Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
21 Tsopano Yesu atakweza maso ake, anaona anthu olemela akuponya mphatso zawo m’zoponyamo zopeleka.* 2 Kenako anaona mkazi wamasiye wosauka akuponyamo tumakobili tuwili tocepa mphamvu kwambili.* 3 Kenako anati: “Ndithu ndikukuuzani, mayi wamasiye wosaukayu waponyamo zambili kuposa onse. 4 Pakuti onsewa aponyamo mphatso zimene atapapo pa zoculuka zimene ali nazo. Koma mayiyu, ngakhale kuti ndi wosauka, wapeleka zonse zimene anali nazo, zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”
5 Pambuyo pake, pamene anthu ena anali kukambilana zokhudza kacisi, mmene anamukongoletsela ndi miyala yokongola komanso zinthu zopelekedwa kwa Mulungu, 6 iye anati: “Kunena za zinthu izi zomwe mukuona palipano, masiku adzafika pamene sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.” 7 Kenako anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti makamaka, nanga cizindikilo cakuti zinthu zimenezi zili pafupi kucitika cidzakhala ciyani?” 8 Iye anati: “Samalani kuti asadzakusoceletseni, pakuti ambili adzabwela m’dzina langa n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine.’ Adzanenanso kuti, ‘Nthawi ija ili pafupi.’ Musakawatsatile. 9 Komanso mukadzamva za nkhondo ndiponso zacipolowe,* musadzacite mantha. Pakuti zimenezi ziyenela kucitika coyamba, koma mapeto sadzafika nthawi yomweyo.”
10 Kenako anawauza kuti: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. 11 Kudzakhala zivomezi zamphamvu, ndipo kumalo osiyanasiyana kudzakhala njala ndi milili. Ndipo kudzaoneka zinthu zocititsa mantha, komanso kumwamba kudzaoneka zizindikilo zodabwitsa.
12 “Koma zinthu zonsezi zisanacitike, anthu adzakugwilani n’kukuzunzani, ndipo adzakupelekani kumasunagoge komanso ku ndende. Adzakupelekani kwa mafumu ndi kwa abwanamkubwa cifukwa ca dzina langa. 13 Zimenezi zidzakupatsani mwayi wocitila umboni. 14 Conco tsimikizani m’mitima yanu kuti musayeseze pasadakhale mmene mukadzitetezele. 15 Pakuti ine ndidzakuuzani mawu amene mudzakamba, ndi kukupatsani nzelu zimene onse okutsutsani sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa. 16 Komanso ngakhale makolo anu, abale anu, acibale anu ndi anzanu adzakupelekani, ndipo iwo adzapha ena a inu. 17 Ndiponso anthu onse adzakudani cifukwa ca dzina langa. 18 Koma ngakhale tsitsi limodzi la m’mutu mwanu silidzawonongeka. 19 Mukadzapilila mudzasunga miyoyo yanu.*
20 “Koma mukadzaona kuti Yerusalemu wazungulilidwa ndi magulu ankhondo, mukadziwe kuti ciwonongeko cake cayandikila. 21 Pamenepo, amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawila ku mapili, ndipo amene adzakhale mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Komanso amene adzakhale m’madela a kumidzi asadzalowemo, 22 cifukwa amenewa adzakhala masiku opeleka ciweluzo,* kuti zinthu zonse zimene zinalembedwa zikwanilitsidwe. 23 Tsoka kwa akazi apathupi komanso oyamwitsa m’masiku amenewo! Cifukwa padzakhala mavuto aakulu padzikoli, komanso mkwiyo udzakhala pa anthu awa. 24 Iwo adzaphedwa ndi lupanga, ndipo adzatengedwa ukapolo n’kupita nawo ku mitundu ina yonse. Anthu a mitundu* ina adzapondaponda Yerusalemu mpaka nthawi zoikika za anthu a mitundu* inayo zitakwana.
25 “Komanso padzakhala zizindikilo pa dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi. Anthu padziko lapansi pano adzakhala m’masautso aakulu, ndipo adzathedwa nzelu cifukwa ca mkokomo wa nyanja ndi kuwinduka kwake. 26 Anthu adzakomoka cifukwa ca mantha komanso cifukwa coyembekezela zinthu zimene zidzacitikila dziko lapansi kumene kuli anthu. Pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 27 Ndiyeno iwo adzaona Mwana wa munthu akubwela mu mtambo, ali ndi mphamvu komanso ulemelelo waukulu. 28 Koma zinthu zimenezi zikadzayamba kucitika, mukaime cilili ndi kutukula mitu yanu, cifukwa cipulumutso canu cayandikila.”
29 Iye atakamba zimenezi, anawauza fanizo kuti: “Yang’anani mtengo wamkuyu ndi mitengo ina yonse. 30 Mukaona kuti mitengoyo yayamba kuphuka, mumadziwa kuti dzinja layandikila. 31 Mofananamo, inunso mukadzaona zinthu zimenezi zikucitika, mukadziwe kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. 32 Ndithu ndikukuuzani, m’badwo uwu sudzatha wonse mpaka zinthu zonsezi zitacitika. 33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mawu anga sadzacoka ayi.
34 “Koma samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambili, kumwa kwambili, komanso nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikileni modzidzimutsa 35 monga msampha. Pakuti tsikulo lidzafikila onse okhala pa dziko lapansi. 36 Conco khalanibe maso, ndipo muzipemphela mopembedzela, kuti mukathe kuthawa zinthu zonsezi zimene ziyenela kucitika, komanso kuti mukathe kuimilila pamaso pa Mwana wa munthu.”
37 Masana, iye anali kuphunzitsa m’kacisi, koma usiku anali kutuluka mu mzinda n’kukagona ku phili lochedwa Phili la Maolivi. 38 Ndipo anthu onse anali kubwela kukacisi m’mamawa kudzamumvetsela.