Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MARCH 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 3
Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Yehova
ijwbv nkhani na. 14 ¶4-5
Miyambo 3:5, 6—“Usamadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
“Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” Timasonyeza kuti timadalira Mulungu tikamachita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake. Timafunika kumakhulupirira Mulungu ndi mtima wathu wonse. Nthawi zambiri Baibulo likamanena za mtima, limanena zokhudza mmene munthuwe ulili mumtima mwako, zomwe zikuphatikizapo mmene umamvera, zolinga zako, maganizo ako komanso mmene umaonera zinthu. Choncho, kukhulupirira Mulungu ndi mtima wathu wonse kumaphatikizapo zinthu zambiri osangoti mmene timamvera. Ndi zimene timasankha chifukwa chokhulupirira kwambiri kuti Mlengi wathu amadziwa zinthu zomwe ndi zothandiza kwambiri kwa ife.—Aroma 12:1.
“Usamadalire luso lako lomvetsa zinthu.” Popeza si ife angwiro, timafunika kudalira Mulungu osati luso lathu la kuganiza. Tikamadzidalira kapena kumangochita zinthu chifukwa cha mmene tikumvera, tikhoza kusankha zinthu zomwe poyamba zingaoneke zabwino koma zotsatira zake zingakhale zoipa. (Miyambo 14:12; Yeremiya 17:9) Nzeru za Mulungu ndi zapamwamba kwambiri kuposa zathu. (Yesaya 55:8, 9) Tikamatsogoleredwa ndi maganizo ake, zinthu zimatiyendera bwino.—Salimo 1:1-3; Miyambo 2:6-9; 16:20.
ijwbv nkhani na 14 ¶6-7
Miyambo 3:5, 6—“Usamadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
“Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse.” Timafunika kuyendera maganizo a Mulungu pa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu komanso tikamasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Timachita zimenezi tikamapemphera kwa iye kuti azititsogolera ndiponso tikamatsatira zimene amatiuza m’Mawu ake, Baibulo.—Salimo 25:4; 2 Timoteyo 3:16, 17.
“Iye adzawongola njira zako.” Mulungu amawongola njira zathu potithandiza kuti tizitsatira mfundo zake zolungama pa moyo wathu. (Miyambo 11:5) Zimenezi zimatithandiza kuti tisamakumane ndi mavuto opeweka ndipo timakhala moyo wosangalala kwambiri.—Salimo 19:7, 8; Yesaya 48:17, 18.
Khalani Womapitabe Patsogolo
Munthu akaona zambiri m’moyo, angalingalire kuti: ‘Zimenezi sizachilendo kwa ine. Ndikudziwa zochita.’ Kodi imeneyi ingakhale nzeru? Miyambo 3:7 imachenjeza kuti: “Usadziyese wekha wanzeru.” Inde, kudziwa zambiri kuyeneradi kutithandiza kuona mbali zosiyanasiyana pochita ndi mikhalidwe ina m’moyo. Koma ngati tikupita patsogolo mwauzimu, kudziwa kwathu zambiri kuyenera kuthandizanso maganizo athu ndi mitima yathu kudziwa kuti tifunikira thandizo la Yehova kuti tipambane. Choncho, taona kuti kupita kwathu patsogolo kumaonekera osati mwa kudzidalira tokha pochita ndi mikhalidwe, koma mwa kutembenukira kwa Yehova mwachangu kuti atitsogolere m’miyoyo yathu. Kumaonekera mwa kukhala ndi chidaliro chakuti palibe chingatheke popanda chilolezo chake. Kumaonekeranso mwa kusunga unansi wathu wokhulupirira Atate wathu wakumwamba ndi kumukonda.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
3:3. Tiyenera kuona kuti kukhala wokoma mtima mwachikondi ndi wachoonadi ndi makhalidwe amtengo wapatali, ndipo tiyenera kuwasonyeza ngati mmene tingachitire ndi mkanda wa pakhosi womwe uli wokwera mtengo. Tikufunikiranso kukhomereza makhalidwe amenewa pamtima pathu, kuwachititsa kukhala mbali yaikulu ya moyo wathu.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Muzidalira Yehova Pamene Mapeto Akuyandikira
7 Abale athu ambiri amatumikira m’madera amene amafunika kupirira kwambiri. Mneneri Yeremiya anatumikiranso m’dera lotereli. Iye ankalalikira mu ufumu wa Yuda utatsala pang’ono kuwonongedwa ndipo iyi inali nthawi yovuta kwambiri. Tsiku lililonse chikhulupiriro cha Yeremiya chinkayesedwa chifukwa chomvera Mulungu pogwira ntchito yolalikira uthenga wa chiweruzo Chake. Pa nthawi ina ngakhale Baruki, yemwe anali mlembi wake wokhulupirika, anadandaula chifukwa chotopa. (Yer. 45:2, 3) Kodi Yeremiya anagwa ulesi chifukwa cha zimenezi? Pa nthawi zina iye ankavutika kwambiri maganizo mpaka anafika ponena kuti: “Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!” Ananenanso kuti: “N’chifukwa chiyani ndinabadwa? Kodi ndinabadwa kuti ndidzagwire ntchito yakalavulagaga ndi kukhala wachisoni, ndi kuti moyo wanga ufike kumapeto kwake ndili wamanyazi?”—Yer. 20:14, 15, 18.
8 Koma Yeremiya sanasiye ntchito yake. Iye anapitiriza kudalira Yehova. Zotsatira zake zinali zakuti mneneriyu anaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yehova olembedwa pa Yeremiya 17:7, 8 akuti: “Wodala ndi munthu aliyense amene amakhulupirira Yehova, amene amadalira Yehova. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi. Kutentha kukadzafika iye sadzadziwa, koma masamba ake adzachuluka ndi kukhala obiriwira. Pa nthawi ya chilala sadzada nkhawa kapena kusiya kubala zipatso.”
9 Mofanana ndi mtengo wa zipatso wobiriwira “wobzalidwa m’mphepete mwa madzi” kapena m’munda wa zipatso wothiriridwa bwino, Yeremiya ‘sanasiye kubala zipatso.’ Iye sanalole kufooketsedwa ndi anthu oipa amene ankamunyoza. M’malomwake, iye nthawi zonse ankadalira Kasupe wa “madzi” opatsa moyo ndipo ankatsatira zonse zimene Yehova anamuuza. (Werengani Salimo 1:1-3; Yer. 20:9) Apatu Yeremiya anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri makamaka ngati tikutumikira Mulungu m’madera ovuta. Ngati mukutumikira m’dera lovuta, pitirizani kudalira kwambiri Yehova amene angakuthandizeni kupirira “polengeza dzina lake kwa anthu ena.”—Aheb. 13:15.
10 Yehova watipatsa paradaiso wauzimu wokhala ndi zinthu zambiri pofuna kutithandiza kuti tipirire mavuto a pa moyo wathu masiku otsiriza ano. Zina mwa zinthu zimene watipatsa ndi Baibulo lonse, lomwe ndi Mawu ake, ndipo likumasuliridwa molondola m’zinenero zambirimbiri. Iye wapereka chakudya chauzimu chambiri ndiponso pa nthawi yake kudzera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Iye watipatsanso abale ndi alongo amene amatilimbikitsa tikamacheza nawo pa misonkhano yampingo ndi ikuluikulu. Kodi mumagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimene watipatsazi? Anthu onse amene amagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimenezi “adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.” Koma amene samvera Mulungu ‘adzalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo adzafuula chifukwa chosweka mtima.’—Yes. 65:13, 14.
MARCH 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 4
“Muziteteza Mtima Wanu”
Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?
4 Pa Miyambo 4:23, mawu akuti “mtima” akutanthauza “munthu wamkati” kapena kuti “munthu wobisika.” (Werengani Salimo 51:6.) Choncho tinganene kuti mawu akuti “mtima” amanena za maganizo athu, mmene tikumvera mumtima, zolinga zathu komanso zimene timalakalaka. Tingati ndi mmene tilili mkati mwathu osati mmene timaonekera kwa anthu ena.
Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?
10 Kuti titeteze mtima wathu tiyenera kuzindikira zinthu zimene zingatisokoneze n’kumazipewa mwamsanga. Mawu amene anamasuliridwa kuti ‘kuteteza’ pa Miyambo 4:23 amatikumbutsa za ntchito imene mlonda amagwira. Pa nthawi ya Mfumu Solomo, alonda ankaima pampanda wa mzinda n’kumachenjeza anthu akaona zoopsa. Mfundo imeneyi imatithandiza kudziwa zimene tiyenera kuchita kuti Satana asasokoneze maganizo athu.
11 Kale, alonda apampanda ankagwira ntchito mogwirizana ndi alonda apachipata. (2 Sam. 18:24-26) Iwo ankathandizana poteteza mzinda ndipo ankaonetsetsa kuti mageti atsekedwa pamene adani akubwera. (Neh. 7:1-3) Chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo chimakhala ngati mlonda ndipo chimatichenjeza pamene Satana akufuna kuwononga mtima wathu kapena kuti pamene akuyesetsa kusokoneza maganizo athu, zolinga zathu kapena zimene timalakalaka. Chikumbumtima chathu chikatichenjeza tiyenera kumvera n’kuchita zinthu mwamsanga ngati mlonda amene watseka geti.
Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?
14 Kuti titeteze mtima wathu tiyeneranso kuutsegula kuti mulowe zinthu zabwino. Chitsanzo cha mzinda chija chingatithandizenso pa nkhaniyi. Mlonda ankatseka geti ngati kukubwera adani koma nthawi zina ankatsegula kuti anthu alowetse chakudya ndi zinthu zina zofunika. Mageti akanati azikhala otseka nthawi zonse ndiye kuti anthu amumzindawo akanafa ndi njala. Nafenso tiyenera kutsegula mtima wathu kuti muzilowa maganizo a Yehova.
‘Tetezani Mtima Wanu’
N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza mtima wathu wophiphiritsira? Mulungu anauzira Mfumu Solomo kulemba kuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miyambo 4:23) Kuti tikhale ndi moyo wabwino panopo komanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo zimadalira mmene mtima wathu wophiphiritsira ulili. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Mulungu amaona zimene zili mumtima mwathu. (1 Samueli 16:7) Mulungu akafuna kudziwa kuti ndife munthu wotani amayang’ana “munthu wobisika wamumtima” kapena kuti zimene zili mumtima mwathu.—1 Petulo 3:4.
Mfundo Zothandiza
Kodi Mudzayembekezera Yehova Moleza Mtima?
4 Lemba la Miyambo 4:18 limatiuza kuti: “Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” Mawuwa akutithandiza kumvetsa kuti Yehova amaulula cholinga chake kwa atumiki ake pang’onopang’ono. Koma mawu a palembali akutithandizanso kumvetsa mmene Mkhristu amasinthira zinthu pa moyo wake n’cholinga choti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Komabe pangatenge nthawi kuti Mkhristu akhale wolimba mwauzimu. Koma ngati timachita khama kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito malangizo amene timapeza m’Mawu a Mulungu komanso m’gulu lake, pang’ono ndi pang’ono tidzayamba kukhala ndi makhalidwe ofanana ndi a Khristu ndipo tingamudziwe bwino Mulungu. Tiyeni tione fanizo limene Yesu anapereka pankhaniyi.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwfq nkhani na. 19
N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Isitala?
● Chikondwerero cha pa Isitala n’chosagwirizana ndi Baibulo.
● Yesu anatilamula kuti tizikumbukira imfa yake, osati kuukitsidwa kwake. Timakumbukira imfa imeneyi chaka chilichonse pa tsiku limene Yesuyo anaphedwa, mogwirizana ndi kalendala yotchulidwa m’Baibulo.—Luka 22:19, 20.
● Timakhulupirira kuti Mulungu sasangalala ndi miyambo ya pa Isitala chifukwa inachokera kumiyambo yakale yokhudzana ndi kulambira milungu imene anthu ankakhulupirira kuti ili ndi mphamvu zobereketsa. Mulungu amafuna kuti anthu ‘azidzipereka kwa iye yekha,’ ndipo amakhumudwa anthu akamachita miyambo imene iye sasangalala nayo.—Ekisodo 20:5; 1 Mafumu 18:21.
Timakhulupirira kuti zimene tinasankha zoti tisamakondwerere nawo Isitala n’zogwirizana kwambiri ndi Baibulo, lomwe limatilimbikitsa kuti tizigwiritsa ntchito “nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino” m’malo mongotsatira miyambo ya anthu. (Miyambo 3:21; Mateyu 15:3) Anthu ena akatifunsa zimene timakhulupirira pa nkhani ya Isitala, timawauza. Komabe, timalemekeza zimene munthu aliyense wasankha kuti azikhulupirira pa nkhaniyi.—1 Petulo 3:15.
MARCH 17-23
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 5
Muzitalikirana Kwambiri ndi Chiwerewere
Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli
Mwambiwu, ukusonyeza kuti munthu wamakhalidwe oipa ndi “mkazi wachiwerewere.” Mawu amene amakopa nawo anthu amene amagona nawo ndi otsekemera ngati chisa cha uchi ndi osalala kuposa mafuta a maolivi. Kodi kukopana kuti muchite chiwerewere nthawi zambiri sikuyamba chonchi? Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira mtsikana wina wokongola wa zaka 27 dzina lake Amy yemwe ankagwira ntchito ya usekilitale. Iye anati: “Mwamuna ameneyu kuntchito kwathu amachita zinthu zambiri zosonyeza kuti amandifuna ndipo amanditamanda nthawi iliyonse. N’zosangalatsa kuti ena amakuganizira. Koma ndikutha kuona bwino kuti akusangalala nane chifukwa choti akufuna adzagone nane. Sindingatengeke ndi zochita zakezo.” Mawu okopa a mwamuna kapena mkazi kawirikawiri amakhala abwino pokhapokha ngati tazindikira pamenedi akuchokera. Pa chifukwachi tikufunika kugwiritsa ntchito luso lathu la kulingalira.
Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli
Zotsatira za chiwerewere n’zowawa kwambiri ngati chitsamba chowawa komanso n’zakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse ndipo n’zopweteka komanso zakupha. Nthawi zambiri zotsatirapo za khalidwe limeneli zimakhala kuvutika ndi chikumbumtima, kutenga mimba yosaifuna, kapena matenda opatsirana pogonana. Ndipo taganizirani mmene mwamuna kapena mkazi wa munthu amene wachita zosakhulupirikayo amavutikira maganizo. Kusakhulupirika ngakhale kamodzi kokha kungabweretse mabala aakulu mumtima omwe akhoza kukhala kwa moyo wonse. Inde, chiwerewere chimavulaza.
Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli
Tifunika kuchita zonse zomwe tingathe kuti tipewe anthu amene angatilimbikitse kuchita chiwerewere. N’chifukwa chiyani sitiyenera kumvetsera nyimbo zotukwana, kuonerera zosangalatsa zoipa, kapena kumaonera zolaula? (Miyambo 6:27; 1 Akorinto 15:33; Aefeso 5:3-5) Ndipotu n’kupusa kwambiri kukopana nawo kapena kuvala ndi kudzikongoletsa mosayenera—1 Timoteyo 4:8; 1 Petulo 3:3, 4.
Mfundo Zothandiza
Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli
Motero Solomo akunenetsa mavuto aakulu ogwera m’chiwerewere. Chigololo ndi kutaya ulemu, kapena kudzilemekeza, zimayendera pamodzi. Kodi si zochititsadi manyazi kuti munthu ungokhala chabe wokhutiritsa chilakolako chako choipa cha kugonana kapena cha munthu wina? Kodi sizisonyeza kusadzilemekeza kugonana ndi munthu wina amene sitinakwatirane naye?
MARCH 24-30
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 6
Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Nyerere?
it-1 115 ¶1-2
Nyerere
‘Nzeru Zachilengedwe.’ Nyerere zimachita zinthu ‘mwanzeru,’ osati chifukwa choti zimaganiza kwambiri, koma chifukwa cha mmene Mlengi anazilengera. Baibulo limanena za nyerere kuti “imakonza chakudya chake m’chilimwe, ndipo imasonkhanitsa chakudya chake pa nthawi yokolola.” (Miy 6:8) Mtundu wina wa nyerere zodziwika bwino zomwe zimapezeka ku Palesitina (Messor semirufus), zimasunga chakudya chochuluka m’nyengo yokolola komanso yotentha ndipo zimagwiritsa ntchito chakudyachi m’nyengo imene chimasowa, kuphatikizapo nyengo yozizira. Nthawi zambiri nyerere zimenezi zimapezeka m’malo opunthira mbewu omwe pamakhala mbewu zambiri. Ngati mvula yachititsa kuti mbewuzi zinyowe, nyererezi zimazitutira panja kukaziyanika padzuwa kuti ziume. Zimadziwikanso kuti zimaluma kamtima ka mbewu zimene zasunga n’cholinga choti zisamere. Pamalo pamene pamakhala nyererezi pamadziwika bwino ndi tinjira take komanso mankhusu a mbewu amapezeka pamene zimalowera.
Zimapereka Chitsanzo Chabwino. Pofotokoza mwachidule zimene nyerere zimachita, Baibulo limanena kuti: “Pita kwa nyerere waulesi iwe, ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru.” (Miy 6:6) Nyerere sikuti zimangodziwika bwino ndi kukonzekera zam’tsogolo basi, koma zimadziwikanso kuti zimagwira ntchito mwakhama. Nthawi zambiri zimanyamula zinthu zolemera kuwirikiza kawiri kulemera kwake kapena kuposa ndipo zimayesetsa mmene zingathere kuti zimalize ntchito zimene zikugwira. Sizifooka ngakhale zitagwa, kuterereka kapena kugubuduka zikamayenda malo ovuta kuyendapo. Chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti, zimachita zinthu mogwirizana poyesetsa kuti malo amene zimakhala azikhala aukhondo komanso zimachita zinthu moganizira zinzawo zimene zavulala kapena zimene zatopa ndipo nthawi zambiri zimazithandiza kuti zibwerere kudzenje.
Tetezani Dzina Lanu
Mofanana ndi nyerere, kodi nafenso sitifunikira kuchita khama? Kugwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa kuti tichite bwino pantchito yathu n’kwabwino kwa ife kaya pali wotiyang’anira kapena ayi. Inde, kusukulu, kuntchito kwathu, komanso pogwira ntchito zauzimu ndi anzathu, tiyenera kuchita bwino koposa. Monga momwe nyerere zimapindulira ndi khama lawo, momwemonso Mulungu akufuna kuti ‘tione zabwino m’ntchito zathu zonse.’ (Mlaliki 3:13, 22; 5:18) Chikumbumtima chabwino ndi chikhutiro ndizo mphoto ya kugwira ntchito molimbika.”—Mlaliki 5:12.
Pogwiritsa ntchito mafunso awiri odzutsa chidwi, Solomo akuyesa kugalamutsa waulesi kuti asachite zala lende, akumati: “Udzagona mpaka liti, waulesi iwe? Udzauka ku tulo tako liti?” Mwa kuyerekezera kulankhula kwa munthu waulesi, mfumuyo ikupitiriza kuti: “Tulo ta pang’ono, kuodzera pang’ono, kungomanga manja pang’ono, ndi kugona; ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala, ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa [“msilikali,” NW].” (Miyambo 6:9-11) Pamene waulesi akadagona, umphawi umam’fikira mofulumira ngati wakuba, ndipo kusauka kumam’kantha ngati munthu wonyamula lupanga. Minda ya munthu waulesi siichedwa kumera thengo ndi khwisa. (Miyambo 24:30, 31) Bizinesi yake imalowa pansi pa kanthawi kochepa. Kodi wolemba anthu ntchito angalekerere waulesi kwautali wotani? Ndipo kodi wophunzira amene n’ngwaulesi n’kuwerenga angayembekezere kuchita bwino kusukulu?
Mfundo Zothandiza
Tetezani Dzina Lanu
Zinthu 7 zomwe lemba la miyambo likutchula ndi zimene zili zikuluzikulu ndipo zikuphatikizapo pafupifupi mitundu yonse ya machimo. “maso odzikweza” ndi “mtima umene umakonza ziwembu” ndi machimo omwe amachitidwa m’maganizo. “Lilime lonama” ndi “mboni yachinyengo imene nthawi zonse imanena mabodza” ndi machimo amene anthu amachita akamalankhula. “Manja amene amakhetsa magazi a anthu osalakwa” ndi “mapazi othamangira kukachita zoipa” ndi machimo amene anthu amachita m’zochita zawo. Ndipo chomwe Yehova amadana nacho kwambiri ndicho mthirakuwiri yemwe amakonda kuyambanitsa anthu omwe akanatha kukhalira limodzi mwamtendere. Kuwonjezeka kwa chiwerengerocho kuchoka pa 6 kufika pa 7 kukusonyeza kuti ndandandayo sinafike kumapeto, chifukwa chakuti anthu akupitirizabe kuwonjezera zoipa zomwe amachita.
MARCH 31–APRIL 6
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 7
Muzipewa Zochitika Zimene Zingakuikeni M’mayesero
“Uzisunga Malamulo Anga Kuti Upitirize Kukhala Ndi Moyo”
Windo lomwe Solomo ankasuzumira linali lamatabwa omwe n’kutheka kuti anali osemedwa mwaluso. Pamene dzuwa linkalowa, kachisisira kanayamba ndipo mdima unayamba kuoneka mum’sewumo. Ndiyeno anaona mnyamata yemwe ankaonekeratu kuti ali pangozi. Mopanda nzeru, kapena kuti mosaganiza bwino, akuchita zimene mtima wake ukufuna. N’zodziwikiratu kuti akudziwa bwino zochitika za m’dera lomwe wapitalo komanso zomwe zingakamuchitikire kumeneko. Mnyamatayu akuyandikira “mphambano” ndipo akulowera kunyumba ya mkaziyo. Kodi mkaziyu ndi ndani? Nanga akufuna chiyani?
“Uzisunga Malamulo Anga Kuti Upitirize Kukhala Ndi Moyo”
Mkazi ameneyu ali m’pakamwa pochenjeretsa. Mkaziyu akulankhula mawu ake molimba mtima. Chilichonse chimene akunena, akuchinena mochenjera kwambiri kuti akope mnyamatayo. Ponena kuti wapereka nsembe zamgwirizano komanso kuti tsiku lomwelo wakwaniritsa zimene analonjeza, akufuna kudzionetsa ngati ndi wolungama kuti mnyamatayo amuone ngati ndi munthu wauzimu. Nsembe zamgwirizano ku kachisi wa ku Yerusalemu zinkaphatikizapo nyama, ufa, mafuta, ndi vinyo. (Levitiko 19:5, 6; 22:21; Numeri 15:8-10) Popeza kuti wopereka nsembe amatha kutenga chigawo china cha nsembe yoyamika ndi kukadya limodzi ndi banja lake, mkaziyu akufotokoza kuti kunyumba kwake kuli zakudya ndi zakumwa zochuluka. Mfundo yake ndi yodziwikiratu, iye akutanthauza kuti: Mnyamatayo akasangalala kwambiri kumeneko. Wachoka kunyumba kwakeko kudzafunafuna iyeyu basi. Komatu munthu atati akhulupirire nkhani imeneyo ingam’gwire mtima kwabasi koma angalembe m’madzi. Katswiri wina wodziwa za Baibulo anati: “N’zoona kuti anatuluka kukafunafuna winawake, koma kodi anatuluka kukafuna mnyamata wake ameneyu yekha basi? Ndi munthu wopanda nzeru yekha amene angakhulupirire mkaziyu, ndipo munthu ameneyu anali mnyamatayu.”
Atadzikometsera ndi zovala zake, timawu take tosalala, kumugwira ndi manja ake komanso kumukisa, mkazi wonyengererayu akufuna amukope pogwiritsa ntchito zonunkhira. Akuti: “Ndayala zofunda zabwino pabedi panga, nsalu za ku Iguputo zokongola kwambiri. Ndawaza pabedi panga zonunkhiritsa za mule, aloye ndi sinamoni.” (Miyambo 7:16, 17) Wayala bedi lake mwaluso ndi nsalu zake zokongola za ku Iguputo ndipo wathirapo zonunkhiritsa za mule, aloye ndi sinamoni.
Iye akupitiriza kuti: “Bwera tisonyezane chikondi mpaka m’mawa ndipo chitikwane. Tiye tisangalatsane pochita zachikondi.” Akumuitanira zinazake osati chakudya chokoma chokha cha anthu awiri. Akumulonjeza kukasangalala mwa kugonana. Kwa mnyamatayu, pempholi n’lochititsa chidwi ndi losangalatsa. Popitiriza kum’nyengerera, akunena kuti: “Chifukwa mwamuna wanga sali panyumba. Iye wachoka, wapita kutali. Wanyamula chikwama cha ndalama, ndipo adzabwera kunyumba tsiku limene mwezi udzaoneke wathunthu.” (Miyambo 7:18-20) Akumutsimikizira kuti palibe aliyense akawapezerere, chifukwa chakuti mwamuna wake wachoka wapita kukachita bizinesi ndipo akakhala kumeneko kwakanthawi ndithu asanabwerere kunyumba. N’katswiridi pokopa mnyamata ndi mawu onyengerera. “Wasocheretsa mnyamatayo pochita zinthu zambiri zomukopa. Wamunyengerera ndi mawu okopa.” (Miyambo 7:21) Ndi munthu wanzeru komanso wakhalidwe labwino ngati Yosefe yekha amene angathe kupewa mawu onyengerera ngati amenewa. (Genesis 39:9, 12) Kodi mnyamatayu angafanane ndi Yosefe?
“Uzisunga Malamulo Anga Kuti Upitirize Kukhala Ndi Moyo”
Pempholi linali losapeweka kwa mnyamata ameneyu. Mopanda nzeru, akutsatira mkaziyu “ngati ng’ombe yamphongo imene ikupita kukaphedwa.” Monga momwe mwamuna womangidwa unyolo m’miyendo sangathe kuthawa chilango, momwemonso mnyamatayo akukokedwa kuti akachite tchimo. Sakuona kuopsa kwake kufikira pamene “muvi utaboola chiwindi chake” kapena kuti mpaka pamene walandira chilonda chomwe chingathe kumupha. Angafedi chifukwa chakuti angatenge matenda akupha opatsirana pogonana. Chilondacho chingamuphenso mwauzimu; ‘zingachititse kuti ataye moyo wake.’ Umunthu wake wonse ndi moyo wake womwe, zili pangozi yaikulu ndipo wachimwira kwambiri Mulungu. Choncho akuthamangira mumsampha wa imfa ngati mbalame yothamangira mumsampha.
Mfundo Zothandiza
“Uzisunga Malamulo Anga Kuti Upitirize Kukhala Ndi Moyo”
Solomo akupitiriza kuti: “Uwamange [malamulo anga] kuzala zako, ndipo uwalembe pamtima pako.” (Miyambo 7:3) Monga zala zomwe timaziona mosavuta komanso zimatithandiza pochita zomwe tikufuna, momwemonso zimene timaphunzira m’Malemba ziyenera kumatikumbutsa nthawi zonse ndi kutitsogolera pa chilichonse chomwe timachita. Tilembe malangizowa pamtima pathu, kuwapanga kukhala mbali ya moyo wathu.
APRIL 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 8
Muzimvetsera Nzeru Yomwe Ikulankhula Ngati Munthu
“Ndimakonda Atate”
7 Mu vesi 22, nzeru ikunena kuti: “Ine ndinali woyamba kulengedwa ndi Yehova, ndinali woyambirira pa zinthu zonse zimene anapanga kalekale kwambiri.” Lembali silikungonena za nzeru zenizeni chifukwa nzeru sizinachite “kulengedwa.” Nzeru zilibe chiyambi chifukwa Yehova wakhala alipo kuyambira kalekale ndipo nthawi zonse ndi wanzeru. (Salimo 90:2) Koma Mwana wa Mulungu ali ndi chiyambi chifukwa ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” Iye anachita kupangidwa kapena kuti kulengedwa ndipo ndi woyamba pa zonse zimene Yehova analenga. (Akolose 1:15) Mwanayu analipo Mulungu asanalenge dziko lapansi komanso kumwamba ngati mmene buku la Miyambo likufotokozera. Monga Mawu, kapena kuti wolankhula m’malo mwa Mulungu, iye anasonyeza bwino kwambiri nzeru zimene Yehova ali nazo.—Yohane 1:1.
“Ndimakonda Atate”
8 Kodi Mwanayu ankachita chiyani pa nthawi yonse imene anali kumwamba asanabwere padziko lapansi? Vesi 30 likusonyeza kuti Yesu anali pambali pa Mulungu monga “mmisiri waluso.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Lemba la Akolose 1:16 limanena kuti: “Kudzera mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi . . . Analenga zinthu zina zonse kudzera mwa iye ndiponso chifukwa cha iye.” Choncho Yehova, yemwe ndi Mlengi, anagwiritsa ntchito Mwana wake, amene ndi Mmisiri Waluso, polenga zinthu zonse monga angelo kumwamba, zinthu zonse zakuthambo, dziko lapansi ndi zinthu zonse zodabwitsa monga zomera komanso nyama. Analenganso munthu, yemwe ndi wapamwamba kuposa chinthu chilichonse padziko lapansi. Mgwirizano wa Atate ndi Mwana wakeyu tingauyerekezere ndi wa katswiri wolemba mapulani a nyumba ndi mmisiri wake amene amatsatira mapulaniwo pomanga nyumba. Tikamachita chidwi ndi zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe, kwenikweni timakhala tikutamanda Yehova, Katswiri Wamkulu Wolemba Mapulani. (Salimo 19:1) Komanso tingakumbukire mgwirizano wabwino umene unalipo kwa nthawi yaitali pakati pa Mlengi ndi ‘mmisiri wake waluso’ ameneyo.
9 Anthu awiri opanda ungwiro akamagwira ntchito limodzi nthawi zina amasemphana maganizo. Koma si mmene zinalili pakati pa Yehova ndi Mwana wake. Mwanayu anagwira ntchito limodzi ndi Atate wake kwa nthawi yaitali kwambiri ndipo iye ananena kuti: “Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.” (Miyambo 8:30) Iye ankasangalala kukhala ndi Atate wake ndipo ankakondana kwambiri. Mwanayu anayamba kuchita zinthu mofanana kwambiri ndi Atate wake ndipo anatengera makhalidwe ake. Mpake kuti Atate ndi Mwanayu anayamba kukondana kwambiri. Choncho tinganene motsimikiza kuti palibe amene amakondana kwambiri kuposa Atate ndi Mwana wakeyu. Iwo anayamba kukondana kalekale.
Kuzindikira Yesu Monga Davide Wamkulu Ndiponso Solomo Wamkulu
14 Ndi munthu mmodzi yekha amene anali ndi nzeru kuposa Solomo. Munthu ameneyu anali Yesu Khristu. Iye anadzitcha kuti “wina woposa Solomo.” (Mat. 12:42) Mawu a Yesu anali “mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:68) Chitsanzo cha zimenezi ndi mfundo zimene iye ananena mu ulaliki wapaphiri. Mfundo zimenezi zimafotokoza bwino lomwe zinthu zimene Solomo ananena m’miyambi yake ndipo zimatithandiza kumvetsa miyambiyo. Solomo anafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zingawathandize atumiki a Yehova kukhala osangalala. (Miy. 3:13; 8:32, 33; 14:21; 16:20) Yesu anatsindika mfundo yakuti zimene zimabweretsa chisangalalo chenicheni ndi zinthu zokhudza kulambira Yehova komanso kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake. Iye ananena kuti: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” (Mat. 5:3) Anthu amene amagwiritsa ntchito mfundo zimene Yesu anaphunzitsa amakhala pa ubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi “chitsime cha moyo.” (Sal. 36:9; Miy. 22:11; Mat. 5:8) Zoonadi, Khristu ndi “nzeru za Mulungu.” (1 Akor. 1:24, 30) Monga Mfumu Mesiya, Yesu Khristu ali ndi “mzimu wanzeru.”—Yes. 11:2.
Mfundo Zothandiza
‘Nzeru Ikufuula’ Kodi Inuyo Mukuimva?
▪ Buku lina linanena kuti: “Baibulo ndi buku lomwe lafalitsidwa komanso kumasuliridwa kambirimbiri m’zinenero zambiri kuposa buku lililonse.” (The World Book Encyclopedia) Baibulo lonse kapena mbali yake likupezeka m’zinenero pafupifupi 2,600. Izi zikusonyeza kuti anthu 90 pa 100 alionse angathe kukhala nalo m’chinenero chawo. Pamenepatu tingati nzeru ikufuula.
▪ Koma nzeru ‘imafuula mokweza’ m’njira inanso. Lemba la Mateyu 24:14 limati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto [a dziko loipali] adzafika.”
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwbq nkhani na. 160
N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu?
Yankho la m’Baibulo
Nthawi zambiri Baibulo limatchula Yesu kuti ndi “Mwana wa Mulungu.” (Yohane 1:49) Mawu akuti “Mwana wa Mulungu,” akusonyeza kuti Mulungu ndiye Mlengi, Kasupe wa zamoyo zonse kuphatikizaponso Yesu. (Salimo 36:9; Chivumbulutso 4:11) Baibulo silinena kuti Mulungu anaberekadi mwana ngati mmene zimakhalira ndi anthu.
Baibulo limatchulanso angelo kuti ndi “ana a Mulungu woona.” (Yobu 1:6) Limanenanso kuti munthu woyambirira Adamu, anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Komabe, popeza kuti Yesu ndi woyambirira kulengedwa komanso kuti analengedwa ndi Mulungu weniweniyo, Baibulo likamanena za Yesu limati ndi Mwana wokondedwa kwambiri wa Mulungu.
Kodi n’zoona kuti Yesu ankakhala kumwamba asanabadwe padziko pano?
Inde. Yesu anali cholengedwa chauzimu asanabwere kudzabadwa ngati munthu padziko lapansi pano. Ndipo Yesuyo ananena kuti: “Ndinatsika kuchokera kumwamba.”—Yohane 6:38; 8:23.
Mulungu analenga Yesu asanalenge china chilichonse. Baibulo limanena za Yesu kuti:
● “Iye ndiye . . . woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.”—Akolose 1:15.
● Ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.”—Chivumbulutso 3:14.
Yesu anakwaniritsa ulosi wonena za ‘munthu amene wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, [amene] wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.’—Mika 5:2; Mateyu 2:4-6.
Kodi Yesu ankagwira ntchito yanji asanabwere padzikoli?
Anali ndi udindo wapamwamba. Yesu ankanena za udindo umenewu pamene anapemphera kuti: “Atate, . . . mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.”—Yohane 17:5.
Ankathandiza Atate ake kulenga zinthu zonse: Yesu ankagwira ntchito limodzi ndi Mulungu monga “mmisiri waluso.” (Miyambo 8:30) Ponena za Yesu, Baibulo limanena kuti: “Chifukwa kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.”—Akolose 1:16.
Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu polenga china chilichonse kuphatikizapo angelo, ngakhalenso zinthu zomwe timaziona m’chilengedwechi. (Chivumbulutso 5:11) Tinganene kuti Mulungu ndi Yesu anachita zinthu mogwirizana, ngati mmene zimakhalira pakati pa munthu waluso lojambula mapulani a nyumba ndi mmisiri womanga nyumba. Munthu waluso amajambula pulani ya nyumba, pamene mmisiri ndi amene amamanga nyumbayo potsatira pulaniyo.
Ankatumikira monga Mawu. Baibulo limanena kuti Yesu asanakhale munthu, ankatchedwa kuti “Mawu.” (Yohane 1:1) Izi zikusonyeza kuti Mulungu ankagwiritsa ntchito Yesu kuti apereke uthenga komanso malangizo kwa angelo ena.
Zikuonekanso kuti nthawi zina Yesu ankagwira ntchito monga Womulankhulira Mulungu akafuna kulankhula ndi anthu padziko lapansi pano. N’kuthekanso kuti Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu monga Mawu popereka malangizo kwa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. (Genesis 2:16, 17) Akhozanso kukhala Yesu yemweyo amene anali mngelo wotsogolera Aisiraeli m’chipululu ndipo Aisiraeliwo ankayenera kumvera mawu ake onse.—Ekisodo 23:20-23.
APRIL 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 9
Mukhale Anzeru, Osati Onyoza
‘Imva Mawu a Anthu Anzeru’
4 Kunena zoona zingakhale zovuta kuvomereza malangizo amene tikupatsidwa mwachindunji. Mwinanso tikhoza kukhumudwa. Chifukwa chiyani? Ngakhale kuti timavomereza kuti si ife angwiro, komabe zingativute kuvomereza malangizo, munthu wina akatiuza zenizeni zimene talakwitsa. (Werengani Mlaliki 7:9.) Tikhoza kumadziikira kumbuyo. Mwinanso tingamakaikire zolinga za munthu amene watipatsa malangizoyo kapenanso kukhumudwa ndi mmene watipatsira. Tikhozanso kuyamba kumupezera zifukwa n’kumanena kuti: ‘Kodi iyeyu ndi ndani kuti andipatse malangizo? Nayenso amalakwitsa zinthu.’ Komanso ngati malangizo amene tapatsidwa sanatisangalatse, sitingawamvere komanso mwina tikhoza kukafunsa kwa munthu wina amene angatipatse malangizo amene angatikomere.
‘Imva Mawu a Anthu Anzeru’
12 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizivomera kupatsidwa malangizo? Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumakumbukira kuti si ife angwiro ndipo nthawi zina tingachite zinthu mosaganiza bwino. Monga taonera kale, Yobu ankaona zinthu molakwika. Koma pambuyo pake anasintha mmene ankaganizira ndipo Yehova anamudalitsa. N’chifukwa chiyani? Chifukwa Yobu anali wodzichepetsa. Iye anasonyeza kuti analidi wodzichepetsa povomera malangizo amene Elihu anamupatsa, ngakhale kuti Elihuyo anali wamng’ono kwa iye. (Yobu 32:6, 7) Kudzichepetsa kudzatithandiza kuti tigwiritse ntchito malangizo amene tapatsidwa ngakhale pamene tikuona kuti sitimayenera kupatsidwa malangizowo, kapenanso ngati amene watipatsa malangizoyo ndi wamng’ono kwa ife. Mkulu wina wa ku Canada ananena kuti: “Popeza sitimadziona ngati mmene ena amationera, kodi tingapite bwanji patsogolo ngati palibe amene akutipatsa malangizo?” Ndi ndani wa ife amene safuna kupita patsogolo pokulitsa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa kapenanso pa ntchito yathu yolalikira?—Werengani Salimo 141:5.
13 Tiziona kuti kupatsidwa malangizo ndi umboni wakuti Yehova amatikonda. Yehova amatifunira zabwino. (Miy. 4:20-22) Iye akatipatsa malangizo kudzera m’Mawu ake, m’mabuku ofotokoza Baibulo kapena kudzera mwa Mkhristu mnzathu, amakhala akutisonyeza chikondi chake. Lemba la Aheberi 12:9, 10 limati, ‘amatilangiza kuti tipindule.’
14 Tiziganizira kwambiri malangizowo osati mmene aperekedwera. Nthawi zina tingaone ngati munthu sanatipatse malangizo m’njira yoyenera. N’zoona kuti aliyense amene akufuna kupereka malangizo ayenera kuyesetsa kuchita zimenezo m’njira yabwino. (Agal. 6:1) Ngati ndife amene tikulangizidwa, tingachite bwino kuganizira malangizo amene tapatsidwa, ngakhale titaona kuti munthu amene watipatsa malangizowo akanatha kuchita zimenezo m’njira yabwino. Mwina tingadzifunse kuti: ‘Ngakhale kuti sindinakonde njira imene wandipatsira malangizowo kodi pali zimene ndingaphunzirepo? Kodi ndinganyalanyaze zimene amene wandipatsa malangizoyo amalakwitsa, n’kugwiritsa ntchito malangizo amene waperekawo?’ Tingakhale anzeru ngati nthawi zonse timayesetsa kuti tizipindula ndi malangizo amene tapatsidwa.—Miy. 15:31.
‘Ndi Nzeru Masiku Athu Adzachuluka’
Munthu wanzeru amaona kudzudzulidwa mosiyana ndi mmene wonyoza amakuonera. Solomo anati: “Dzudzula wanzeru adzakukonda. Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake.” (Miyambo 9:8b, 9a) Munthu wanzeru amadziwa kuti “chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwe[re]tsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11) Ngakhale uphungu ukhale wopweteka, kodi pali chifukwa chochitira ukali kapena kuukana ngati kuulandira kudzatiwonjezera nzeru?
“Ukaphunzitsa wolungama adzawonjezera kuphunzira,” ikupitiriza motero mfumu yanzeru. (Miyambo 9:9b) Aliyense ayenera kupitiriza kuphunzira kaya wanzeru kwambiri kapena wokalamba kwambiri. N’zosangalatsa kwambiritu kuona ngakhale okalamba akulandira choonadi ndi kudzipatulira kwa Yehova! Nafenso tiyeni tiyesetse kukhalabe ndi mtima wofuna kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito ubongo wathu.
‘Ndi Nzeru Masiku Athu Adzachuluka’
Ndi udindo wa aliyense kuyesetsa kupeza nzeru. Ponenetsa mfundo imeneyi, Solomo anati: “Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo? Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.” (Miyambo 9:12) Munthu wanzeru amapindula nayo yekha, koma wonyoza adzavutika yekha. Ndithudi, timakolola zomwe tinafesa. Tsono tiyenitu ‘titchere makutu athu ku nzeru.’—Miyambo 2:2.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
9:17—Kodi “madzi akuba” n’chiyani ndipo n’chifukwa chiyani ‘amatsekemera’? Popeza kuti Baibulo limayerekezera kusangalala ndi kugonana kumene kumachitika muukwati ndi kumwa madzi otsitsimula otungidwa pachitsime, madzi akuba akuimira kuchita zachiwerewere mobisa. (Miyambo 5:15-17) Maganizo ochita zachiwerewere popanda kugwidwa ndiwo amene amachititsa kuti madzi oterowo azioneka ngati otsekemera.
APRIL 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 10
Kodi N’chiyani Chimathandiza Munthu Kumasangalaladi pa Moyo?
‘Madalitso Ali pa Wolungama’
Wolungama amapindulanso m’njira ina. “Wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa. Wokolola m’malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakututa ndi mwana wochititsa manyazi.”—Miyambo 10:4, 5.
Mawu a mfumuwa akutanthauza zambiri makamaka kwa ogwira ntchito yotuta. Nthawi yotuta si nthawi yogona. Ndi nthawi yogwira ntchito mwakhama kwa maola ochuluka. Ndithudi imeneyi imakhala nthawi yofunika kuchita changu.
Pamene Yesu anali kulingalira za kututa anthu osati zokolola zakumunda, anauza ophunzira ake kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta [Yehova Mulungu] kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:35-38) M’chaka cha 2000, anthu oposa 14 miliyoni anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu; kuwirikiza kawiri chiwerengero cha Mboni za Yehova. Motero ndani angatsutse kuti ‘m’minda mwayera kufikira kumweta’? (Yohane 4:35) Olambira oona amapempha Mwini ntchito kuti atumize antchito ena. Akamatero amakhalanso akudzipereka zolimba m’ntchito yopanga ophunzira mogwirizana ndi mapemphero awowo. (Mateyu 28:19, 20) Ndipotu Yehova wadalitsa khama lawo mosaneneka! M’chaka chautumiki cha 2000, munabatizidwa anthu atsopano oposa 280,000. Amenewanso amayesetsa kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Tikhaletu achimwemwe ndi okhutira panthawi yotuta ino mwa kugwira nawo mokwanira ntchito yopanga ophunzira.
Yendani ‘M’njira Yoongoka’
Solomo akufotokoza kufunika kwa chilungamo. Anati: “Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba; koma umphawi wawo uwononga osauka. Ntchito za wolungama zipatsa moyo; koma phindu la oipa lichimwitsa.”—Miyambo 10:15, 16.
Chuma chingatchinjirize kumavuto ena amene angagwe mwadzidzidzi, monga momwe tauni yam’mpanda nthawi zina imatchinjirizira anthu amene akukhalamo. Ndipo umphawi ungakhale wopweteka pakagwa vuto mwadzidzidzi. (Mlaliki 7:12) Komabe, mfumu yanzeruyo inalangizanso za ngozi zokhudza chuma ndi umphawi womwe. Munthu wolemera angamakhulupirire chuma chake chokha basi, n’kumaganiza kuti zinthu zamtengo wapatali zimene ali nazozo ndizo “khoma lalitali.” (Miyambo 18:11) Nayenso munthu wosauka angamaganize molakwika kuti alibe tsogolo lililonse chifukwa cha umphawi wakewo. Motero, onsewo amalephera kukondweretsa Mulungu.
it-1 340
Madalitso
Yehova Amadalitsa Anthu. “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa munthu, ndipo popereka madalitsowa Mulungu sawonjezerapo ululu.” (Miy. 10:22) Yehova amadalitsa anthu amene wawavomereza. Amawadalitsa powateteza, powathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino, powatsogolera, powathandiza kuti apambane pa zochita zawo ndiponso powapatsa zofunikira pa moyo wawo. Zimenezi zimawapindulitsa anthuwo.
Mfundo Zothandiza
Ubwino Woyenda Mwangwiro
18 “Madalitso a Yehova” ndiwo akuthandiza anthu ake kuti zinthu ziziwayendera bwino mwauzimu. Ndipo akutitsimikizira kuti “sawonjezerapo chisoni.” (Miyambo 10:22) Ndiyeno n’chifukwa chiyani ambiri mwa anthu okhulupirika a Mulungu amakumana ndi mavuto ndiponso mayesero, omwe amachititsa kuti azivutika kwambiri? Timavutika chifukwa cha zinthu zitatu makamaka. (1) Zochita zathu zauchimo. (Genesis 6:5; 8:21; Yakobo 1:14, 15) (2) Satana ndi ziwanda zake. (Aefeso 6:11, 12) (3) Dziko loipa. (Yohane 15:19) Ngakhale kuti Yehova amalola kuti zinthu zoipa zizitichitikira, sikuti iye ndiye amachititsa zinthuzo. Ndipotu, “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko.” (Yakobo 1:17) Madalitso a Yehova sabweretsa mavuto.
APRIL 28–MAY 4
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 11
Musamalankhule
Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
Kuwongoka mtima kwa olungama ndiponso zimene woipa amachita zimakhudzanso anthu ena. Mfumu ya Israyeli inati: “Wonyoza Mulungu awononga mnzake ndi m’kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.” (Miyambo 11:9) Kodi alipo angatsutse zoti bodza, miseche, mawu otukwana, ndi njerengo zachabe zimavulaza ena? Kusiyana ndi zimenezi, wolungama amalankhula zabwino, amaganiza kaye asanalankhule, ndiponso amaganizira ena. Wolungama amapulumuka mwa zimene akudziwa chifukwa kuwongoka mtima kwake kumam’thandiza kukhala ndi umboni wofunika kusonyeza kuti anthu amene akumuimba mlandu ndi abodza.
Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
Anthu amene amachita zinthu zolungama pamudzi amalimbikitsa mtendere ndi moyo wabwino ndiponso amalimbikitsa ena. Motero, amakuza mudzi, zinthu zimayenda bwino pamudzipo. Amene amalankhula zojeda anzawo, zokhumudwitsa, ndiponso zinthu zachabe amayambitsa chisokonezo, chisoni, kusagwirizana ndi mavuto. Zimenezi zimakhala choncho makamaka ngati amene akuchita zimenezo ndi anthu amene ali ndi udindo pamudzipo. Pamudzi wotero pamakhala chisokonezo, katangale, makhalidwe oipa ndiponso mwina mavuto a zachuma.
Mfundo ya pa Miyambo 11:11 imagwiranso ntchito chimodzimodzi kwa anthu a Yehova akamasonkhana pamodzi m’mipingo yawo yonga midzi. Anthu auzimu—amene amatsatira kuwongoka mtima—akamatsogolera mpingo, anthu mumpingomo amakhala achimwemwe, okangalika ndiponso amakhala othandiza. Zimenezi zimalemekeza Mulungu. Yehova amadalitsa mpingowo, ndipo umayenda bwino mwauzimu. Nthawi zina, anthu ochepa odandaula ndi osakondwa, omwe amapeza anzawo zifukwa ndipo amalankhula moipidwa ndi mmene zinthu zikuyendera, ali ngati ‘muzu wowawa’ umene ungafalikire ndi kuipitsa anthu ena amene poyamba analibe maganizo otero. (Ahebri 12:15) Nthawi zambiri anthu oterowo amafuna mpando ndi kutchuka. Amayambitsa mphekesera zakuti mumpingomo kapena akulu sakuchita chilungamo, pali kusankhana mafuko, kapena zinthu zina. Pakamwa pawo pangagawanitsedi mpingo. Kodi si bwino kusamvera zimene akunena ndi kuyesetsa kukhala anthu auzimu amene tingalimbikitse mtendere ndi mgwirizano mumpingo?
Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
Inde, munthu wosazindikira, kapena ‘wosowa nzeru’ amayambitsa mavuto aakulu. Kulankhula kwake kosadziletsa amafika nako pochita miseche kapena kuchita chipongwe. Akulu oikidwa ayenera kuthetsa zinthu zoipa ngati zimenezi mwamsanga. Kusiyana ndi ‘wosowa nzeru,’ munthu wozindikira amadziwa pamene afunikira kutonthola. Amabisa mawu, m’malo mowanditsa zinsinsi. Munthu wozindikira amakhala “wokhulupirika mtima” chifukwa amadziwa kuti lilime lingavulaze kwambiri ngati salilamulira. Amakhulupirika kwa okhulupirira anzake ndipo saulula nkhani zachinsinsi zimene zingawaike pangozi. Anthu oongoka mtima amenewa amapindulitsa mpingo.
Mfundo Zothandiza
g20.1 11, bokosi
Zimene Mungachite Kuti Muchepetse Nkhawa
“GONJETSANI NKHAWA POCHITIRA ENA ZABWINO”
“Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake, koma munthu wankhanza amachititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.”—MIYAMBO 11:17.
Buku lina lofotokoza za nkhawa lili ndi mutu wakuti “Gonjetsani Nkhawa Pochitira Ena Zabwino.” (Overcoming Stress) Mlembi wa bukuli dzina lake Dr. Tim Cantopher ananena kuti kuchitira ena zabwino kumathandiza kuti munthu akhale wathanzi komanso azisangalala. Koma munthu amene sachitira ena zabwino kapena wankhanza, sasangalala chifukwa anthu amamupewa.
Tingachepetsenso nkhawa ngati timayesetsa kuchita zinthu modziganizira. Mwachitsanzo, sitiyenera kumadzikhaulitsa kapena kudzipanikiza komanso tisamadzikayikire. Yesu Khristu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”—Maliko 12:31.