Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
Chilengezo
Chinenero chatsopano chomwe chilipo: Betsileo
  • Lero

Lolemba, October 27

Amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondera matupi awo.—Aef. 5:28.

Yehova amafuna kuti mwamuna azikonda mkazi wake ndipo azimupezera zofunika pa moyo, azikhala mnzake wapamtima komanso azimuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehovayo. Kuganiza bwino, kulemekeza akazi komanso kukhala odalirika, kungakuthandizeni kuti mukhale mwamuna wabwino. Mukadzakwatira, mukhoza kudzakhala ndi ana. Ndiye kodi mungaphunzire chiyani kwa Yehova pa nkhani yokhala bambo wabwino? (Aef. 6:4) Yehova ankauza Mwana wake Yesu kuti amamukonda ndiponso kuti amamusangalatsa kwambiri. (Mat. 3:17) Nanunso mukadzakhala ndi ana, muzidzawauza pafupipafupi kuti mumawakonda. Nthawi zonse muzidzawayamikira akachita zabwino. Abambo amene amatsanzira Yehova, amathandiza ana awo kuti akule mwauzimu. Mungakonzekere udindo umenewu posamalira mwachikondi anthu a m’banja lanu ndiponso a mumpingo. Komanso pouza anthu ena kuti mumawakonda ndiponso kuwayamikira.—Yoh. 15:9. w23.12 28-29 ¶17-18

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachiwiri, October 28

[Yehova] adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.​—Yes. 33:6.

Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupirika a Yehova, mofanana ndi anthu onse, timakumana ndi mavuto komanso matenda. Nthawi zinanso timatsutsidwa kapena kuzunzidwa ndi anthu odana ndi anthu a Mulungu. Yehova samatiteteza kuti tisakumane ndi mavuto, koma amatilonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Iye akatithandiza timapitirizabe kukhala osangalala, timasankha zinthu mwanzeru komanso timakhalabe okhulupirika kwa iye ngakhale pamene zili zovuta kutero. Yehova amatilonjeza kuti atipatsa “mtendere [wake]” wotchulidwa m’Baibulo. (Afil. 4:6, 7) Munthu akakhala ndi mtendere umenewu, mtima ndi maganizo ake zimakhala m’malo chifukwa choti ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mtenderewu ndi woti “anthu sangathe kuumvetsa” ndipo ndi wodabwitsa kuposa mmene tingaganizire. Kodi inunso mtima wanu unayamba wakhalapo m’malo mutapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima? Munamva choncho chifukwa cha “mtendere wa Mulungu.” w24.01 20 ¶2; 21 ¶4

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachitatu, October 29

Moyo wanga utamande Yehova. Chilichonse cha mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.​—Sal. 103:1.

Kukonda Mulungu kumachititsa anthu okhulupirika kuti azitamanda dzina lake ndi mtima wonse. Mfumu Davide ankadziwa kuti kutamanda dzina la Yehova kumatanthauza kutamanda Yehovayo. Choncho tikamva dzinali timaganizira makhalidwe ake abwino komanso ntchito zake zodabwitsa. Davide ankafuna aziona kuti dzina la Atate wake ndi loyera komanso kumalitamanda. Iye ankafuna azichita zimenezo ndi “chilichonse cha mkati [mwake]” kapena kuti ndi mtima wonse. Mofanana ndi Davide, Alevi nawonso ankatsogolera potamanda Yehova. Modzichepetsa, iwo anavomereza kuti mawu awo sakanatha kufotokoza mokwanira ulemerero umene dzina loyera la Yehova liyenera kulandira. (Neh. 9:5) Mosakayikira, Yehova anasangalala ndi kudzichepetsa komanso kumutamanda kochokera pansi pamtima kumeneku. w24.02 9 ¶6

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena