LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 3/1 masa. 13-122
  • Mmene Tingakhalilebe ndi Maganizo Oyenela

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingakhalilebe ndi Maganizo Oyenela
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • GWILITSILANI NCHITO BAIBULO KUTI MUKHALE NDI MAGANIZO OYENELA
  • MKAZI WAMASIYE WOSAUKA
  • “COTSANI MOYO WANGA”
  • “PEMPHELO LA MUNTHU WOSAUTSIKA”
  • Kodi Nthawi Zina Umaona kuti Uli Wekha Ndipo Ukucita Mantha?
    Phunzitsani Ana Anu
  • Mwana wa Mkazi Wamasiye Aukitsidwa
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yehova Alimbikitsa Eliya
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Dalilani Yehova Pamene Muli na Nkhawa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 3/1 masa. 13-122

Mmene Tingakhalilebe ndi Maganizo Oyenela

“Munthu atakhala ndi moyo zaka zambili, m’zaka zonsezo azisangalala.”—MLAL. 11:8.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi n’ciani cingatilepheletse kukhalabe ndi maganizo oyenela?

  • Kodi tingagwilitsile nchito bwanji Baibulo kuti tikhalebe ndi maganizo oyenela?

  • Kodi zitsanzo za mkazi wamasiye wosauka, Eliya, ndi wolemba Salimo 102, zingatithandize bwanji kukhala ndi maganizo oyenela?

1. Kodi Yehova watidalitsa bwanji kuti tikhale osangalala?

YEHOVA afuna kuti tikhale acimwemwe, ndipo amatipatsa madalitso ambili kuti tikhale osangalala. Mwacitsanzo, tili ndi moyo, conco tiyenela kugwilitsila nchito moyo wathu kutamanda Mulungu popeza watikokela ku kulambila koona. (Sal. 144:15; Yoh. 6:44) Yehova amatitsimikizila kuti amatikonda ndipo amatithandiza kupilila pom’tumikila. (Yer. 31:3; 2 Akor. 4:16) Timasangalala ndi paladaiso wa kuuzimu, mmene timapeza cakudya ca kuuzimu ca mwana alilenji ndi ubale wacikondi wa padziko lonse. Kuonjezela apo, tili ndi ciyembekezo cabwino ca mtsogolo.

2. Kodi atumiki ena okhulupilika a Mulungu amavutika ndi ciani?

2 Ngakhale kuti tili ndi zifukwa zokhalila osangalala, atumiki ena okhulupilika a Mulungu amavutika ndi maganizo olakwika. Angazidziona kuti ndi acabe-cabe ndi kuti utumiki wao kwa Yehova ndi wopanda phindu. Anthu amene amakhalabe ndi maganizo amenewo, amaona mfundo yokhala ndi “zaka zambili” kuti ndi loto cabe. Kwa io moyo ungakhale masiku a mdima okha-okha.—Mlal. 11:8.

3. N’ciani cingacititse kuti tikhale ndi maganizo ofooketsa?

3 Abale ndi alongo amenewa angakhale ndi maganizo ofooketsa cifukwa ca matenda, ukalamba kapena zokhumudwitsa. (Sal. 71:9; Miy. 13:12; Mlal. 7:7) Ndiponso, Mkristu aliyense ayenela kuvomeleza kuti mtima ndi wonyenga ndi kuti ungatitsutse ngakhale kuti Mulungu amakondwela ndi zocita zathu. (Yer. 17:9; 1 Yoh. 3:20) Mdyelekezi amafalitsa mabodza ponena za atumiki a Mulungu. Ndipo anthu amene amatengela maganizo a Satana angaticititse kuganiza kuti ndife osafunika kwa Mulungu, monga mmene Elifazi wopanda cikhulupililo ananenela. Bodza limenelo linafala m’nthawi ya Yobu, ndipo lafalanso masiku ano.—Yobu 4:18, 19.

4. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

4 Yehova amatitsimikizila kupyolela m’malemba kuti adzakhala ndi anthu amene ‘akuyenda m’cigwa ca mdima wandiweyani.’ (Sal. 23:4) Njila imodzi imene Yehova amakhalila nafe ndi kupyolela m’Mau ake. Baibulo lili ndi mphamvu za Mulungu zogwetsa nazo “zinthu zozikika molimba,” kuphatikizapo mabodza ndi maganizo olakwika. (2 Akor. 10:4, 5) Conco, tiyeni tione mmene tingagwilitsile nchito Baibulo kuti tikhalebe ndi maganizo oyenela. Tikacita zimenezo tidzapindula kwambili ndipo tidzalimbikitsanso ena.

GWILITSILANI NCHITO BAIBULO KUTI MUKHALE NDI MAGANIZO OYENELA

5. Kodi ndi kudziyesa kotani kumene kungatithandize kukhala ndi maganizo oyenela?

5 Mtumwi Paulo anafotoza zinthu zina zimene zingatithandize kukhala ndi maganizo oyenela. Anauza anthu a mumpingo wa ku Korinto kuti: ‘Pitilizani kudziyesa kuti muone ngati mukali olimba m’cikhulupililo.’ (2 Akor. 13:5) “Cikhulupililo” ndico ziphunzitso zonse zacikristu zopezeka m’Baibulo. Ngati zokamba ndi zocita zathu zigwilizana ndi ziphunzitso zimenezo, ndiye kuti tikhoza mayeso ndi kuonetsa kuti tili “m’cikhulupililo.” Ndipo tifunikanso kutsatila ziphunzitso zonse zacikritsu paumoyo wathu. Sitingasankhe ziphunzitso zimene tingatsatile.—Yak. 2:10, 11.

6. N’cifukwa ciani tiyenela kudziyesa kuti tione ‘ngati tikali olimba m’cikhulupililo?’ (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

6 Mwina mungazengeleze kudziyesa, maka-maka ngati muona kuti mudzalephela kucita zimenezo. Komabe, cofunika kwambili ndi mmene Yehova amationela osati mmene timadzionela, cifukwa iye amadziŵa zambili kutiposa. (Yes. 55:8, 9) Iye amafufuza atumiki ake ndi colinga cakuti aone makhalidwe ao abwino ndi kuwathandiza osati kuti awapeze zifukwa. Mukagwilitsila nchito Mau a Mulungu kudziyesa kuti ‘muone ngati mukali olimba m’cikhulupililo,’ mudzayamba kudziona monga mmene Mulungu amakuonelani. Zimenezi zingakuthandizeni kupewa kudziona kuti ndinu wosafunika kwa Mulungu. Ndipo zimenezi ndi zogwilizana ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti: Ndinu amtengo wapatali pamaso pa Yehova. Kucita zimenezi kuli ngati kutsegula nsalu yochinga kuti dzuŵa liunikile m’cipinda.

7. Kodi tingapindule bwanji ndi zitsanzo za anthu okhulupilika a m’Baibulo?

7 Njila yabwino yodziyesela ngati tili m’cikhulupililo ndiyo kusinkha-sinkha za anthu okhulupilika a m’Baibulo. Yelekezelani umoyo wao ndi wanu ndi mmene anali kumvela, ndi kuona zimene mukanacita mukanakhala io. Tiyeni tione zitsanzo zitatu zimene zionetsa mmene mungagwilitsile nchito Baibulo kuti muone ngati muli “m’cikhulupililo.” Zimenezi zidzakuthandizani kudziona moyenela.

MKAZI WAMASIYE WOSAUKA

8, 9. (a) Kodi zinthu zinali bwanji kwa mkazi wamasiye wosauka? (b) Kodi iye akanakhala ndi maganizo olakwika ati?

8 Pamene Yesu anali pa kacisi, anaona zimene mkazi wamasiye wosauka anacita. Citsanzo cake cingatithandize kukhalabe ndi maganizo oyenela ngakhale kuti sitingathe kucita zambili. (Ŵelengani Luka 21:1-4.) Ganizilani mmene zinthu zinalili kwa mkazi wamasiye. Iye anavutika cifukwa cotaikilidwa mwamuna wake, ndipo anapondelezedwa ndi atsogoleli acipembedzo amene anali ‘kudyelela nyumba za akazi amasiye’ m’malo mowathandiza. (Luka 20:47) Iye anali wosauka kwambili cakuti copeleka cake cinali cofanana ndi malipilo a munthu amene waseŵenza mphindi zocepa.

9 Ganizilani mmene mkazi wamasiye anamvelela pamene analoŵa m’kacisi ndi tumakobidi tuŵili twatung’ono. Kodi anali kuganizila za kucepa kwa copeleka cake poyelekezela ndi zimene akanapeleka mwamuna wake akanakhala ndi moyo? Kodi anamva manyazi poona kuculuka kwa zopeleka za ena amene anali patsogolo pake, ndi kuganizila kuti mwina copeleka cake cinali ca cabe-cabe? Ngakhale kuti akanakhala ndi maganizo amenewo, iye anacilikizabe kulambila koona mmene akanathela.

10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti mkazi wamasiye anali wamtengo wapatali kwa Mulungu?

10 Yesu anaonetsa kuti mkazi wamasiye ndiponso copeleka cake zinali zamtengo wapatali kwa Yehova. Iye anati mkaziyo “waponya zoculuka kuposa [olemela] onse amene aponya.” Copeleka cake cinali kudzaikidwa pamodzi ndi zopeleka za ena, koma Yesu anayamikila cabe mkazi wamasiye. Oŵelengela ndalama m’kacisi sakanadziŵa kuti tumakobidi tuŵili tumenetu ndi amene anatupeleka, anali amtengo wapatali kwa Yehova. Komabe, cofunika ndi mmene Mulungu anaonela zinthu, osati mmene anthu anali kuganizila kapena mmene mkazi wamasiye anali kudzionela. Kodi mungagwilitsile nchito nkhaniyi kudziyesa kuti muone ngati mukali m’cikhulupililo?

11. Kodi mungaphunzile ciani pa nkhani ya mkazi wamasiye?

11 Mmene zinthu zilili paumoyo wanu zingakhudze zimene mumapeleke kwa Yehova. Ena amalephela kucita zoculuka mu ulaliki cifukwa ca ukalamba kapena kudwala. Conco, sayenela kuona kuti lipoti la utumiki wao n’losafunika. Ngakhale kuti ndinu wacicepele kapena muli ndi thanzi labwino, mungaziona kuti zocita zanu mu utumiki ndi zocepa poyelekezela ndi za anthu ena a Mulungu. Nkhani ya mkazi wamasiye wosauka itiphunzitsa kuti Yehova amaona ndipo amayamikila zilizonse zimene timam’citila, maka-maka ngati tizicita panthawi zovuta. Ganizilani zimene munacitila Yehova mu utumiki caka catha. Kodi pali nthawi ina imene munacita utumiki ngakhale kuti zinthu zinali zovuta? Ngati n’conco, dziŵani kuti Mulungu amayamikila kwambili zimene munacita. Ngati mumatumikila Yehova ndi mtima wonse, monga mmene mkazi wamasiye anacitila, mungakhale ndi cidalilo cakuti muli “m’cikhulupililo.”

“COTSANI MOYO WANGA”

12-14. (a) Kodi Eliya anavutika ndi maganizo ofooketsa ati? (b) Nanga n’cifukwa ciani iye anamva conco?

12 Mneneli Eliya anali wokhulupilika kwa Yehova ndipo anali ndi cikhulupililo colimba. Komabe, panthawi ina anakhumudwa kwambili cakuti anapempha Yehova kuti afe. Iye anati: “Basi ndatopa nazo. Tsopano cotsani moyo wanga Yehova.” (1 Maf. 19:4) Anthu amene sanakumanepo ndi mavuto amenewa angaone kuti zimene Eliya anapempha ndi “zopanda pake.” (Yobu 6:3) Ndithudi, n’zomveka kuti anamva conco. Onani kuti Yehova sanamudzudzule Eliya, koma anam’thandiza.

13 Kodi n’ciani cinapangitsa Eliya kukhala ndi maganizo amenewo? Zimenezi zisanacitike, Eliya anacita cozizwitsa cimene cinaonetsa kuti Yehova ndi Mulungu woona. Pambuyo pa cozizwitsa cimeneci, aneneli a Baala okwana 450 anaphedwa. (1 Maf. 18:37-40) Eliya anali ndi ciyembekezo cakuti anthu a Mulungu adzayambanso kulambila koona, koma zimenezo sizinacitike. Mfumukazi yoipa Yezebeli anatumiza uthenga kwa Eliya wakuti adzamupha. Pofuna kuteteza moyo wake, Eliya anathaŵila kumwela m’dziko la Yuda ndi kupita ku cipululu copanda kanthu.—1 Maf. 19:2-4.

14 Ali yekha m’cipululu, Eliya anayamba kuganiza kuti nchito yake monga mneneli inali yacabe-cabe. Iye anauza Yehova kuti: “Sindine woposa makolo anga.” Mfundo yake inali yakuti iye anadziona wacabe-cabe monga fumbi ndi mafupa a makolo ake akufa. Iye anali kuona kuti walephela nchito yake monga mneneli ndi kuti anali wosafunika kwa Yehova ndi kwa anthu onse.

15. Kodi Mulungu anam’tsimikizila bwanji Eliya kuti anali wofunikabe kwa iye?

15 Koma Mulungu Wamphamvuyonse anaona Eliya mosiyanako. Eliya anali wamtengo wapatali kwa Mulungu, ndipo Yehova anam’tsimikizila kuti ndi wofunika. Mulungu anatumiza mngelo kukam’limbikitsa. Yehova anam’patsanso cakudya ndi madzi paulendo wake wa masiku 40 wopita kumwela ku Phili la Horebe. Ndiponso mokoma mtima, Mulungu anaongolela maganizo olakwika a Eliya akuti Aisiraeli onse analeka kutumikila Yehova. Mulungu anam’patsanso nchito zina, ndipo iye anazilandila. Eliya anapindula ndi thandizo la Yehova, ndipo anayambanso kugwila nchito ndi mphamvu.—1 Maf. 19:5-8, 15-19.

16. Kodi muona kuti Mulungu wakuthandizani m’njila ziti?

16 Nkhani ya Eliya ingakuthandizeni kuona ngati mukali m’cikhulupililo, ndi kuyamba kudziona moyenela. Coyamba, ganizilani mmene Yehova wakuthandizilani. Panthawi imene munali kufuna thandizo, kodi mmodzi wa atumiki ake, monga mkulu kapena Mkristu wokhwima anakuthandizamponi? (Agal. 6:2) Kodi Baibulo, zofalitsa zathu ndi misonkhano ya mpingo imakuthandizani kudziŵa kuti Mulungu amakusamalilani? Conco, mukadzalandila thandizo mwanjila zimenezi, mukakumbukile Gwelo la thandizolo ndi kuyamikila Mulungu m’pemphelo.—Sal. 121:1, 2.

17. Kodi Yehova amayang’ana ciani mwa atumiki ake?

17 Caciŵili, dziŵani kuti kudziona mosayenela kungakhale konyenga. Cofunika kwambili ndi mmene Mulungu amationela. (Ŵelengani Aroma 14:4.) Yehova amayamikila kudzipeleka ndi kukhulupilika kwathu kwa iye. Kukhala wofunika kwa iye, sikumadalila pa kuculuka kwa zimene timacita. Ndipo mofanana ndi Eliya, mwina mwacita zambili mu utumiki wanu kwa Yehova kuposa mmene mumaonela. Kapena mwathandiza ena mumpingo popanda inu kudziŵa. Ndipo mwina anthu a m’gawo lanu anamva coonadi cifukwa ca khama lanu.

18. Kodi nchito imene Yehova wakupatsani ndi umboni wa ciani?

18 Comalizila, mudziona nchito iliyonse yocokela kwa Yehova kuti ndi umboni wakuti ali ndi inu. (Yer. 20:11) Mofanana ndi Eliya, mwina ndinu wokhumudwa cifukwa utumiki wanu ukuoneka kuti subala zipatso kapena cifukwa cakuti mwalephela kukwanilitsa zolinga zanu za kuuzimu. Komabe, mukali ndi mwai waukulu umene aliyense wa ife ali nao. Mwai umenewu ndiwo kulalikila uthenga wabwino ndi kukhala Mboni ya Yehova. Khalanibe wokhulupilika. Ndiyeno, mau a m’fanizo la Yesu akuti: “Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako,” angagwilenso nchito kwa inu.—Mat. 25:23.

“PEMPHELO LA MUNTHU WOSAUTSIKA”

19. Kodi wolemba Salimo 102 anakumana ndi mavuto otani?

19 Wolemba Salimo 102 anavutika maganizo. Iye ‘anasautsika,’ kutanthauza kuti anavutika mtima. Ndipo analibe mphamvu zolimbana ndi mavuto. (Sal. 102, tumau twa pamwamba) Mau ake amaonetsa kuti iye anakhudzidwa kwambili ndi mavuto ake, ndipo anasungulumwa. (Sal. 102:3, 4, 6, 11) Iye anaona kuti Yehova afuna kumutaya.—Sal. 102:10.

20. Kodi pemphelo lingathandize bwanji munthu amene akulimbana ndi maganizo olakwika?

20 Komabe, wamasalimo anapitiliza kutamanda Yehova. (Ŵelengani Salimo 102:19-21.) Salimo 102 ionetsa kuti ngakhale anthu amene ali m’cikhulupililo, angasautsike ndi kukhudzidwa kwambili ndi mavuto ao. Wamasalimo anadziona ngati “mbalame imene ili yokha-yokha padenga,” kapena kuti pamtenje. Iye anadziona monga kuti wazingidwa ndi mavuto okha-okha. (Sal. 102:7) Mukakhala ndi maganizo amenewo, tulilani Yehova nkhawa zanu monga anacitila wamasalimo. Mapemphelo anu angakuthandizeni polimbana ndi maganizo olakwika. Yehova walonjeza kuti, “adzamvetsela pemphelo la anthu amene alandidwa ciliconse, ndipo sadzapeputsa pemphelo lao.” (Sal. 102:17) Dalilani lonjezo limenelo.

21. Kodi munthu amene akuvutika ndi maganizo olakwika angakhale bwanji ndi maganizo oyenela?

21 Salmo 102 lionetsanso mmene mungakhalile ndi maganizo oyenela. Wamasalimo anacita zimenezo mwa kuganizila za ubwenzi wake ndi Yehova. (Sal. 102:12, 27) Iye anapeza citonthozo podziŵa kuti nthawi zonse Yehova adzacilikiza anthu ake pamene akumana ndi mavuto. Conco, ngati maganizo osayenela akulepheletsani kucita zambili mu utumiki wa Mulungu, ipempheleleni nkhaniyo. Pemphani Mulungu kuti amvetsele pemphelo lanu kotelo kuti mupeze mtendele pamene muvutika, ndiponso “kuti dzina la Yehova lilengezedwe.”— Sal. 102:20, 21.

22.  Kodi aliyense wa ife angakondweletse bwanji Yehova?

22 Ndithudi, tingagwilitsile nchito Baibulo kudziŵa ngati tili m’cikhulupililo ndi kuona ngati tili wofunika kwa Yehova. N’zoona kuti m’dongosolo lino la zinthu sitingathetse maganizo onse olakwika kapena zofooketsa. Komabe, aliyense wa ife angakondweletse Yehova ndi kupeza cipulumutso ngati tipitilizabe kumutumikila mokhulupilika.—Mat. 24:13.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani