Lingaliro la Baibulo
Kodi Akristu Ayenera Kugwiritsa Ntchito Njira Yotchedwa Fêng Shui?
KU ASIA, anthu ali ndi njira inayake yosankhira manda. Amaigwiritsa ntchito pomanga ndi kukongoletsa nyumba. Anthu amagula ndiponso kugulitsa katundu pogwiritsa ntchito njirayi. M’chilankhulo cha ku China njira imeneyi amaitcha kuti fêng shui, ndipo ndi njira yowombeza n’cholinga chofuna kudziŵa ngati chinthu chinachake cha panthaka chikulosera zam’tsogolo. Ngakhale kuti ku Asia anthu ambiri akhala akugwiritsa ntchito njira imeneyi kwa zaka mazana ambiri, njirayi yafikanso ku mayiko a azungu zaka zaposachedwapa. Akatswiri ena akuigwiritsa ntchito polemba mapulani a nyumba zosanjikizana zazitali kwambiri, maofesi, ndi nyumba zogona. Amayi ena amene sali pantchito akugwiritsa ntchito njirayi pokongoletsa nyumba zawo. Mabuku ndiponso Malo Achidziŵitso ambiri pa Intaneti amalimbikitsa ndi kuphunzitsa anthu za njirayi.
Kodi n’chifukwa chiyani njirayi yayamba kutchuka motere? Munthu wina amene amaikhulupirira anati njira imeneyi ingathe kuchititsa munthu “kukhala ndi moyo wabwino, thanzi labwino, ukwati wabwino kapena kugwirizana ndi anthu, kukhala ndi chuma chambiri, ndiponso mtendere.” Ngakhale kuti zinthu zonsezi n’zosangalatsa, kodi njira imeneyi ndi yotani makamaka, ndipo kodi Akristu ayenera kuiona motani?
Kodi Njirayi N’njotani Kwenikweni?
Mawu a chilankhulo cha ku China akuti fêng shui kwenikweni amatanthauza kuti “mphepo ndiponso madzi.” Fêng shui inayamba kalekale zaka masauzande ambiri zapitazo panthaŵi imene zikhulupiriro zambiri za Kum’maŵa zinkayamba. Chikhulupiriro china chomwe chinali m’gulu limeneli n’chimene ankati n’kulinganizika kwa mphamvu zachikazi ndi zachimuna zotchedwa yin ndi yang (zimene zili mdima ndi kuwala, kutentha ndi kuzizira, zinthu zoyendera pamodzi ndi zosayendera pamodzi). Chikhulupiriro cha yin ndi yang anachiphatikiza ndi chikhulupiriro chotchedwa chʼi, kutanthauza kuti “mpweya.” Mphamvu za yin, yang ndi chʼi, kuphatikizaponso zinthu monga nkhuni, dothi, madzi, moto, ndi chitsulo, zimene ankati ndizo zinthu zisanu zimene zimapanga chilengedwe chonsechi, n’zofunika kwambiri pa chikhulupiriro cha fêng shui. Anthu okhulupirira kwambiri fêng shui amakhulupirira kuti panthaka iliyonse pamadutsa mphamvu zazikulu za mtundu winawake zoyenda m’mizeremizere. Ndiyeno iwo amafuna kupeza malo enieni amene mphamvu (kapena kuti chʼi) za nthaka ndi za mlengalenga zakhala molinganizika. Amatero posintha zinthu zina panthaka yeniyeniyo kapena posintha zinthu zinazake panyumba imene ili pamalowo. Kulinganiza mphamvuzi motere akuti kumapatsa mwayi anthu amene amagwira ntchito kapena amene amakhala m’nyumbayo.
Nthaŵi zambiri akatswiri amene amatsatira njirayi amagwiritsa ntchito kampasi yolozera malo m’njira ya maula.a Kampasiyi ndi yaing’ono ndipo imakhala pakati pa tchati cha okhulupirira nyenyezi. Kampasi imeneyi imakhala ndi mizere yozungulira yokhala m’kati mwa mizere ina, ndipo n’njogaŵikanagaŵikana. Kampasi imeneyi imasonyeza zinthu monga milalang’amba, nyengo, ndiponso nthaŵi imene dziko ndi zinthu zina za mlengalenga zimakhala zikuzungulira dzuŵa. Pofufuza malo omangapo kapena pofufuza nyumba, amaunika malowo kangapo ndi kampasiyo. Katswiri wa fêng shui amaona malo amene muvi wa kampasiyo ukudutsana ndi mizere yowongoka ndiponso yozungulira imene ili kunja kwa kampasiyo, ndipo akatero amadziŵa zimene ayenera kuchita kuti “akonze” malowo.
Pokonza malo kuti akhale olinganizika amaonanso zinthu zopezeka pa malowo, mitsinje, ngalande zonyamula zoipa, ngakhalenso mmene anakhomera mawindo ndi zitseko panyumbayo. Mwachitsanzo, mayi wina wogulitsa m’sitolo ku Canada anapachika galasi lodziyang’anirapo pa chitseko cha kuseli kwa nyumba yake n’cholinga “chokonza” zitseko za m’nyumbayo kuti ziime pabwino. Anthu okhulupirira njira yowombeza malo nawonso angathe kunena kuti, kuti nyumba kapena chipinda chikhale cholinganizika, ndi bwino kusuntha maluŵa ena ake odzala a m’nyumbamo, kapena katundu wina, kuchotsa chithunzi chinachake n’kuikapo china, kuikamo mabelu olizidwa ndi mphepo, kapena kuikamo kadziŵe kansomba.
Mmene Akristu Amaonera Nkhaniyi
Nyumba zambiri zobwereketsa mabuku zimaika mabuku onena za fêng shui pagulu la mabuku onena nkhani zokhudza kukhulupirira nyenyezi ndiponso kuwombeza maula. Mabuku ena amasonyezeratu kuti njira imeneyi ndi njira yowombeza maula. Motero anthu ambiri amavomereza kuti fêng shui ndiponso njira zina zotere zili m’gulu la kuwombeza maula. Njira zimenezi zimaphatikizapo matsenga ndiponso miyambo ina yokhulupirira mizimu. Izi si zachilendo ayi pakati pa anthu.
Aisrayeli atachoka ku Igupto n’kukaloŵa m’dziko la Kanani m’zaka za m’ma 1600 B.C.E., kuwombeza maula kosiyanasiyana kunali kofala m’mayiko aŵiriŵa. Pa Deuteronomo 18:14, Mulungu ananena kudzera mwa Mose kuti: “Amitundu aŵa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero.” Mitundu yambiri ya kuwombeza maula yomwe ankachita ku Igupto ndi ku Kanani inachokera ku Babulo wakale. Yehova atasokoneza chilankhulo cha anthu a ku Babulo, iwo anafalikira kumadera osiyanasiyana ndipo anatenganso miyambo ya ku Babulo ya kuwombeza ndiponso kukhulupirira mizimu.—Genesis 11:1-9.
Yehova Mulungu anawauzitsa Aisrayeli mobwerezabwereza kuti asayambe miyambo ya kuwombeza imene mitundu ina inali kuchita. Iye anati: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga . . . Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu.” (Deuteronomo 18:9-12; Levitiko 19:26, 31) Anthu owombeza maula anayenera kuphedwa basi.—Eksodo 22:18; Levitiko 20:27.
N’chifukwa chiyani Mulungu analetsa kuwombeza maula mwamphamvu chonchi? Lemba la Machitidwe 16:16-19 limasimba za mayi wina amene anali ndi ‘mzimu wambwebwe.’ Inde kuwombeza maula n’kogwirizana kwambiri ndi ziwanda. Motero kuchita chilichonse chogwirizana ndi kuwombeza maula kungathe kum’chititsa munthu kuyamba kumvana ndi Satana ndi ziwanda zake. Mapeto ake munthuyo angafe mwauzimu.—2 Akorinto 4:4.
Njira zina zokongoletsera nyumba ndiponso zokonzera pabwalo, kaya zochokera kumayiko a ku Asia kapena kumayiko a azungu n’kutheka kuti zinabwera chifukwa cha zikhulupiriro zabodza zachipembedzo monga chikhulupiriro cha fêng shui. Komabe nthaŵi zambiri, anthu saganizako n’komwe zoti njirazi zinayamba mwachipembedzo. Komabe kugwiritsa ntchito njira ya fêng shui polosera zam’tsogolo mwa kuwombeza kapena pofuna kuti mukhale ndi mwayi kapena thanzi labwino n’kuphwanya poyera lamulo la Mulungu. Kutero n’kuphwanya lamulo la m’Baibulo losapita m’mbali lakuti tiyenera kupeŵa kukhudza chilichonse chodetsedwa.—2 Akorinto 6:14-18.
[Mawu a M’munsi]
a M’mayiko a azungu anthu ogwiritsa ntchito njirayi ayesa kuchititsa kuti ioneke ngati ndi sayansi, ndipo ena mpaka amagwiritsa ntchito makompyuta kuti afufuze malo ena ake.
[Chithunzi patsamba 15]
Kampasi yowombezera
[Mawu a Chithunzi]
Masamba 2 ndi 23: Bungwe la Hong Kong Tourism Board