Khalanibe ‘Oyera Mtima’ Masiku Ovuta Ano
MTOLANKHANI wina wa Katolika dzina lake Vittorio Messori ananena mu nyuzipepala ina kuti: “Palibe amene angatsutse mfundo yakuti anthu ambiri m’matchalitchi si oyera mtima.” Iye ananena zimenezi akhristu ambiri a ku Italy atapezeka ndi milandu ya chiwerewere. Iye ananenanso kuti, “vuto limeneli silingathetsedwe mwa kungolola kuti ansembe azikwatira chifukwa yambiri mwa milanduyi imakhala ya kugonana kwa amuna okhaokha ndiponso kugwirira ana.”—La Stampa.
Mosakayikira zinthu zoipa zimene zafala m’dzikoli, ndi umboni wakuti tili ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo lino la zinthu. (2 Tim. 3:1-5) Malipoti akusonyeza kuti amene amachita makhalidwe oipawa si anthu wamba okha, koma ngakhalenso anthu amene amanena kuti amatumikira Mulungu. Iwo amachita makhalidwe oipawa chifukwa cha mitima yawo yoipa ndi yodetsedwa. (Aef. 2:2) N’chifukwa chake Yesu ananena kuti zinthu monga “maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za umbala, maumboni onama, zonyoza Mulungu zimachokera mu mtima.” (Mat. 15:19) Koma Yehova Mulungu amafuna kuti atumiki ake azikhala ‘oyera mtima.’ (Miy. 22:11) Ndiyeno kodi Mkhristu angatani kuti akhalebe woyera masiku ovuta ano?
Kodi Kukhala ‘Woyera Mtima’ Kumatanthauza Chiyani?
M’Baibulo mawu akuti “mtima” kawirikawiri amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa. Buku lina linanena kuti, m’Baibulo, mawu akuti mtima amanena za “munthu wamkati” ndipo “mbaliyi ndi imene Mulungu amaona kuti ndi yofunika kwambiri. Ubwenzi wa munthu ndi Mulungu, umadalira pa mbali imeneyi ndipo ndi mbali imene imachititsa munthu kukhala ndi khalidwe labwino kapena loipa.” Mtima umaimira umunthu wathu wamkati. Malinga ndi mawu a pamwambawa, Yehova amayang’ana mtima wa munthu. Iye amasangalala akaona kuti atumiki ake ali ndi mtima wabwino.—1 Pet. 3:4.
M’Baibulo mawu akuti “kuyera” amatanthauza ukhondo. Koma mawu omwewa amanenanso za kusadetsedwa ndi makhalidwe oipa kapena chipembedzo chonyenga. Pa Ulaliki wa pa phiri, Yesu ananena kuti: “Osangalala ali iwo amene ali oyera mtima.” Ponena zimenezi Yesu ankatanthauza anthu amene umunthu wawo wamkati ndi woyera. (Mat. 5:8) Zinthu zimene amakonda ndiponso kulakalaka zimakhala zoyera. Iwo amakhalanso ndi zolinga zabwino. Chifukwa chokonda Yehova ndiponso kuyamikira, iwo amasonyeza chikondi chawo pa iye ndi mtima wawo wonse, wopanda chinyengo. (Luka 10:27) Kodi inuyo mumafuna kukhala munthu woyera chonchi?
Kukhala ‘Oyera Mtima’ N’kovuta
Mtumiki wa Yehova ayenera kukhala “woyera m’manja” ndiponso “woona m’mtima.” (Sal. 24:3, 4) Koma masiku ano, ndi zovuta kwambiri kuti mtumiki wa Mulungu akhalebe ‘woona mtima.’ Satana, dziko limene lili m’manja mwakeli, ndiponso kupanda ungwiro kwathu, zingatichititse kuti titalikirane ndi Yehova. Kuti zonsezi zisatisokoneze, tifunika kukhala ‘oyera mtima’ ndiponso kuyesetsa kuti tikhalebe otero. Kuchita zimenezi kudzatiteteza ndiponso kudzathandiza kuti tikhalebe mabwenzi a Mulungu. Koma kodi tingatani kuti tikhalebe oyera mtima?
Pa Aheberi 3:12 pali chenjezo lakuti: “Samalani abale, kuti mwa inu, wina asakhale ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro pokanganuka kwa Mulungu wa moyo.” N’zosatheka kukhalabe ‘oyera mtima’ ngati tili ndi mtima “wopanda chikhulupiriro.” Kodi ndi mfundo ziti zimene Satana Mdyerekezi wafalitsa, zomwe zingatichititse kusakhulupirira Mulungu? Mfundo zake ndi monga yakuti zamoyo zinachita kusanduka, komanso yakuti anthu azingoyendera makonda pankhani ya makhalidwe abwino ndiponso chipembedzo. Mfundo ina ndi yakuti amachititsanso anthu kukayikira zoti Malemba Oyera anauziridwa ndi Mulungu. Tiyenera kusamala kuti mfundo zoipazi zisatisocheretse. (Akol. 2:8) Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse ndiponso kusinkhasinkha kungatiteteze ku zinthu zoterezi. Kudziwa molondola Mawu a Mulungu kungatithandize kuti tizikonda kwambiri Yehova ndiponso kuti tiziyamikira zochita zake. Chikondi choterechi ndiponso kuyamikira zingatithandize kuti tikane maganizo olakwikawa ndiponso kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova. Kuchita zimenezi kungachititse kuti tikhalebe oyera mtima.—1 Tim. 1:3-5.
Khalanibe Oyera Mtima Polimbana ndi Zilakolako za Thupi
Zinthu zina zimene zingatilepheretse kukhalabe ‘oyera mtima’ ndi zilakolako za thupi ndiponso kulakalaka chuma. (1 Yoh. 2:15, 16) Kukondetsa ndalama ndiponso kufunitsitsa kukhala ndi chuma, zingawononge mtima wa munthu ndipo zingapangitse Mkhristu kuchita zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna. Anthu ena amachita zinthu mosaona mtima kuntchito, amanama, ndiponso amaba ndalama kapena zinthu zina.—1 Tim. 6:9, 10.
Koma tikamaopa kukhumudwitsa Yehova, tikamakonda chilungamo ndiponso tikamayesetsa kukhala ndi chikumbumtima choyera, timasonyeza kuti timafuna kukhala ‘oyera mtima.’ Zimenezi zimatithandiza ‘kuchitabe zinthu zonse moona mtima.’ (Aheb. 13:18) Tikamachita zinthu moona mtima tingapeze mwayi wolalikira anthu ena. M’bale wina wa ku Italy dzina lake Emilio anali dalaivala wa basi pa kampani ina, ndipo tsiku lina anapeza chikwama muli ndalama zokwana madola 680 a ku United States. Iye anakapereka chikwamacho kwa bwana wake ndipo zimenezi zinadabwitsa anzake akuntchito. Bwanayo anapereka chikwamacho kwa mwini wake. Anzake ena anadabwa kwambiri ndi zimene Emilio anachitazi moti anachita chidwi ndi mfundo za m’Baibulo n’kuyamba kuphunzira. Zotsatira zake zinali zakuti anthu 7 ochokera m’mabanja awiri anaphunzira choonadi. Zoonadi, kukhala woona mtima chifukwa chakuti ndife oyera mtima kungachititse ena kutamanda Mulungu.—Tito 2:10.
Chinthu china chimene chingalepheretse Mkhristu kukhala woyera mtima, ndicho kukhala ndi maganizo olakwika pa nkhani ya kugonana. Anthu ambiri amaona kuti palibe vuto ndi zinthu monga kugonana asanalowe m’banja, kugonana ndi munthu amene si mkazi kapena mwamuna wawo ndiponso kugonana ndi mkazi kapena mwamuna mnzawo. Zimenezi zingawononge mtima wa Mkhristu. Munthu wachiwerewere amakhala moyo wachiphamaso chifukwa amabisa tchimo lake. Zimenezi zimasonyeza kuti munthuyu si ‘woyera mtima.’
Mnyamata wina dzina lake Gabriele, anabatizidwa ali ndi zaka 15 ndipo anayamba upainiya. Koma kenako anayamba kucheza m’mabala ndi anthu osalongosoka. (Sal. 26:4) Zimenezi zinachititsa kuti ayambe moyo wachiwerewere ndiponso wachinyengo moti anachotsedwa mumpingo. Chilango chochokera kwa Yehova chimene analandirachi chinachititsa kuti aganize mofatsa za moyo wake. Gabriele anati: “Ndinayamba kuchita zinthu zonse zimene poyamba ndinkazinyalanyaza. Ndinayamba kuwerenga Baibulo tsiku lililonse n’kumaona zimene Yehova akunena ndipo ndinkaphunzira mosamala mabuku ofotokoza Baibulo. Ndinayamba kuona kuti kuphunzira Baibulo pandekha n’kothandiza ndiponso n’kosasangalatsa kwambiri. Ndinayambanso kupeza mphamvu chifukwa cha kuwerenga Baibulo ndiponso kupemphera kuchokera pansi pa mtima.” Zimenezi zinamuthandiza Gabriele kusiya khalidwe lake lachiwerewere n’kukhalanso paubwenzi ndi Yehova.
Panopa Gabriele anayambiranso kuchita upainiya limodzi ndi mkazi wake. Zimene zinamuchitikirazi, zikusonyeza kuti kuphunzira Baibulo ndiponso mabuku ofalitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kungathandize munthu kukhala woyera mtima ndiponso kupewa chiwerewere.—Mat. 24:45; Sal. 143:10.
Kukhala ‘Woyera Mtima’ Poyesedwa
Atumiki a Mulungu ena amavutika chifukwa cha kutsutsidwa, mavuto a zachuma ndiponso matenda akulu. Nthawi zina, zimenezi zimachititsa kuti azivutika mu mtima mwawo. Izi n’zimene zinachitikiranso Mfumu Davide. Iye anati: “Mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m’kati mwanga.” (Sal. 143:4) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira pa nthawi yovuta imeneyi? Davide anakumbukira zimene Mulungu anachitira atumiki Ake ndiponso mmene anamupulumutsira iyeyo. Anaganizira zimene Yehova anali atachita chifukwa cha dzina Lake lalikulu. Davide ankaganizira kwambiri ntchito za Mulungu. (Sal. 143:5) Ifenso, tikamaganizira za Mlengi wathu, zimene anatichitira ndiponso zimene akutichitira, tidzatha kupirira tikamayesedwa.
Munthu wina akatilakwira kapena ifeyo tikamaganiza kuti watilakwira, tingakwiye kwambiri. Kumangoganizirabe nkhaniyo kungachititse kuti tiyambe kudana ndi abale athu. Tingasiye kucheza ndi anthu, kumangokhala tokhatokha ndiponso osasonyeza chidwi kwenikweni kwa anthu ena. Komatu kuchita zimenezi sikungatithandize kukwaniritsa cholinga chathu chokhala ‘oyera mtima.’ Choncho kuti tikhale oyera mtima tiyenera kukhala bwino ndi Akhristu anzathu.
M’dziko limene likuipiraipirabeli, Akhristu oonafe timakhala osiyana ndi anthu ena chifukwa chakuti timakhala ‘oyera mtima.’ Timakhala osangalala chifukwa chakuti kuchita chifuniro cha Mulungu kumatipatsa mtendere wa mumtima. Koposa zonse, timakhala paubwenzi ndi Mlengi wathu Yehova Mulungu amene amakonda anthu ‘oyera mtima.’ (Sal. 73:1) Yesu analonjeza kuti anthu ‘oyera mtima’ amakhala osangalala chifukwa “adzaona Mulungu” ndipo izi zimachitika Yehova akamawathandiza. Ifenso tingakhale m’gulu la anthu oterewa.—Mat. 5:8.