PHUNZIRO 46
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudzipereka Ndiponso Kubatizidwa?
Munthu amadzipereka kwa Yehova akamulonjeza m’pemphero kuti azilambira iye yekha basi ndiponso kuti aziika zofuna za Mulungu pamalo oyamba pa moyo wake. (Salimo 40:8) Kenako amabatizidwa. Umenewu umakhala umboni wakuti anadzipereka kwa Yehova. Choncho, kudzipereka kwa Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri chimene munthu ayenera kuchita pa moyo wake. Ndiye popeza kudzipereka kwa Yehova n’kofunika kwambiri ndiponso kungasinthe moyo wanu, n’chiyani chingakulimbikitseni kuti musankhe kuchita zimenezi?
1. N’chifukwa chiyani munthu amasankha kudzipereka kwa Yehova?
Timadzipereka kwa Yehova chifukwa chakuti timamukonda kwambiri. (1 Yohane 4:10, 19) Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.” (Maliko 12:30) Zolankhula komanso zochita zathu zimasonyeza kuti timakonda Mulungu. Zimenezi tingaziyerekezere ndi mwamuna ndi mkazi omwe amasankha kukwatirana chifukwa choti akondana. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene amakonda Yehova. Chikondicho chimamupangitsa kuti adzipereke kwa iye komanso kubatizidwa.
2. Kodi Yehova amadalitsa bwanji atumiki ake amene abatizidwa?
Mukabatizidwa mudzalowa m’banja labwino kwambiri la Yehova. Kenako mudzaona kuti Yehova amakukondani kwambiri m’njira zosiyanasiyana ndipo mudzakhala naye pa ubwenzi wolimba kuposa panopa. (Werengani Malaki 3:16-18.) Mudzayamba kuona kuti Yehova ndi Atate wanu ndipo mudzakhala ndi abale ndi alongo padziko lonse lapansi amene amakonda Yehova komanso omwe amakukondani kwambiri. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Komabe, pali zinthu zina zimene mukuyenera kuchita musanabatizidwe. Mukufunika kuphunzira zokhudza Yehova, kumukonda komanso kukhulupirira Mwana wake. Kenako mudzipereke kwa Yehova, kutanthauza kuti mumuuze m’pemphero kuti mudzamutumikira moyo wanu wonse. Mukachita zinthu zimenezi n’kubatizidwa mudzakhala ndi mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amanena kuti: “Tsopano ubatizo . . . ukupulumutsanso inuyo.”—1 Petulo 3:21.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake mukuyenera kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa.
3. Tonsefe tifunika kusankha amene tikufuna kumutumikira
Kale ku Isiraeli, anthu ena ankaganiza kuti akhoza kumalambira Yehova kwinaku akulambira Baala amene anali mulungu wabodza. Koma Yehova anatumiza mneneri wake Eliya kuti akathandize anthuwo kuzindikira kuti kuchita zimenezi si koyenera. Werengani 1 Mafumu 18:21, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Aisiraeli ankafunika kusankha kuchita chiyani?
Mofanana ndi Aisiraeli, ifenso tikufunikira kusankha amene tikufuna kumutumikira. Werengani Luka 16:13, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani sitikuyenera kumalambira Yehova kwinaku tikulambiranso munthu kapena chinthu chinachake?
Kodi Yehova tingamusonyeze bwanji kuti tinasankha kutumikira iye yekha basi?
4. Muziganizira zimene Yehova amachita posonyeza kuti amakukondani
Yehova watipatsa mphatso zambiri zamtengo wapatali. Ndiye kodi ifeyo tingamupatse chiyani? Onerani VIDIYO.
Kodi Yehova wakusonyezani chikondi m’njira ziti? Werengani Salimo 104:14, 15 ndi 1 Yohane 4:9, 10, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi mphatso ziti zimene Yehova wakupatsani zimene mumaziyamikira kwambiri?
Kodi mphatso zimenezo zikukuchititsani kuti muzimuona bwanji Yehova?
Munthu akatipatsa mphatso inayake imene yatisangalatsa kwambiri timamuyamikira. Werengani Deuteronomo 16:17, kenako mukambirane funso ili:
Mukaganizira zonse zimene Yehova amakuchitirani, kodi mukuona kuti mungamupatse chiyani?
5. Tikadzipereka kwa Yehova timapeza madalitso ambiri
Anthu ambiri amaganiza kuti angakhale osangalala ngati atakhala otchuka, ngati akugwira ntchito yabwino kapenanso ngati ali ndi ndalama zambiri. Koma kodi zimenezi n’zoona? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
N’chifukwa chiyani Andrey anasankha kusiya kusewera mpira ngakhale kuti ankaukonda kwambiri?
Kodi mukuganiza kuti anachita bwino kusiya kusewera mpira n’kudzipereka kwa Yehova? N’chifukwa chiyani mukutero?
Mtumwi Paulo asanakhale Mkhristu ankagwira ntchito yapamwamba. Iye anali atachita maphunziro okhudza malamulo Achiyuda ndipo anaphunzitsidwa ndi mphunzitsi wotchuka kwambiri pa nthawiyo. Koma anasiya zonsezi n’kukhala Mkhristu. Kodi Paulo ananong’oneza bondo ndi zimene anasankhazi? Werengani Afilipi 3:8, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti zimene ankachita poyamba asanakhale Mkhristu zinali ngati “mulu wa zinyalala”?
Nanga anapeza madalitso otani chifukwa cha zimene anasankhazi?
Kodi mukuganiza kuti moyo wanu ungakhale wabwino kwambiri ngati mutasankha kutumikira Yehova? N’chifukwa chiyani mukutero?
Paulo atakhala Mkhristu anapeza zinthu zambiri kuposa zimene anasiya
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Munthu sufunika kuchita kudzipereka kwambiri kwa Mulungu, bola ngati umapemphera basi.”
N’chifukwa chiyani mukuona kuti kudzipereka kwa Yehova n’kofunika kwambiri?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Timadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa chifukwa choti timamukonda.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kumukonda komanso kumulambira ndi mtima wathu wonse?
Kodi Yehova amadalitsa bwanji atumiki ake omwe abatizidwa?
Kodi inuyo mungakonde kupereka moyo wanu kwa Yehova?
ONANI ZINANSO
Onani chifukwa chake woimba wina komanso katswiri wamasewera a mpira anasankha kudzipereka kwa Yehova.
Zimene Achinyamata Amafunsa—Kodi Ndidzachita Zotani Pamoyo Wanga?—Zimene Anasankha (6:54)
Onani zifukwa zinanso zimene zingapangitse munthu kuti adzipereke kwa Yehova.
“N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudzipereka kwa Yehova?” (Nsanja ya Olonda, January 15, 2010)
Onerani nyimboyi kuti muone mmene anthu omwe amadzipereka kwa Yehova amasangalalira.
Munkhani yakuti, “Kwa Zaka Zambiri Ndinkadzifunsa Kuti, ‘Kodi Mulungu Anatilengeranji Anthufe?’” onani zimene zinachititsa munthu wina kuganiziranso zinthu zimene ankaziona kuti ndi zofunika pa moyo wake.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2012)