NYIMBO 128
Tipirire Mpaka Mapeto
Losindikizidwa
1. Mawu a Mulungu wathu
Amalimbikitsa.
Zinthu zomwe waphunzira
Zonse ndi zolondola.
Uzikhulupirikabe
Podikira mapeto.
Usaope mayesero
Udzakhala wolimba.
2. Chikondi chako kwa M’lungu
Chisachepe mphamvu.
Upirirebe ngakhale
Mayesero akule.
Kaya akhale otani
Usamachite mantha.
Yehova Mulungu wako
Adzakupulumutsa.
3. Yemwe angapirirebe
Adzapulumuka.
Mayina akulembedwa
Mubuku la moyotu.
Lola kuti kupirira
Kugwire ntchito yake.
Yehova adzachititsa
Kuti usangalale.
(Onaninso Aheb. 6:19; Yak. 1:4; 2 Pet. 3:12; Chiv. 2:4.)