NYIMBO 47
‘Muzipemphera kwa Yehova Nthawi Zonse’
Losindikizidwa
1. Pemphera kwa Yehova amamva.
Ndi mwayi umene wakupatsa.
Umuuze zamumtima mwako,
Ndi wodalirika, bwenzi lako.
Pemphera kwa Yehova.
2. Pemphera kwa Yehova thokoza.
Upemphe akukhululukire.
Umuuze zomwe walakwitsa,
Amadziwa zofooka zako.
Pemphera kwa Yehova.
3. Pemphera kwa Yehova m’mavuto,
Ndi M’lungu wako akuthandiza.
Upemphe kuti akuteteze,
Mukhulupirire usaope.
Pemphera kwa Yehova.
(Onaninso Sal. 65:5; Mat. 6:9-13; 26:41; Luka 18:1.)