Kodi Kutchova Juga Ndi Tchimo?
Yankho la m’Baibulo
Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mwatsatanetsatane zokhudza juga, mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuzindikira kuti Mulungu amaona kuti khalidweli ndi tchimo.—Aefeso 5:17.a
Anthu amatchova juga chifukwa cha dyera ndipo Mulungu amadana ndi khalidwe limeneli. (1 Akorinto 6:9, 10; Aefeso 5:3, 5) Kuti munthu wotchova juga awine, pamafunika kuti anzake aluze, koma Baibulo limaletsa kusirira zinthu za anthu ena mwansanje.—Ekisodo 20:17; Aroma 7:7; 13:9, 10.
Kutchova juga, ngakhale pang’ono pokha, kungachititse munthu kuti ayambe kukonda kwambiri ndalama.—1 Timoteyo 6:9, 10.
Nthawi zambiri anthu otchova juga amadalira matsenga kapena mwayi. Komabe, Mulungu amaona kuti kukhulupirira zimenezi ndi kulambira mafano, komwe sikugwirizana ndi kulambira kumene iye amavomereza.—Yesaya 65:11.
M’malo molimbikitsa khalidwe lomapeza zinthu zomwe sitinazigwirire ntchito, Baibulo limatilimbikitsa kugwira ntchito mwakhama. (Mlaliki 2:24; Aefeso 4:28) Anthu omwe amatsatira malangizowa ‘amadya chakudya chimene achigwirira ntchito.’—2 Atesalonika 3:10, 12.
Kutchova juga kumalimbikitsa khalidwe la mpikisano, lomwe limaletsedwa m’Baibulo.—Agalatiya 5:26.
a M’Baibulo, kutchova juga kumatchulidwa mwachindunji kamodzi kokha pa nkhani yonena za asilikali a Roma omwe anachita maere, kapena kuti “anatchova juga” pa chovala cha Yesu.—Mateyu 27:35; Yohane 19:23, 24; Contemporary English Version; Good News Translation.