NYIMBO 126
Khala Maso, Khala Wolimba, Khala Wamphamvu
Losindikizidwa
1. Khala maso, upirire.
Ukhalebe wamphamvu.
Ukhale wolimba mtima,
Udzapambana ndithu.
Uzimvera mawu a Yesu.
Ukhalebe ku mbali yake.
(KOLASI)
Khala maso, khala wamphamvu.
Limba mpaka mapeto.
2. Khala maso, usagone.
Ukonzeke kumvera,
Uzimvera malangizo
Ochokera kwa Yesu.
Uzimveranso malangizo
Omwe akulu akupatsa.
(KOLASI)
Khala maso, khala wamphamvu.
Limba mpaka mapeto.
3. Tikhale ogwirizana
Poteteza uthenga.
Ngakhale tizitsutsidwa
Tizilalikirabe.
Timutamande mwachimwemwe.
Tsiku lake layandikira.
(KOLASI)
Khala maso, khala wamphamvu.
Limba mpaka mapeto.
(Onaninso Mat. 24:13; Aheb. 13:7, 17; 1 Pet. 5:8.)