PHUNZIRO 03
Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo?
M’Baibulo muli malonjezo komanso malangizo ambiri. N’kutheka kuti mumafunitsitsa mutadziwa zimene limaphunzitsa koma mwina mumachita mantha. Kodi mukuona kuti ndi nzeru kukhulupirira malonjezo komanso malangizo a m’Baibulo lomwe ndi buku limene linalembedwa kalekale? Nanga mungakhulupirire zimene Baibulo limanena zoti n’zotheka kukhala wosangalala panopa komanso m’tsogolo? Anthu ambiri amakhulupirira zimenezi. Tiyeni tione ngati inunso mungazikhulupirire.
1. Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoona kapena n’zongopeka?
Baibulo limanena kuti uthenga wake ndi “mawu olondola a choonadi.” (Mlaliki 12:10) Limafotokoza nkhani zenizeni zokhudza anthu enieni. (Werengani Luka 1:3; 3:1, 2.) Anthu ofufuza mbiri yakale komanso asayansi apeza umboni wakuti madeti, mayina a anthu, malo ndiponso nkhani za m’Baibulo ndi zolondola.
2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo likugwirabe ntchito?
Olemba Baibulo analemba mfundo zimene pa nthawiyo ambiri sankazidziwa. Mwachitsanzo, limatha kufotokoza molondola zinthu zokhudza sayansi. Pa nthawi imene ankalemba zimenezi anthu anali asanadziwe zoona zake pa nkhanizo. Koma asayansi apanopa atsimikizira kuti zimene Baibulo limanena ndi zolondola. Mawu a m’Baibulo “ndi odalirika nthawi zonse, kuyambira panopa mpaka kalekale.”—Salimo 111:8.
3. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo?
M’Baibulo muli maulosia a “zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo.” (Yesaya 46:10) Linaneneratu nkhani zina kutatsala zaka zambiri kuti zichitike. Linaneneratunso ndendende mmene moyo ulili padzikoli masiku ano. M’phunziro lino tikambirana maulosi ena a m’Baibulo. Mudabwa kwambiri kuona kuti anakwaniritsidwa ndendende.
FUFUZANI MOZAMA
Onani kugwirizana pakati pa sayansi ndi Baibulo, ndipo fufuzani maulosi ena ochititsa chidwi a m’Baibulo.
4. Baibulo ndi lolondola pa nkhani za sayansi
Kale anthu ankakhulupirira kuti dzikoli linakhazikika pachinthu chinachake. Onerani VIDIYO.
Ndiyeno onani zimene zinalembedwa m’buku la Yobu zaka 3,500 zapitazo. Werengani Yobu 26:7, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani mfundo yakuti dzikoli lili “m’malere” ndi yodabwitsa?
Cha m’ma 1800 m’pamene anthu anamvetsa bwinobwino za kayendedwe ka madzi. Koma taonani zimene Baibulo linanena zaka pafupifupi 3,500 zapitazo. Werengani Yobu 36:27, 28, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani kufotokoza za kayendedwe ka madzi m’njira yosavuta chonchi n’kochititsa chidwi?
Kodi malemba amene mwawerengawa akuthandizani kuti muzikhulupirira kwambiri Baibulo?
5. Baibulo linaneneratu nkhani zofunika kwambiri
Werengani Yesaya 44:27–45:2, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Baibulo linaneneratu za chiyani kutatsala zaka 200 kuti ufumu wa Babulo ugonjetsedwe?
Olemba mbiri anatsimikizira kuti Mfumu Koresi ya Perisiya, inagonjetsa mzinda wa Babulo mu 539 B.C.E.b Iye ndi asilikali ake anapatutsa madzi a mumtsinje umene unkateteza mzindawo. Iwo anapeza mageti osatseka ndiye analowa mumzindawo n’kuulanda popanda kumenya nkhondo. Panopa, padutsa zaka 2,500 chigonjetsereni Babulo, koma pamalo pamene panali mzindawu sipanamangidwe chilichonse mpaka pano. Taonani zimene Baibulo linaneneratu.
Werengani Yesaya 13:19, 20, kenako mukambirane funso ili:
Kodi zimene zinachitika ku Babulo zimasonyeza bwanji kuti ulosiwu unakwaniritsidwa?
Malo amene panali mzinda wa Babulo ku Iraq
6. Baibulo linaneneratu za zinthu zimene zikuchitika masiku ano
Baibulo limasonyeza kuti masiku ano, ndi “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Taonani zimene Baibulo linaneneratu zokhudza masiku ano.
Werengani Mateyu 24:6, 7, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Baibulo linaneneratu kuti masiku otsiriza kudzachitika zotani?
Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi Baibulo linaneneratu kuti anthu ambiri adzakhala ndi makhalidwe otani?
Kodi ndi makhalidwe ati amene inuyo mwaonapo?
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Baibulo ndi buku la nkhani zongopeka basi.”
Kodi inuyo muli ndi umboni wotani wotsimikizira kuti Baibulo ndi lodalirika?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Mbiri yakale, sayansi komanso maulosi zimasonyeza kuti Baibulo ndi lodalirika.
Kubwereza
Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoona kapena n’zongopeka?
Kodi Baibulo ndi lolondola pa nkhani ziti zokhudza sayansi?
Kodi inuyo mumaona kuti Baibulo limaneneratu zam’tsogolo? N’chifukwa chiyani mukutero?
ONANI ZINANSO
Kodi Baibulo limatsutsana ndi zimene asayansi amanena?
“Kodi Sayansi Imagwirizana ndi Baibulo?” (Nkhani yapawebusaiti)
Kodi ndi zinthu ziti zomwe tiyenera kudziwa pa nkhani ya “masiku otsiriza”?
Maulosi 6 a M’Baibulo Amene Akukwaniritsidwa Masiku Ano” (Nsanja ya Olonda, May 1, 2011)
Kodi ulosi wa m’Baibulo wonena za Ufumu wa Girisi unakwaniritsidwa bwanji?
Kodi maulosi a m’Baibulo anathandiza bwanji munthu wina kusintha mmene ankaonera Baibulo?
“Ndinkaona Kuti Kulibe Mulungu” (Nsanja ya Olonda Na. 5 2017)
a Maulosi ena ndi okhudza uthenga wochokera kwa Mulungu wonena zimene zichitike m’tsogolo.
b B.C.E. amaimira “Before the Common Era,” kutanthauza nthawi yathu isanafike, ndipo C.E. amaimira “Common Era,” kutanthauza nthawi yathu ino.