Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Aisiraeli Sanachite Zimene Analonjeza
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Aisiraeli akuimba komanso kuvinira mwana wa ng’ombe wagolide

      MUTU 24

      Aisiraeli Sanachite Zimene Analonjeza

      Yehova anauza Mose kuti: ‘Bwera kuphiri kuno. Ndilemba malamulo anga pamiyala n’kukupatsa.’ Mose anapita kuphiriko ndipo anakhalako masiku 40. Ali komweko, Yehova analemba Malamulo 10 pamiyala iwiri n’kumupatsa.

      Mose waponya pansi miyala

      Patapita nthawi, Aisiraeli anaganiza kuti Mose wawathawa. Choncho anauza Aroni kuti: ‘Tikufuna mtsogoleri wina. Tipangire mulungu.’ Aroni anawauza kuti: ‘Ndipatseni golide wanu.’ Ndiyeno anasungunula golideyo n’kupanga fano la mwana wa ng’ombe. Zitatero, Aisiraeliwo anati: ‘Uyu ndi Mulungu amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.’ Iwo anayamba kulambira fano la mwana wa ng’ombelo ndipo anachita mwambo wokondwerera fanolo. Kodi ukuganiza kuti zimenezi zinali zabwino? Ayi, chifukwa anthuwo anali atalonjeza kuti azilambira Yehova yekha. Koma zimene anachitazi zinali zosemphana ndi zimene analonjeza.

      Yehova anaona zimene zinkachitikazi ndipo anauza Mose kuti: ‘Pita ukaone zimene anthu aja akuchita. Asiya kundimvera ndipo akulambira mulungu wabodza.’ Mose anatsika m’phirimo atanyamula miyala iwiri ija.

      Atayandikira msasa uja anamva anthu akuimba. Kenako anawaona akuvina komanso kugwadira mwana wa ng’ombe uja. Mose anakwiya kwambiri. Anaponya pansi miyala iwiri ija moti inasweka. Nthawi yomweyo anawotcha fanolo n’kuliperapera. Kenako anafunsa Aroni kuti: ‘Kodi anthuwa akuchitira chiyani kuti uwamvere n’kuchita zinthu zoipa chonchi?’ Aroni anayankha kuti: ‘Pepani musandikwiyire. Mukudziwa bwino mmene anthuwa alili. Iwo amafuna mulungu ndiye ndinangotenga golide n’kumuponya pamoto ndipo panatuluka mwana wang’ombeyu.’ Komatu Aroni sankayenera kuchita zimenezi. Mose anapitanso kuphiri kuja n’kukapempha Yehova kuti akhululukire anthuwo.

      Yehova anakhululukira anthu onse amene analapa n’kuyambiranso kumumvera. Kodi ukuona chifukwa chake zinali zofunika kuti Aisiraeli azimvera zonse zimene Mose ankawauza?

      “Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako, chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu opusa. Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.”​—Mlaliki 5:4

      Mafunso: Kodi Aisiraeli anachita zotani Mose ali kuphiri? Kodi Mose atabwerako anachita chiyani?

      Ekisodo 24:12-18; 32:1-30

  • Chihema Cholambiriramo
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Chihema ndi bwalo la chihemacho

      MUTU 25

      Chihema Cholambiriramo

      Mose ali kuphiri la Sinai, Yehova anamuuza kuti akonze tenti yapadera yolambiriramo ndipo ankaitchula kuti chihema. Iwo anachikonza m’njira yoti azitha kuchinyamula kulikonse kumene akupita.

      Yehova anauza Mose kuti: ‘Uza anthu kuti akupatse zinthu zimene angakwanitse kuti upangire chihema.’ Aisiraeli anapereka golide, siliva, kopa, miyala yamtengo wapatali komanso zodzikongoletsera. Anaperekanso ubweya wa nkhosa, nsalu, zikopa zanyama komanso zinthu zina zambiri. Anthuwo anapereka zinthu zambiri mpaka Mose anachita kuwauza kuti: ‘Basi zakwana. Musabweretsenso zina.’

      Aisiraeli abweretsa mphatso zothandizira kumanga chihema

      Amuna ndi akazi ambiri aluso anagwira nawo ntchito yomanga chihemachi. Yehova anawapatsa nzeru zowathandiza pogwira ntchitoyi. Ena ankapanga ulusi, kuwomba nsalu komanso kuzikongoletsa. Panalinso ena amene ankapanga zinthu pogwiritsa ntchito miyala, golide kapena mitengo.

      Anthuwo anapanga chihema potsatira malangizo amene Yehova anawapatsa. Anapanga katani yokongola imene inagawa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa. M’Malo Oyera Koposa munali bokosi lotchedwa likasa la pangano. Bokosili linapangidwa ndi golide komanso matabwa a mtengo wa mthethe. M’Malo Oyera munali choikapo nyali chagolide, tebulo ndi guwa lansembe zofukiza. Ndipo pabwalo la chihema panali beseni lakopa ndi guwa lalikulu loperekera nsembe zopsereza. Likasa la pangano linkakumbutsa Aisiraeli kuti analonjeza zoti azimvera Yehova. Kodi ukudziwa kuti pangano n’chiyani? Ndi lonjezo lapadera limene anthu amachita.

      Yehova anasankha Aroni ndi ana ake aamuna kuti azigwira ntchito kuchihema n’kumapereka nsembe. Ankayenera kusamalira chihemacho komanso kupereka nsembe kwa Yehova. Aroni yekha, yemwe anali mkulu wa ansembe ndi amene ankaloledwa kulowa m’Malo Oyera Koposa. Iye ankachita zimenezi kamodzi chaka chilichonse pokapereka nsembe ya machimo ake, a banja lake komanso a Aisiraeli onse.

      Aisiraeli anamaliza kupanga chihemachi patangotha chaka chimodzi kuchokera pamene anatuluka m’dziko la Iguputo. Apa tsopano anali ndi malo olambirira Yehova.

      Ulemerero wa Yehova unadzaza m’chihemacho ndipo mtambo unkakhala pamwamba pake. Mtambowo ukakhala pamwamba pa chihema, Aisiraeli ankakhalabe pamalo omwewo. Koma ukachoka, ankadziwa kuti nthawi yoti anyamuke yakwana. Choncho ankaphwasula chihema chija n’kumatsatira mtambowo ndipo ankakachimanga pamalo ena.

      “Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu akuti: ‘Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu ndipo iye azidzakhala nawo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulunguyo adzakhala nawo.’”​—Chivumbulutso 21:3

      Mafunso: Kodi Yehova anauza Mose kuti apange chiyani? Kodi Yehova anapatsa Aroni ndi ana ake udindo wotani?

      Ekisodo 25:1-9; 31:1-11; 40:33-38; Aheberi 9:1-7

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena