PHUNZIRO 11
Kulankhula ndi Mtima Wonse
Aroma 12:11
MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula ndi mtima wonse kuti muziwafika pamtima anthu amene mukukambirana nawo.
MMENE MUNGACHITIRE:
Muzilankhula kuchokera mumtima. Mukamakonzekera komanso kukamba nkhani, muziganizira mmene ingathandizire anthu. Muziidziwa bwino nkhaniyo moti muzilankhula mfundo zanu kuchokera mumtima.
Muziganizira anthu. Muziganizira mmene mfundo imene mungawerenge kapena kuphunzitsa ingathandizire anthu. Muzifotokoza mfundozo m’njira yoti anthu aziona kuti ndi zothandiza.
Nkhani yanu izikhala yamoyo. Muzisonyeza kuti nkhaniyo yakufikani pamtima. Ndiyeno manja ndi nkhope yanu zizisonyeza mmene mukumvera mumtima.