Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/12 tsamba 29
  • Zochitika Padzikoli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zochitika Padzikoli
  • Galamukani!—2012
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuopsa Koheda Mpira
  • Magalimoto Oyendera Magetsi ndi Oopsa kwa Anthu Oyenda Pansi
  • Kodi Mumalidziŵa Bwino Motani Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mpira Wachitanyu Wolimbirana Chikho Chapadziko Lonse—Maseŵera Kapena Nkhondo?
    Galamukani!—1991
  • Zochitika Padzikoli
    Galamukani!—2009
Galamukani!—2012
g 11/12 tsamba 29

Zochitika Padzikoli

Ku Germany, ana pafupifupi 33 pa 100 alionse amene anabadwa mu 2010 anali apathengo. Chiwerengero chimenechi chakwera kwambiri poyerekeza ndi cha mu 1993 chomwe chinali ana 15 pa 100 alionse.—ÄRZTE ZEITUNG ndi THE LOCAL, GERMANY.

Malinga ndi kalembera yemwe anachitika mu 2010 ku United States, ana pafupifupi 70 pa 100 alionse ankakhala ndi makolo onse awiri, ana 23 pa 100 alionse ankakhala ndi mayi awo okha, ana atatu pa 100 alionse ankakhala ndi bambo awo okha ndipo ana 4 pa 100 alionse sankakhala ndi makolo awo.—​U.S. CENSUS BUREAU, U.S.A.

Mu 2011, ndalama pafupifupi madola 380 biliyoni zinawonongedwa chifukwa cha masoka a chilengedwe. Koma chivomezi cha ku Japan chinawonongetsa “ndalama zambiri kuposa kale lonse. Ndalamazi zinakwana madola 210 biliyoni, osaphatikazapo ndalama zimene zinawonongeka ku Fukushima, komwe amapangirako mphamvu zamagetsi.”​—NEW SCIENTIST, BRITAIN.

Padziko lonse, chakudya chomwe anthu amakonda kuba ndi tchizi. Padziko lonse 3 peresenti ya katundu amene amagulitsidwa m’mashopu amabedwa ndi anthu odzagula komanso anthu ogwira ntchito mushopumo.​—CENTRE FOR RETAIL RESEARCH, BRITAIN.

Kuopsa Koheda Mpira

Posewera mpira wamiyendo, osewera ambiri amakonda kumenya mpira ndi mutu. Koma kafukufuku wa posachedwapa wasonyeza kuti anthu amene amakonda kuheda mpira, m’kupita kwa nthawi akhoza kuvulala m’mutu. Malinga ndi zimene ofufuza a payunivesite ina mumzinda wa New York ku United States, ananena, kuheda mpira “kungachititse kuti munthu avulale ubongo komanso angamavutike kuphunzira ndi kumvetsa zinthu.” (Albert Einstein College of Medicine) Kafukufuku anasonyeza kuti anthu amene amangosewera mpira mwa apo ndi apo, amaheda mpira nthawi pakati pa 1,000 ndi 1,500 pa chaka, ndipo ofufuzawo anapeza kuti ubongo wa anthu amenewa unavulala. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu amene amasewera mpira nthawi zonse akhoza kuvulala kwambiri ubongo kuposa amene amangosewera mwa apo ndi apo.

Magalimoto Oyendera Magetsi ndi Oopsa kwa Anthu Oyenda Pansi

Lipoti lina lochokera ku dipatimenti yoona za kayendedwe ku United States linanena kuti: “Anthu ena akudera nkhawa anthu oyenda pansi chifukwa cha magalimoto oyendera magetsi. Magalimotowa sapanga phokoso lililonse akamayenda moti munthu amene akuyenda pansi kapena wapanjinga sangamve kuti kukubwera galimoto akafuna kuwoloka msewu. Magalimotowa akamayenda akhoza kugunda anthu ambiri poyerekeza ndi magalimoto wamba.” Chifukwa cha zimenezi, bungwe loona za kupewa ngozi zapamsewu linapempha makampani opanga magalimoto kuti aziwapanga m’njira yakuti akayamba kuyenda pang’onopang’ono azimveka kaphokoso kenakake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena