Kondwerani ndi Mawu a Mulungu
WODALA munthu amene “m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake.” Munthu woteroyo amaŵerenga Mawu a Mulungu ndi ‘kulingiriramo usana ndi usiku.’ (Sal. 1:1, 2) Kodi inuyo mumakhala nacho chisangalalo choterocho? Nanga mungapeze bwanji chimwemwe chowirikiza m’Mawu a Mulungu?
Mvetserani Pamene Yehova Alankhula
Musamangoŵerenga mawu okha ayi. Muziziona m’maganizo mwanu zochitika zimene mukuŵerengazo. Yerekezani ngati kuti mukumva kulankhula kwa anthu amene mukuŵerenga mawu awo. Pamene muŵerenga machaputala oyambirira a Baibulo, khalani ngati kuti mukumumva Yehova mwiniyo akuvumbula, chimodzi ndi chimodzi, zimene akuchita pokonza dziko lapansi kukhala malo oyenera kukhalamo anthu. Mvetserani pamene akuuza Mwana wake, Mmisiri Wamkuluyo, kuti nthaŵi yakwana yoti apange anthu oyamba. Onani zochitika izi m’maganizo mwanu: Adamu ndi Hava akupanduka, Mulungu akupereka chiweruzo pa iwo, kenako akuwapirikitsa m’Paradaiso. (Genesis, machap. 1-3) Imvani nthumanzi inayake pamene muŵerenga zakuti mawu ochokera kumwamba akudziŵitsa Yesu Kristu monga Mwana wa Mulungu, wokondedwa, amene Mulungu anam’tuma kudzataya moyo wake m’malo mwa anthu onse. (Mat. 3:16, 17) Yesani kuona m’maganizo mwanu mmene mtumwi Yohane akuchitira atamva Yehova akulengeza kuti: “Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.” (Chiv. 21:5) Ndithudi, kuŵerenga Mawu a Mulungu mwa njira imeneyi ndi chinthu chokondweretsa kwabasi!
Pitirizani kuŵerenga nkhani zouziridwazo, ndipo mudzam’dziŵa Yehova monga Mulungu waulemerero ndi wochititsa mantha. Mudzakopeka ndi Iyeyo amene amatikonda, amene amachita nafe mwachifundo, amene amatithandiza ngati tiyesetsabe kuchita chifuniro chake modzichepetsa, komanso amene amatiphunzitsa mmene tingapambanire pa zochita zathu zonse.—Yos. 1:8; Sal. 8:1; Yes. 41:10.
Mukamathera nthaŵi yochuluka kuŵerenga Baibulo, mumakhalanso wokhutira kwambiri pamene mudziŵa zambiri zimene Mulungu amafuna kwa inu. Koma chisangalalo chanu chidzaposa pamenepo. Pamene kuŵerengako kukuthandizani kuthana ndi mavuto mwanzeru, mudzamva mmene anamvera wamasalmo yemwe anati: ‘Mboni zanu [“malangizo anu,” NW] n’zodabwitsa; Chifukwa chake moyo wanga uzisunga.’ (Sal. 119:129) Inunso mudzakondwa pamene muzindikira m’Malemba mfundo za makhalidwe abwino zomwe zimathandiza kutsogolera maganizo anu ndi zokhumba zanu m’njira ya Mulungu.—Yes. 55:8, 9.
Baibulo limapereka malangizo a chikhalidwe omwe amatiteteza ku ngozi ndipo amatisonyeza njira yoyenera. Poliŵerenga, timaona kuti Yehova ndi Tate wodziŵa bwino mavuto omwe angatsatirepo ngati tigonja ku zilakolako za thupi. Sakufuna kuti tikakumane ndi zovuta zomwe zingatipeze mosapeŵeka ngati tinyoza miyezo yake yapamwamba ya makhalidwe. Amatisamala ndipo amafuna kuti tisangalale ndi moyo wabwino koposa. Kuŵerenga Mawu ake kumatithandiza kuzindikira bwino lomwe kuti ndi dalitso losaneneka pamene iye ali Mulungu wathu ndi Atate wathu wakumwamba.
Ŵerengani Baibulo Tsiku ndi Tsiku
Ponena za munthu woŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku, wamasalmo anati: “Zonse azichita apindula nazo.” (Sal. 1:3) Inde, ngakhale tili opanda ungwiro, ngakhale tikukhala m’dziko la Satana, ndipo ngakhale Mdyerekezi angayesetse kuti atikhadzule, ngati nthaŵi zonse tiŵerenga ndi kuchita zimene zili m’Mawu a Mulungu, tidzapambana pochita chilichonse chokhudzana ndi unansi wathu ndi Yehova.
Popeza tili opsinjidwa ndi dziko lakaleli, kusinkhasinkha malingaliro a Mlengi, ngakhale kwa mphindi zochepa chabe tsiku ndi tsiku, kungatipatse nyonga. Ena amene anatsekeredwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo anatha kungoŵerenga mavesi a apa ndi apo omwe anawapeza atagwidwa mawu m’nkhani za m’nyuzipepala. Iwo anali kudula mavesiwo, kuwaloŵeza, ndi kumawasinkhasinkha. Yehova anadalitsa khama lawo chifukwa anachita zimene mikhalidwe yawo inawalola kuphunzira za Mawu a Mulungu. (Mat. 5:3) Komabe, ambirife tili ndi ufulu waukulu kuposa umenewo. Tisaganize kuti kungoŵerenga vesi imodzi ya Baibulo patsiku kumapereka mphamvu yozizwitsa ayi. Komabe, tidzapindula ngati tisintha zochita zathu ndi kuika patsogolo zinthu zofunikira kwambiri kotero kuti tizitha kuŵerenga gawo la m’Baibulo patsiku, kusinkhasinkha zomwe taŵerengazo, ndi kuzigwiritsa ntchito pamoyo wathu.
Koma kunena zoona, zolinga zathu zabwino kwambiri zikhoza kusokonezeka. Zimenezo zikachitika, timasamala choyamba zinthu zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, sitingakhale dala tsiku limodzi kapena aŵiri osamwa madzi. Mofananamo, ngakhale titakumana ndi zotani pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku, tiyenera kumapatula nthaŵi yoti timwe madzi otsitsimutsa a choonadi.—Mac. 17:11.
Ŵerengani Mawu Onse a Mulungu
Kodi inuyo panokha mwaliŵerengapo Baibulo lonse? Ena agwa ulesi poganiza za kuŵerenga kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso. Choncho, ambiri amene anafuna kuŵerenga Baibulo lonse anayamba mwa kuŵerenga choyamba Malemba Achigiriki Achikristu. Chifukwa chiyani? Mwina anaona mmene mabuku a Baibulowo anawakhudzira msanga payekhapayekha poyesetsa kuyenda m’mapazi a Kristu. Kapenanso chinali chifukwa chakuti Malemba Achigiriki Achikristu sanaoneke kukhala ochuluka kwambiri—amangopitirira pang’ono pa limodzi mwa magawo anayi a Baibulo lonse. Koma atamaliza kuŵerenga mabuku 27, anatembenukira ku mabuku 39 a Malemba Achihebri nayamba kuwaŵerenga ndi kusangalala nawo. Pamene anamaliza Malemba Achihebri, anali atakhazikitsa chizoloŵezi choŵerenga Baibulo nthaŵi zonse, choncho anapitiriza kutero, akumaŵerenganso kachiŵiri Malemba Achigiriki Achikristu, ndipo sanasiye mpaka pano. Inunso khalani ndi chizoloŵezi cha moyo wonse choŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku.
Kodi alipo wina m’banja mwanu kapena mumpingo amene sakhoza kuŵerenga? Bwanji osadzipereka kuti muzimuŵerengera Baibulo nthaŵi ndi nthaŵi? Inuyo mudzapindula, koma iyenso adzapindula pamene asinkhasinkha zimene akumva ndi kuzigwiritsa ntchito pamoyo wake.—Chiv. 1:3.
M’kupita kwa nthaŵi, mungafune kuyamba mapulogalamu apadera okhudzana ndi kuŵerenga Baibulo kwanu. Ena mwa amenewo angakuthandizeni kuzindikira bwino lomwe mgwirizano womwe ulipo pakati pa mbali zosiyanasiyana za Baibulo. Ngati Baibulo lanu lili ndi malemba owonjezera a m’danga lapakati, amenewo angakuthandizeni kudziŵa zinthu za m’mbiri yakale ndi nkhani zina zofanana. Angakuthandizeni kuzindikira mikhalidwe imene inachititsa kuti masalmo osiyanasiyana alembedwe limodzinso ndi makalata olembedwa ndi atumwi a Yesu Kristu. Buku lakuti Insight on the Scriptures lili ndi mbiri yakale yopindulitsa yonena za anthu, malo, ndi mikhalidwe yotchulidwa m’Baibulo. Machati amasonyeza kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo, amaonetsa mafumu ndi aneneri omwe anakhalapo m’nthaŵi yofanana, ndipo amasonyezanso madeti apafupifupi a zochitika zambiri za m’Baibulo.
Pamene musinkhasinkha zimene mwaphunzira, mudzazindikira chifukwa chake mikhalidwe ina inakhalapo pakati pa anthu a Mulungu. Mudzadziŵanso chifukwa chake Yehova anachita ndi anthu ake mmene anachitiramo. Mudzamvetsa mmene Yehova amaonera machitidwe a maboma, mitundu ya anthu, komanso anthu onse mmodzi ndi mmodzi. Zimenezi zidzakuthandizani kuzindikira bwino malingaliro ake.
Mbiri yakale ya m’Baibulo idzakusangalatsani kwambiri pamene muyesa kuona m’maganizo mwanu maderawo kumene zinthuzo zinachitikira. Mapu a malo otchulidwa m’Baibulo amasonyeza nthaka ndi mitunda ya malo osiyanasiyana. Mwachitsanzo, kodi m’pati makamaka pamene Aisrayeli anawolokera Nyanja Yofiira? Kodi Dziko Lolonjezedwalo linali lalikulu motani? Kodi Yesu anayenda mpaka kuti pochita utumiki wake wa padziko lapansi? Kodi mtumwi Paulo anaona malo osiyanasiyana otani pamaulendo ake aumishonale? Mapu ndi mafotokozedwe a malo amavumbula zinthu zimene zidzachititsa kuŵerenga kwanu kukhala kosangalatsa. Kodi mapu osonyeza malo a m’Baibulo mungawapeze kuti? Ena ali m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures. Buku la Insight lili ndi mapu 70, ndipo lili ndi cholozera mapu kumapeto kwa voliyumu yake yoyamba. Gwiritsani ntchito Watch Tower Publications Index kuti mupeze mapu ena. Ngati simungathe kukhala ndi mabuku amenewo, gwiritsani ntchito mapu ofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda kuti akuthandizeni pa pulogalamu yanu yoŵerenga Baibulo.
M’Malemba Achihebri, Mfumu Davide anatamanda Yehova, amvekere: “Ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Maŵerengedwe ake ndi ambirimbiri!” (Sal. 139:17) M’Malemba Achigiriki Achikristu, mtumwi Paulo anatamanda Yehova chifukwa chakuti Iye “anawala m’mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.” (2 Akor. 4:6) Davide ndi Paulo anakhalapo ndi moyo panthaŵi zosiyana ndi zaka mazana ambiri; komabe, onse aŵiri anakondwa ndi Mawu a Mulungu. Inunso mukhoza kutero ngati mupatula nthaŵi ndi kuŵerenga zonse zimene Yehova wakupatsani m’masamba a Mawu ake ouziridwa.