NYIMBO 45
“Zimene Ndimaganizira Mozama”
Losindikizidwa
1. Zomwe ndimaganizira
Mozama mumtima mwanga,
Zizikusangalatsani
Kuti ndikhale wolimba.
Pamene ndili ndi nkhawa
N’kumalephera kugona,
Ndiganizire mozama
Zinthu zondilimbikitsa.
2. Zilizonse zolungama,
Zofunika ndi zoona,
Ndikamaziganizira
Zizindipatsa mtendere.
Nzeru zanu n’zofunika
Komanso ndi zochuluka,
Choncho ndiziganizira
Zonena zanu mozama.
(Onaninso Sal. 49:3; 63:6; 139:17, 23; Afil. 4:7, 8; 1 Tim. 4:15.)