye pamene Aisiraeli anjala ankathamangira ku msasa wa Asiriya kuti akakunkhe chakudya, anam’pondaponda mpaka anafa. Anaona chakudya ndi maso ake, koma sanadye nawo.—2Mf 6:24–7:20.

Mfundo Zothandiza

it-2 195 ¶7

Nyale

Mafumu Amene Anali Mumzere wa Davide. Yehova Mulungu anaika Mfumu Davide pa mpando wachifumu wa Isiraeli. Mothandizidwa ndi Yehova, Davideyo anasonyeza kuti anali mtsogoleri wanzeru. Choncho iye ankatchedwa “nyale ya Isiraeli.” (2Sa 21:17) Mu pangano la Ufumu limene Yehova anachita ndi Davide, anamuuza kuti: “Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.” (2Sa 7:11-16) Choncho mzere wa mafumu kuchokera pa Davide kukafika pa mwana wake Solomo unalidi ngati “nyale” ya Isiraeli.—1Mf 11:36; 15:4; 2Mf 8:19; 2Mb 21:7.

NOVEMBER 21-27

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 9-10

“Anachita Zinthu Molimba Mtima, Modzipereka Komanso Mofunitsitsa”

w11 11/15 3 ¶2

Yehu Anamenyera Nkhondo Kulambira Koyera

Yehu anadzozedwa kukhala mfumu ya Isiraeli pamene dzikolo linali loipa kwambiri chifukwa cha munthu woipa Yezebeli. Pa nthawiyi, Ahabu, mwamuna wake, anali ataphedwa ndipo amene ankalamulira anali mwana wake dzina lake Yehoramu. Yezebeli ankalimbikitsa kulambira Baala m’malo molambira Yehova. Anapha aneneri a Mulungu ndiponso anasocheretsa anthu chifukwa cha “dama” lake ndi ‘zamatsenga.’ (2 Maf. 9:22; 1 Maf. 18:4, 13) Yehova analamula kuti anthu onse a m’nyumba ya Ahabu aphedwe, kuphatikizapo Yehoramu ndi Yezebeli. Mulungu anasankha Yehu kuti atsogolere ntchito imeneyi.

w11 11/15 4 ¶2-3

Yehu Anamenyera Nkhondo Kulambira Koyera

Yehu anakana kuyankha chilichonse kwa anthu awiri amene Yehoramu anawatuma. Kenako Mfumu Yehoramu inanyamuka limodzi ndi mfumu ya Yuda, Ahaziya. Aliyense ananyamuka pa galeta lake kukakumana ndi Yehu. Mfumu Yehoramu inamufunsa kuti: “Kodi ukubwerera zamtendere Yehu?” Ndipo Yehu anamuyankha kuti: “Mtendere ungakhalepo bwanji pali dama la Yezebeli mayi ako ndi amatsenga ake ambirimbiri?” Yehoramu anachita mantha ndi yankho limeneli ndipo anayamba kuthawa. Koma mwamsangamsanga Yehu anakoka uta n’kubaya Yehoramu kumsana moti muviwo unatulukira pamtima pake. Yehoramu anagwera m’galeta lake n’kufera pompo. Ahaziya anathawa koma Yehu anamutsatira mpaka kumupeza n’kulamula kuti aphedwe.—2 Maf. 9:22-24, 27.

Munthu wina wa m’nyumba ya Ahabu amene anafunika kuphedwa anali Mfumukazi Yezebeli yomwe inali yoipa kwambiri. Yehu ananena kuti iye anali ‘munthu wotembereredwa.’ Yehu atafika ku Yezereeli anaona Yezebeli ataima pawindo la nyumba yachifumu n’kumayang’ana kunja. Nthawi yomweyo Yehu anauza nduna zina kuti zimuponye pansi kudzera pawindo. Zitamuponya, Yehu anam’pondaponda ndi mahatchi ake munthu amene anaipitsa Isiraeliyu. Kenako Yehu anapitiriza kuwononga anthu ena a m’banja la Ahabu.—2 Maf. 9:30-34; 10:1-14.

w11 11/15 5 ¶3-4

Yehu Anamenyera Nkhondo Kulambira Koyera

N’zoona kuti Yehu anapha anthu ambiri. Koma Malemba amanena kuti iye anali munthu wolimba mtima amene anamasula Aisiraeli mu ulamuliro wopondereza wa Yezebeli ndi banja lake. Kuti wolamulira wa Isiraeli akwanitse kuchita zimenezi, anayenera kukhala munthu wolimba mtima, wakhama ndiponso wosabwerera m’mbuyo. Buku lina lofotokoza Baibulo limati iye anagwira ntchito ‘yovuta ndipo sanalekerere aliyense. Mwina akanachita zinthu mwachifatse sakanakwanitsa kuthetsa kulambira Baala mu Isiraeli.’

Apa tsopano mutha kuona kuti zinthu zina zimene Akhristu amakumana nazo masiku ano zimafuna kuti iwo asonyeze makhalidwe amene Yehu anali nawo. Mwachitsanzo, kodi tiyenera kutani ngati tikuyesedwa kuti tichite zinthu zimene Yehova amadana nazo? Tiyenera kukana mwamsanga, molimba mtima ndiponso mosanyengerera. Sitiyenera kulekerera zinthu pa nkhani zokhudza kudzipereka kwathu kwa Yehova.

Mfundo Zothandiza

w11 11/15 5 ¶6-7

Yehu Anamenyera Nkhondo Kulambira Koyera

N’kutheka kuti Yehu ankaganiza kuti popeza ufumu wa Isiraeli unali utagawikana ndi wa Yuda, ndiye kuti pafunika kuti asiyanenso pa nkhani ya kulambira. Ndiyeno mofanana ndi mafumu ena a Isiraeli, iye analimbikitsa kulambira ana a ng’ombe pofuna kuti akhalebe osiyana ndi ufumu wa Yuda. Apatu anasonyeza kuti sankakhulupirira kwambiri Yehova, amene anamudzoza kuti akhale mfumu.

Yehova anayamikira Yehu chifukwa chakuti ‘anachita zoyenera pamaso pake.’ Komabe, Yehu “sanayesetse kuyenda motsatira malamulo a Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.” (2 Maf. 10:30, 31) Mukaganizira zimene anadzachita pamapeto ake poyerekezera ndi zonse zimene Yehu anachita kumbuyoku, mukhoza kudabwa ndiponso kumva chisoni. Koma zimene iye anachitazi zikutipatsa phunziro. Ubwenzi wathu ndi Yehova sitiyenera kuuona mwachibwanabwana. Tsiku lililonse tiyenera kuyesetsa kukhala okhulupirika kwa Mulungu. Kuphunzira Baibulo, kusinkhasinkha zimene taphunzira ndiponso kupemphera ndi mtima wonse kwa Atate wathu wakumwamba kungatithandize kuchita zimenezi. Choncho tiyeni tiyesetse kwambiri kutsatira malamulo a Yehova ndi mtima wathu wonse.—1 Akor. 10:12.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w13 5/15 8-9 ¶3-6

Kodi Ndinu “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”?

Lemba la Yesaya 9:7 limafotokoza mmene Yehova adzachitire zinthu zabwino mu ulamuliro wa Mwana wake. Limati: “Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.” Mawu amenewa amasonyeza kuti Yehova amafunitsitsa kupulumutsa anthu. Popeza kuti Yehova amachita zinthu modzipereka, ifenso timalimbikitsidwa kugwira ntchito imene watipatsa modzipereka. Timatsanzira Yehova tikamathandiza anthu mofunitsitsa kuti aphunzire za iye. Popeza ndife antchito anzake a Mulungu, kodi timafunitsitsa kugwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri?—1 Akor. 3:9.

Nayenso Yesu ndi wodzipereka potumikira Mulungu. Iye anapereka chitsanzo pa nkhani yolalikira mwakhama. Ngakhale kuti ankatsutsidwa kwambiri, anapitiriza kudzipereka pa ntchito yolalikira mpaka pamene anafa mozunzika. (Yoh. 18:36, 37) Khama lake lofuna kuthandiza anthu kuti adziwe Yehova linkawonjezeka kwambiri pamene imfa yake inkayandikira.

Mwachitsanzo, chakumapeto kwa 32 C.E., Yesu anapereka fanizo la munthu amene anali ndi mtengo wa mkuyu m’munda mwake. Mtengowu unakhala wosabala zipatso kwa zaka zitatu. Wosamalira munda atauzidwa kuti audule, anapempha kuti athire kaye manyowa. (Werengani Luka 13:6-9.) Pa nthawiyo, ophunzira ochepa okha ndi amene anali ngati zipatso za ntchito yolalikira ya Yesu. Iye anali ngati wosamalira mundawo ndipo analalikira mwakhama kwambiri ku Yudeya ndi ku Pereya pa miyezi 6 imene inatsala asanaphedwe. Ndipo kutatsala masiku ochepa kuti aphedwe, Yesu analirira anthu a mtundu wake amene “anamva ndi makutu awo koma osalabadira.”—Mat. 13:15; Luka 19:41

Popeza kuti tili m’masiku otsiriza enieni, ifenso tiyenera kulalikira mwakhama kwambiri kuposa kale. (Werengani Danieli 2:41-45.) Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala Mboni za Yehova. Ndife tokha m’dzikoli amene timauza anthu mmene mavuto athu adzathere. Munthu wina wolemba nkhani m’nyuzipepala anafotokoza za funso lovuta limene anthu sangapeze yankho lake. Funso lake ndi lakuti, “N’chifukwa chiyani anthu abwino amakumananso ndi mavuto?” Ndi udindo wathu komanso mwayi waukulu kuuza anthu mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso ngati amenewa. Pali zifukwa zambiri zotilimbikitsa ‘kuyaka ndi mzimu’ pogwira ntchito imene Mulungu watipatsa. (Aroma 12:11) Yehova amatidalitsa tikamalalikira modzipereka ndipo tidzatha kuthandiza anthu kuti ayambe kudziwa komanso kukonda Yehova.

NOVEMBER 28–DECEMBER 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 11-12

“Mzimayi Woipa Komanso Wodzimva Analangidwa”

it-1 209

Ataliya

Mofanana ndi mayi ake Yezebeli, Ataliya analimbikitsa mwamuna wake Yehoramu kuchita zoipa pamaso pa Yehova kwa zaka 8 zimene ankalamulira. (1Mf 21:25; 2Mb 21:4-6) Komanso iye anapha anthu osalakwa ngati mmene mayi akewo ankachitira. Mwana wake Ahaziya yemwe anali woipa anamwalira atalamulira kwa chaka chimodzi. Zitatero, Ataliya anapha anthu onse a m’banja lachifumu, kupatulapo Yehoasi yemwe panthawiyo anali wakhanda ndipo anabisidwa ndi mkulu wa ansembe ndi mkazi wake yemwe anali azakhali ake a Yehoasiyo. Pasanapite nthawi, Ataliya anadziika yekha kukhala mfumukazi ndipo analamulira kwa zaka 6, kuyambira mu 905-899 B.C.E. (2Mb 22:11, 12) Ana ake anaba zinthu zopatulika za m’nyumba ya Yehova n’kukazipereka kwa Baala.—2Mb 24:7.

it-1 209

Ataliya

Yehoasi atakwanitsa zaka 7, Mkulu wa Ansembe Yehoyada, yemwe anali woopa Mulungu, anamutulutsa mwanayo kumene anakam’bisa kuja ndipo anamuika kukhala woyenera kudzalowa ufumu. Atamva phokoso la anthu, Ataliya anathamangira ku kachisi, ndipo ataona zimene zinkachita, analira n’kumati, “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!” Mkulu wa Ansembe Yehoyada analamula kuti amutulutse panja pa kachisi ndipo akamuphere pakhomo la kunyumba ya mfumu lolowera mahatchi. N’kutheka kuti Ataliya anali womaliza wa m’nyumba ya Ahabu. (2Mf 11:1-20; 2Mb 22:1–23:21) Zimene zinakwaniritsa mawu amene ananenedweratu akuti: “Mawu onse a Yehova otsutsa nyumba ya Ahabu amene Yehova analankhula, adzakwaniritsidwa.”—2Mf 10:10, 11; 1Mf 21:20-24.

Mfundo Zothandiza

it-1 1265-1266

Yehoasi

Kenako zinthu zinapitiriza kumuyendera bwino kwambiri Yehoasi kwa nthawi yonse imene Mkulu wa Ansembe Yehoyada anali moyo ndipo ankachita zinthu ngati bambo ake komanso mlangizi wake. Yehoasi anakwatira ali ndi zaka 21 ndipo anali ndi akazi awiri, mmodzi wa akaziwo dzina lake linali Yehoadana. Iye anakhala ndi ana aamuna komanso aakazi. Zimenezi zinachititsa kuti mzere wa Davide umene Mesiya anali kudzabadwira, omwe unatsala pang’ono kuwonongedweratu, ukhalenso wamphamvu.—2Mf 12:1-3; 2Mb 24:1-3; 25:1.

DECEMBER 5-11

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 13-15

“Kuchita Zinthu Ndi Mtima Wonse Kumabweretsa Madalitso Ambiri”

w10 4/15 26 ¶11

Kodi Mukutsatira Khristu ndi Mtima Wonse?

Kuti timvetse kufunika kokhala achangu potumikira Mulungu, tiyeni tione zimene zinachitika pa moyo wa Mfumu Yehoasi ya Isiraeli. Iye anada nkhawa kuti mwina Aaramu agonjetsa Aisiraeli, choncho anapita kwa Elisa akulira. Mneneriyu anamuuza kuti aponye muvi wake kumene kunali Suriya kudzera pa zenera, posonyeza kuti iwo adzagonjetsa mtunduwo mothandizidwa ndi Yehova. Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa mfumuyi. Kenako Elisa anauza Yehoasi kuti atenge mivi yake n’kukwapula pansi. Yehoasi anangokwapula katatu kokha. Elisa anakwiya kwambiri ndi zimenezi chifukwa chakuti akanakwapula ka 5 kapena 6, ‘akadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha.’ Choncho, Yehoasi anangopambana katatu kokha chifukwa chakuti anachita zinthu mwamphwayi. (2 Maf. 13:14-19) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi? Yehova adzatidalitsa kwambiri ngati tigwira ntchito yake mwakhama ndiponso ndi mtima wonse.

w13 11/1 11 ¶5-6

“Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna Ndi Mtima Wonse”

Kodi Yehova amapereka mphoto kwa ndani? Paulo ananena kuti amapereka mphoto “kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Buku lina lomasulira Baibulo linanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “omufunafuna ndi mtima wonse” satanthauza ‘kungomufunafuna’ chabe, koma amatanthauza “kulambira Mulungu mwakhama.” Buku linanso limafotokoza kuti verebu lachigiriki limeneli, limanena za kuchita zinthu mobwerezabwereza kapena mwakhama. Choncho, Yehova amapereka mphoto kwa anthu amene amamulambira ndi mtima wonse.—Mateyu 22:37.

Kodi Yehova amapereka bwanji mphoto kwa atumiki ake okhulupirika? Iye amawalonjeza mphoto ya mtengo wapatali imene imasonyeza kuti ndi wachikondi komanso si woumira. Mphoto imeneyi ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Chivumbulutso 21:3, 4) Koma ngakhale pano, anthu amene amafunafuna Yehova ndi mtima wonse amadalitsidwa kwambiri. Iwo amadalitsidwa ndi mzimu woyera komanso amakhala anzeru chifukwa chotsatira Mawu ake. Amakhalanso ndi moyo wabwino umene amakhutira nawo.—Salimo 144:15; Mateyu 5:3.

Mfundo Zothandiza

w05 8/1 11 ¶3

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Wachiwiri

13:20, 21—Kodi chozizwitsa cha pa lembali chimasonyeza kuti kulambira zinthu zakale zopatulika sikulakwa? Ayi sichitero. Baibulo silisonyeza kuti mafupa a Elisa analambiridwapo. Mphamvu ya Mulungu ndi imene inachititsa chozizwitsa chimenechi, ndipo ndi imenenso inachititsa zozizwitsa zonse zimene Elisa anachita mmene anali ndi moyo.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

km 8/03 1

Ntchito Imene Imatsitsimula

1 Uthenga wa m’Baibulo umatsitsimula anthu onse amene amaulandira ndi kuugwiritsa ntchito pa moyo wawo. (Sal. 19:7, 8) Umawathandiza kumasuka ku ziphunzitso zonyenga ndi kusiya makhalidwe oika moyo pachiswe ndiponso umawapatsa chiyembekezo chodalirika cha m’tsogolo. Komabe, amene amapindula si anthu amene amalandira uthenga wabwino okhawo ayi. Anthu amene amauza ena choonadi chotsitsimula cha m’Baibulo nawonso amatsitsimulidwa.—Miy. 11:25.

2 Kupeza Mphamvu Chifukwa cha Utumiki: Yesu ananena kuti amene amasenza goli lokhala wophunzira wa Khristu, limene limaphatikizapo ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira, ‘adzapeza mpumulo wa miyoyo yawo.’ (Mat. 11:29) Iyenso payekha anaona kuti kulalikira kwa ena kunam’patsa mphamvu. Kwa iye, ntchito imeneyi inali ngati chakudya. (Yoh. 4:34) Pamene Yesu anatumiza ophunzira 70 kuti akalalikire, ophunzirawo anasangalala ataona kuti Yehova wadalitsa khama lawo.—Luka 10:17.

3 Mofananamo, Akhristu ambiri masiku ano amapezanso mphamvu akamagwira nawo ntchito yolalikira. Mlongo wina anati: “Utumiki ndi wotsitsimula chifukwa umandithandiza kukhala ndi cholinga pa moyo. Mavuto anga ndi nkhawa za tsiku ndi tsiku zimachepa ndikamalalikira.” Mtumiki wina wachangu anati: “Utumiki . . . umandichititsa kuti ndizimuona Yehova kukhala weniweni tsiku ndi tsiku ndipo umandithandiza kukhala ndi mtendere komanso chimwemwe cha mumtima chimene sichingapezeke m’njira ina iliyonse.” Tili ndi mwayi waukulu wokhala “antchito anzake a Mulungu.”—1 Akor. 3:9.

4 Goli la Khristu N’lofewa: Ngakhale kuti Akhristu akulimbikitsidwa ‘kuyesetsa [“mwakhama,” NW],’ Yesu sakufuna kuti tichite zinthu zimene sitingathe. (Luka 13:24) Ndipotu, amatipempha mwachikondi ‘kusenza goli lake.’ (Mat. 11:29) Amene akukumana ndi mavuto pamoyo wawo angakhulupirire kuti utumiki wawo umene amachita ndi mtima wonse, ngakhale kuti ndi wochepa, umasangalatsa Mulungu.—Marko 14:6-8; Akol. 3:23.

5 N’zotsitsimula kwambiri kutumikira Mulungu amene amayamikira zilizonse zimene timachita chifukwa cha dzina lake. (Aheb. 6:10) Tiyenitu tiyesetse kum’patsa zonse zimene tingathe.

DECEMBER 12-18

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 16-17

“Kuleza Mtima kwa Yehova Kuli ndi Malire”

it-2 908 ¶5

Salimanesere

Kugonjetsa Isiraeli. Mu ulamuliro wa Mfumu Hoshiya ya Isiraeli, (c. 758-740 B.C.E.), Salimanesere wa 5 anayamba kulamulira Palesitina ndipo Hoshiya ankapereka msonkho kuti azimuteteza. (2Mf 17:1-3) Koma kenako patapita nthawi, Hoshiya analephera kupereka msonkho ndipo zinaoneka kuti wachita mgwirizano ndi Mfumu So ya Iguputo kuti achite chiwembu. Zimenezi zinachititsa kuti Salimanesere aike Hoshiya m’ndende ndipo kenako anazungulira mzinda wa Samariya kwa zaka zitatu omwe, ngakhale kuti unali wolimba kwambiri, pamapeto pake unagwa ndipo Aisiraeli anapita ku ukapolo.—2Mf 17:4-6; 18:9-12; yerekezerani ndi Ho 7:11; Eze 23:4-10.

it-1 414-415

Ukapolo

Zomwe zinachititsa kuti ufumu wakumpoto wa Isiraeli wa mafuko 10 ndi ufumu wakum’mwera wa Yuda wa mafuko awiri utengedwe kupita ku ukapolo zinali zofanana. Onse anasiya kulambira Yehova, n’kumalambira milungu yonyenga. (De 28:15, 62-68; 2Mf 17:7-18; 21:10-15) Yehova anayesetsa mbali yake, moti anatumiza aneneri ake mobwerezabwereza kuti akawachenjeze koma sizinkaphula kanthu. (2Mf 17:13) Panalibe mfumu ngakhale imodzi mwa mafumu a mafuko 10 a Isiraeli yomwe inathetseratu kulambira konyenga komwe kunayamba ndi mfumu yoyamba, Yerobowamu. Ufumu wa Yuda womwe unali kum’mwera, nawonso sunamvere machenjezo achindunji a Yehova komanso sunaphunzirepo kanthu kuchokera pa zimene zinachitikira Aisiraeli omwe anatengedwa kupita ku ukapolo. (Yer 3:6-10) Anthu onse a m’ma ufumu awiriwa anatengedwa kupita ku ukapolo.

Mfundo Zothandiza

it-2 847

Msamariya

Mawu akuti “Asamariya” amapezeka koyamba m’Baibulo pambuyo poti ufumu wa ma fuko 10 wa Samariya wagonjetsedwa mu 740 B.C.E. Ndipo ankatanthauza anthu amene ankakhala kumpoto kwa ufumuwo usanagonjetsedwe omwe anali osiyana ndi anthu a m’mayiko ena amene anachita kubwera kuchokera ku ufumu wa Asuri. (2Mf 17:29) Zikuoneka kuti Asuri sanathamangitse Aisiraeli onse omwe ankakhala m’dzikolo chifukwa nkhani imene ili pa 2 Mbiri 34:6-9, (yerekezerani ndi 2Mf 23:19, 20) imafotokoza kuti pa nthawi imene Mfumu Yosiya inkalamulira, Aisiraeli ena anali adakali m’dzikolo. Patapita nthawi dzina lakuti “Asamariya” linayamba kutanthauza anthu omwe anatsala ku Samariya komanso omwe anachita kubwera ndi Asuri. Choncho n’zosakayikitsa kuti ena ankatchedwa Asamariya chifukwa chakuti ankabadwa kuchokera ku mabanja a Asamariya enieni ndi a Asamariya omwe anabwera aja. Patapita nthawi dzinali linayamba kutanthauza gulu la chipembedzo osati mtundu wa anthu kapena kumene anachokera. “Msamariya” ankatanthauza munthu amene anali m’chipembedzo chimene chinali pafupi ndi Sekemu komanso Samariya wakale ndipo chikhulupiriro chawo chinali chosiyana kwambiri ndi cha Chiyuda.—Yoh 4:9.

DECEMBER 19-25

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 18-19

“Zimene Adani Athu Amachita Pofuna Kutifooketsa”

w05 8/1 11 ¶5

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Wachiwiri

18:19-21, 25—Kodi Hezekiya anachita pangano ndi dziko la Igupto? Ayi. Apa kazembeyu ananena zabodza, ndipo ananamanso ponena kuti ‘anakwerera malowo ndi Yehova,’ kapena kuti Yehova ndiye anamuuza kuti apite ku Yerusalemu. Hezekiya anali mfumu yokhulupirika ndipo ankadalira Yehova yekha basi.

w10 7/15 13 ¶3

“Usaope Ndidzakuthandiza”

Mochenjera, Rabisake anagwiritsa ntchito mawu ochititsa anthu kukayikira. Iye anafunsa kuti, kodi Yehova “sindiye amene Hezekiya wam’chotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake? . . . Yehova anati kwa ine, kwelera dziko ili ndi kuliwononga.” (2 Maf. 18:22, 25) Apa Rabisake ankatanthauza kuti Yehova sangamenyere nkhondo anthu ake chifukwa chakuti sakusangalala nawo. Koma izi sizinali zoona. Yehova ankasangalala kwambiri ndi Hezekiya ndiponso Ayuda amene anayambiranso kulambira koona.—2 Maf. 18:3-7.

w13 11/15 19 ¶14

Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?

14 Mfumu ya Asuri inamanga misasa ku Lakisi kum’mwera chakumadzulo kwa Yerusalemu. Ndiyeno inatumiza nthumwi zitatu kukauza anthu kuti angololera kuti agonja. Amene ankalankhula anali ndi dzina laudindo lakuti Rabisake ndipo anayesa kuopseza Ayuda m’njira zosiyanasiyana. Iye analankhula mu Chiheberi ndipo analimbikitsa anthu kuti asiye kutsatira mfumu yawo n’kugonjera Asuri. Anawanamiza kuti adzapita nawo kudziko lina kumene akasangalala kwambiri. (Werengani 2 Mafumu 18:31, 32.) Kenako Rabisake ananena kuti Yehova sadzatha kupulumutsa Ayuda kwa Asuri chifukwa milungu ina inalephera kuteteza anthu awo. Ayudawo anachita mwanzeru ndipo sanayankhe mabodzawo. Izi ndi zimene atumiki a Yehova masiku ano amachitanso nthawi zambiri.—Werengani 2 Mafumu 18:35, 36.

yb74 177 ¶1

Mbali Yachiwiri—Germany

N’zochititsa chidwi kuti nthawi zambiri asilikali ankachita zinthu mwa ukathyali pofuna kuchititsa wina kuti asaine chikalata chonena kuti wasiya kukhala wa Mboni. Akasainadi, nthawi zambiri ankamuchitira nkhanza kwambiri kuposa poyamba. Karl Kirscht anavomereza zimenezi ndipo anati: “A Mboni za Yehova ndi amene ankapusitsidwa kwambiri kundende zozunzirako anthu. Ankaona kuti imeneyi inali njira yabwino imene ingachititse a Mboniwo kusaina chikalatacho. Tinkauzidwa kuchita zimenezi mobwerezabwereza. Ena ankasainadi, koma nthawi zambiri ankafunika kudikira kwa nthawi yoposa chaka kuti atulutsidwe. Pa nthawi imene ankadikirayi iwo ankanyozedwa kwambiri ndi asilikaliwo pamaso pa anthu onse ndipo ankawanena kuti anali anthu achinyengo komanso amantha ndipo ankawauza kuti aziyenda pamaso pa abale ndi alongo awo asanatuluke.”

Mfundo Zothandiza

it-1 155 ¶4

Zinthu Zakale

Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Mfumu Senakeribu ya Asuri inaphedwa ndi ana ake awiri Adarameleki ndi Sarezere, kenako Esari-hadoni mwana wake wina anayamba kulamulira m’malo mwake. (2Mf 19:36, 37) Pomwe mbiri ya Babulo imanena kuti pa 20 m’mwezi wa Tebeti, Senakeribu anaukiridwa ndi mwana wake n’kuphedwa. Wansembe wa ku Babulo dzina lake Berossus, yemwe anakhalako zaka za m’ma 200 B.C.E., komanso Nabonidasi mfumu ya Babulo yemwe analamulira zaka za m’ma 500 B.C.E., onse ananena zofanana kuti Senakeribu anaphedwa ndi mwana wake mmodzi. Komabe pachidutswa chomwe chapezeka posachedwapa cha Esari-hadoni, mwana wa Senakeribu yemwe analowa ufumu m’malo mwake, analembapo momveka bwino kuti azichimwene ake (ambiri) anaukira n’kupha bambo awo kenako anathawa. Philip Biberfeld anapereka ndemanga pa nkhaniyi ndipo ananena kuti: “Mbiri ya Babulo, Nabonidasi komanso Berossus onse ankalakwitsa, Baibulo lokha ndi limene limanena zoona. Ngakhale zinthu zing’onozing’ono zimene Baibulo linafotokoza zinatsimikiziridwa ndi zimene Esari-hadoni analemba ndipo ndi zolondola pa nkhaniyi yonena za Ababulo ndi Asuri kuposa zimene Ababulo eni akewo anafotokoza. N’chifukwa chake tiyenera kufufuza mosamala kwambiri tisanakhulupirire ngakhale maumboni awiri ofanana omwe tapeza koma sakugwirizana ndi zimene Baibulo limafotokoza.”—Universal Jewish History 1948, Vol. I, tsa. 27.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w20.11 15 ¶14

Limbani Mtima Chifukwa Yehova Akuthandizani

Kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani? Tingathe kupempherera ‘mafumu ndi anthu onse apamwamba,’ pamene akusankha zinthu zimene zingakhudze kulambira kwathu. (1 Tim. 2:1, 2; Neh. 1:11) Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi, ifenso timapempherera mosalekeza abale ndi alongo athu amene ali m’ndende. (Werengani Machitidwe 12:5; Aheb. 13:3) Kuwonjezera apo tingapemphererenso asilikali a kundende amene akuyang’anira abale ndi alongo anthu. Tingapemphe Yehova kuti achititse anthu amenewa kukhala ndi maganizo ofanana ndi Yuliyo kuti ‘azikomera mtima’ abale ndi alongo athu amene ali m’ndende.—Mac. 27:3.

DECEMBER 26–JANUARY 1

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 20-21

“Pemphero Linachititsa Yehova Kuchitapo Kanthu”

ip-1 394 ¶23

Chikhulupiriro cha Mfumu Chifupidwa

Panthawi imene Sanakeribu akudzaukira Yuda kwa nthawi yoyamba, Hezekiya akudwala matenda akayakaya. Yesaya akumuuza kuti adzamwalira. (Yesaya 38:1) Mfumuyo ya zaka 39 ikusautsika mtima kwambiri. Siikudera nkhawa moyo wake wokha komanso tsogolo la anthu ake. Yerusalemu ndi Yuda ali pachiopsezo cha kugonjetsedwa ndi Asuri. Ngati Hezekiya amwalira, ati atsogolere nkhondoyo ndani? Panthawiyi, Hezekiya alibe mwana wamwamuna woti n’kupitiriza ulamulirowo. M’pemphero la mtima wonse, Hezekiya akuchonderera Yehova kuti am’chitire chifundo.—Yesaya 38:2, 3.

w17.03 21 ¶16

Tizitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

Kenako Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa. Iye anachonderera Yehova kuti akumbukire zoti anali munthu wokhulupirika. (Werengani 2 Mafumu 20:1-3.) Tikudziwa kuti panopa sitingayembekezere Yehova kutichiritsa mozizwitsa kapena kutalikitsa moyo wathu. Komabe mofanana ndi Hezekiya tingathe kupemphera kwa Yehova kuti: “Kumbukirani kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wathunthu.” Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Yehova angathe kukuthandizani pamene mukudwala?—Sal. 41:3.

g01 8/8 23 ¶4

Kodi Pemphero Lingandithandize Bwanji?

M’nthawi za m’Baibulo amuna ena achikhulupiriro anayankhidwa mapemphero awo mwachindunji, ngakhalenso mozizwitsa. Mwachitsanzo mfumu Hezekiya atadwala kwambiri, anapemphera kwa Mulungu kuti am’chiritse. Mulungu anam’yankha kuti: “Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa.” (2 Mafumu 20:1-6) Amuna ndi akazi ena owopa Mulungu nawonso anathandizidwa ndi Mulungu.—1 Samueli 1:1-20; Danieli 10:2-12; Machitidwe 4:24-31; 10:1-7.

Mfundo Zothandiza

it-2 240 ¶1

Thabwa Lowongolera

Thabwa lowongolera limagwiritsidwa ntchito pomanga nyumba kuti iwongoke bwinobwino komanso kuti ikhale yolimba. Yehova ananeneratu za mzinda wa Yerusalemu womwe unali wosamvera kuti, ndidzauyeza “ndi chingwe chimene ndinayezera Samariya, ndiponso ndidzamuyeza ndi thabwa lowongolera limene ndinayezera nyumba ya Ahabu.” Yehova anayeza ndipo anapeza kuti mzinda wa Samariya komanso nyumba ya Mfumu Ahabu zinali zoipa ndipo anaziwononga. Mofananamo, Mulungu anali kudzaweruza Yerusalemu ndi olamulira ake, kuula zoipa zimene ankachita komanso kuwononga mzindawo. Zimenezi zinachitika mu 607 B.C.E. (2Mf 21:10-13; 10:11) Kudzera mwa Yesaya anthu oipa omwe anali onyada komanso atsogoleri a anthu a ku Yerusalemu, anauzidwa za chiweruzo chawo chimene chinali kubwera komanso zimene Yehova ananena zakuti: “Chilungamo ndidzachisandutsa chingwe choyezera ndipo ndidzachisandutsanso chipangizo chowongolera.” Mfundo za chilungamo komanso za choonadi ndi zimene zikanasonyeza amene anali atumiki enieni a Mulungu komanso amene ankayenera kupulumutsidwa kapena kuwonongedwa.—Yes 28:14-19.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena