Macitidwe a Atumwi
6 Tsopano m’masiku amenewo pamene ophunzila anali kuwonjezeka, Ayuda okamba Cigiriki anayamba kudandaula za Ayuda okamba Ciheberi, cifukwa akazi amasiye a Cigiriki anali kunyalanyazidwa pa kagawidwe ka cakudya ca tsiku ndi tsiku. 2 Conco atumwi 12 aja anasonkhanitsa khamu la ophunzila n’kunena kuti: “Sibwino* kuti ife tilekeze kuphunzitsa mawu a Mulungu n’kuyamba kugawa cakudya. 3 Conco abale, sankhani amuna 7 pakati panu a mbili yabwino, odzala ndi mzimu komanso nzelu kuti tiwapatse udindo wosamalila nchitoyi. 4 Koma ife tidzadzipeleka pa kupemphela ndi kuphunzitsa mawu a Mulungu.” 5 Zimene anakamba zinasangalatsa khamu lonse, moti anasankha Sitefano munthu wacikhulupililo colimba, ndiponso wodzala ndi mzimu woyela. Anasankhanso Filipo, Pulokoro, Nikanora, Timoni, Pamenasi, komanso Nikolao wocokela ku Antiokeya, wotembenukila ku Ciyuda. 6 Iwo anawapeleka kwa atumwi, ndipo atumwiwo atawapemphelela anaika manja pa amunawo.
7 Zitatelo, mawu a Mulungu anapitiliza kufalikila, ndipo ciwelengelo ca ophunzila cinali kuwonjezeka kwambili mu Yerusalemu. Ngakhale ansembe ambili anakhala okhulupilila.
8 Tsopano Sitefano wokondedwa ndi Mulungu, komanso amene Mulungu anamupatsa mphamvu, anali kucita zodabwitsa zazikulu ndi zizindikilo pakati pa anthu. 9 Koma amuna ena a gulu lochedwa Sunagoge wa Omasulidwa anabwela pamodzi ndi anthu a ku Kurene, a ku Alekizandiriya, ku Kilikiya komanso ku Asia kudzatsutsana ndi Sitefano. 10 Koma iwo sanathe kulimbana naye cifukwa ca nzelu zake komanso mzimu umene anali nawo polankhula. 11 Zitatelo, iwo ananyengelela mseli anthu kuti anene kuti: “Ife tamumva akulankhula zinthu zonyoza Mose komanso Mulungu.” 12 Iwo anatuntha gulu la anthu, akulu komanso alembi, kuti amugwile modzidzimutsa n’kupita naye ku Bungwe Lalikulu la Ayuda.* 13 Iwo anabweletsa mboni zonama zimene zinakamba kuti: “Munthu uyu akungolankhula zinthu zambili zonyoza malo oyelawa komanso Cilamulo. 14 Mwacitsanzo, tamumva akunena kuti Yesu Mnazareti adzagwetsa malo ano n’kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”
15 Ndipo anthu onse amene anali m’Bungwe Lalikulu la Ayuda, atamuyang’anitsitsa Sitefano, anaona kuti nkhope yake inali kuoneka ngati ya mngelo.