Kwa Aefeso
4 Cotelo, ine amene ndine mkaidi cifukwa ca Ambuye, ndikukucondelelani kuti muziyenda malinga ndi ciitano cimene munalandila. 2 Muziyenda modzicepetsa kwambili,* mofatsa, moleza mtima, ndiponso muzilolelana wina ndi mnzake mwacikondi. 3 Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi umene mzimu woyela umatithandiza kukhala nao kudzela mu mtendele, umene uli ngati comangila cotigwilizanitsa. 4 Pali thupi limodzi ndi mzimu umodzi, mogwilizana ndi ciyembekezo cimodzi cimene anakuitanilani. 5 Palinso Ambuye mmodzi, cikhulupililo cimodzi, ndi ubatizo umodzi. 6 Palinso Mulungu mmodzi, amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwila nchito kudzela mwa onse, ndipo ali mwa onse.
7 Tsopano aliyense wa ife anacitilidwa cisomo malinga ndi mmene Khristu anamupimila mphatso yauleleyi. 8 Paja Malemba amati: “Atakwela pamalo apamwamba anatenga anthu ogwidwa ukapolo, ndipo anapeleka mphatso za amuna.” 9 Ndiye kodi liu lakuti “atakwela” limatanthauza ciani? Limatanthauza kuti coyamba anatsika pansi, kutanthauza padziko lapansi. 10 Amene anatsikayo ndi amenenso anakwela kukakhala pamwamba kwambili kuposa kumwamba konse, kuti akwanilitse zinthu zonse.
11 Pa mphatso zimene anapelekazo, anapeleka ena kukhala atumwi, ena aneneli, ena alaliki,* ena abusa, ndipo ena aphunzitsi. 12 Anatelo pofuna kuthandiza* oyelawo kuti aziyenda m’njila yoyenela, kuti azigwila nchito yotumikila ena, komanso kuti amange mpingo umene ndi thupi la Khristu. 13 Colinga n’cakuti tonse tidzakhale ogwilizana pa zimene timakhulupilila, komanso podziwa molondola Mwana wa Mulungu. Zikadzatelo, tidzakhala acikulile, amene afika pamsinkhu wa munthu wamkulu, ngati umene Khristu anafikapo. 14 Conco tisakhalenso ana, otengeka-tengeka ngati kuti mafunde akutikankha, ndiponso otengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya ciphunzitso conyenga ca anthu, ya mabodza amene anthu amapeka mwamacenjela. 15 Koma tizilankhula zoona ndiponso kuonetsana cikondi. Tikatelo tidzakhala acikulile m’zinthu zonse, ndipo tidzatha kucita zinthu mogwilizana ndi Khristu, amene ndi mutu. 16 Tili ngati thupi, ndipo cifukwa ca iye, ziwalo zonse za thupi limeneli ndi zolumikizana bwino, ndipo zimathandizana kuti thupilo lizigwila bwino nchito. Ciwalo ciliconse ca thupili cikamagwila nchito yake thupili limakula bwino ndipo limamangika m’cikondi.
17 Conco ndikunena komanso kucitila umboni mwa Ambuye, kuti muleke kuyenda ngati mmene anthu a mitundu ina amayendela, potsatila maganizo ao opanda pake.* 18 Maganizo ao ali mumdima, ndipo iwo ndi otalikilana ndi moyo wocokela kwa Mulungu cifukwa ca umbuli wao, komanso cifukwa ca kuuma mtima kwao. 19 Popeza iwo sakukwanitsanso kuzindikila makhalidwe abwino, anadzipeleka okha ku khalidwe lotayilila,* kuti acite zonyansa za mtundu uliwonse mwadyela.
20 Koma inu simunaphunzile Khristu kukhala wotelo. 21 Zikanakhala conco ngati munamvadi zimene anali kuphunzitsa komanso ngati iye ndiye anakuphunzitsani, paja coonadi cili mwa Yesu. 22 Munaphunzitsidwa kuti mubvule umunthu wakale umene umagwilizana ndi makhalidwe anu akale umenenso ukuipitsidwa ndi zilakolako za umunthuwo. 23 Ndipo pitilizani kusintha kuti mukhale atsopano pa kaganizidwe kanu.* 24 Komanso mubvale umunthu watsopano umene unalengedwa malinga ndi cifunilo ca Mulungu m’cilungamo ceniceni ndi kukhulupilika.
25 Conco, popeza tsopano mwataya cinyengo, aliyense wa inu azilankhula zoona kwa mnzake, cifukwa ndife ziwalo zolumikizana. 26 Kwiyani, koma musacimwe. Dzuwa lisalowe muli cikwiile. 27 Musamupatse mpata* Mdyelekezi. 28 Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwila nchito mwakhama. Azigwila nchito yabwino ndi manja ake kuti azikwanitsa kupeza zinthu zimene angagawane ndi munthu wosowa. 29 Pakamwa panu pasamatuluke mau owola, koma pazituluka mau abwino okha, kuti alimbikitse ena pakafunika kutelo, kutinso apindulile anthu amene akumvetsela. 30 Komanso musamamvetse cisoni mzimu woyela wa Mulungu, umene iye anausewenzetsa pokuikani cidindo kaamba ka tsiku limene mudzapulumutsidwe ndi dipo.
31 Cidani, kupsya mtima, mkwiyo, kulalata, mau acipongwe, komanso zinthu zonse zoipa zicotsedwe mwa inu. 32 Koma muzikomelana mtima, muzicitilana cifundo, komanso muzikhululukilana ndi mtima wonse, ngati mmene inunso Mulungu anakukhululukilani ndi mtima wonse kupitila mwa Khristu.