NKHANI YOPHUNZIRA 24
NYIMBO NA. 98 Malemba Anauziridwa Ndi Mulungu
Zimene Tikuphunzira pa Ulosi wa Yakobo Atatsala Pang’ono Kumwalira—Gawo 1
“Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzachitike kwa inu mʼtsogolo.”—GEN. 49:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi, tiona zimene tikuphunzira pa ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira wokhudza Rubeni, Simiyoni, Levi ndi Yuda.
1-2. Kodi Yakobo anachita chiyani atatsala pang’ono kumwalira, nanga n’chifukwa chiyani? (Onaninso chithunzi .)
PANALI patapita zaka pafupifupi 17 kuchokera pamene Yakobo, yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova anachoka ku Kanani kupita ku Igupto ndi banja lake. (Gen. 47:28) Pa nthawiyo iye anasangalala kukumananso ndi mwana wake Yosefe yemwe ankamukonda kwambiri komanso kuona banja lake lonse lili pamodzi. Koma tsopano Yakobo anadziwa kuti anali atatsala pang’ono kumwalira, choncho anakonza zoti alankhule ndi banja lake lonse.—Gen. 49:28.
2 Pa nthawiyo sizinali zachilendo kuti munthu yemwe ndi mutu wabanja aitanitse banja lake lonse kuti apereke malangizo omaliza. (Yes. 38:1) Pamsonkhano umenewo, n’kutheka kuti iye ankatchulanso munthu amene angatsogolere banjalo iye akamwalira.
Yakobo atatsala pang’ono kumwalira akupereka ulosi kwa ana ake 12 (Onani ndime 1-2)
3. Mogwirizana ndi Genesis 49:1, 2, n’chifukwa chiyani zimene Yakobo analankhula zili zofunika kwambiri?
3 Werengani Genesis 49:1, 2. Umenewu si unalitu msonkhano wamba. Yakobo anali mneneri ndipo pamsonkhanowu, Yehova anauzira mtumiki wakeyu kuti anene zinthu zofunika kwambiri zokhudza ana ake, zomwe zidzachitike m’tsogolo. Choncho zimene Yakobo analankhula pa nthawiyo zinali ulosi.
4. Kodi tiziganizira chiyani tikamakambirana ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira? (Onaninso tchati chakuti “Banja la Yakobo.”)
4 Mu nkhaniyi, tiona zimene Yakobo anauza ana ake 4 omwe ndi Rubeni, Simiyoni, Levi ndi Yuda. Ndipo munkhani yotsatira, tidzaona zimene anauza ana ake ena 8. Monga mmene tionere, zimene Yakobo analankhula ndi ana ake zinkakhudzanso mbadwa zawo, zomwe zinadzakhala mtundu wa Isiraeli. Zimene zinachitikira mtunduwu zitithandiza kuona mmene ulosi wa Yakobo unakwaniritsidwira. Ndipo tikamakambirana zimene Yakobo ananena, tionanso mfundo zofunika zomwe zingatithandize kuti tizisangalatsa Atate wathu wakumwamba Yehova.
RUBENI
5. Kodi Rubeni ayenera kuti ankayembekezera kulandira madalitso otani kuchokera kwa bambo ake?
5 Poyankhula ndi mwana wake Rubeni, Yakobo anati: “Iwe ndi mwana wanga woyamba kubadwa.” (Gen. 49:3) Monga mwana woyamba kubadwa, Rubeni ayenera kuti ankayembekezera kulandira chuma chambiri kuposa abale ake. Ayeneranso kuti ankayembekezera kukhala mtsogoleri wa banjalo bambo ake akamwalira komanso kudzapatsira ana ake cholowachi.
6. Kodi chinachitika n’chiyani kuti Rubeni asalandire cholowa cha mwana woyamba kubadwa? (Genesis 49:3, 4)
6 Rubeni anataya mwayi wolandira cholowa cha mwana woyamba kubadwa. (1 Mbiri 5:1) Chifukwa chiyani? Zaka zingapo m’mbuyomo, iye anagona ndi mkazi wamng’ono wa bambo ake dzina lake Biliha. Biliha anali wantchito wa Rakele yemwe anali mkazi wokondedwa wa Yakobo. (Genesis 35:19, 22) Rubeni anali mwana wa mkazi wina wa Yakobo dzina lake Leya. N’kutheka kuti Rubeni anagona ndi Biliha chifukwa cholephera kukhala wodziletsa kapenanso poopa kuti bambo ake angayambe kukonda kwambiri Bilihayo m’malo mwa mayi ake. Kaya iye anachita izi pa zifukwa zotani, zimene anachitazo sizinasangalatse Yehova komanso bambo ake.—Werengani Genesis 49:3, 4.
7. Kodi n’chiyani chinachitikira Rubeni ndi mbadwa zake? (Onaninso bokosi lakuti “Ulosi wa Yakobo Atatsala Pang’ono Kumwalira.”)
7 Yakobo anauza Rubeni kuti: “Sudzakhala wapamwamba kuposa abale ako.” Mawu amenewa anakwaniritsidwa chifukwa palibe mwana aliyense wa Rubeni amene anadzakhala mfumu, wansembe kapena mneneri. Komabe Yakobo anapatsa Rubeni cholowa ndipo banja lake linakhala limodzi mwa mafuko a Isiraeli. (Yos. 12:6) Rubeni anasonyeza makhalidwe abwino pa zochitika zina ndipo palibe paliponse pomwe pamanena kuti iye anachitanso chiwerewere.—Gen. 37:20-22; 42:37.
8. Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera kwa Rubeni?
8 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kuyesetsa kuti tikhale odziletsa n’kumapewa chiwerewere. Ngati tayesedwa kuti tichite tchimo, tiziima kaye n’kuganizira mmene zingakhudzire Yehova, banja lathu komanso anthu ena. Tizikumbukira kuti “chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agal. 6:7) Zimene zinachitikira Rubeni zikutikumbutsanso kuti Yehova ndi wachifundo. Ngakhale kuti Yehova sangatiteteze ku zotsatirapo za zimene talakwitsa, iye adzatidalitsa tikamayesetsa kuchita zabwino.
SIMIYONI NDI LEVI
9. N’chifukwa chiyani Yakobo sanasangalale ndi Simiyoni ndi Levi? (Genesis 49:5-7)
9 Werengani Genesis 49:5-7. Kenako Yakobo analankhula mawu amphamvu osonyeza kuti sanasangalale ndi Simiyoni ndi Levi. Zaka zingapo m’mbuyomo, mwana wamkazi wa Yakobo dzina lake Dina anagwiriridwa ndi mwamuna wina wa Chikanani dzina lake Sekemu. N’zoona kuti ana Yakobo anakwiya ndi zimene zinachitikira mchemwali wawo, koma Simiyoni ndi Levi analephera kulamulira mkwiyo wawo. Iwo ananama kuti akhazikitsa mtendere ndi amuna a ku Sekemu ngati angavomere kuti adulidwe ndipo iwo anavomera. Amunawo akumvabe ululu chifukwa cha kudulidwako, Simiyoni ndi Levi, “aliyense anatenga lupanga lake nʼkukalowa mumzindawo anthuwo asakuyembekezera ndipo anapha mwamuna aliyense.”—Gen. 34:25-29.
10. Kodi ulosi wa Yakobo wokhudza Simiyoni ndi Levi unakwaniritsidwa bwanji? (Onaninso bokosi lakuti “Ulosi wa Yakobo Atatsala Pang’ono Kumwalira.”)
10 Yakobo anakhumudwa kwambiri ndi zachiwawa zimene ana ake awiri anachita. Iye analosera kuti mbadwa zawo zidzamwazikana komanso kubalalitsidwa mu Isiraeli. Ulosi umenewu unakwaniritsidwa patapita zaka 200 pamene Aisiraeli analowa m’Dziko Lolonjezedwa. Ana a Simiyoni anapatsidwa mizinda ina pakati pa cholowa cha fuko la Yuda. (Yos. 19:1) Ana a Levi anapatsidwa mizinda 48 m’dziko lonse la Isiraeli.—Yos. 21:41.
11. Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene mafuko a Simiyoni ndi Levi anachita?
11 Ana a Simiyoni ndi Levi sanabwereze zoipa zimene makolo awo anachita. Ana a fuko la Levi ankalambira Yehova mokhulupirika. Pamene Mose anapita m’phiri la Sinai kukalandira Chilamulo kuchokera kwa Yehova, Aisiraeli ambiri anayamba kulambira mwana wa ng’ombe. Koma Alevi anakhala kumbali ya Mose ndipo anamuthandiza powononga fanolo komanso anthu amene ankalilambira. (Eks. 32:26-29) Yehova anapatula mtundu wa Levi ndipo anawapatsa mwayi wamtengo wapatali woti azitumikira monga ansembe. (Eks. 40:12-15; Num. 3:11, 12) Pamene ankalanda Dziko Lolonjezedwa, ana a Simiyoni molimba mtima anamenya nkhondo limodzi ndi ana a Yuda mogwirizana ndi zimene Yehova ankafuna.—Ower. 1:3, 17.
12. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Simiyoni ndi Levi?
12 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tisamalole kusankha kapena kuchita zinthu titakwiya. N’zoona kuti ifeyo kapena munthu yemwe timamukonda akachitiridwa zopanda chilungamo tingakhumudwe. (Sal. 4:4) Komabe tizikumbukira kuti Yehova samasangalala ngati titalankhula kapena kuchita zinthu chifukwa chosonyeza kuti takwiya. (Yak. 1:20) Mkhristu mnzathu kapena munthu wina akatichitira zopanda chilungamo, timagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo n’cholinga choti zolankhula kapena zochita zathu zisavulaze ena. (Aroma 12:17, 19; 1 Pet. 3:9) Ngakhale makolo anu atachita zinthu zimene sizikusangalatsa Yehova, muzikumbukira kuti simuyenera kutengera chitsanzo chawo. Musamaganize kuti simungathe kusangalatsa Yehova kapenanso kuti iye sangakudalitseni. Yehova adzakudalitsani komanso kukuthandizani kuti mupitirize kuchita zoyenera.
YUDA
13. Kodi Yuda ayenera kuti ankadera nkhawa za chiyani itafika nthawi yoti bambo ake amulankhule?
13 Tsopano inali nthawi yoti Yakobo alankhule ndi mwana wake Yuda. Atamva zimene bambo ake anauza azichimwene ake, Yuda ayenera kuti anada nkhawa chifukwa nayenso anali atalakwitsapo zinthu zina. Iye anathandizana ndi abale ake pokalanda katundu wa mumzinda wa Sekemu. (Gen. 34:27) Iye anagwirizananso ndi abale ake pogulitsa Yosefe ngati kapolo ndiponso kunamiza bambo awo za zimene zinachitika. (Gen. 37:31-33) Pambuyo pake anagona ndi mpongozi wake Tamara poganiza kuti anali hule.—Gen. 38:15-18.
14. Kodi ndi zabwino ziti zomwe Yuda anachita? (Genesis 49:8, 9)
14 Mouziridwa, Yakobo anangopereka madalitso komanso kuyamikira Yuda. (Werengani Genesis 49:8, 9.) Yuda anasonyeza kuti ankakonda komanso kuganizira bambo ake omwe anali achikulire. Komanso pa nthawi ina anasonyeza kuti ankakonda kwambiri mng’ono wake Benjamini.—Gen. 44:18, 30-34.
15. Kodi malonjezo amene Yuda anapatsidwa anakwaniritsidwa bwanji?
15 Yakobo analosera kuti Yuda azidzatsogolera abale ake. Koma panatenga nthawi yaitali kuti ulosiwu ukwaniritsidwe. Patapita zaka 200, pamene Aisiraeli ankachoka ku Igupto kudutsa m’chipululu kupita ku Dziko Lolonjezedwa, fuko la Yuda ndi limene linkayambirira kunyamuka ndipo mafuko enawo ankawatsatira. (Num. 10:14) M’zaka zotsatira, fuko la Yuda ndi limene linatsogolera pa nkhondo yogonjetsa Akanani m’Dziko Lolonjezedwa. (Ower. 1:1, 2) Komanso Davide, yemwe anali mbadwa ya Yuda, ndi amene anali woyamba mumzere wa mafumu ochokera m’fukoli. Komatu si zokhazi.
16. Kodi ulosi wa pa Genesis 49:10 unakwaniritsidwa bwanji? (Onaninso bokosi lakuti “Ulosi wa Yakobo Atatsala Pang’ono Kumwalira.”)
16 Yakobo ananena kuti Wolamulira amene adzalamulire anthu mpaka kalekale adzachokera m’fuko la Yuda. (Werengani Genesis 49:10 ndi mawu a m’munsi.) Wolamulira ameneyo ndi Yesu Khristu amene Yakobo anamutchula kuti Silo. Ponena za Yesu, mngelo ananena kuti: “Yehova Mulungu adzamupatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake.” (Luka 1:32, 33) Yesu amatchedwanso “Mkango wa fuko la Yuda.”—Chiv. 5:5.
17. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani ya mmene timaonera anthu ena?
17 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova anadalitsa Yuda ngakhale kuti analakwitsa zinthu zina. Koma kodi n’kutheka kuti abale ake a Yuda anadabwa kuti Yehova anaona chiyani mwa iye kuti amudalitse? Kaya ankaganiza zotani, Yehova anaona zabwino mwa Yuda ndipo anamudalitsa chifukwa cha zimenezo. Ndiye kodi tingamutsanzire bwanji Yehova? Mkhristu mnzathu akapatsidwa mwayi winawake wa utumiki n’kutheka kuti tingayambe kuganizira zimene amalakwitsa. Koma tingachite bwino kukumbukira kuti Yehova amasangalala ndi makhalidwe ake abwino. Yehova amaona zabwino mwa atumiki ake. Ifenso tiziyesetsa kuchita zimenezo.
18. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima?
18 Chinthu china chimene tingaphunzire pa zimene zinachitikira Yuda ndi kufunika kokhala oleza mtima. Nthawi zonse Yehova amakwaniritsa zimene walonjeza koma si nthawi zonse pamene amachita zimenezi m’njira kapena pa nthawi imene ife timayembekezera. Mbadwa za Yuda sizinayambe nthawi yomweyo kutsogolera anthu a Mulungu. Koma iwo ankathandiza mokhulupirika anthu amene Yehova wawasankha, kaya ndi Mose yemwe anali Mlevi, Yoswa yemwe anali wa fuko la Efuraimu, kapenanso Mfumu Sauli yemwe anali wa fuko la Benjamini. Ifenso tizithandiza aliyense amene Yehova angasankhe kuti azititsogolera masiku ano.—Aheb. 6:12.
19. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza Yehova kuchokera pa ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira?
19 Kodi pofika pano taphunzira chiyani pa ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira? N’zoonekeratu kuti “mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera.” (1 Sam. 16:7) Yehova ndi woleza mtima kwambiri komanso ndi wokhululuka. Ngakhale kuti samalekerera zoipa, sayembekezeranso kuti atumiki ake azichita zinthu osalakwitsa kalikonse. Iye akhoza kudalitsa anthu amene analakwitsa kwambiri zinthu m’mbuyomu ngati analapa n’kuyamba kuchita zabwino. Munkhani yotsatira, tidzakambirana zimene Yakobo anauza ana ake ena 8.
NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse