LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • nwt Luka 1:1-24:53
  • Luka

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Luka
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Luka

UTHENGA WABWINO WOLEMBEDWA NDI LUKA

1 Anthu ambili analemba nkhani yofotokoza zinthu zonse zimene zinacitika, zomwe ifenso timazikhulupilila.* 2 Enanso amene kucokela paciyambi anali mboni zoona ndi maso, komanso alengezi a uthenga wa Mulungu anatiuza zinthu zimenezi. 3 Conco inu wolemekezeka koposa, a Teofilo, ine ndasanthula zinthu zonsezi molondola kucokela paciyambi, ndipo inenso ndatsimikiza mtima kukulembelani zinthu zimenezi mwatsatanetsatane. 4 Ndacita izi kuti mutsimikize kuti zinthu zimene anakuphunzitsani ndi mawu apakamwa n’zoona.

5 M’masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe wina dzina lake Zekariya wa m’gulu la ansembe la Abiya. Mkazi wake anali wocokela mwa ana aakazi a Aroni, ndipo dzina lake anali Elizabeti. 6 Onse awili anali olungama pamaso pa Mulungu. Ndipo anali kutsatila mokhulupilika malamulo onse a Yehova. 7 Komatu analibe mwana, cifukwa Elizabeti anali wosabeleka, ndipo onse awili anali okalamba.

8 Tsopano inali nthawi yakuti gulu lake litumikile pa kacisi. Ndipo iye anali kutumikila monga wansembe pamaso pa Mulungu. 9 Mwa cizolowezi ca ansembe,* inali nthawi yake yakuti alowe m’nyumba yopatulika ya Yehova kuti akapeleke nsembe zofukiza. 10 Gulu lonse la anthu linali kupemphela panja panthawi yopeleka nsembe zofukiza. 11 Ndiyeno mngelo wa Yehova anaonekela kwa iye ataimilila ku lamanja kwa guwa lansembe zofukiza. 12 Zekariya anavutika maganizo ndi zimene anaonazo, ndipo anacita mantha kwambili. 13 Koma mngeloyo anamuuza kuti: “Usacite mantha Zekariya, cifukwa pemphelo lako locondelela lamveka, mkazi wako Elizabeti adzakubelekela mwana wamwamuna, ndipo udzamupatse dzina lakuti Yohane. 14 Iwe udzasangalala ndi kukondwela kwambili, ndipo ambili adzakondwela ndi kubadwa kwake, 15 cifukwa iye adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova. Koma asadzamwe vinyo kapena cakumwa ciliconse coledzeletsa ngakhale pang’ono, ndipo iye adzadzazidwa ndi mzimu woyela ngakhale asanabadwe.* 16 Iye adzabwezeletsa ana ambili a Isiraeli kwa Yehova Mulungu wawo. 17 Komanso Mulungu adzamutumiza patsogolo pake ali ndi mzimu ndiponso mphamvu monga za Eliya. Adzamutumiza kuti akatembenuze mitima ya atate kuti ikhale ngati ya ana,* komanso kuti akathandize anthu osamvela kukhala ndi nzelu za anthu olungama, n’colinga cakuti akonzekeletse anthu kutumikila Yehova.”

18 Zekariya anafunsa mngeloyo kuti: “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Cifukwa ndine wokalamba, ndipo mkazi wanga nayenso ndi wokalamba.” 19 Mngeloyo anamuyankha kuti: “Ine ndine Gabirieli, ndimaimilila pafupi ndi Mulungu, ndipo ndatumidwa kuti ndidzalankhule nawe komanso kuti ndidzalengeze uthenga wabwino umenewu kwa iwe. 20 Koma tamvela! Udzakhala cete ndipo sudzatha kulankhula mpaka tsiku limene zinthu zimenezi zidzacitike, cifukwa sunakhulupilile mawu anga amene adzakwanilitsidwa pa nthawi yake yoikika.” 21 Pa nthawiyi, anthu anali kungomuyembekezela Zekariya, ndipo iwo anadabwa kuti watenga nthawi yaitali kwambili m’nyumba yopatulikayo. 22 Atatuluka, iye sanathe kulankhula nawo. Ndipo iwo anazindikila kuti waona masomphenya m’nyumba yopatulikayo. Iye anali kungolankhula nawo ndi manja cifukwa sanali kukwanitsa kutulutsa mawu. 23 Masiku ake a utumiki* wopatulika atatha, iye anabwelela kunyumba kwake.

24 Patapita masiku angapo, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pathupi. Ndipo anakhala kwayekha miyezi isanu. Iye anati: 25 “Izi n’zimene Yehova wandicitila masiku ano. Iye wandikumbukila n’kucotsa kunyozeka kwanga pakati pa anthu.”

26 Elizabeti ali woyembekezela kwa miyezi 6, Mulungu anatuma mngelo Gabirieli ku mzinda wa Galileya wochedwa Nazareti. 27 Anam’tumiza kwa namwali amene Yosefe wa m’nyumba ya Davide anamulonjeza* kuti adzamukwatila. Ndipo namwaliyo dzina lake anali Mariya. 28 Mngeloyo ataonekela kwa iye, anamuuza kuti: “Moni, iwe munthu wodalitsika kwambili. Yehova ali nawe.” 29 Koma iye anadabwa kwambili ndi mawu a mngeloyo, ndipo anayamba kuganizila tanthauzo la moni umenewo. 30 Conco mngeloyo anamuuza kuti: “Usacite mantha Mariya, cifukwa Mulungu wakukomela mtima. 31 Tamvela! Udzakhala ndi pathupi, ndipo udzabeleka mwana wamwamuna. Mwanayo udzamupatse dzina lakuti Yesu. 32 Ameneyo adzakhala wamkulu ndipo adzachedwa Mwana wa Wapamwambamwamba. Yehova Mulungu adzamupatsa mpando wacifumu wa Davide atate wake. 33 Iye adzalamulila monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, ndipo Ufumu wake sudzatha.”

34 Koma Mariya anafunsa mngeloyo kuti: “Nanga zimenezi zidzatheka bwanji popeza sindinagonepo ndi mwamuna?” 35 Mngeloyo anamuyankha kuti: “Mzimu woyela udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wapamwambamwamba idzakuphimba. Pa cifukwa cimeneci, amene adzabadweyo adzachedwa woyela, Mwana wa Mulungu. 36 Ndipotu tamvela! Elizabeti m’bale wako, amene anthu amamucha mayi wosabeleka, nayenso ali ndi pathupi pa mwana wamwamuna ku ukalamba wake, ndipo mwezi uno tsopano ndi wa 6. 37 Pakuti zilizonse zimene Mulungu wakamba zimatheka.”* 38 Ndiyeno Mariya anati: “Ndine pano kapolo wa Yehova. Zicitike kwa ine monga mwanenela.” Zitatelo, mngeloyo anacoka pamaso pake.

39 Conco m’masiku amenewo, Mariya ananyamuka mwamsanga kupita ku dziko la mapili, ku mzinda wa m’dela la fuko la Yuda. 40 Ndipo analowa m’nyumba ya Zekariya n’kupeleka moni kwa Elizabeti. 41 Tsopano Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana amene anali m’mimba mwake analumpha, ndipo Elizabetiyo anadzazidwa ndi mzimu woyela. 42 Ndiyeno, iye analankhula mokweza mawu kuti: “Ndiwe wodalitsika kuposa akazi onse, ndipo mwana amene udzabeleke, nayenso ndi wodalitsika! 43 Ndine ndani ine kuti mayi wa Ambuye wanga abwele kudzandiona? 44 Cifukwa n’tamva moni wako, mwana amene ali m’mimba mwangamu walumpha ndi cisangalalo. 45 Komanso ndiwe wacimwemwe pakuti unakhulupilila, cifukwa Yehova adzakwanilitsa zonse zimene anakuuza.”

46 Kenako Mariya anati: “Ndikulemekeza* Yehova, 47 ndipo mtima wanga ndi wokondwa kwambili cifukwa ca Mulungu, Mpulumutsi wanga, 48 cifukwa waona malo otsika a ine kapolo wake wamkazi. Ndipo kuyambila tsopano mpaka m’tsogolo, mibadwo yonse idzandichula wacimwemwe, 49 cifukwa wamphamvuyo wandicitila zazikulu ndipo dzina lake ndi loyela. 50 Ku mibadwomibadwo, iye amacitila cifundo anthu amene amamuopa. 51 Iye wacita zinthu zamphamvu ndi dzanja lake. Wabalalitsa anthu amene ndi odzikuza m’mitima yawo. 52 Watsitsa anthu amphamvu pa mipando yacifumu, ndipo wakweza anthu onyozeka. 53 Wakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, koma olemela wawabweza cimanjamanja. 54 Wathandiza Isiraeli mtumiki wake pokumbukila cifundo cake kwamuyaya, 55 monga anakambila kwa makolo athu akale, Abulahamu ndi mbadwa* zake.” 56 Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu, kenako anabwelela kwawo.

57 Tsopano nthawi inakwana yakuti Elizabeti abeleke mwana, ndipo anabeleka mwana wamwamuna. 58 Anthu okhala naye pafupi, ndi acibale ake, anamva kuti Yehova wamuonetsa cifundo cacikulu, ndipo anakondwela naye limodzi. 59 Pa tsiku la 8, iwo anabwela kuti amucite mdulidwe mwanayo, ndipo anafuna kum’patsa dzina la atate ake lakuti Zekariya. 60 Koma mayi ake anakamba kuti: “Iyayi! dzina lake akhale Yohane.” 61 Iwo atamva izi anamuuza kuti: “Palibe wacibale wako aliyense wochedwa ndi dzina limeneli.” 62 Ndiyeno iwo anafunsa tate wake mocita kulankhula ndi manja kuti awauze dzina limene anali kufuna kum’patsa mwanayo. 63 Iye anapempha kuti am’patse polemba, ndipo analembapo kuti: “Dzina lake ndi Yohane.” Anthu onsewo ataona izi, anadabwa kwambili. 64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatseguka, ndipo lilime lake linamasuka moti anayamba kulankhula ndi kutamanda Mulungu. 65 Anthu onse okhala m’delalo anagwidwa ndi mantha, ndipo nkhani imeneyi inali m’kamwam’kamwa m’dela lonse la mapili la Yudeya. 66 Ndipo onse amene anamva zimenezi anayamba kuganizilapo mozama, n’kumati: “Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani?” Cifukwa dzanja la Yehova linalidi pa iye.

67 Ndiyeno Zekariya tate wake anadzazidwa ndi mzimu woyela, ndipo ananenela kuti: 68 “Yehova Mulungu wa Isiraeli atamandike cifukwa wakumbukila anthu ake ndiponso wawabweletsela cipulumutso. 69 Watiutsila mpulumutsi wamphamvu* m’nyumba ya Davide mtumiki wake. 70 Izi n’zimene anakambilatu kupitila mwa aneneli ake oyela akale, 71 zakuti adzatipulumutsa kwa adani athu komanso m’manja mwa onse odana nafe. 72 Adzakwanilitsa zimene analonjeza makolo athu akale ndi kuwaonetsa cifundo. Ndipo adzakumbukila cipangano cake coyela, 73 lumbilo limene analumbila kwa Abulahamu kholo lathu, 74 kuti pambuyo potipulumutsa m’manja mwa adani athu, atipatse mwayi wocita utumiki wopatulika kwa iye mopanda mantha, 75 mokhulupilika, komanso mwacilungamo pamaso pake masiku athu onse. 76 Koma ponena za iwe mwana wamng’onowe, udzachedwa mneneli wa Wapamwambamwamba, cifukwa Yehova adzakutumiza patsogolo pake kuti ukakonze njila zake, 77 komanso kuti ukalengeze kwa anthu ake uthenga wa cipulumutso cimene cidzatheka Mulungu akadzawakhululukila macimo awo, 78 cifukwa ca cifundo ca Mulungu wathu. Mwa cifundo cake cimeneci, kuwala kwa m’mamawa kudzatifikila kucokela kumwamba, 79 kuti anthu okhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa aone kuwala. Kuwala kumeneko kudzatsogolelanso mapazi athu pa njila ya mtendele.”

80 Conco mwana wamng’onoyo anakula, ndipo anakhala wolimba kuuzimu. Iye anapitiliza kukhala ku cipululu mpaka tsiku limene anadzionetsa poyela kwa Aisiraeli.

2 Tsopano m’masiku amenewo, Kaisara Augasito anapeleka lamulo lakuti anthu onse m’dzikolo akalembetse m’kaundula. 2 (Kulembetsa koyamba kumeneko kunacitika pamene Kureniyo anali bwanamkumbwa wa Siriya.) 3 Ndipo anthu onse anapita kukalembetsa, aliyense ku mzinda wakwawo. 4 Nayenso Yosefe anacoka ku Galileya mu mzinda wa Nazareti n’kupita ku Yudeya, ku mzinda wa Davide wochedwa Betelehemu, cifukwa iye anali wa m’banja la Davide komanso wa fuko limenelo. 5 Anapita kukalembetsa pamodzi ndi Mariya amene anakwatilana naye mwa pangano lawo. Ndipo panthawiyi n’kuti Mariya atatsala pang’ono kubeleka. 6 Ali komweko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe. 7 Iye anabeleka mwana wake woyamba wamwamuna, ndipo anamukulunga m’nsalu n’kumugoneka modyelamo ziweto, cifukwa sanapeze malo m’nyumba ya alendo.

8 M’dela limenelo munalinso abusa amene anali kugona panja kumalo odyetsela ziweto, ndipo anali kuyang’anila nkhosa zawo usiku wonse. 9 Mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova anaimilila pafupi nawo, ndipo ulemelelo wa Yehova unawala pa malopo, moti iwo anacita mantha kwambili. 10 Koma mngeloyo anawauza kuti: “Musaope ayi. Ine ndabwela kudzalengeza uthenga wabwino kwa inu, uthenga wa cimwemwe cacikulu cimene anthu onse adzakhala naco. 11 Pakuti lelo, mu mzinda wa Davide mwabadwa mpulumutsi wanu, amene ndi Khristu Ambuye. 12 Ndipo ndikupatsani cizindikilo ici: Kumeneko mukapeza mwana wakhanda wokulunga m’nsalu atamugoneka m’codyela ziweto.” 13 Mwadzidzidzi, panaonekanso khamu lalikulu la angelo akumwamba, lili pamodzi ndi mngeloyo. Iwo anali kutamanda Mulungu n’kumati: 14 “Ulemelelo kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo padziko lapansi pano mtendele kwa anthu amene Mulungu amakondwela nawo.”

15 Ndiyeno angelowo atacoka n’kubwelela kumwamba, abusawo anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu tikaone zimene zacitika, zimene Yehova watidziwitsa.” 16 Iwo anapita mofulumila, ndipo anakapeza Mariya ndi Yosefe, komanso mwana wakhandayo atam’goneka modyelamo ziweto. 17 Ataona zimenezi, iwo anafotokoza uthenga umene anauzidwa, wokhudza mwana wamng’onoyo. 18 Ndipo onse amene anamva, anadabwa kwambili ndi zimene abusawo anawauza. 19 Koma Mariya anasunga mawu onsewa ndi kuganizila tanthauzo la zimenezi mumtima mwake. 20 Ndiyeno abusawo anabwelela akulemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zonse zimene anamva ndi kuona, mogwilizana ndi zimene anauzidwa.

21 Pambuyo pa masiku 8, nthawi ya mdulidwe wa mwanayo itakwana, anamupatsa dzina lakuti Yesu. Ili ndi dzina limene mngelo uja anamupatsa, Mariya asanakhale ndi pathupi.

22 Komanso nthawi yowayeletsa itakwana malinga ndi Cilamulo ca Mose, anapita naye ku Yerusalemu kukamupeleka kwa Yehova. 23 Izi zinali zogwilizana ndi zimene zinalembedwa m’Cilamulo ca Yehova kuti: “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa* adzakhala woyela kwa Yehova.” 24 Ndipo iwo anapeleka nsembe malinga ndi zimene Cilamulo ca Yehova cimanena kuti: “Njiwa ziwili kapena ana a nkhunda awili.”

25 Ndiyeno mu Yerusalemu, munali munthu wina dzina lake Simiyoni. Mwamunayu anali wolungama komanso wodzipeleka kwa Mulungu. Iye anali kuyembekezela nthawi ya kutonthozedwa kwa Isiraeli, ndipo mzimu woyela unali pa iye. 26 Kuwonjezela apo, Mulungu anamuululila mwa mzimu woyela kuti sadzafa kufikila ataona Khristu wa Yehova. 27 Tsopano motsogoleledwa ndi mzimu, iye anapita ku kacisi. Ndiyeno pamene makolo a mwana wa mng’onoyo, Yesu, anabwela naye kuti amucitile zimene Cilamulo cinali kunena, 28 iye ananyamula mwanayo m’manja mwake ndi kutamanda Mulungu kuti: 29 “Tsopano Ambuye Wamkulukulu, mukulola kapolo wanu kupita mumtendele pakuti mwakwanilitsa lonjezo lanu, 30 cifukwa maso anga aona njila yanu ya cipulumutso 31 imene mwakonza pamaso pa anthu a mitundu yonse, 32 kuunika kocotsa nsalu yophimba mitundu ya anthu kuti isamaone, komanso ulemelelo wa anthu anu Aisiraeli.” 33 Ndiyeno tate ndi mayi a mwanayo anali kungodabwa ndi zimene zinali kunenedwa zokhudza mwanayo. 34 Komanso Simiyoni anawadalitsa ndipo anauza Mariya, mayi wa mwanayo kuti “Tamvela! Mwana uyu waikidwa kuti ambili mu Isiraeli agwe kapena kuimililanso, komanso kuti akhale cizindikilo cimene anthu angacitsutse 35 (inde, lupanga lalitali lidzakulasa), kuti zimene zili m’mitima ya anthu ambili zionekele poyela.”

36 Tsopano kunali mneneli wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuweli wa fuko la Aseri. Mayi ameneyu anali wokalamba, ndipo atakwatilana ndi mwamuna wake,* anakhala m’cikwati zaka 7 zokha, 37 koma tsopano iye anali mkazi wamasiye wa zaka 84. Mayiyu sanali kuphonya pa kacisi. Anali kucita utumiki wopatulika usana ndi usiku ndi kusala kudya komanso kupeleka mapemphelo ocondelela. 38 Mu ola limenelo, iye anabwela pafupi ndi iwo, ndi kuyamba kuyamika Mulungu komanso kulankhula zokhudza mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezela cipulumutso ca Yerusalemu.

39 Conco iwo atacita zonse malinga ndi Cilamulo ca Yehova, anabwelela ku Galileya ku mzinda wawo wa Nazareti. 40 Mwana wamng’onoyo anapitiliza kukula komanso kukhala wamphamvu. Nzelu zake zinali kuwonjezeka, ndipo Mulungu anapitiliza kukondwela naye.

41 Makolo ake anali ndi cizolowezi copita ku Yerusalemu caka ndi caka, ku cikondwelelo ca Pasika. 42 Ndipo iye ali ndi zaka 12, anapita naye ku cikondweleloco mwacizolowezi cawo. 43 Masiku a cikondweleloco atatha komanso pamene anali kubwelela, mnyamatayo Yesu anatsalila ku Yerusalemu, ndipo makolo ake sanadziwe zimenezo. 44 Iwo anaganiza kuti iye ali nawo pamodzi pa gulu la anthu a pa ulendowo, moti anayenda mtunda wa tsiku limodzi. Ndiyeno anayamba kumufunafuna pakati pa acibale awo ndi anzawo. 45 Koma cifukwa sanamupeze, anabwelela ku Yerusalemu, ndipo anamufunafuna mwakhama. 46 Patapita masiku atatu, anamupeza m’kacisi atakhala pakati pa aphunzitsi, ndipo anali kuwamvetsela ndi kuwafunsa mafunso. 47 Koma onse amene anali kumumvetsela, anadabwa kwambili ndi luso lake lomvetsa zinthu komanso mayankho ake. 48 Makolo ake atamuona, anadabwa kwambili. Ndipo mayi ake anamufunsa kuti: “Mwanawe, n’cifukwa ciyani wativutitsa conci? Ine ndi atate akowa tinada nkhawa kwambili, ndipo tinali kukufunafuna.” 49 Koma iye anawayankha kuti: “N’cifukwa ciyani munali kundifunafuna? Kodi simudziwa kuti ndiyenela kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?” 50 Koma iwo sanamvetse zimene iye anali kuwauza.

51 Kenako iye anabwelela nawo ku Nazareti, ndipo anapitiliza kuwamvela.* Komanso mayi ake anasunga mawu onsewa mosamala mumtima mwawo. 52 Nzelu za Yesu zinapitiliza kuwonjezeka, komanso anali kukula mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiliza kukondwela naye.

3 M’caka ca 15 ca ulamulilo wa Kaisara Tiberiyo, Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode* anali kulamulila cigawo* ca Galileya, Filipo m’bale wake anali kulamulila madela a Itureya ndi Tirakoniti. Ndipo Lusaniyo anali kulamulila cigawo ca Abilene. 2 M’masiku amenewo, Anasi anali wansembe wamkulu, ndipo Kayafa anali mkulu wa ansembe. Pa nthawiyo, Yohane mwana wa Zekariya ali m’cipululu, uthenga wa Mulungu unafika kwa iye.

3 Conco iye anapita m’madela onse ozungulila Yorodani, ndipo anali kulalikila kuti anthu ayenela kubatizika monga cizindikilo ca kulapa kuti macimo awo akhululukidwe. 4 Izi zinacitika malinga ndi zimene zinalembedwa m’buku la mneneli Yesaya kuti: “Winawake akufuula m’cipululu kuti: ‘Konzani njila ya Yehova. Wongolani misewu yake. 5 Cigwa ciliconse cifoceledwe, ndipo phili lililonse komanso citunda ciliconse zisalazidwe. Njila zokhotakhota ziwongoledwe, ndipo njila zokumbikakumbika zisalazidwe. 6 Anthu onse adzaona cipulumutso ca Mulungu.’”*

7 Ndiyeno Yohane anayamba kulankhula ndi gulu la anthu omwe anali kubwela kuti iye awabatize. Anati: “Ana a njoka inu, ndani wakucenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwela? 8 Ndiye balani zipatso zoonetsa kulapa. Musadzinamize n’kumati, ‘Tili ndi Abulahamu atate wathu.’ Pakuti ndikukuuzani kuti Mulungu angathe kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abulahamu. 9 Ndithudi, nkhwangwa yaikidwa kale pa mizu ya mitengo. Cotelo mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”

10 Ndiyeno khamu la anthulo linamufunsa kuti: “Kodi tiyenela kucita ciyani?” 11 Iye anawayankha kuti: “Amene ali ndi zovala ziwili* apatseko munthu amene alibe, ndipo amene ali ndi cakudya acitenso cimodzimodzi.” 12 Nawonso okhometsa misonkho anabwela kwa iye kuti abatizidwe, ndipo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi tiyenela kucita ciyani?” 13 Iye anawayankha kuti: “Musamalipilitse anthu* zopitilila pa mtengo wa msonkho.” 14 Nawonso asilikali anali kumufunsa kuti: “Kodi tiyenela kucita ciyani?” Iye anawauza kuti: “Musamavutitse aliyense* kapena kunamizila munthu aliyense mlandu. Koma muzikhutila ndi malipilo anu.”

15 Tsopano anthu anali kuyembekezela Khristu, ndipo onse anali kudzifunsa m’mitima yawo zokhudza Yohane kuti: “Kodi ameneyu angakhale Khristu kapena?” 16 Yohane anawayankha onsewo kuti: “Ine ndikukubatizani ndi madzi. Koma wamphamvu kuposa ine akubwela, ndipo sindine woyenelela kumasula nthambo za nsapato zake. Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyela komanso moto. 17 Fosholo yake youluzila ili m’manja mwake kuti ayeletse kothelatu malo ake opunthila mbewu. Komanso kuti tiligu amututile m’nkhokwe yake, koma mankhusu* awatenthe pa moto wosazimitsika.”

18 Iye anapelekanso malangizo ena ambili, ndipo anapitiliza kulalikila uthenga wabwino kwa anthu. 19 Yohane anadzudzula Herode wolamulila cigawo, cifukwa ca Herodiya mkazi wa m’bale wake, komanso cifukwa ca zoipa zonse zimene Herode anacita. 20 Koma cifukwa codzudzulidwa, Herodeyo anacitanso coipa cina kuwonjezela pa zonsezi: Anatsekela Yohane m’ndende.

21 Pamene anthu onse anali kubatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Ndipo pamene iye anali kupemphela, kumwamba kunatseguka, 22 ndiponso mzimu woyela wooneka ngati nkhunda unatsika n’kudzatela pa iye. Kenako kumwamba kunamveka mawu akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondeka, ndimakondwela nawe.”

23 Yesu anayamba utumiki wake ali ndi zaka pafupifupi 30. Anthu anali kumudziwa kuti anali mwana,

wa Yosefe,

mwana wa Heli,

24 mwana wa Matati,

mwana wa Levi,

mwana wa Meliki,

mwana wa Yanai,

mwana wa Yosefe,

25 mwana wa Matatiyo,

mwana wa Amosi,

mwana wa Nahumu,

mwana wa Esili,

mwana wa Nagai,

26 mwana wa Maati,

mwana wa Matatiyo,

mwana wa Semeini,

mwana wa Yoseki,

mwana wa Yoda,

27 mwana wa Yoanani,

mwana wa Resa,

mwana wa Zerubabele,

mwana wa Salatiyeli,

mwana wa Neri,

28 mwana wa Meliki,

mwana wa Adi,

mwana wa Kosamu,

mwana wa Elimadama,

mwana wa Ere,

29 mwana wa Yesu,

mwana wa Eliezere,

mwana wa Yorimu,

mwana wa Matati,

mwana wa Levi,

30 mwana wa Sumeyoni,

mwana wa Yudasi,

mwana wa Yosefe,

mwana wa Yonamu,

mwana wa Eliyakimu,

31 mwana wa Meleya,

mwana wa Mena,

mwana wa Matata,

mwana wa Natani,

mwana wa Davide,

32 mwana wa Jese,

mwana wa Obedi,

mwana wa Boazi,

mwana wa Salimoni,

mwana wa Nasoni,

33 mwana wa Aminadabu,

mwana wa Arini,

mwana wa Hezironi,

mwana wa Perezi,

mwana wa Yuda,

34 mwana wa Yakobo,

mwana wa Isaki,

mwana wa Abulahamu,

mwana wa Tera,

mwana wa Nahori,

35 mwana wa Serugi,

mwana wa Reu,

mwana wa Pelegi,

mwana wa Ebere,

mwana wa Shela,

36 mwana wa Kainani,

mwana wa Aripakisadi,

mwana wa Semu,

mwana wa Nowa,

mwana wa Lameki,

37 mwana wa Metusela,

mwana wa Inoki,

mwana wa Yaredi,

mwana wa Mahalaliyeli,

mwana wa Kainani,

38 mwana wa Enosi,

mwana wa Seti,

mwana wa Adamu,

mwana wa Mulungu.

4 Yesu atadzazidwa ndi mzimu woyela, anacoka ku Yorodani, ndipo mzimuwo unali kumutsogolela m’cipululu 2 kwa masiku 40. Kumeneko Mdyelekezi anamuyesa. Yesu sanadye ciliconse pa masiku amenewo. Conco masikuwo atatha, anamva njala. 3 Mdyelekezi ataona izi anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mtanda wamkate.” 4 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha ayi.’”

5 Kenako anapita naye pa malo okwela ndi kumuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kocepa. 6 Ndiyeno Mdyelekezi anamuuza kuti: “Ulamulilo wonsewu ndi ulemelelo ndikupatsani cifukwa zinapelekedwa kwa ine, ndipo ndingazipeleke kwa aliyense amene ndafuna. 7 Conco ngati mungagwade pansi ndi kundilambilako kamodzi kokha, zonsezi zikhala zanu.” 8 Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kum’lambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’”

9 Ndiyeno anapita naye ku Yerusalemu n’kumukwezeka pamwamba penipeni pa* kacisi. Kenako anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, dziponyeni pansi kucokela pano, 10 cifukwa Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu kuti akutetezeni,’ 11 ndipo, ‘Iwo adzakuwakhani ndi manja awo kuti phazi lanu lisagunde mwala.’” 12 Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Usamuyese Yehova Mulungu wako.’” 13 Conco Mdyelekezi atatsiliza mayeselo onsewo anacoka n’kumusiya, ndipo anayembekezela nthawi ina yabwino.

14 Tsopano Yesu atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu anabwelela ku Galileya. Ndipo mbili yake yabwino inafalikila m’madela onse ozungulila. 15 Komanso iye anayamba kuphunzitsa m’masunagoge awo, ndipo anthu onse anali kumulemekeza.

16 Ndiyeno anapita ku Nazareti kumene anakulila. Mwacizolowezi cake, pa tsiku la Sabata analowa m’sunagoge ndi kuimilila kuti awelenge. 17 Conco anamupatsa mpukutu wa mneneli Yesaya. Iye anautambasula ndipo anapeza pamene panalembedwa mawu akuti: 18 “Mzimu wa Yehova uli pa ine cifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kuti ndilengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ukapolo, komanso kuti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula anthu opondelezedwa, 19 ndi kudzalalikila za caka covomelezeka ca Yehova.” 20 Atatelo, anapinda mpukutuwo n’kuubweza kwa mtumiki wa m’sunagogemo. Kenako anakhala pansi. Maso a anthu onse m’sunagogemo anangoti dwii pa iye. 21 Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lelo, lemba limene mwangolimva kumeneli lakwanilitsidwa.”

22 Anthu onsewo anayamba kum’tamanda ndipo anadabwa ndi mawu acisomo otuluka pakamwa pake. Iwo anali kufunsana kuti: “Kodi ameneyu si mwana wa Yosefe?” 23 Iye atamva zimenezi anawauza kuti: “Mosakayikila, mudzakamba mwambi uwu pa ine wakuti ‘Iwe wocilitsa anthu, dzicilitse wekha. Zinthu zimene tinamva kuti unazicita ku Kaperenao, uzicitenso kuno kwanu.’” 24 Conco iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneli amene amalandilidwa kwawo. 25 Mwacitsanzo, ndithu ndikukuuzani kuti: Mu Isiraeli munali akazi ambili amasiye m’masiku a Eliya pamene kumwamba kunatsekedwa kwa zaka zitatu ndi miyezi 6, ndipo m’dziko lonselo munagwa njala yaikulu. 26 Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akaziwo. M’malomwake, anatumizidwa kwa mkazi wamasiye wa ku Zarefati m’dziko la Sidoni. 27 Komanso m’nthawi ya mneneli Elisa, mu Isiraeli munali anthu ambili akhate. Koma palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anacilitsidwa,* kupatulapo Namani wa ku Siriya.” 28 Tsopano onse amene anali kumvetsela zimenezi m’sunagogemo anakwiya kwambili. 29 Iwo ananyamuka ndipo mofulumila anamutulutsila kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phili pamene panamangidwa mzinda wawo, kuti akamuponye kuphompho. 30 Koma iye anangodutsa pakati pawo n’kumapita.

31 Ndiyeno anapita ku Kaperenao, mzinda wa ku Galileya. Ndipo anali kuphunzitsa anthu pa Sabata. 32 Anthuwo anadabwa kwambili ndi kaphunzitsidwe kake cifukwa anali kukamba mwaulamulilo. 33 Tsopano m’sunagogemo munali munthu wina wogwidwa ndi mzimu, inde ciwanda conyansa. Munthuyo anali kukuwa mwamphamvu kuti: 34 “Aa! Mufuna ciyani kwa ife inu Yesu Mnazareti? Kodi mwabwela kudzatiwononga? Ine ndikudziwa bwino kuti ndinu Woyela wa Mulungu.” 35 Koma Yesu anaudzudzula mzimuwo kuti: “Khala cete, ndipo tuluka mwa iye.” Pamenepo ciwandaco cinamugwetsela pansi munthuyo pakati pawo, basi n’kutuluka mwa iye popanda kumuvulaza. 36 Anthu onsewo ataona izi, anadabwa kwambili, ndipo anayamba kukambilana kuti: “Onani, mawu ake ndi amphamvu kwambili cifukwa mwa ulamulilo ndi mphamvu akulamula mizimu yonyansa kutuluka, ndipo ikutulukadi!” 37 Conco mbili yake inafalikila paliponse m’madela onse ozungulila.

38 Atatuluka m’sunagoge muja, anakalowa m’nyumba ya Simoni. Pa nthawiyo, apongozi aakazi a Simoni anali kudwala malungo aakulu. Conco iwo anamupempha kuti awathandize. 39 Ndiyeno iye anaimilila pafupi ndi mayiwo n’kudzudzula malungowo, ndipo malungowo anathelatu. Nthawi yomweyo mayiwo anaimilila n’kuyamba kuwakonzela cakudya.

40 Koma pamene dzuwa linali kulowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweletsa kwa iye. Ndipo anawacilitsa mwa kuika manja ake pa aliyense wa iwo. 41 Nazonso ziwanda zinatuluka mwa anthu ambili zikufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma anali kuzidzudzula ndipo sanali kuzilola kuti zilankhule, cifukwa zinali kumudziwa kuti ndi Khristu.

42 Kutaca m’mawa, iye anacoka n’kupita ku malo opanda anthu. Koma khamu la anthu linayamba kumufunafuna,* mpaka anafika kumene iye anali. Ndipo iwo anamucondelela kuti asawasiye. 43 Koma iye anawauza kuti: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso, cifukwa n’zimene ndinatumidwa kudzacita.” 44 Atatelo, anapita kukalalikila m’masunagoge a ku Yudeya.

5 Pa nthawi ina, khamu la anthu linali kupanikizana kuti lipite kwa Yesu kukamvetsela mawu a Mulungu. Apo n’kuti iye waimilila m’mbali mwa nyanja ya Genesareti.* 2 Iye anaona mabwato awili okoceza m’mbali mwa nyanjayo. Koma asodzi anali atatulukamo ndipo anali kutsuka maukonde awo. 3 Atalowa mu imodzi ya mabwatowo, imene inali ya Simoni, anamupempha kuti aikankhile m’nyanja pang’ono. Kenako iye anakhala pansi m’bwatomo n’kuyamba kuphunzitsa khamu la anthulo. 4 Atatsiliza kulankhula, anauza Simoni kuti: “Palasila kozama, ndipo muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” 5 Koma Simoni anayankha kuti: “Mlangizi, tagwila nchito usiku wonse, koma sitinaphe kanthu. Komabe poti ndinu mwakamba, ndiponya maukondewa.” 6 Atacita zimenezi, anapha nsomba zambilimbili, moti maukonde awo anayamba kung’ambika. 7 Conco iwo anakodola anzawo amene anali m’bwato linalo kuti abwele kudzawathandiza. Atafika, anadzaza nsombazo m’mabwato onse awili, moti mabwatowo anayamba kumila. 8 Simoni Petulo ataona izi, anagwada pamaso pa Yesu n’kumuuza kuti: “Ambuye cokani pano pali ine cifukwa ndine munthu wocimwa.” 9 Simoni ndi amene anali naye anadabwa kwambili ndi kuculuka kwa nsomba zimene anaphazo. 10 Nawonso ana a Zebedayo, Yakobo ndi Yohane, amene anali kupha nsomba pamodzi ndi Simoni anadabwa kwambili. Koma Yesu anauza Simoni kuti: “Usacite mantha. Kuyambila lelo, uzisodza anthu amoyo.” 11 Pamenepo iwo anakokela mabwatowo ku mtunda, ndipo anasiya zonse n’kuyamba kum’tsatila.

12 Nthawi ina pamene Yesu anali mu mzinda wina, munthu wina wakhate thupi lonse ataona Yesu, anagwada mpaka nkhope yake pansi, ndipo anamucondelela kuti: “Ambuye, ngati mufuna mungandiyeletse.” 13 Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Ndifuna! Khala woyela.” Nthawi yomweyo, khate lake linathelatu. 14 Ndiyeno analamula munthuyo kuti asauze aliyense. Koma anamuuza kuti: “Pita ukadzionetse kwa wansembe, ndipo kaamba ka kuyeletsedwa kwako, ukapeleke nsembe malinga ndi zimene Mose analamula, kuti ukhale umboni kwa iwo.” 15 Koma mbili yake inapitiliza kufalikila, ndipo makamu a anthu anali kusonkhana pamodzi kuti amumvetsele, ndi kuwacilitsa matenda awo. 16 Komabe, nthawi zambili iye anali kupita ku malo kwayekha kukapemphela.

17 Tsiku lina pamene Yesu anali kuphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi a Cilamulo ocokela m’midzi yosiyanasiyana ku Galileya, Yudeya, ndi Yerusalemu, anabwela n’kudzakhala pansi pamenepo. Ndipo Yehova anapatsa Yesu mphamvu kuti athe kucilitsa. 18 Ndiyeno anthu anamubweletsela munthu wofa ziwalo ali pa macila. Ndipo iwo anali kufunafuna njila yomulowetsela mkati kuti amuike pafupi ndi Yesu. 19 Koma popeza kuti njila sanaipeze yomufikitsila pa iye cifukwa ca kuculuka kwa anthu, iwo anakwela pa mtenje n’kupanga cibowo. Kenako anatsitsa munthuyo ali pa macilawo kudzela pa cibowoco. Anamufikitsa pakati pa anthu amene anali pamaso pa Yesu. 20 Iye ataona cikhulupililo cawo anati: “Bwanawe, macimo ako akhululukidwa.” 21 Ndiyeno alembi ndi Afarisi anayamba kufunsana amvekele: “Ameneyu ndani kuti azinyoza Mulungu conci? Ndaninso wina angakhululukile macimo kupatulapo Mulungu?” 22 Koma Yesu atazindikila maganizo awo, anawafunsa kuti: “Mukuganiza ciyani m’mitima yanu? 23 Kodi capafupi n’citi, kukamba kuti ‘Macimo ako akhululukidwa,’ kapena kukamba kuti, ‘Nyamuka uyambe kuyenda?’ 24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu zokhululukila macimo padziko lapansi—” iye anauza munthu wofa ziwaloyo kuti: “Ndikukuuza kuti, Nyamuka, nyamula macila akowa, pita ku nyumba kwanu.” 25 Pamenepo iye anaimilila iwo akuona, n’kunyamula cimene anagonapo. Basi anapita kwawo akutamanda Mulungu. 26 Onsewo anadabwa kwambili ndipo anayamba kutamanda Mulungu. Iwo anacita mantha kwambili, n’kunena kuti: “Koma lelo taona zinthu zodabwitsa!”

27 Izi zitacitika iye anacoka, ndipo anaona munthu wina wokhometsa misonkho dzina lake Levi, atakhala pansi mu ofesi yokhomelamo misonkho. Ndipo anamuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” 28 Iye anasiya zonse, ndipo ananyamuka n’kuyamba kumutsatila. 29 Ndiyeno Levi anakonzela Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake, ndipo kunali anthu ambili okhometsa misonkho komanso ena amene anali kudya nawo.* 30 Afarisi ndi alembi awo ataona izi, anayamba kung’ung’udza n’kufunsa ophunzila ake kuti: “N’cifukwa ciyani mumadya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa misonkho komanso ocimwa?” 31 Yesu anawayankha kuti: “Anthu athanzi safunikila dokotala, koma odwala ndiwo amamufunikila. 32 Ine ndinabwela kudzaitana anthu ocimwa kuti alape, osati olungama.”

33 Iwo anamuuza kuti: “Ophunzila a Yohane amasala kudya kawilikawili, ndipo amapemphela mopembedzela. Ophunzila a Afarisi nawonso amacita cimodzimodzi. Koma ophunzila anu amadya ndi kumwa.” 34 Yesu anawayankha kuti: “Simungauze anzake a mkwati kuti asale kudya pamene mkwatiyo ali nawo limodzi, mungatelo kodi? 35 Koma masiku adzafika ndithu pamene mkwatiyo adzacotsedwa pakati pawo. Ndipo m’masiku amenewo adzasala kudya.”

36 Komanso anawauza fanizo lakuti: “Palibe amene amadula cigamba catsopano pa covala cakunja catsopano n’kucisokelela pa covala cakale. Akatelo, cigamba catsopanoco cimacoka ndipo cigamba ca nsalu yatsopanoco sicigwilizana ndi covala cakale. 37 Komanso palibe amene amathila vinyo watsopano m’matumba acikumba akale. Akatelo, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba a vinyoyo, ndipo vinyoyo amatayika, komanso matumba a vinyowo amawonongeka. 38 Koma vinyo watsopano ayenela kuthilidwa m’matumba acikumba atsopano. 39 Munthu akamwa vinyo wakale, safunanso kumwa watsopano, cifukwa amakamba kuti, ‘Wakale ndi wokoma kwambili.’”

6 Tsiku lina pa Sabata, Yesu anali kudutsa m’minda ya tiligu, ndipo ophunzila ake anali kubudula ngala za tiligu, kuzifilikita m’manja mwawo n’kumadya. 2 Afarisi ena ataona izi anati: “N’cifukwa ciyani mukucita zosaloleka pa Sabata?” 3 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kodi simunawelengepo zimene Davide anacita pamene iye ndi amuna omwe anali naye anamva njala? 4 Kodi si paja analowa m’nyumba ya Mulungu n’kulandila mitanda ya mkate wacionetselo ndipo anadya n’kupatsako amuna amene anali naye, umene sikunali kololeka munthu aliyense kudya koma ansembe okha?” 5 Kenako anawauza kuti: “Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”

6 Tsiku linanso pa Sabata, iye analowa m’sunagoge n’kuyamba kuphunzitsa. Ndipo mmenemo munali munthu wina wopuwala* dzanja lamanja. 7 Tsopano alembi ndi Afarisi anali kumuyang’anitsitsa Yesu kuti aone ngati amucilitse munthuyo pa Sabata. Colinga cawo cinali cakuti amuimbe mlandu. 8 Koma iye anadziwa maganizo awo. Conco anauza munthu wopuwala* dzanjayo kuti: “Nyamuka, dzaimilile pakatipa.” Munthuyo ananyamuka n’kubwela pamenepo. 9 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ndikufunseni funso amunanu. Kodi cololeka n’citi pa Sabata, kucita cabwino kapena coipa? Kupulumutsa moyo kapena kuupha?” 10 Yesu atawayang’ana onsewo, anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhala bwino. 11 Koma iwo anakwiya koopsa, ndipo anayamba kukambilana zimene angamucite Yesu.

12 Tsiku lina Yesu anapita ku phili kukapemphela, ndipo anapemphela kwa Mulungu usiku wonse. 13 Kutaca anaitana ophunzila ake, ndipo anasankhapo ophunzila 12, amenenso anawacha atumwi. 14 Anasankha Simoni, amene anamupatsanso dzina lakuti Petulo, Andireya m’bale wake, Yakobo, Yohane, Filipo, Batulomeyo, 15 Mateyo, Thomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Simoni wochedwa “wokangalika,” 16 Yudasi mwana wa Yakobo, komanso Yudasi Isikariyoti, amene anadzapeleka Yesu.

17 Ndiyeno anatsika nawo n’kuimilila pa malo afulati. Panalinso khamu lalikulu la ophunzila ake, komanso cigulu ca anthu ocokela ku Yudeya konse, ku Yerusalemu konse, komanso a kumbali kwa nyanja ya ku Turo ndi ku Sidoni. Anthu onsewo anabwela kudzamumvetsela komanso kuti adzacilitsidwe matenda awo. 18 Ngakhale amene anali kuvutitsidwa ndi mizimu yonyansa anacilitsidwa. 19 Ndipo khamu lonselo linali kufuna kumukhudza cifukwa mphamvu zinali kutuluka mwa iye, moti anthu onsewo anali kucila.

20 Ndiyeno iye atayang’ana ophunzila ake, anayamba kukamba kuti:

“Ndinu acimwemwe inu osauka, cifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wanu.

21 “Ndinu acimwemwe inu anjala palipano, cifukwa mudzakhuta.

“Ndinu acimwemwe inu amene mukulila palipano, cifukwa mudzaseka.

22 “Ndinu acimwemwe anthu akamadana nanu, akamakusalani, akamakunyozani, komanso akamaipitsa* dzina lanu cifukwa ca Mwana wa munthu. 23 Zotelezi zikakucitikilani, kondwelani ndipo lumphani mwacimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, popeza zimenezi n’zimene makolo awo akale anali kucitila aneneli.

24 “Koma tsoka kwa inu olemela, cifukwa mwalandililatu zonse zokusangalatsani.

25 “Tsoka kwa inu okhuta palipano, cifukwa mudzamva njala.

“Tsoka kwa inu amene mukuseka palipano, cifukwa mudzamva cisoni ndipo mudzalila.

26 “Muli ndi tsoka inu amene anthu onse amakukambilani zabwino, cifukwa n’zimene makolo awo akale anacitila aneneli onyenga.

27 “Koma inu amene mukumvetsela ndikukuuzani kuti: Pitilizani kukonda adani anu, kucitila zabwino anthu odana nanu, 28 kudalitsa amene amakutembelelani, komanso kupemphelela amene amakunyozani. 29 Munthu amene wakumenya ku tsaya limodzi, mupatsenso linalo. Ndipo munthu amene wakulanda covala cako cakunja, usamuletse kutenganso covala camkati. 30 Munthu aliyense akakupempha cinthu mupatse, ndipo munthu amene wakulanda zinthu zako usamuuze kuti akubwezele.

31 “Komanso zimene mumafuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.

32 “Ngati mumakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzapeza phindu lanji? Pakuti ngakhale ocimwa amakonda anthu amene amawakonda. 33 Ndipo ngati mumacitila zabwino anthu okhawo amene amakucitilani zabwino, kodi mudzapeza phindu lanji? Pakuti ngakhale ocimwa amacita cimodzimodzi. 34 Komanso ngati mumabweleketsa* anthu okhawo amene muyembekezela kuti angakubwezeleni, kodi pali phindu lanji? Pakuti ngakhale ocimwa amabweleketsa ocimwa anzawo kuti adzawabwezele. 35 Mosiyana ndi amenewo, inuyo pitilizani kukonda adani anu ndi kucita zabwino, komanso kubweleketsa popanda kuyembekezela kanthu. Mukatelo, mudzalandila mphoto yaikulu, ndipo mudzakhala ana a Wapamwambamwamba, cifukwa iye ndi wokoma mtima kwa osayamikila ndi oipa. 36 Pitilizani kukhala acifundo monga Atate wanu amenenso ndi wacifundo.

37 “Komanso, lekani kuweluza ena, ndipo inunso simudzaweluzidwa. Lekani kutsutsa ena, ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitilizani kukhululukila ena,* ndipo inunso mudzakhululukidwa.* 38 Khalani opatsa, ndipo inunso anthu adzakupatsani. Iwo adzakukhuthulilani muyeso wabwino pa malaya anu, wosindilika, wokhuchumuka, komanso wosefukila. Pakuti muyeso umene mukupimila ena, inunso adzakupimilani womwewo.”

39 Ndiyeno anawauzanso fanizo lakuti: “Munthu wakhungu sangatsogolele wakhungu mnzake, angatelo ngati? Ngati angatelo, onse adzagwela m’dzenje, si conco? 40 Wophunzila saposa mphunzitsi wake, koma munthu aliyense wophunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake. 41 Nanga n’cifukwa ciyani ukuyang’ana kacitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaona mtanda wa mtenje wa nyumba umene uli m’diso lako? 42 Ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘M’bale, leka ndikucotse kacitsotso kamene kali m’diso lako,’ pamene iwe sukuona mtanda wa mtenje wa nyumba umene uli m’diso lako? Wonyenga iwe! Coyamba, cotsa mtanda wa nyumba umene uli m’diso lakowo. Ukatelo, udzatha kuona bwinobwino mmene ungacotsele kacitsotso kamene kali m’diso la m’bale wako.

43 “Kulibe mtengo wabwino umene umabala zipatso zoipa, ndipo kulibe mtengo woipa umene umabala zipatso zabwino. 44 Pakuti mtengo uliwonse umadziwika ndi zipatso zake. Mwacitsanzo, anthu sathyola nkhuyu mu mtengo wa minga, kapena kudula mphesa pa citsamba ca minga. 45 Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’cuma cabwino ca mumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’cuma cake coipa. Pakuti pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima.

46 “Nanga n’cifukwa ciyani mumandichula kuti ‘Ambuye! Ambuye!’ koma osacita zimene ndimanena? 47 Aliyense wobwela kwa ine ndi kumvetsela mawu anga komanso kuwacita, ndikuuzani amene amafanana naye: 48 Iye ali ngati munthu amene pomanga nyumba, anakumba mozama kwambili n’kuyala maziko pa thanthwe. Mtsinje utasefukila, madzi anawomba nyumbayo. Koma sinagwedezeke cifukwa inali yomangidwa bwino. 49 Koma munthu amene amamva mawu osacitapo kanthu, ali ngati munthu amene anamanga nyumba yopanda maziko. Madzi a mtsinje ataiwomba, nyumbayo inagwa nthawi yomweyo, ndipo kuwonongeka kwake kunali kwakukulu.”

7 Yesu atatsiliza kukamba zimene anali kufuna kuuza anthu, analowa mu mzinda wa Kaperenao. 2 Tsopano kapitawo wa asilikali anali ndi kapolo amene anali kum’konda kwambili. Kapoloyo anadwala kwambili, ndipo anali atatsala pang’ono kumwalila. 3 Kapitawoyo atamva za Yesu, anatumiza akulu a Ayuda kuti akamupemphe kuti abwele kudzacilitsa kapolo wakeyo. 4 Iwo anafika kwa Yesu n’kuyamba kumucondelela ndi mtima wonse kuti: “Munthu ameneyu ndi woyeneladi kum’citila zimenezi, 5 cifukwa amatikonda ife Ayuda, ndipo ndiye anatimangila ngakhale sunagoge wathu.” 6 Conco Yesu anapita nawo limodzi. Koma atatsala pang’ono kufika pa nyumba, kapitawo wa asilikali uja anali atatuma kale anzake kuti akauze Yesu kuti: “Bambo, musavutike kudzalowa m’nyumba mwanga, ine sindine woyenelela kuti inu mudzalowe m’nyumba mwanga. 7 N’cifukwa cake ndaona kuti sindine woyenela kubwela kwa inu. Conco mungokamba mawu kuti wanchito wanga acile. 8 Pakuti inenso ndili ndi akuluakulu amene amandilamulila, ndipo ndili ndi asilikali amene ndimawalamulila. Ndikauza uyu kuti, ‘Pita!’ amapita. Ndikauza wina kuti, ‘Bwela!’ amabwela, ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Cita ici!’ amacita.” 9 Yesu atamva zimenezi anadabwa naye kwambili munthuyo, ndipo anatembenuka n’kuuza khamu la anthu limene linali kumutsatila kuti: “Kukuuzani zoona, ngakhale mu Isiraeli sindinapezemo munthu wa cikhulupililo cacikulu ngati ici.” 10 Amene anatumidwawo atabwelela kunyumba kwa kapitawo wa asilikaliyo, anapeza kuti kapolo uja wacila.

11 Posapita nthawi, iye ananyamuka n’kupita ku mzinda wochedwa Naini, ndipo ophunzila ake pamodzi ndi khamu lalikulu la anthu anali kuyenda naye limodzi. 12 Atatsala pang’ono kufika pa geti ya mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula malilo. Amene anamwalilayo anali mwana wamwamuna mmodzi yekhayo wa mayi amenenso anali wamasiye. Ndipo gulu lalikulu ndithu la anthu ocokela mu mzindawo linali naye. 13 Ambuye atamuona mayiyo, anamumvela cisoni ndipo anamuuza kuti: “Usalile.” 14 Atatelo, anafika pafupi n’kugwila macila, ndipo onyamula mtembowo anaima. Kenako Yesu anati: “Mnyamatawe, ndikukuuza kuti, uka!” 15 Munthu wakufayo anakhala tsonga n’kuyamba kulankhula, ndipo Yesu anamupeleka kwa mayi ake. 16 Ndiyeno anthu onsewo anagwidwa ndi mantha, ndipo anayamba kutamanda Mulungu, amvekele: “Mneneli wamkulu waonekela pakati pathu,” ndipo anali kunenanso kuti, “Mulungu wakumbukila anthu ake.” 17 Mbili yokhudza iye inafalikila mu Yudeya monse komanso m’madela onse ozungulila.

18 Tsopano ophunzila a Yohane anamufotokozela zinthu zonsezi Yohaneyo. 19 Conco Yohane anaitana awili mwa ophunzila ake, ndipo anawatuma kwa Ambuye kukafunsa kuti: “Kodi Mesiya uja amene tikumuyembekezela ndinu, kapena tiyembekezelebe wina?” 20 Amunawo atafika kwa iye, anamuuza kuti: “Yohane M’batizi watituma kuti tidzakufunseni kuti, ‘Kodi Mesiya uja amene tikumuyembekezela ndinu, kapena tiyembekezelebe wina?’” 21 Nthawi imeneyo Yesu anacilitsa anthu ambili odwala matenda aang’ono komanso aakulu. Ndipo anatulutsa mizimu yonyansa ndi kuthandiza anthu ambili akhungu kuyamba kuona. 22 Poyankha iye anawauza kuti: “Pitani mukamuuze Yohane zimene mwaona ndi kumva: Tsopano akhungu akuona, olemala akuyenda, akhate akuyeletsedwa, ogontha akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo osauka akuuzidwa uthenga wabwino. 23 Wacimwemwe ndi munthu amene sapeza copunthwitsa mwa ine.”

24 Ophunzila a Yohane atapita, Yesu anayamba kulankhula ndi khamu la anthulo za Yohane kuti: “Kodi munapita ku cipululu kukaona ciyani? Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo? 25 Nanga munapita kukaona ciyani? Munthu wovala zovala zapamwamba?* Iyai, anthu ovala zovala zabwino kwambili komanso okhala umoyo wawofuwofu amapezeka m’nyumba za mafumu. 26 Ndiye munapita kukacita ciyani kumeneko? Kukaona mneneli? Inde, ndikukuuzani kuti iye amaposanso aneneli. 27 Uyu ndi amene Malemba amati za iye: ‘Taona! Ndikutumiza mthenga wanga patsogolo pako,* amene adzakukonzela njila.’ 28 Ndikukuuzani kuti, pa anthu onse obadwa kwa akazi, palibe aliyense wamkulu kuposa Yohane. Koma wocepelapo mu Ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.” 29 (Pamene anthu onse ndi okhometsa misonkho anamva zimenezi, anavomeleza kuti Mulungu ndi wolungama, popeza onsewo anabatizidwa ndi ubatizo wa Yohane. 30 Koma Afarisi ndi anthu odziwa bwino Cilamulo ananyalanyaza uphungu* umene Mulungu anawapatsa, cifukwa sanabatizidwe ndi Yohane.)

31 “Ndiye kodi amuna a m’badwo uwu ndiwayelekezele ndi ndani? Nanga kodi afanana ndi ndani? 32 Ali ngati ana aang’ono opezeka m’misika, amene akuitanana kuti: ‘Tinakuimbilani citolilo, koma inu simunavine ayi. Tinalila mokweza, koma inu simunalile ayi.’ 33 Mofananamo, Yohane M’batizi anabwela ndipo sakudya mkate kapena kumwa vinyo, koma inu mukumunena kuti: ‘Iye ali ndi ciwanda.’ 34 Mwana wa munthu wabwela, ndipo amadya ndi kumwa, koma inu mumati: ‘Taonani! Munthu wosusuka komanso wokondetsetsa kumwa vinyo, bwenzi la okhometsa misonkho ndi ocimwa!’ 35 Mulimonsemo, nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama mwa zotulukapo zake.”*

36 Tsopano mmodzi wa Afarisi anali kumucondelela kuti akadye naye. Conco Yesu analowa m’nyumba ya Mfarisiyo, ndipo anadya naye pa thebulo. 37 Ndipo mayi wina amene anali kudziwika kuti ndi wocimwa mu mzindamo, anadziwa kuti Yesu akudya cakudya* m’nyumba ya Mfarisiyo. Conco iye anabweletsa botolo lamwala wa alabasitala, mmene munali mafuta onunkhila. 38 Mayiyo anagwada pa mapazi ake n’kuyamba kulila, ndipo ananyowetsa mapazi a Yesu ndi misozi yake. Kenako anawapukuta ndi tsitsi lake. Komanso anapsompsona mapazi ake ndi kuwathila mafuta onunkhila. 39 Mfarisi amene anamuitanayo ataona zimenezo, anati mumtima mwake: “Munthuyu akanakhaladi mneneli, akanadziwa kuti mayiyu ndi munthu wotani. Akanadziwa kuti ndi wocimwa.” 40 Koma Yesu anamuuza kuti: “Simoni, ndifuna ndikuuze zinazake.” Iye anati: “Mphunzitsi, ndiuzeni!”

41 “Amuna awili anali ndi nkhongole kwa munthu wokongoza ndalama. Mmodzi anali ndi nkhongole yokwana madinari 500, koma winayo madinari 50. 42 Iwo atasowa comubwezela, wowakongozayo anawakhululukila onse awili ndi mtima wonse. Pa awiliwo, ndani adzakonda kwambili wowakongozayo?” 43 Simoni anayankha kuti: “Ndiona kuti ndi uja amene anali ndi nkhongole yaikulu.” Yesu anamuuza kuti: “Wayankha bwino.” 44 Pamenepo Yesu anayang’ana mayiyo n’kuuza Simoni kuti: “Wamuona mayiyu? Ndalowa m’nyumba mwako, koma iwe sunandipatse madzi osambikila mapazi anga. Koma mayiyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake n’kuwapukuta ndi tsitsi lake. 45 Iwe sunandipsompsone. Koma mayiyu, kucokela pomwe ndalowa muno, sanaleke kupsompsona mapazi anga mwacikondi. 46 Iwe sunathile mafuta pamutu panga, koma mayiyu wathila mapazi anga mafuta onunkhila. 47 Pa cifukwa cimeneci, ndikukuuza kuti ngakhale kuti macimo ake ndi ambili,* iye wakhululukidwa cifukwa waonetsa cikondi cacikulu. Koma amene wakhululukidwa zocepa, amaonetsa cikondi cocepa.” 48 Kenako anamuuza kuti: “Macimo ako akhululukidwa.” 49 Anthu amene anali kudya naye pa thebulopo anayamba kufunsana kuti: “Munthu ameneyu ndani kodi, amene amatha ngakhale kukhululukila macimo?” 50 Koma iye anauza mayiyo kuti: “Cikhulupililo cako cakupulumutsa, pita mu mtendele.”

8 Posakhalitsa, Yesu anayamba kuyenda mzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi, akumalalikila ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye. 2 Analinso ndi azimayi ena omwe anawatulutsa mizimu yonyansa ndi kuwacilitsa matenda awo. Maina awo anali Mariya wochedwanso Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7; 3 Jowana mkazi wa Kuza amene anali woyang’anila nyumba ya Herode, Suzana, ndi azimayi ena ambili amene anali kutumikila Yesu ndi atumwiwo pogwilitsa nchito zinthu zawo.

4 Tsopano khamu lalikulu la anthu litasonkhana pamodzi ndi amene anali kumulondola kucokela m’mizinda yosiyanasiyana, anawafotokozela fanizo lakuti: 5 “Munthu wina anapita kukafesa mbewu. Pamene anali kufesa mbewuzo, zina zinagwela m’mbali mwa msewu, ndipo mbalame zinabwela n’kuzidya. 6 Zina zinagwela pa thanthwe,* ndipo zitamela zinauma cifukwa panalibe cinyontho. 7 Mbewu zina zinagwela pa minga, ndipo minga zimene zinakulila pamodzi ndi mbewuzo zinalepheletsa mbewuzo kukula. 8 Koma zina zinagwela pa nthaka yabwino, ndipo zitamela zinabala zipatso kuwilikiza maulendo 100.” Iye atakamba izi, analankhula mokweza kuti: “Amene ali ndi matu akumva, amve!”

9 Koma ophunzila ake anamufunsa tanthauzo la fanizo limeneli. 10 Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi womvetsa zinsinsi za Ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawa, zonse ndi mafanizo cabe, kuti ngakhale aone, kuona kwawo kukhale kopanda phindu, ndipo ngakhale amve, kumva kwawo kukhale kopanda phindu. 11 Tsopano tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. 12 Mbewu zogwela m’mbali mwa msewu zija ndi anthu amene amamva mawu, koma Mdyelekezi amabwela n’kucotsa mawuwo m’mitima yawo n’colinga cakuti asakhulupilile ndi kupulumutsidwa. 13 Mbewu zogwela pa thanthwe zija ndi anthu amene amamva mawu, ndipo amawalandila mwacimwemwe. Koma mawuwo sazika mizu mwa iwo ayi. Iwo amakhulupilila kwa kanthawi, koma nthawi yoyesedwa ikafika amagwa. 14 Mbewu zimene zimagwela pa minga ndi anthu amene amamva mawu, koma amatengeka ndi nkhawa, cuma, komanso zosangalatsa za moyo uno, moti amalephela kukula ndipo zipatso zawo sizikhwima. 15 Koma mbewu zimene zinagwela pa nthaka yabwino ndi anthu a mtima wabwino, amene pambuyo pomva mawu, amawasunga ndipo amabala zipatso mopilila.

16 “Palibe munthu amene amati akayatsa nyale, amaibwinikila ndi ciwiya kapena kuiika kunsi kwa bedi. Koma amaiika pa coikapo nyale kuti olowa m’nyumbamo aziona kuwala. 17 Pakuti palibe cobisika cimene sicidzaululika. Palibenso ciliconse cobisidwa mosamalitsa cimene sicidzadziwika kapena kuonekela poyela. 18 Conco, muzimvetsela mosamala kwambili, cifukwa aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zoculuka. Koma aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene amaganiza kuti ali nazo.”

19 Tsopano amayi ake ndi abale ake anabwela kwa iye. Koma sanathe kufika pafupi naye cifukwa ca khamu la anthu. 20 Conco, iye anauzidwa kuti: “Mayi anu ndi abale anu aimilila panja, afuna kuonana nanu.” 21 Iye anawayankha kuti: “Mayi anga ndi abale anga ndi awa amene amamvetsela mawu a Mulungu ndi kucita zimene mawuwo amanena.”

22 Tsiku lina, Yesu ndi ophunzila ake anakwela m’bwato, ndipo anauza ophunzilawo kuti: “Tiyeni tiwolokele ku tsidya lina la nyanja.” Conco anayamba kupalasila kumeneko. 23 Koma pamene iwo anali kupalasila kumeneko, Yesu anagona. Ndipo pa nyanjapo panauka namondwe woopsa, moti madzi anayamba kulowa m’bwatomo, ndipo bwatolo linatsala pang’ono kumila. 24 Pamenepo iwo anapita kukamuutsa n’kumuuza kuti: “Mlangizi, Mlangizi, tikufa!” Iye atamva zimenezi, ananyamuka n’kudzudzula mphepoyo ndi mafunde amphamvuwo, ndipo zinaleka. Kenako panakhala bata. 25 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Cikhulupililo canu cili kuti?” Koma iwo anacita mantha ndipo anadabwa kwambili, moti anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani makamaka? Cifukwa akulamula ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zikumumvela!”

26 Ndiyeno iwo anakoceza bwato lawo m’mbali mwa nyanja, m’cigawo ca Agerasa, cimene n’copenyana ndi Galileya. 27 Yesu atatuluka m’bwato n’kufika kumtunda, anakumana ndi munthu wina wogwidwa ndi ciwanda wocokela mumzindawo. Kwa nthawi ndithu, munthuyo anali kukhala wosavala, ndipo sanali kukhala m’nyumba koma kumanda.* 28 Iye ataona Yesu, anakuwa n’kugwada pamaso pake, ndipo anafuula mokweza kuti: “Mufuna ciyani kwa ine, inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wapamwambamwamba? Ndikukucondelelani kuti musandizunze ayi.” 29 (Pakuti Yesu anali atauza mzimu wonyansawo kuti utuluke mwa munthuyo. Nthawi zambili, mzimuwo unali kumugwila* mwamphamvu, ndipo mobwelezabweleza anali kumumanga ndi macheni, kumuika m’matangadza, komanso kumulonda. Koma anali kudula macheniwo n’kuthawila kumalo opanda anthu motsogoleledwa ndi ciwandaco.) 30 Yesu anamufunsa kuti: “Dzina lako ndani?” Iye anati: “Ndine Khamu.” Anatelo cifukwa mwa iye munali mutalowa ziwanda zambili. 31 Koma ziwandazo zinali kumucondelela Yesu kuti asazilamule kuti zipite kuphompho. 32 Tsopano gulu lalikulu la nkhumba linali kudya kumeneko paphili. Conco, ziwandazo zinamucondelela kuti azilole zikalowe m’nkhumbazo, ndipo anazilola. 33 Pamenepo ziwandazo zinatuluka mwa munthuyo n’kukalowa m’nkhumbazo. Zitatelo, nkhumbazo zinathamangila ku phompho mpaka kukagwela m’nyanja ndipo zinamila. 34 Koma owetela nkhumbazo ataona zimene zinacitikazo, anathawa n’kukafotokozela anthu mumzinda ndi m’midzi.

35 Ndiyeno anthu anapita kukaona zimene zinacitikazo. Atafika kwa Yesu, anapeza kuti munthu uja amene anatulutsidwa ziwanda ali khale ku mapazi a Yesu, atavala komanso maganizo ake ali bwinobwino. Iwo anacita mantha. 36 Amene anaona zimene zinacitikazo, anawafotokozela mmene munthu wogwidwa ndi ziwandayo anacilitsidwila. 37 Kenako gulu lalikulu la anthu ocokela m’madela ozungulila cigawo ca Agerasa linapempha Yesu kuti acoke m’cigawoco, cifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Zitatelo, iye anapita kukakwela bwato n’kucoka. 38 Komabe, munthu amene anam’tulutsa ziwanda uja anacondelela Yesu mobwelezabweleza kuti apite naye. Koma Yesu anamubweza n’kunena kuti: 39 “Pita kwanu, ndipo uzifotokoza zimene Mulungu wakucitila.” Conco iye anacoka n’kuyamba kulengeza mumzinda wonsewo zimene Yesu anamucitila.

40 Yesu atafika ku Galileya, khamu la anthu linamulandila bwino cifukwa anali kumuyembekezela. 41 Koma kunabwela munthu wina dzina lake Yairo, ndipo munthu ameneyo anali mtsogoleli wa sunagoge. Iye anagwada pa mapazi a Yesu n’kuyamba kumucondelela kuti apite kunyumba kwake, 42 cifukwa mwana wake wamkazi mmodzi yekhayo, wa zaka pafupifupi 12 anali pafupi kumwalila.

Pamene Yesu anali kupita kumeneko, khamu la anthu linali kumupanikiza. 43 Tsopano panali mayi wina wodwala matenda otaya magazi kwa zaka 12, ndipo palibe amene anakwanitsa kumucilitsa. 44 Mayiyo anayandikila Yesu kumbuyo n’kugwila ulusi wopota wa covala cake cakunja, ndipo nthawi yomweyo matenda ake otaya magazi anatha. 45 Conco Yesu anafunsa kuti: “Ndani wandigwila?” Pamene onse anali kukana, Petulo anati: “Mlangizi, simukuona kuti khamuli lakuzungulilani ndipo likukupanikizani?” 46 Koma Yesu anati: “Munthu wina wandigwila. Ndadziwa cifukwa mphamvu yatuluka mwa ine.” 47 Mayiyo ataona kuti wadziwika, anapita kwa Yesu n’kugwada pamaso pake akunjenjemela. Ndipo anafotokoza pamaso pa anthu onsewo cifukwa cake anamugwila, komanso mmene anacilila nthawi yomweyo. 48 Koma Yesu anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele.”

49 Ali mkati molankhula, kunabwela mthenga wocokela kunyumba ya mtsogoleli wa sunagoge uja. Iye anati: “Mwana wanu wamwalila. Musamuvutitse Mphunzitsiyu.” 50 Yesu atamva zimenezi, anauza Yairo kuti: “Usacite mantha. Ungokhala ndi cikhulupililo ndipo mwana wako akhalanso ndi moyo.”* 51 Atafika kunyumbako, iye sanalole aliyense kulowa naye, kupatulapo Petulo, Yohane, Yakobo, komanso tate ndi mayi a mtsikanayo. 52 Koma anthu onse anali kulila ndi kudziguguda pa cifuwa mwacisoni kaamba ka mwanayo. Conco iye anati: “Tontholani, cifukwa mwanayu sanamwalile koma wagona.” 53 Anthuwo atamva zimenezi, anayamba kumuseka monyodola cifukwa anadziwa kuti mwanayo wamwaliladi. 54 Koma Yesu anamugwila dzanja n’kumuitana kuti: “Mwanawe, uka!” 55 Zitatelo, mzimu* wa mtsikanayo unabwelela mwa iye, ndipo nthawi yomweyo anauka. Kenako Yesu anawauza kuti am’patse cakudya mtsikanayo. 56 Makolo a mtsikanayo anakondwela kwambili, koma iye anawauza kuti asauzeko aliyense zimene zinacitikazo.

9 Ndiyeno Yesu anasonkhanitsa atumwi ake 12 aja n’kuwapatsa mphamvu ndi ulamulilo kuti azitha kutulutsa ziwanda zonse ndi kucilitsa matenda. 2 Iye anawatumiza kuti akalalikile za Ufumu wa Mulungu, komanso kucilitsa anthu. 3 Anawauza kuti: “Musanyamule ciliconse pa ulendowu, kaya ndodo, cola ca zakudya, mkate, ndalama,* kapena zovala ziwili.* 4 Koma nthawi zonse mukalowa m’nyumba, muzikhala mmenemo mpaka nthawi yocoka kumeneko. 5 Ndipo kulikonse kumene anthu sakakulandilani, pocoka mu mzindawo muzikutumula fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni wowatsutsa.” 6 Ndiyeno ananyamuka n’kuyamba kuyenda m’cigawoco mudzi ndi mudzi akulengeza uthenga wabwino ndi kucilitsa anthu kulikonse.

7 Tsopano Herode* wolamulila cigawo* ca Galileya, anamva zonse zimene zinali kucitika. Iye anadabwa kwambili, cifukwa anthu ena anali kunena kuti Yohane waukitsidwa kwa akufa. 8 Koma ena anali kunena kuti Eliya waonekela, ndipo ena anali kunena kuti mmodzi wa aneneli akale wauka. 9 Herode anati: “Yohane ndinamudula mutu, nanga amene akucita zimene ndikumvazi ndani?” Conco iye anali kufunitsitsa kuona Yesu.

10 Atumwiwo atabwelako, anafotokozela Yesu zonse zimene iwo anacita. Pambuyo pake, iye anawatenga n’kupita nawo kwaokha ku mzinda wochedwa Betsaida. 11 Koma khamu la anthu litadziwa zimenezi linamutsatila, ndipo iye anawalandila mokoma mtima. Kenako anayamba kuwauza za Ufumu wa Mulungu, komanso anacilitsa odwala. 12 Ndiyeno madzulo tsiku limenelo, atumwi ake 12 aja anabwela kwa iye n’kumuuza kuti: “Uzani khamu la anthuwa kuti apite m’midzi ya pafupi ndi m’madela ozungulila kuti akapezeko malo ogona komanso cakudya, cifukwa kuno tili n’kopanda anthu.” 13 Koma iye anawauza kuti: “Inuyo muwapatse cakudya.” Iwo anati: “Tili cabe ndi mitanda isanu ya mkate ndi nsomba ziwili. Kapena mwina tipite ndife kukagula cakudya ca anthu onsewa?” 14 Panali amuna pafupifupi 5,000. Koma iye anauza ophunzila ake kuti: “Auzeni anthuwa kuti akhale pansi m’magulumagulu a anthu pafupifupi 50.” 15 Ophunzilawo anatelo, ndipo anthu onsewo anakhala pansi. 16 Atatenga mitanda isanu ija ndi nsomba ziwili zija, anayang’ana kumwamba n’kuzidalitsa. Kenako anazinyemanyema n’kuyamba kuzipeleka kwa ophunzila ake kuti agawile khamu la anthulo. 17 Cotelo onse anadya n’kukhuta. Zotsala anazisonkhanitsa pamodzi, ndipo zinadzaza matadza 12.

18 Patapita nthawi Yesu akupemphela kwayekha, ophunzila ake anabwela kwa iye, ndipo anawafunsa kuti: “Kodi anthu amati ndine ndani?” 19 Iwo poyankha anati: “Amati ndinu Yohane M’batizi, koma ena amati ndinu Eliya. Ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneli akale amene wauka.” 20 Ndiyeno anafunsa ophunzilawo kuti: “Nanga inu mumati ndine ndani?” Petulo anamuyankha kuti: “Ndinu Khristu wa Mulungu.” 21 Ndiyeno anawalamula mwamphamvu kuti asauzeko aliyense zimenezi. 22 Iye anakambanso kuti: “Mwana wa munthu ayenela kukumana ndi masautso ambili, ndiponso kukanidwa ndi akulu, ansembe aakulu, komanso alembi, kenako adzaphedwa. Ndipo pa tsiku lacitatu adzaukitsidwa.”

23 Ndiyeno anauza onsewo kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatila adzikane yekha, ndipo anyamule mtengo wake wozunzikilapo* tsiku ndi tsiku n’kupitiliza kunditsatila. 24 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine ndi amene adzaupeza. 25 Kunena zoona, kodi pali phindu lanji munthu atapeza zinthu zonse za m’dzikoli, koma n’kutaya moyo wake kapena kudzivulaza? 26 Pakuti aliyense wocita manyazi ndi ine komanso mawu anga, Mwana wa munthu adzacitanso naye manyazi akadzabwela mu ulemelelo wake, wa Atate wake, komanso wa angelo oyela. 27 Koma ndithu ndikukuuzani, pali ena pano amene sadzalawa imfa ngakhale pang’ono, mpaka coyamba ataona Ufumu wa Mulungu.”

28 Patapita masiku pafupifupi 8 Yesu atakamba mawu amenewa, anatenga Petulo, Yohane, ndi Yakobo n’kukwela nawo m’phili kukapemphela. 29 Ali mkati mopemphela, maonekedwe a nkhope yake anasintha. Zovala zakenso zinayela mbee n’kunyezimila. 30 Kenako panaonekela amuna awili akulankhula naye. Amunawo anali Mose ndi Eliya. 31 Maonekedwe awo anali aulemelelo, ndipo anayamba kukambilana za mmene Yesu adzacokele pa dziko. Izi zinali zitatsala pang’ono kukwanilitsika ku Yerusalemu. 32 Tsopano Petulo ndi amene anali naye anamva tulo kwambili. Koma tulo tutawathela, anaona ulemelelo wa Yesu komanso amuna awili ataimilila naye. 33 Pamene amunawo anali kusiyana naye, Petulo anauza Yesu kuti: “Mlangizi, zili bwino kuti ife tizikhala pompano. Ngati mufuna, ndingakhome matenti atatu pano. Ina yanu, ina ya Mose, inanso ya Eliya.” Iye sanadziwe zimene anali kukamba. 34 Koma pamene anali kukamba izi, kunacita mtambo ndipo unayamba kuwaphimba. Pamene mtambowo unali kuwaphimba, iwo anacita mantha. 35 Kenako mumtambomo munamveka mawu akuti: “Uyu ndi Mwana wanga amene ndinamusankha. Muzimumvela.” 36 Pamene mawuwo anali kumveka, iwo anangoona kuti Yesu ali yekha. Koma pa masiku amenewo, iwo anangokhala cete osauzako aliyense zimene anaonazo.

37 Tsiku lotsatila iwo atatsika m’phili muja, khamu lalikulu linamucingamila. 38 Ndiyeno munthu wina anafuula m’khamulo kuti: “Mphunzitsi, ndikukupemphani kuti mudzaone mwana wanga wamwamuna, cifukwa ndi mmodzi yekhayo. 39 Mzimu umamugwila, ndipo mwadzidzidzi amakuwa. Zikatelo, umamugwetsela pansi ndipo amayamba kupalapata uku akucoka thovu kukamwa. Komanso umavuta kuti umuleke ngakhale utamuvulaza. 40 Ndinacondelela ophunzila anu kuti autulutse koma analephela.” 41 Yesu anayankha kuti: “Inu m’badwo wopanda cikhulupililo komanso wopotoka maganizo, kodi ndikhalabe nanu ndi kukupililani mpaka liti? M’bweletse kuno mwana wako.” 42 Koma ngakhale pamene mwanayo anali kupita kwa iye, ciwandaco cinamugwetsela pansi, n’kumupangitsa kupalapata mwamphamvu. Koma Yesu anakalipila mzimu wonyansawo ndi kucilitsa mnyamatayo, ndipo anamupeleka kwa atate ake. 43 Anthu onsewo anadabwa ndi mphamvu zazikulu za Mulungu.

Pamene anthu onsewo anali kudabwa ndi zonse zimene Yesu anali kucita, iye anauza ophunzila ake kuti: 44 “Mvetselani mwachelu ndipo muzikumbukila mawu awa, cifukwa Mwana wa munthu adzapelekedwa m’manja mwa anthu.” 45 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la zimene iye anali kukamba. Zinabisidwa kwa iwo kuti asamvetse tanthauzo lake, ndipo anaopa kumufunsa tanthauzo la zimene ananenazo.

46 Kenako ophunzilawo anayamba kukangana pakati pawo zakuti wamkulu kwambili ndani. 47 Yesu atazindikila zimene anali kuganiza m’mitima yawo, anatenga mwana wamng’ono n’kumuimika pambali pake. 48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense wolandila mwana wamng’ono ngati uyu* cifukwa ca dzina langa, walandilanso ine. Ndipo aliyense wolandila ine walandilanso Iye amene anandituma. Pakuti aliyense wocita zinthu ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndiye wamkulu.”

49 Ndiyeno Yohane anati: “Mlangizi, ife taona winawake akutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndipo tamuletsa cifukwa sayenda nafe.” 50 Koma Yesu anati kwa iye: “Musamuletse, cifukwa aliyense amene satsutsana nanu ali ku mbali yanu.”

51 Masiku atayandikila* oti Yesu atengedwe kupita kumwamba, iye anatsimikiza mtima kupita ku Yerusalemu. 52 Conco anatumiza ena mwa ophunzila ake kuti atsogole. Iwo anapita ndipo anakalowa m’mudzi winawake wa Asamariya kuti akonzekele kufika kwake. 53 Koma anthu a m’mudziwo ataona kuti Yesu watsimikiza mtima kuti apita ku* Yerusalemu, sanamulandile. 54 Ophunzila ake, Yakobo ndi Yohane ataona izi, anati: “Ambuye, kodi mufuna kuti tiwaitanile moto kucokela kumwamba kuti uwanyeketse?” 55 Koma iye anaceuka n’kuwadzudzula. 56 Cotelo iwo anapita ku mudzi wina.

57 Pamene iwo anali kuyenda m’njila, munthu wina anauza Yesu kuti: “Ndikutsatilani kulikonse kumene mungapite.” 58 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga awo, ndipo mbalame za mumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibe nyumba yakeyake.”* 59 Kenako anauza munthu wina kuti: “Khala wotsatila wanga.” Munthuyo anati: “Ambuye, ndiloleni coyamba ndipite ndikaike malilo a atate anga.” 60 Koma iye anamuyankha kuti: “Aleke akufa aike akufa awo. Koma iwe pita ukalengeze Ufumu wa Mulungu kulikonse.” 61 Winanso anati: “Ine ndikutsatilani Ambuye, koma ndiloleni coyamba ndipite ndikalayile kwa a m’banja langa.” 62 Yesu anamuuza kuti: “Munthu wogwila pulawo n’kumayang’ana zinthu zakumbuyo sayenelela Ufumu wa Mulungu.”

10 Pambuyo pa zimenezi, Ambuye anasankha anthu ena 70 n’kuwatumiza awiliawili kuti atsogole kupita ku mizinda ndi ku malo osiyanasiyana kumene iye anali kufunika kupitako. 2 Kenako anawauza kuti: “Zoonadi, zokolola n’zoculuka koma anchito ndi ocepa. Conco pemphani Mwini zokolola kuti atumize anchito okakolola. 3 Pitani! Taonani, ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu. 4 Musanyamule zikwama za ndalama, kapena cola ca zakudya, kapenanso nsapato. Ndipo musapatse moni* munthu aliyense m’njila. 5 Mukalowa m’nyumba iliyonse, muzinena kuti: ‘Mtendele ukhale panyumba ino.’ 6 Ndipo ngati panyumbapo pali munthu wokonda mtendele, mtendele wanu udzakhala pa iye. Koma ngati palibe, mtendele wanu udzabwelela kwa inu. 7 Muzikhala m’nyumba imeneyo, ndipo muzidya ndi kumwa zimene angakupatseni. Pakuti wanchito ayenela kulandila malipilo ake. Musamacoke kumene mwafikilako n’kupita kunyumba zina.

8 “Ndiponso mukalowa mumzinda, anthuwo n’kukulandilani, muzidya zimene akukonzelani. 9 Komanso muzicilitsa odwala mumzindawo ndi kuwauza kuti: ‘Ufumu wa Mulungu wakuyandikilani.’ 10 Koma mukalowa mumzinda ndipo sanakulandileni, muzipita m’misewu yake n’kunena kuti: 11 ‘Tikukutumula fumbi la mumzinda wanu limene lakhala ku mapazi athu, monga umboni wokutsutsani. Koma dziwani kuti Ufumu wa Mulungu wayandikila.’ 12 Ndikukuuzani kuti cilango ca Sodomu cidzakhala cocepelako poyelekezela ndi ca mzinda umenewo.

13 “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwenso Betsaida! Cifukwa nchito zamphamvu zimene zacitika mwa inu, zikanacitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu kumeneko akanalapa kalekale, ndipo akanavala masaka aciguduli n’kukhala pa phulusa. 14 Conco, cilango ca Turo ndi Sidoni pa Tsiku la Ciweluzo cidzakhala cocepelako poyelekezela ndi canu. 15 Ndipo iwe Kaperenao, kodi mwina udzakwezedwa kumwamba? Ayi udzatsikila ku Manda!*

16 “Amene amakumvelani amamvelanso ine. Ndipo amene amakunyalanyazani amanyalanyazanso ine. Komanso amene amanyalanyaza ine amanyalanyazanso Iye amene anandituma.”

17 Ndiyeno ophunzila 70 aja anabwelela ali ndi cimwemwe, ndipo anati: “Ambuye, ngakhale ziwanda zinali kutigonjela tikagwilitsa nchito dzina lanu.” 18 Iye atamva zimenezi anati: “Ndikuona Satana atagwa kale ngati mphenzi kucokela kumwamba. 19 Taonani! ndakupatsani ulamulilo wopondaponda njoka ndi zinkhanila, komanso ulamulilo wogonjetsa mphamvu zonse za mdani. Ndipo palibe ciliconse cimene cidzakuvulazani. 20 Komabe, musakondwele kuti mizimu yakugonjelani. Koma kondwelani cifukwa cakuti maina anu alembedwa kumwamba.” 21 Pa nthawi imeneyo, iye anakondwela kwambili mwa mzimu woyela, ndipo anati: “Ndikukutamandani inu Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, cifukwa zinthu zimenezi mwazibisa mosamala kwa anthu anzelu komanso ophunzila kwambili, koma mwaziulula kwa ana aang’ono. Inde Atate, cifukwa munaona kuti zimenezi ndiye zili bwino. 22 Atate wanga wapeleka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akumudziwa bwino Mwana kupatulapo Atate. Palibenso amene akuwadziwa bwino Atate kupatulapo Mwana, komanso aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululila za Atatewo.”

23 Kenako mseli Yesu anauza ophunzila akewo kuti: “Odala ndi anthu amene akuona zinthu zimene inu mukuona. 24 Pakuti ndikukuuzani kuti aneneli ambili komanso mafumu anali kulakalaka kuona zimene inu mukuona, ndi kumva zimene inu mukumva.”

25 Ndiyeno munthu wina wodziwa Cilamulo anaimilila kuti amuyese. Anati: “Mphunzitsi, ndiyenela kucita ciyani kuti ndikalandile moyo wosatha?” 26 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi m’Cilamulo munalembedwa ciyani? Umawelengamo zotani?” 27 Munthuyo anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, mphamvu zako zonse, ndi maganizo ako onse.’ Komanso ‘uzikonda munthu mnzako mmene umadzikondela wekha.’” 28 Yesu anati: “Wayankha molondola, pitiliza kucita zimenezo, ndipo udzapeza moyo.”

29 Koma munthuyo pofuna kudzionetsela kuti ndi wolungama, anafunsanso Yesu kuti: “Kodi munthu mnzanga amene ndiyenela kumukonda ndani makamaka?” 30 Yesu poyankha anati: “Munthu wina anali kucokela ku Yerusalemu kupita ku Yeriko, ndipo anakumana ndi acifwamba amene anamuvula zovala, kumumenya, ndi kumusiya atatsala pang’ono kufa. 31 Tsopano zinangocitika kuti wansembe wina anali kudutsa mu msewuwo. Koma ataona munthuyo, anamulambalala. 32 Ndiyeno Mlevi anafika pa malopo, ndipo nayenso atamuona anamulambalala. 33 Koma Msamariya wina amene anali kuyenda mu msewuwo anafika pamalopo, ndipo atamuona anamva cisoni. 34 Conco iye anafika pamene panali munthuyo n’kuthila mafuta ndi vinyo pa zilonda zake n’kuzimanga. Ndiyeno anamukwezeka pa bulu wake n’kupita naye kunyumba ya alendo kuti akamusamalile. 35 Tsiku lotsatila anatenga madinari awili n’kupatsa wosamalila alendoyo, ndipo anamuuza kuti: ‘Umusamalile, ndipo zilizonse zimene utaye kuwonjezela pa zimenezi, ndidzakubwezela pobwelela.’ 36 Kodi pa atatuwa, ukuona kuti ndani anaonetsa cikondi kwa munthu uja amene anakumana ndi acifwamba?” 37 Munthuyo anati: “Ndi uja amene anamucitila cifundo.” Kenako Yesu anamuuza kuti: “Pita iwenso uzikacita zimenezo.”

38 Tsopano iwo anapitiliza ulendo wawo, ndipo analowa m’mudzi winawake. Kumeneko mayi wina dzina lake Marita anamulandila m’nyumba yake monga mlendo. 39 Mayiyo anali ndi m’bale wake dzina lake Mariya. Mariyayo anakhala pansi ku mapazi a Ambuye n’kumamvetsela zimene anali kukamba.* 40 Koma Marita anatangwanika ndi nchito zambili. Conco iye anafika kwa Yesu n’kunena kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekelela kuti ndigwile ndekha nchito? Muuzeni kuti abwele andithandize.” 41 Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa komanso kutangwanika ndi zinthu zambili. 42 Koma zofunikila n’zocepa cabe, mwinanso n’cimodzi cokha. Pakuti Mariya wasankha gawo labwino,* ndipo gawoli silidzalandidwa kwa iye.”

11 Tsopano Yesu anali kupemphela pa malo enaake, ndipo atatsiliza, mmodzi wa ophunzila ake anamuuza kuti: “Ambuye, tiphunzitseni mopemphelela monga mmene Yohane anaphunzitsila ophunzila ake.”

2 Pamenepo anawauza kuti: “Nthawi zonse mukamapemphela, muzinena kuti: ‘Atate, dzina lanu liyeletsedwe.* Ufumu wanu ubwele. 3 Mutipatse cakudya ca tsiku lililonse malinga ndi zofunikila zathu pa tsikulo. 4 Ndipo mutikhululukile macimo athu, cifukwa nafenso timakhululukila aliyense amene watilakwila,* ndiponso mutithandize kuti tisagonje tikamayesedwa.’”

5 Kenako anawauza kuti: “Tiyelekeze kuti mmodzi wa inu ali ndi mnzake, ndipo iye wapita kwa mnzakeyo pakati pa usiku n’kumuuza kuti, ‘Mnzangawe, ndibwelekeko mitanda itatu ya mkate, 6 cifukwa mnzanga wina wangofika kumene kucokela ku ulendo, ndipo ndilibe ciliconse comupatsa.’ 7 Koma mnzakeyo akuyankha ali m’nyumba kuti: ‘Usandivutitse, citseko takhoma kale. Ndipo ine ndi ana anga tagona kale. Sindingauke kuti ndikupatse kanthu.’ 8 Ndithu ndikukuuzani, munthuyo adzaukabe ndi kum’patsa ciliconse cimene akufuna, osati cifukwa cakuti ndi bwenzi lake, koma cifukwa ca kulimbikila kwake. 9 Conco ndikukuuzani kuti, pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe ndipo adzakutsegulilani. 10 Pakuti aliyense wopempha amalandila, ndipo aliyense wofunafuna amapeza, ndiponso aliyense wogogoda adzamutsegulila. 11 Ndithudi, kodi pali tate pakati panu amene mwana wake akam’pempha nsomba angamupatse njoka m’malo mwa nsomba? 12 Kapenanso ngati angamupemphe dzila, kodi angamupatse cinkhanila? 13 Cotelo ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapeleka mzimu woyela kwa amene amamupempha.”

14 Zitatha izi, Yesu anatulutsa ciwanda mwa munthu winawake comwe cinali kumulepheletsa kulankhula. Ciwandaco citatuluka, munthu wosalankhulayo anayamba kulankhula, ndipo khamu la anthu linadabwa kwambili. 15 Koma ena a iwo anati: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule,* wolamulila ziwanda.” 16 Koma ena pofuna kumuyesa, anayamba kumukakamiza kuti awaonetse cizindikilo cocokela kumwamba. 17 Yesu atadziwa maganizo awo anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawikana umatha, ndipo nyumba iliyonse yogawikana imagwa. 18 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana nayenso ndi wogawikana, kodi ufumu wake ungakhalepo bwanji? Pakuti inu mukunena kuti ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule. 19 Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule, nanga ophunzila anu amazitulutsa ndi mphamvu za ndani? Ndiye cifukwa cake iwo adzakuweluzani. 20 Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi cala ca Mulungu, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikanidi modzidzimutsa. 21 Munthu wamphamvu amene ali ndi zida zokwanila akamalonda nyumba yake, katundu wake umakhala wotetezeka. 22 Koma munthu wina wamphamvu kuposa iye akabwela n’kumugonjetsa, amamulanda zida zake zonse zimene anali kudalila, ndipo amagawila anthu ena katundu amene walandayo. 23 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana nane, ndipo aliyense amene sakundithandiza kusonkhanitsa anthu kwa ine akuwamwaza.

24 “Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa m’malo opanda madzi kufunafuna popumulila. Koma ngati sunapeze malo alionse, umati, ‘Ndibwelela kunyumba yanga imene ndinatulukamo.’ 25 Ndipo ukafika, umapeza kuti m’nyumbamo ndi mopsela komanso mokonza bwino. 26 Kenako umapita n’kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambili kuposa umenewo, ndipo yonse imadzalowa m’nyumbamo n’kumakhala mmenemo. Pamapeto pake munthuyo amakhala woipa kwambili kuposa poyamba.”

27 Ali mkati mokamba zimenezi, mayi wina pagulu la anthu limenelo anafuula kwa iye kuti: “Wacimwemwe ndi mayi amene anakubelekani, amenenso munayamwa mawele ake!” 28 Koma iye anati: “Ayi, m’malo mwake, acimwemwe ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”

29 Pamene khamu la anthu linali kuculukilaculukila, iye anayamba kunena kuti: “M’badwo uwu ndi woipa. Ukufuna cizindikilo, koma sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse kupatulapo cizindikilo ca Yona. 30 Monga mmene Yona anakhalila cizindikilo kwa anthu a ku Nineve, Mwana wa munthu nayenso adzakhala cizindikilo ku m’badwo uwu. 31 Mfumukazi ya kum’mwela idzaukitsidwa pa Tsiku la Ciweluzo pamodzi ndi anthu a m’badwo uwu ndipo idzawatsutsa, cifukwa inacokela ku malekezelo a dziko lapansi n’kubwela kuti idzamve nzelu za Solomo. Koma onani! winawake woposa Solomo ali pano. 32 Anthu a ku Nineve adzauka pa Tsiku la Ciweluzo pamodzi ndi m’badwo uwu, ndipo adzautsutsa cifukwa analapa atamva ulaliki wa Yona. Koma onani! winawake woposa Yona ali pano. 33 Munthu akayatsa nyale, saiika pa malo obisika kapena kuibwinikila ndi thadza,* koma amaiika pa coikapo nyale kuti olowa m’nyumbamo aziona kuwala. 34 Nyale ya thupi ndi diso lako. Diso lako likalunjika pa cinthu cimodzi,* thupi lako lonse limakhala lowala. Koma ngati ndi ladyela,* nalonso thupi lako limacita mdima. 35 Conco khala maso kuti kuwala kumene kuli mwa iwe kusakhale mdima. 36 Cotelo ngati thupi lako lonse n’lowala, ndipo palibe mbali imene ili ndi mdima, thupi lako lonse lidzakhala lowala mmene nyale imawalila pokuunikila.”

37 Yesu atatsiliza kulankhula izi, Mfarisi wina anamupempha kuti akadye naye cakudya. Conco anakalowa m’nyumba yake ndipo anakhala pathebulo n’kuyamba kudya naye. 38 Koma Mfarisiyo anadabwa ataona kuti Yesu akudya cakudya cosasamba m’manja.* 39 Cotelo Ambuye anamuuza kuti: “Inu Afarisi mumayeletsa kunja kwa kapu ndi mbale, koma mumtima mwanu ndi modzala dyela komanso zinthu zoipa. 40 Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga kunja si amenenso anapanga mkati? 41 Koma mphatso zacifundo* zimene mumapeleka zizicokela mu mtima. Ndipo onani! zonse zokhudza inu zidzakhala zoyela. 42 Koma tsoka kwa inu Afarisi, cifukwa mumapeleka cakhumi ca minti ndi luwe, komanso ca mbewu zilizonse zakudimba,* koma mumanyalanyaza cilungamo ndi cikondi ca Mulungu. Unali udindo wanu kucita zinthu zimenezi, koma simunafunike kunyalanyaza zinthu zinazo. 43 Tsoka kwa inu Afarisi, cifukwa mumakonda kukhala pa mipando ya kutsogolo* m’masunagoge, ndiponso mumakonda kupatsidwa moni m’misika! 44 Tsoka kwa inu, cifukwa muli ngati manda* aja amene sakuoneka bwinobwino,* ndipo anthu amayenda pa mandawo koma osadziwa!”

45 Poyankha, mmodzi wa odziwa Cilamulo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, pamene mwakamba izi, ndiye kuti nafenso mwatinyoza.” 46 Kenako Yesu anati: “Tsoka kwa inunso odziwa Cilamulo, cifukwa mumanyamulitsa anthu katundu wovuta kunyamula, koma inuyo simuyesa kuukhudza ngakhale ndi cala canu cokha!

47 “Tsoka kwa inu, cifukwa mumamanga manda* a aneneli koma makolo anu ndiwo anawapha! 48 Mosakayikila, inu ndinu mboni pa zimene makolo anu anacita, ndipo mukugwilizana nazo, cifukwa iwo anapha aneneliwo koma inu mukumanga manda awo. 49 Ndiye cifukwa cake nzelu ya Mulungu inanenanso kuti: ‘Ndidzawatumizila aneneli ndi atumwi, ndipo iwo adzapha ena a iwo ndi kuwazunza. 50 Adzacita izi kuti mlandu wa magazi onse amene akhetsedwa a aneneli, kuyambila pa ciyambi ca dziko, ukhale pa m’badwo uwu.* 51 Kuyambila magazi a Abele mpaka magazi a Zekariya yemwe anaphedwa pakati pa guwa la nsembe ndi kacisi.’* Ndithu ndikukuuzani, mlandu wa magazi amenewo udzakhala pa m’badwo uwu.*

52 “Tsoka kwa inu odziwa Cilamulo, cifukwa munalanda anthu kiyi yodziwila zinthu. Inuyo simunalowemo, ndipo mukutsekeleza anthu ofuna kulowamo!”*

53 Conco atacoka kumeneko, alembi ndi Afarisi anayamba kumupanikiza koopsa ndi kumuthila mafunso ena ambili, 54 ndipo anamuchela msampha kuti amukole pa zimene angakambe.

12 Pa nthawiyi, khamu la anthu masauzande ambilimbili anasonkhana pamodzi, moti anali kupondanapondana. Coyamba, Yesu analankhula ndi ophunzila ake kuti: “Samalani ndi zofufumitsa za Afarisi zimene ndi cinyengo. 2 Koma palibe cobisidwa mosamala kwambili cimene sicidzaululidwa, ndipo palibe cinsinsi cimene sicidzadziwika. 3 Conco ciliconse cimene munganene mu mdima, cidzamveka poyela. Ndipo zilizonse zimene mukunong’onezana kwanokha m’zipinda zanu, zidzalalikidwa pa mitenje ya nyumba. 4 Komanso ndikukuuzani mabwenzi anga, musamaope amene amapha thupi, omwe pambuyo pake sangathe kucita ciliconse. 5 Koma ndikuuzani amene muyenela kumuopa. Muziopa amene pambuyo pa kupha munthu, amakhalanso ndi mphamvu zoponya munthuyo m’Gehena.* Inde ndikukuuzani, muziopa ameneyo. 6 Mpheta zisanu amazigulitsa makobili awili ocepa mphamvu, si conco kodi? Koma palibe ngakhale mpheta imodzi imene Mulungu amaiiwala.* 7 Ndipo ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu amaliwelenga lonse. Conco musaope, ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zambili.

8 “Ndikukuuzani kuti, aliyense wondivomela pamaso pa anthu, Mwana wa munthu nayenso adzamuvomela pamaso pa angelo a Mulungu. 9 Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu, adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu. 10 Ndipo aliyense wokamba mawu onyoza Mwana wa munthu adzakhululukidwa, koma aliyense wonyoza mzimu woyela sadzakhululukidwa. 11 Akadzakupelekani ku mabwalo a milandu, kwa akuluakulu a boma ndi olamulila, musadzade nkhawa kuti mukadziteteza bwanji kapena mukakamba ciyani, 12 cifukwa mzimu woyela udzakudziwitsani* pa nthawi yomweyo zoyenela kunena.”

13 Ndiyeno munthu wina m’khamulo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, uzani m’bale wanga kuti andigawileko colowa.” 14 Iye anamuyankha kuti: “Munthu iwe, ndani anandiika kukhala woweluza pakati panu kapena wogawa cuma canu?” 15 Kenako anati kwa iwo: “Khalani maso, ndipo samalani ndi dyela la mtundu uliwonse,* cifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zoculuka motani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.” 16 Atakamba zimenezi, iye anawafotokozela fanizo lakuti: “Munda wa munthu wina wolemela unabala bwino. 17 Zitatelo iye anayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndicite ciyani tsopano popeza ndilibe kosungila zokolola zangazi?’ 18 Ndiyeno anati, ‘Ndidzacita izi: Ndidzapasula nyumba zanga zosungilamo zinthu ndi kumanga zina zikuluzikulu, ndipo mmenemo ndidzaikamo mbewu zanga zonse ndi zinthu zanga zonse. 19 Ndiye ndidzati kwa ine mwini:* “Uli* ndi zinthu zambili zabwino zimene ungazigwilitse nchito kwa zaka zambili. Mtima m’malo, idya, imwa, ndi kusangalala.”’ 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopusa iwe, usiku womwe uno anthu aufune moyo wako. Kodi ndani adzatenga zinthu zimene wasungazi?’ 21 Umu ndi mmenenso zidzakhalila ndi munthu wodziunjikila cuma, amene si wolemela kwa Mulungu.”

22 Ndiyeno anauza ophunzila ake kuti: “Ndiye cifukwa cake ndikukuuzani kuti, lekani kudela nkhawa za moyo* wanu kuti mudzadya ciyani, kapena za matupi anu kuti mudzavala ciyani. 23 Pakuti moyo ndi wofunika kwambili kuposa cakudya, ndipo thupi ndi lofunika kwambili kuposa covala. 24 Ganizilani za akhwangwala: Safesa mbewu kapena kukolola. Iwo alibe nkhokwe kapena nyumba yosungilamo zinthu, koma Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ndinu ofunika kwambili kuposa mbalame? 25 Ndani wa inu angatalikitse moyo wake ngakhale pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa? 26 Conco ngati simungakwanitse kucita kanthu kakang’ono aka, n’cifukwa ciyani mukuda nkhawa ndi zinthu zinazo? 27 Ganizilani mmene maluwa amakulila: Iwo sagwila nchito kapena kupanga nsalu. Koma ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemelelo wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. 28 Tsopano ngati umu ndi mmene Mulungu amavekela zomela zakuchile, zimene zimangokhalapo lelo mawa n’kuziponya pa moto, ndiye kuti inu adzakuvekani kuposa pamenepo, a cikhulupililo cocepa inu! 29 Conco, lekani kuda nkhawa kuti mudzadya ciyani komanso kuti mudzamwa ciyani. Ndipo lekani kuda nkhawa ndi zimene zingakucitikileni, 30 pakuti anthu a mitundu ina m’dzikoli akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu akudziwa kuti mufunikila zinthu zimenezi. 31 M’malo mwake, pitilizani kufunafuna Ufumu wake, ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.

32 “Kagulu ka nkhosa inu, musaope, cifukwa Atate wanu wavomeleza kukupatsani Ufumu. 33 Gulitsani zinthu zanu ndi kupeleka mphatso zacifundo. Mupange zikwama za ndalama zimene sizikutha, kutanthauza cuma cosatha kumwamba, kumene mbala singafikeko komanso njenjete sizingawononge. 34 Pakuti kumene kuli cuma canu, mitima yanu idzakhalanso komweko.

35 “Valani ndi kukhala okonzeka ndipo nyale zanu zikhale zikuyaka. 36 Mukhale ngati anthu amene akuyembekezela mbuye wawo kuti abwele kucokela ku phwando la ukwati, n’colinga coti akafika ndi kugogoda am’tsegulile nthawi yomweyo. 37 Acimwemwe ndi akapolo omwe mbuye wawo pofika adzawapeza ali maso! Ndithu ndikukuuzani, iye adzavala zovala kuti ayambe kuwatumikila, ndipo adzawauza kuti adye naye pathebulo n’kumawatumikila. 38 Ndipo ngati angafike paulonda waciwili,* ngakhale wacitatu,* n’kuwapeza ali okonzeka, iwo adzakhala acimwemwe! 39 Koma dziwani izi, ngati mwininyumba angadziwe ola limene mbala ingabwele, sangalole kuti mbalayo ithyole n’kulowa m’nyumba mwake. 40 Inunso khalani okonzeka, cifukwa pa ola limene simukuganizila, Mwana wa munthu adzafika.”

41 Ndiyeno Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, kodi mukuuza ife tokha fanizo ili kapena mukuuzanso aliyense?” 42 Ambuye anati: “Ndani kwenikweni amene ali woyang’anila* wokhulupilika komanso wanzelu, amene mbuye wake adzamuika kuti aziyang’anila gulu la anchito ake,* ndiponso kuwapatsa cakudya pa nthawi yoyenela? 43 Kapoloyo adzakhala wacimwemwe ngati mbuye wake pobwela adzamupeza akucita zimenezo! 44 Ndithu ndikukuuzani, adzamuika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse. 45 Koma ngati kapoloyo mumtima mwake anganene kuti, ‘Mbuye wanga akucedwa,’ ndiyeno n’kuyamba kumenya anchito anzake aamuna komanso aakazi ndiponso n’kumadya, kumwa ndi kuledzela, 46 mbuye wa kapoloyo adzabwela pa tsiku limene iye sakuliyembekezela, komanso pa ola limene sakulidziwa. Pamenepo adzamupatsa cilango cowawa zedi, n’kumuika pamodzi ndi anthu osakhulupilika. 47 Ndiyeno kapolo amene anadziwa zimene mbuye wake anali kufuna, koma sanakhale wokonzeka kapena kucita zimene mbuye wakeyo anamupempha,* adzakwapulidwa zikoti zambili. 48 Koma amene sanadziwe ndipo anacita zinthu zomukwapulitsa, adzakwapulidwa zikoti zocepa. Ndithudi, aliyense wopatsidwa zambili, zambilinso zidzafunidwa kwa iye. Ndipo amene anaikidwa kuyang’anila zoculuka, zoculukanso zidzafunidwa kwa iye.

49 “Ine ndinabwela kudzayatsa moto padziko lapansi. Ndiye ndingafunenso ciyani ngati motowo wayatsidwa kale? 50 Ndithudi, pali ubatizo winawake umene ndiyenela kubatizika nawo, ndipo ndikuvutika kwambili m’maganizo kufikila utacitika! 51 Kodi muganiza ndinabwela padziko lapansi kudzakupatsani mtendele? Ayi ndithu, koma kudzagawanitsa anthu. 52 Pakuti kuyambila tsopano, anthu asanu a m’nyumba imodzi adzasemphana maganizo. Atatu kukangana ndi awili, awili kukangana ndi atatu. 53 Iwo adzagawikana. Tate adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, ndipo mwana wamwamuna adzakangana ndi atate ake. Mayi adzakangana ndi mwana wake wamkazi, ndipo mwana wamkazi adzakangana ndi amayi ake. Apongozi aakazi adzakangana ndi mkazi wa mwana wawo, ndipo mkazi wokwatiwa adzakangana ndi apongozi ake aakazi.”

54 Ndiyeno anauzanso khamu la anthulo kuti: “Mukaona mtambo kumadzulo ukukwela m’mwamba, nthawi yomweyo mumati, ‘Kukubwela cimvula,’ ndipo zimacitikadi. 55 Ndipo mukaona mphepo ya kum’mwela ikuwomba, mumati, ‘Kudzatentha,’ ndipo zimacitikadi. 56 Onyenga inu, mumadziwa maonekedwe a dziko lapansi ndi kumwamba, nanga n’cifukwa ciyani simudziwa tanthauzo la zimene zikucitika pa nthawi ino? 57 N’cifukwa ciyani panokha simudziwa cimene cili colungama? 58 Mwacitsanzo, ukamapita kwa wolamulila ndi munthu wokuimba mlandu, muli m’njila uziyesetsa kukamba naye kuti uthetse mlanduwo. Uzicita zimenezi kuti mwina iye asakakupeleke kwa woweluza, komanso kuti woweluzayo asakakupeleke kwa msilikali wapakhoti, msilikaliyo n’kukuponya m’ndende. 59 Ndikukuuza kuti, sudzatulukamo mpaka utalipila kakhobili kothela.”*

13 Pa nthawi imeneyo, ena amene analipo anamufotokozela za anthu a ku Galileya amene Pilato anasakaniza magazi awo ndi nsembe zawo. 2 Iye anawayankha kuti: “Muganiza kuti Agalileyawo anali ocimwa kwambili kuposa Agalileya ena onse cifukwa zimenezo zinawacitikila? 3 Ayi ndithu. Koma ndikukuuzani kuti ngati simungalape, nonsenu mudzawonongedwa ngati iwo. 4 Kapena muganiza kuti anthu 18 aja omwe nsanja inawagwela ku Siloamu n’kuwapha anali ocimwa kwambili kuposa anthu ena onse okhala mu Yerusalemu? 5 Ayi ndithu, koma ndikuuzani kuti ngati simulapa, nonsenu mudzawonongedwa ngati iwo.”

6 Ndiyeno anayamba kuwauza fanizo ili: “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu m’munda wake wampesa, ndipo anapita kukafuna zipatso mu mtengowo, koma sanapezemo ciliconse. 7 Kenako munthuyo anauza wosamalila munda wa mpesawo kuti, ‘Kwa zaka zitatu ndakhala ndikubwela kudzafunafuna zipatso mu mtengo wamkuyu uwu, koma sindikupezamo kalikonse. Udule! N’cifukwa ciyani ukungowononga nthaka?’ 8 Poyankha, wosamalila mundayo anati, ‘Mbuyanga, ulekeni kwa caka cina cimodzi, ndipo ndidzakumba m’mbali mwake n’kuikamo manyowa. 9 Ngati udzabala zipatso m’tsogolo zidzakhala bwino. Koma ngati sudzabala mudzaudule.’”

10 Tsopano Yesu anali kuphunzitsa m’sunagoge winawake pa Sabata. 11 Ndiyeno mmenemo munali mayi wina amene anali ndi mzimu umene unali kumufooketsa* kwa zaka 18. Iye anali wopindika kwambili msana, ndipo sanali kuwelamuka ngakhale pang’ono. 12 Yesu atamuona mayiyo analankhula naye n’kumuuza kuti: “Mayinu, mwamasulidwa ku matenda anu.” 13 Ndiyeno anaika manja ake pa mayiyo, ndipo nthawi yomweyo anawelamuka n’kuyamba kutamanda Mulungu. 14 Koma mtsogoleli wa sunagoge ataona izi anakwiya, cifukwa cakuti Yesu anacilitsa munthu pa Sabata. Conco anauza khamu la anthulo kuti: “Pali masiku 6 amene tiyenela kugwila nchito. Cotelo muzibwela kudzacilitsidwa pa masiku amenewo, osati pa tsiku la Sabata ayi.” 15 Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Onyenga inu, kodi aliyense wa inu samasula ng’ombe yake kapena bulu wake m’khola pa Sabata n’kupita naye kukamumwetsela madzi? 16 Kodi mayiyu, amene ndi mwana wamkazi wa Abulahamu, amenenso Satana anamumanga kwa zaka 18, sayenela kumasulidwa m’maunyolo amenewa pa tsiku la Sabata?” 17 Iye atakamba zimenezi, anthu onse omutsutsa anacita manyazi. Koma khamu lonse la anthu linayamba kukondwela cifukwa ca zinthu zodabwitsa zimene iye anacita.

18 Conco anapitiliza kunena kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati ciyani, nanga ndingauyelekezele ndi ciyani? 19 Uli ngati kanjele ka mpilu, kamene munthu anatenga n’kukabyala m’munda wake. Ndiyeno kanakula n’kukhala mtengo, ndipo mbalame za mumlengalenga zinamanga zisa m’nthambi zake.”

20 Iye anakambanso kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu ndingauyelekezele ndi ciyani? 21 Uli ngati zofufumitsa zimene mayi wina anatenga n’kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zikuluzikulu zopimila,* ndipo mtanda wonsewo unafufuma.”

22 Ndiyeno iye anayenda mzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi akuphunzitsa, n’kupitiliza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 23 Tsopano munthu wina anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi amene adzapulumuka ndi ocepa?” Iye anawauza kuti: 24 “Yesetsani mwamphamvu kulowa pa khomo lopanikiza, cifukwa ndikukuuzani kuti ambili adzafuna kulowa koma sadzakwanitsa kutelo. 25 Mwininyumba akadzauka n’kukhoma citsekoco, mudzaimilila panja n’kumagogoda, ndipo mudzakamba kuti ‘Ambuye, titsegulileni.’ Koma iye adzakuyankhani kuti: ‘Sindikudziwani.’ 26 Ndiyeno mudzayamba kukamba kuti, ‘Tinali kudya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munali kuphunzitsa m’misewu yathu ikuluikulu.’ 27 Koma ine ndidzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwani. Cokani pamaso panga nonsenu ocita zosalungama!’ 28 Kumeneko, muzikalila ndi kukukuta mano mukadzaona Abulahamu, Isaki, Yakobo, ndi aneneli onse mu Ufumu wa Mulungu, koma inu mutaponyedwa kunja. 29 Komanso anthu adzabwela kucokela kum’mawa ndi kumadzulo, ndiponso kucokela kumpoto ndi kum’mwela n’kudzakhala pathebulo mu Ufumu wa Mulungu. 30 Ndipo pali othela amene adzakhala oyamba, komanso pali oyamba amene adzakhala othela.”

31 Nthawi yomweyo Afarisi ena anabwela n’kumuuza kuti: “Pitani, cokani kuno, cifukwa Herode akufuna kukuphani.” 32 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Pitani mukaiuze nkhandwe imeneyo kuti, ‘Ndikutulutsa ziwanda ndi kucilitsa anthu lelo komanso mawa, ndipo ndidzatsiliza pa tsiku lacitatu.’ 33 Ngakhale n’telo, ndipitiliza kugwila nchito yanga lelo, mawa, komanso mkuca. Pambuyo pake, ndidzapita ku Yerusalemu, cifukwa n’kosayenela* kuti mneneli amuphele kunja kwa Yerusalemu. 34 Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneli komanso woponya miyala anthu otumidwa kwa iwe. Mobwelezabweleza ndinafuna kusonkhanitsa pamodzi ana ako, monga mmene nkhuku imasonkhanitsila anapiye ake m’mapiko ake! Koma inu simunafune zimenezo. 35 Tsopano mvelani, Mulungu wakusiyilani nyumba yanu. Ndikukuuzani kuti, simudzandionanso kufikila mutanena kuti: ‘Wodalitsika ndi iye wobwela m’dzina la Yehova!’”

14 Pa nthawi ina, Yesu anapita kukadya cakudya m’nyumba ya mmodzi wa atsogoleli a Afarisi pa Sabata, ndipo iwo anali kumuyang’anitsitsa. 2 Patsogolo pake panali mwamuna wodwala matenda otupikana.* 3 Ndiyeno Yesu anafunsa anthu odziwa bwino Cilamulo ndi Afarisi kuti: “Kodi n’kololeka kucilitsa munthu pa Sabata kapena ayi?” 4 Koma iwo anangokhala cete. Zitatelo, iye anagwila munthuyo n’kumucilitsa, ndipo anamuuza kuti azipita. 5 Kenako iye anawafunsa kuti: “Ndani wa inu amene mwana wake, kapena ng’ombe yake ikagwela m’citsime pa tsiku la Sabata sangaitulutse nthawi yomweyo?” 6 Iwo sanathe kumuyankha funso limeneli.

7 Ndiyeno anthu oitanidwawo anawauza fanizo ataona kuti akudzisankhila malo apamwamba kwambili. Iye anati: 8 “Munthu akakuitanila ku phwando la ukwati, usakhale pa malo apamwamba kwambili. Mwina anaitananso munthu wina wolemekezeka kuposa iwe. 9 Ndiyeno munthu amene anakuitanani nonse awilinu adzabwela kwa iwe n’kukuuza kuti, ‘Pepani, musiyile awa malowo.’ Zikatelo, udzanyamuka mwamanyazi n’kukakhala pa malo otsika kwambili. 10 Koma ukaitanidwa, pita ukakhale pa malo otsika kwambili kuti munthu amene anakuitanayo akabwela, adzakuuze kuti, ‘Mnzangawe, khala pa malo apamwambawa.’ Zikatelo, udzalemekezeka pamaso pa anzako onse oitanidwa. 11 Pakuti aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo aliyense wodzicepetsa adzakwezedwa.”

12 Ndiyeno anauzanso munthu amene anamuitanayo kuti: “Ukakonza cakudya camasana, kapena cakudya camadzulo, usaitane anzako, abale ako, acibale ako, kapena anthu olemela amene umakhala nawo pafupi, cifukwa nawonso angakakuitane ndipo zidzakhala ngati akukubwezela. 13 Koma iwe ukakonza phwando uziitana osauka, ogolontha, olemala, ndi akhungu, 14 ndipo udzakhala ndi cimwemwe cifukwa iwo alibe coti akubwezele. Pakuti Mulungu adzakubwezela pa kuuka kwa olungama.”

15 Mmodzi wa alendo anzake atamva zimenezi anamuuza kuti: “Wacimwemwe ndi munthu amene adzadya cakudya* mu Ufumu wa Mulungu.”

16 Yesu anamuuza kuti: “Munthu wina anakonza phwando lalikulu la cakudya camadzulo, ndipo anaitana anthu ambili. 17 Pa nthawi ya cakudya camadzuloco, iye anatuma kapolo wake kukauza oitanidwawo kuti, ‘Bwelani, cifukwa zonse zakonzedwa tsopano.’ 18 Koma onse anayamba kupeleka zifukwa zokanila. Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndinagula munda ndipo ndifuna ndipite ndikauone. Pepani, sindibwela.’ 19 Ndipo wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ng’ombe 10 za pajoko ndipo ndifuna ndikaziyese. Pepani, sindibwela.’ 20 Winanso ananena kuti, ‘Ndangokwatila kumene. Pa cifukwa cimeneci, sindibwela.’ 21 Conco kapoloyo anabwela n’kufotokozela mbuye wake zimenezi. Mbuyeyo atamva zimenezi anakwiya kwambili n’kuuza kapolo wake kuti, ‘Pita mwamsanga m’misewu ikuluikulu ndi m’njila za mumzinda, ndipo ukaitane osauka, ogolontha,* akhungu, komanso olemala.’ 22 Kapoloyo atabwelako anati, ‘Mbuyanga, ndacita zimene mwandiuza, koma malo akalimo.’ 23 Ndiyeno mbuye wa kapolo uja anati, ‘Pita m’misewu ya kunja kwa mzinda, ukalimbikitse anthu kubwela kuno kuti nyumba yanga idzale. 24 Ndithu ndikukuuzani, palibe ngakhale mmodzi mwa anthu aja omwe anaitanidwa poyamba, amene adzalawako cakudya canga camadzulo.’”

25 Tsopano khamu lalikulu la anthu linali kuyenda ndi Yesu. Ndiyeno iye anaceuka, n’kuwauza kuti: 26 “Ngati wina afuna kunditsatila, koma osadana* ndi atate ake, amayi ake, mkazi wake, ana ake, abale ake, ndi alongo ake, inde, ngakhale moyo wake, sangakhale wophunzila wanga. 27 Aliyense amene sananyamule mtengo wake wozunzikilapo* n’kunditsatila, sangakhale wophunzila wanga. 28 Mwacitsanzo, ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja, sayamba wakhala pansi n’kuwelengela mtengo wake, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanila zotsilizila nsanjayo? 29 Cifukwa ngati sangacite zimenezo, angayale maziko ake koma osakwanitsa kuitsiliza, ndipo onse oona angayambe kumuseka 30 n’kumanena kuti: ‘Munthu uyu anayamba bwinobwino kumanga, koma camukanga kuti atsilize.’ 31 Kapena ndi mfumu iti ingapite kukamenyana ndi mfumu ina ku nkhondo, siyamba yakhala pansi n’kuganizila mofatsa ngati asilikali ake 10,000 angalimbane ndi asilikali 20,000 a mfumu inayo, imene ikubwela kudzamenyana naye? 32 Ngati waona kuti sangakwanitse kulimbana nayo, mfumuyo ikali kutali, adzatumiza akazembe kukapempha mtendele. 33 Mofanana ndi zimenezi, dziwani kuti palibe aliyense wa inu amene angakhale wophunzila wanga ngati sangasiye* zinthu zake zonse.

34 “Kukamba zoona, mcele ndi wabwino. Koma ngati mcele watha mphamvu yake, kodi mphamvuyo angaibwezeletse ndi ciyani? 35 Mcelewo siwoyenela kuuthila m’nthaka kapena m’manyowa. Anthu amangoutaya. Amene ali ndi matu akumva, amve.”

15 Tsopano okhometsa misonkho onse ndi ocimwa anapitiliza kusonkhana kwa iye kuti amumvetsele. 2 Ndiyeno Afarisi ndi alembi anali kung’ung’udza kuti: “Munthuyu amalandila ocimwa ndipo amadya nawo.” 3 Kenako iye anawauza fanizo. Anati: 4 “Ndani pakati panu amene ngati ali ndi nkhosa 100, koma imodzi n’kusowa, sangasiye nkhosa 99 zinazo m’cipululu, n’kukafunafuna imodzi imene yasowa mpaka ataipeza? 5 Akaipeza amainyamula pamapewa ake, ndipo amakondwela. 6 Akafika kunyumba, amasonkhanitsa mabwenzi ake ndi anthu okhala nawo pafupi n’kuwauza kuti, ‘Sangalalani nane, cifukwa nkhosa yanga imene inali yosowa ndaipeza.’ 7 Ndithu ndikukuuzani kuti mofanana ndi zimenezi, kumwamba kudzakhala cisangalalo coculuka munthu mmodzi wocimwa akalapa, kuposa cisangalalo cimene cidzakhalako kaamba ka anthu 99 olungama amene safunika kulapa.

8 “Kapena ndi mayi uti amene akakhala ndi ndalama zokwana madalakima 10, ndipo imodzi n’kutayika, sangayatse nyale ndi kupsela m’nyumba yake n’kuifunafuna mosamala mpaka ataipeza? 9 Ndipo akaipeza amasonkhanitsa mabwenzi* ake ndi okhala naye pafupi n’kuwauza kuti, ‘Sangalalani nane, cifukwa ndalama ya dalakima imene inasowa ndaipeza.’ 10 Mofananamo, ndikukuuzani kuti, angelo a Mulungu amasangalala kwambili munthu mmodzi wocimwa akalapa.”

11 Ndiyeno anati: “Munthu wina anali ndi ana awili aamuna. 12 Wamng’ono anauza atate ake kuti, ‘Atate, mundipatsiletu colowa canga pa cuma canu.’ Conco, iye anagawila anawo cuma cake. 13 Patangopita masiku ocepa, mwana wamng’ono uja anasonkhanitsa zinthu zake zonse n’kupita kudziko lakutali. Kumeneko, anasakaza cuma cake conse mwa kukhala umoyo wotayilila.* 14 Atawononga cuma conseco, m’dziko lonselo munagwa njala yaikulu, ndipo iye anayamba kuvutika. 15 Anafika mpaka pokadziphatika kwa nzika ina ya m’dzikolo, imene inamutuma kuchile kuti azikawetela nkhumba zake. 16 Iye anafika pomalakalaka cakudya cimene nkhumba zinali kudya, koma palibe amene anali kumupatsa kanthu.

17 “Nzelu zitamubwelela anati, ‘Anchito ambili a atate ali ndi cakudya coculuka, koma ine ndikufa ndi njala kuno! 18 Ndidzanyamuka n’kubwelela kwa atate ndipo ndikawauza kuti: “Atate, ndacimwila kumwamba komanso inu. 19 Sindinenso woyenela kuchedwa mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.”’ 20 Conco iye ananyamuka n’kupita kwa atate ake. Akubwela capatali, atate akewo anamuona ndipo anamva cifundo. Iwo anamuthamangila ndi kumukumbatila, ndipo anam’psompsona mwacikondi. 21 Ndiyeno mwanayo anauza atate ake kuti, ‘Atate, ndacimwila kumwamba komanso inu. Sindinenso woyenela kuchedwa mwana wanu.’ 22 Koma tateyo anauza akapolo ake kuti, ‘Fulumilani! Bweletsani mkanjo wabwino koposa mumuveke. Ndipo mumuveke mphete ku dzanja lake, ndi nsapato ku mapazi ake. 23 Mubweletsenso mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa uja, ndipo mumuphe kuti tidye ndi kusangalala. 24 Cifukwa mwana wangayu anali wakufa, koma wakhalanso ndi moyo, anali wotayika koma wapezeka.’ Conco anayamba kusangalala.

25 “Tsopano mwana wamkulu anali kumunda. Pamene anali kubwelela n’kuyandikila kunyumbako, anamva nyimbo ndi anthu akuvina. 26 Conco iye anaitana mmodzi wa anchito n’kumufunsa zimene zinali kucitika. 27 Wanchitoyo anamuuza kuti, ‘M’bale wanu wabwela, ndipo atate anu amuphela mwana wa ng’ombe wonenepa uja, cifukwa wabwelela kwa iwo ali bwinobwino.’* 28 Koma iye anakwiya kwambili, ndipo anakana kulowa m’nyumbamo. Ndiyeno atate ake anatuluka m’nyumbamo ndi kuyamba kumucondelela. 29 Mwanayo anayankha atate akewo kuti, ‘Onani! Zaka zambili zonsezi ndakhala ndikukugwililani nchito ngati kapolo, ndipo sindinaphwanyepo malamulo anu ngakhale kamodzi, koma simunandipatsepo ngakhale kamwana ka mbuzi kuti ndisangalaleko pamodzi ndi mabwenzi anga. 30 Koma mwana wanuyu, amene anasakaza* cuma canu ndi mahule, pamene wangofika mwamuphela mwana wa ng’ombe wonenepa.’ 31 Kenako tateyo anamuuza kuti, ‘Mwana wanga, iwe wakhala nane nthawi zonse, ndipo zinthu zanga zonse ndi zako. 32 Koma tinayeneladi kukondwela ndi kusangalala, cifukwa m’bale wakoyu anali wakufa, koma wakhalanso ndi moyo. Anali wotayika koma wapezeka.’”

16 Ndiyeno Yesu anauzanso ophunzila ake kuti: “Munthu wina wacuma anali ndi woyang’anila nyumba yake amene anali kunenezedwa kuti anali kumuwonongela cuma cake. 2 Conco anamuitana n’kumuuza kuti, ‘Ndamva kuti ukucita zoipa. Ndipatse lipoti la mmene wakhala ukugwilila nchito yako yoyang’anila nyumba yanga cifukwa sungapitilize kugwila nchitoyi.’ 3 . Kenako woyang’anilayo anati mumtima mwake, ‘Ndidzacita ciyani pakuti bwana wanga akufuna kundicotsa pa nchitoyi? Ndilibe mphamvu zolima, ndipo ndingacite manyazi kukhala wopemphapempha. 4 Ahaa! Ndadziwa zimene ndidzacita kuti akandicotsa nchito anthu akandilandile bwino m’nyumba zawo.’ 5 Conco anaitana munthu aliyense amene anali ndi nkhongole kwa bwana wake. Anafunsa woyamba kuti, ‘Uli ndi nkhongole yaikulu bwanji kwa bwana wanga?’ 6 Iye anayankha kuti, ‘Mitsuko* 100 ya mafuta a maolivi.’ Woyang’anilayo anamuuza kuti, ‘Tenga cipepala ca pangano ukhale pansi, ndipo mwamsanga ulembepo mitsuko 50.’ 7 Kenako anafunsa wina kuti, ‘Nanga iwe uli ndi nkhongole yaikulu bwanji?’ Iye anayankha kuti, ‘Masaka* 100 akuluakulu a tiligu.’ Ndiyeno anamuuza kuti, ‘Tenga cipepala cako ca pangano ndipo ulembepo masaka 80.’ 8 Bwana wake anamuyamikila woyang’anilayo ngakhale kuti anali wosalungama, cifukwa anacita zinthu mwanzelu.* Pakuti ana a m’nthawi ino* ndi anzelu akamacita zinthu ndi anthu a m’badwo wawo kuposa ana a kuwala.

9 “Inunso ndikukuuzani kuti: Pezani mabwenzi pogwilitsa nchito cuma cosalungama, kuti cumaco cikadzatha, iwo akakulandileni kumalo okhala amuyaya. 10 Munthu wokhulupilika pa cinthu cacing’ono amakhalanso wokhulupilika pa cacikulu, ndipo munthu wosakhulupilika pa cinthu cacing’ono amakhalanso wosakhulupilika pa cacikulu. 11 Conco ngati simunaonetse kukhulupilika kwanu pa cuma cosalungama, ndani angakusungizeni cuma ceniceni? 12 Ndipo ngati simunaonetse kukhulupilika kwanu pa cinthu ca munthu wina, ndani adzakupatsani mphoto imene anakusungilani? 13 Palibe mtumiki amene angakhale kapolo wa ambuye awili, cifukwa adzadana ndi mmodzi n’kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi n’kunyoza winayo. Simungakhale akapolo a Mulungu komanso a Cuma pa nthawi imodzi.”

14 Tsopano Afarisi okonda kwambili ndalama anali kumvetsela zonsezi, ndipo anayamba kumunyodola. 15 Conco Yesu anawauza kuti: “Inu ndinu amene mumakamba pamaso pa anthu kuti ndinu olungama, koma Mulungu akudziwa mitima yanu. Pakuti cimene anthu amaciona kuti n’capamwamba, Mulungu amaciona kuti n’conyansa.

16 “Cilamulo komanso zolemba za aneneli zinali kulengezedwa mpaka m’nthawi ya Yohane. Kucokela nthawi imeneyo, Ufumu wa Mulungu wakhala ukulengezedwa monga uthenga wabwino, ndipo anthu a mtundu uliwonse akuyesetsa kuti akalowemo. 17 Ndithudi, n’capafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zicoke kuposa kuti kambali kakang’ono ka cilembo ca m’Cilamulo kasakwanilitsike.

18 “Aliyense wosudzula* mkazi wake n’kukwatila wina akucita cigololo, ndipo aliyense wokwatila mkazi wosudzulidwa* ndi mwamuna wake, nayenso akucita cigololo.

19 “Panali munthu wina wolemela amene anali kukonda kuvala zovala za mtundu wapepo ndi nsalu zabwino. Iye anali kusangalala ndi kucita madyelelo tsiku lililonse. 20 Koma munthu wina wopemphapempha dzina lake Lazaro, amenenso anali ndi zilonda thupi lonse, anthu anali kumuika pa geti ya munthu wolemelayo. 21 Lazaro anali kulakalaka kudya nyenyeswa zakugwa pa thebulo la munthu wolemelayo. Ndipo agalu anali kubwela kudzanyanguta* zilonda zake. 22 Tsopano m’kupita kwa nthawi, wopemphapempha uja anamwalila ndipo angelo anamutenga n’kukamuika pambali pa Abulahamu.*

“Nayenso munthu wolemela uja anamwalila, ndipo anaikidwa m’manda. 23 Ali m’Mandamo* komanso akuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abulahamu capatali ndi Lazaro ali pambali pake.* 24 Conco iye anaitana mofuula amvekele, ‘Atate Abulahamu, ndicitileni cifundo, ndipo tumani Lazaro kuti aviike nsonga ya cala cake m’madzi kuti adzazizilitse lilime langa, cifukwa ndakhaula m’moto wolilimawu!’ 25 Koma Abulahamu anati, ‘Mwanawe, kumbukila kuti unalandililatu zinthu zabwino panthawi imene unali moyo, koma Lazaro analandila zinthu zoipa. Apa tsopano, iye akutonthozedwa kuno koma iwe ukuzunzika. 26 Komanso, pakati pa iwe ndi ife paikidwa phompho lalikulu, kuti anthu amene akufuna kubwela uko kucoka kuno asakwanitse kutelo, komanso kuti anthu asacoke uko n’kubwela kwa ife.’ 27 Ndiyeno munthu wolemela uja anati, ‘Ngati zili conco, ndikupemphani atate kuti mumutumize kunyumba ya atate anga, 28 akacenjeze abale anga asanu, kuopela kuti nawonso angadzabwele kumalo ano kudzazunzika.’ 29 Koma Abulahamu anakamba kuti, ‘Iwo ali ndi zolemba za Mose komanso zolemba za Aneneli. Aleke amvele zimenezo.’ 30 Kenako anati, ‘Ayi, atate Abulahamu, koma ngati wina wacokela kwa akufa n’kupita kwa iwo, adzalapa ndithu.’ 31 Koma Abulahamu anamuuza kuti, ‘Ngati sakumvela zolemba za Mose komanso zolemba za Aneneli, ngakhale munthu amene waukitsidwa kwa akufa sangamumvele.’”

17 Kenako Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Zopangitsa munthu kupunthwa zidzabwela ndithu, ndipo n’zosapeweka. Koma tsoka kwa munthu wobweletsa zopunthwitsazo! 2 Zingakhale bwino kum’mangilila cimwala camphelo m’khosi ndi kumuponya m’nyanja kuposa kuti apunthwitse mmodzi wa ana aang’ono awa. 3 Khalani osamala. Ngati m’bale wako wakucimwila mudzudzule, ndipo ngati walapa mukhululukile. 4 Ngakhale atakucimwila maulendo 7 patsiku, ndipo wabwela kwa iwe maulendo 7 n’kunena kuti, ‘Ndalapa,’ uyenela kumukhululukila.”

5 Tsopano atumwi anauza Ambuye kuti: “Tiwonjezeleni cikhulupililo.” 6 Ndiyeno Ambuye anati: “Mukanakhala ndi cikhulupililo ngakhale cocepa ngati kanjele ka mpilu, mukanatha kuuza mtengo wa malubeni uwu kuti, ‘Zuka apa ukadzibyale m’nyanja!’ ndipo ukanakumvelani.

7 “Ndani wa inu amene kapolo wake atangofika kumene kucokela kumunda kukalima ndi pulawo, kapena atacokela kuchile kukawetela nkhosa, angamuuze kuti, ‘Fulumila bwela kuno udzadye pathebulo’? 8 Kodi sangamuuze kuti, ‘Ndikonzele cakudya camadzulo, uvale epuloni ndi kuyamba kunditumikila mpaka n’tatsiliza kudya ndi kumwa, pambuyo pake iwenso ungadye ndi kumwa’? 9 Ndipo iye sangamuyamikile kapolo wakeyo, cifukwa zimene wacitazo ndi nchito yake, si conco? 10 Mofanana ndi izi, mukacita zonse zimene munauzidwa kucita, muzinena kuti: ‘Ndife akapolo opanda pake, tangocita zimene tinayenela kucita.’”

11 Pamene iye anali kupita ku Yerusalemu, anadutsa m’malile a Samariya ndi Galileya. 12 Ndipo pamene anali kulowa m’mudzi winawake, amuna 10 akhate anakumana naye, koma iwo anaimilila capatali. 13 Amunawo anafuula kuti: “Yesu, Mlangizi, ticitileni cifundo!” 14 Yesu atawaona anawauza kuti: “Pitani mukadzionetse kwa ansembe.” Ndiyeno pamene iwo anali kupita anayeletsedwa. 15 Mmodzi wa iwo ataona kuti wacilitsidwa, anabwelela akutamanda Mulungu mokweza mawu. 16 Iye anagwada mpaka nkhope yake pansi kumapazi a Yesu, n’kumuyamikila. Munthu ameneyu anali Msamariya. 17 Yesu anakamba kuti: “Anthu onse 10 ayeletsedwa, nanga ena 9 aja ali kuti? 18 Kodi palibenso wina amene wabwelela kudzatamanda Mulungu kupatulapo munthu wa mtundu winayu?” 19 Yesu anauza munthuyo kuti: “Nyamuka uzipita, cikhulupililo cako cakucilitsa.”

20 Afarisi atafunsa Yesu kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela liti, iye anawayankha kuti: “Sikuti Ufumu wa Mulungu udzabwela ndi maonekedwe ocititsa cidwi ayi. 21 Ndipo anthu sadzanena kuti, ‘Onani uli kuno!’ kapena, ‘Uli uko!’ Pakuti Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”

22 Kenako Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Masiku adzabwela pamene mudzalakalaka kuona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa munthu, koma simudzaliona. 23 Ndipo anthu adzakuuzani kuti, ‘Onani ali uko!’ kapena, ‘Onani ali kuno!’ Musakapiteko kapena kuwatsatila. 24 Cifukwa monga mmene mphenzi imang’animila kucokela kumbali ina ya thambo kufika kumbali ina ya thambo, ndi mmenenso zidzakhalile m’tsiku la Mwana wa munthu. 25 Koma coyamba iye ayenela kukumana ndi masautso ambili, ndipo m’badwo uwu udzamukana. 26 Komanso, monga mmene zinacitikila m’masiku a Nowa, ndi mmenenso zidzakhalile m’masiku a Mwana wa munthu. 27 Anthu anali kudya ndi kumwa, amuna anali kukwatila, ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analowa m’cingalawa. Ndipo Cigumula cinabwela n’kuwawononga onsewo. 28 Ndi mmenenso zinalili m’masiku a Loti. Anthu anali kudya ndi kumwa, anali kugula ndi kugulitsa, anali kubyala, komanso kumanga. 29 Koma pa tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule n’kuwawononga onsewo. 30 Ndi mmenenso zidzakhalile patsikulo Mwana wa munthu akadzaonekela.

31 “Patsikulo, munthu amene adzakhale pa mtenje koma katundu wake uli m’nyumba asadzatsike kukautenga. Cimodzimodzinso munthu amene adzakhale ku munda, asadzabwelele ku zinthu zimene wasiya kumbuyo. 32 Kumbukilani mkazi wa Loti. 33 Aliyense wofunitsitsa kuteteza moyo wake adzautaya, koma aliyense woutaya adzausunga. 34 Ndithu ndikukuuzani, anthu awili adzakhala akugona pabedi imodzi, wina adzatengedwa koma wina adzasiyidwa. 35 Akazi awili adzakhala akupela pamphelo imodzi, wina adzatengedwa koma wina adzasiyidwa.” 36* —— 37 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi zimenezi zidzacitikila kuti?” Iye anawauza kuti: “Kumene kuli thupi lakufa, nazonso ziwombankhanga zidzasonkhana kumeneko.”

18 Kenako Yesu anawauzanso fanizo lowaonetsa kuti iwo ayenela kupemphela nthawi zonse, komanso kuti asamataye mtima. 2 Iye anati: “Mumzinda winawake munali woweluza wina amene sanali kuopa Mulungu, ndipo sanali kusamala za munthu. 3 Mumzindawo munalinso mkazi wamasiye amene mobwelezabweleza anali kupita kwa iye kukamupempha kuti, ‘Weluzani mlandu umene ulipo pakati pa ine ndi munthu amene ndikutsutsana naye kuti pacitike cilungamo.’ 4 Kwakanthawi, woweluzayo sanali kufuna kuiweluza nkhaniyo, koma pambuyo pake anati mumtima mwake, ‘Ngakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala za munthu aliyense, 5 ndidzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa mkazi wamasiyeyu, cifukwa iye sakuleka kundivutitsa. Conco kuti aleke kubwela n’kumanditopetsa,* ndidzacita zimene akupempha.’” 6 Ndiyeno Ambuye anati: “Mwamva, izi n’zimene woweluzayo ananena, ngakhale kuti ndi wosalungama! 7 Ndiye kodi Mulungu sadzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa anthu ake osankhidwa, amene amamulilila usana ndi usiku pamene akuwalezela mtima? 8 Ndithu ndikukuuzani, iye adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa iwo mwamsanga. Ngakhale n’telo, kodi Mwana wa munthu akadzabwela adzapezadi cikhulupililo ngati cimeneci* padziko lapansi?”

9 Yesu anafotokozanso fanizo lotsatilali kwa ena amene anali kudzidalila kuti ndi olungama, komanso amene anali kuona ena kuti ndi opanda pake. Iye anati: 10 “Amuna awili anapita ku kacisi kukapemphela. Mmodzi anali Mfarisi ndipo winayo anali wokhometsa misonkho. 11 Mfarisi uja anaimilila n’kuyamba kupemphela camumtima kuti, ‘Mulungu wanga, ndikuyamikilani kuti ine sindili monga ena onsewa, amene ndi olanda, opanda cilungamo, komanso acigololo. Ndiponso sindili ngati uyu wokhometsa misonkho. 12 Ndimasala kudya kawili pa mlungu, ndipo ndimapeleka cakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’ 13 Koma wokhometsa misonkho uja anaimilila capatali, ndipo sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Koma anali kungodziguguda pacifuwa n’kumanena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomeleni mtima* ine munthu wocimwa.’ 14 Ndithu ndikukuuzani, munthu ameneyu atapita kunyumba kwake anaonedwa wolungama kwambili kuposa Mfarisi uja. Conco aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzicepetsa adzakwezedwa.”

15 Tsopano anthu analinso kumubweletsela ana aang’ono kuti awaike manja. Koma ophunzila ake ataona izi anayamba kuwakalipila. 16 Komabe, Yesu anaitana anawo n’kukamba kuti: “Alekeni anawo abwele kwa ine, musawaletse, cifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa. 17 Ndithu ndikukuuzani kuti, aliyense wosalandila Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowamo n’komwe mu Ufumuwo.”

18 Ndiyeno mmodzi wa olamulila anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, kodi ndiyenela kucita ciyani kuti ndikapeze moyo wosatha?” 19 Yesu anamuyankha kuti: “N’cifukwa ciyani ukundichula kuti wabwino? Palibe aliyense wabwino koma Mulungu yekha. 20 Iwe umawadziwa malamulo akuti: ‘Usacite cigololo, usaphe munthu, usabe, usapeleke umboni wonama, ndiponso lakuti uzilemekeza atate ako ndi amayi ako.’” 21 Munthuyo anayankha kuti: “Ndakhala ndikutsatila malamulo onsewa kuyambila ndili mwana.” 22 Yesu atamva zimenezi anamuuza kuti, “Pali cinthu cimodzi cimene cikusowekabe mwa iwe: Kagulitse zinthu zonse zimene uli nazo, ndipo ndalama zake ukazigawile osauka. Ukatelo udzakhala ndi cuma kumwamba. Kenako ubwele udzakhale wotsatila wanga.” 23 Atamva zimenezi, anamva cisoni kwambili cifukwa anali wolemela kwambili.

24 Yesu anamuyang’ana ndipo ananena kuti: “Cidzakhala covuta kwambili kuti anthu a ndalama akalowe mu Ufumu wa Mulungu! 25 Ndithudi, n’capafupi ngamila kulowa pa diso la singano, kusiyana n’kuti munthu wolemela akalowe mu Ufumu wa Mulungu.” 26 Amene anamva zimenezi anafunsa kuti: “Ndiye pali amene angadzapulumuke ngati?” 27 Iye anayankha kuti: “Zinthu zosatheka kwa anthu n’zotheka kwa Mulungu.” 28 Koma Petulo anati: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu n’kukutsatilani.” 29 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe aliyense amene wasiya nyumba, mkazi, abale, makolo, kapena ana cifukwa ca Ufumu wa Mulungu, 30 amene sadzapeza zoculuka kwambili m’nthawi ino, ndipo m’nthawi imene ikubwelayo* adzapeza moyo wosatha.”

31 Ndiyeno iye anatengela pambali ophunzila ake 12 aja n’kuwauza kuti: “Tsopano tikupita ku Yerusalemu, ndipo zinthu zonse zimene zinalembedwa kupitila mwa aneneli zokhudza Mwana wa munthu zidzakwanilitsidwa. 32 Mwacitsanzo, iye adzapelekedwa kwa anthu a mitundu ina ndi kucitidwa zacipongwe, ndipo adzamunyoza ndi kumuthila mata. 33 Pambuyo pomukwapula, adzamupha, koma patsiku lacitatu adzaukitsidwa.” 34 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la zinthu zonsezi, cifukwa mawu amenewa anali obisika kwa iwo, ndipo sanamvetse zimene iye anakamba.

35 Tsopano pamene Yesu anali kuyandikila ku Yeriko, munthu wina wakhungu anali khale m’mbali mwa msewu akupemphapempha. 36 Munthuyo atamva khamu la anthu likudutsa, anayamba kufunsa kuti adziwe zimene zinali kucitika. 37 Anthuwo anamuuza kuti: “Yesu Mnazareti akudutsa!” 38 Pamenepo munthuyo anafuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide, ndicitileni cifundo!” 39 Ndiyeno anthu amene anali patsogolo anayamba kumudzudzula kuti akhale cete, koma m’pamene iye anakuwa kwambili, amvekele: “Mwana wa Davide, ndicitileni cifundo!” 40 Conco Yesu anaima n’kulamula kuti munthuyo amubweletse kwa iye. Atafika pafupi, Yesu anamufunsa kuti: 41 “Ufuna ndikucitile ciyani?” Iye anati: “Ambuye, ndithandizeni ndiyambe kuona.” 42 Yesu anamuuza kuti: “Yamba kuona, cikhulupililo cako cakucilitsa.” 43 Nthawi yomweyo munthuyo anayamba kuona, ndipo anayamba kutsatila Yesu akutamanda Mulungu. Komanso anthu onse ataona izi, anatamanda Mulungu.

19 Kenako Yesu analowa mu Yeriko, koma anali kungodutsamo. 2 Tsopano munthu wina dzina lake Zakeyo anali kumeneko. Iye anali mkulu wa okhometsa misonkho, ndipo anali wolemela. 3 Anali kulakalaka kuona Yesu, koma sanakwanitse kumuona cifukwa ca khamu la anthu, popeza kuti anali wamfupi. 4 Conco anathamangila kutsogolo n’kukwela mu mtengo wamkuyu kuti amuone, cifukwa Yesu anali kupitila njila imeneyo. 5 Yesu atafika pa malowo, anayang’ana m’mwambamo n’kumuuza kuti: “Zakeyo, tsika fulumila, pakuti lelo ndiyenela kukhala m’nyumba yako.” 6 Zakeyo atamva izi anatsika mofulumila, ndipo anamulandila mokondwela kwambili monga mlendo wake. 7 Poona izi, anthu onsewo anayamba kung’ung’udza. Anati: “Wapita kukakhala mlendo kunyumba ya munthu wocimwa.” 8 Koma Zakeyo anaimilila n’kuuza Ambuye kuti: “Ambuye! Hafu ya cuma canga ndidzaipeleka kwa osauka, ndipo ciliconse cimene ndinalanda* munthu aliyense, ndidzamubwezela kuwilikiza kanayi.” 9 Yesu atamva zimenezi anati: “Lelo cipulumutso cafika panyumba ino, cifukwa nayenso ndi mwana wa Abulahamu. 10 Pakuti Mwana wa munthu anabwela kudzafunafuna amene anatayika komanso kudzawapulumutsa.”

11 Pamene iwo anali kumvetsela zimenezi, Yesu anawauza fanizo lina cifukwa iye anali pafupi ndi Yerusalemu, ndipo anthuwo anali kuganiza kuti Ufumu wa Mulungu uonekela nthawi yomweyo. 12 Conco iye anati: “Munthu wina wa m’banja lacifumu anakonza zakuti apite ku dziko lakutali kuti akalandile ufumu, pambuyo pake akabweleko. 13 Ndiyeno anaitana akapolo ake 10 n’kuwapatsa ndalama 10 za mina.* Atatelo anawauza kuti, ‘Ndalamazi muzicitila malonda mpaka n’tabwelako.’ 14 Koma anthu a m’dziko lakwawo anali kudana naye, ndipo anatumiza gulu la akazembe kuti limutsatile likanene kuti, ‘Ife sitifuna kuti munthuyu akhale mfumu yathu.’

15 “Munthuyo atalandila ufumu anabwelako. Ndipo anaitana akapolo ake amene anawapatsa ndalama* aja, kuti adziwe ndalama zimene anapindula pocita malonda awo. 16 Conco woyamba anabwela n’kukamba kuti, ‘Ambuye, pa ndalama yanu ya mina, ndapindula ndalama zina za mina zokwana 10.’ 17 Mbuye wakeyo anamuuza kuti, ‘Unacita bwino, ndiwe kapolo wabwino! Ndipo popeza waonetsa kukhulupilika pa cinthu cacing’ono kwambili, ndikupatsa mizinda 10 kuti uziiyang’anila.’ 18 Tsopano waciwili anabwela n’kunena kuti, ‘Ambuye, pa ndalama yanu ya mina, ndinapindula ndalama zina za mina zokwana zisanu.’ 19 Mbuyeyo anauzanso kapoloyo kuti, ‘Iwenso ukhala woyang’anila mizinda isanu.’ 20 Koma kapolo wina anabwela n’kukamba kuti, ‘Ambuye, tengani ndalama yanu ya mina iyi imene ndinaimanga pansalu n’kuibisa. 21 Ine ndinacita izi cifukwa cokuopani. Inu ndinu munthu wovuta, mumatenga zimene simunasungize, ndipo mumakolola zimene simunafese.’ 22 Mbuyeyo anamuuza kuti, ‘Ndikuweluza mogwilizana ndi mawu ako, kapolo woipa iwe. Ukuti unadziwa kuti ndine munthu wovuta, ndimatenga zimene sindinasungize, ndi kukolola zimene sindinafese? 23 Nanga n’cifukwa ciyani sunaike ndalama yanga* ku banki? Ukanatelo, ine pobwela ndikanaitengela pamodzi ndi ciwongoladzanja cake.’

24 “Atanena zimenezi anauza omwe anaimilila pafupi kuti, ‘Mulandeni ndalama ya minayo, ndipo mupatse amene ali ndi ndalama 10 za mina.’ 25 Koma anthuwo anauza mbuyeyo kuti, ‘Ambuye, munthu ameneyu ali nazo kale ndalama 10 za mina!’— 26 ‘Ine ndikukuuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambili, koma amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo. 27 Komanso bweletsani adani anga amene sanali kufuna kuti ine ndikhale mfumu yawo, ndipo muwaphe ine ndikuona.’”

28 Yesu atakamba zimenezi, anapitiliza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 29 Ndipo atayandikila mzinda wa Betifage ndi Betaniya pa phili lochedwa Phili la Maolivi, anatumiza ophunzila ake awili. 30 Anawauza kuti: “Pitani m’mudzi uwo, ndipo mukalowamo mupeza mwana wamphongo wa bulu amene munthu sanamukwelepo n’kale lonse atamumangilila. Mukamumasule ndi kumubweletsa kuno. 31 Munthu aliyense akakufunsani kuti, ‘N’cifukwa ciyani mukum’masula buluyu?’ Munene kuti, ‘Ambuye akumufuna.’” 32 Conco amene anatumidwawo anapita, ndipo anam’pezadi mwana wa bulu mmene iye anawauzila. 33 Koma pamene anali kum’masula, eniake anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukum’masula buluyu?” 34 Iwo anayankha kuti: “Ambuye akumufuna.” 35 Conco buluyo anapita naye kwa Yesu, kenako anaponya zovala zawo zakunja pa buluyo ndipo Yesu anakwelapo.

36 Pamene iye anali kuyenda, anthu anali kuyanzika zovala zawo zakunja mu msewu. 37 Yesu atangotsala pang’ono kufika mu msewu wocokela m’Phili la Maolivi, gulu lonse la ophunzila linayamba kukondwela ndi kutamanda Mulungu mokweza cifukwa ca nchito zonse zamphamvu zimene anaona. 38 Iwo anali kukamba kuti: “Wodalitsika ndi iye wobwela monga Mfumu m’dzina la Yehova! Mtendele kumwamba, ndi ulemelelo kumwambamwambako!” 39 Koma Afarisi ena m’khamulo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, adzudzuleni ophunzila anuwa.” 40 Koma Yesu poyankha anati: “Ndikukukuuzani kuti, ngati awa angakhale cete, miyala idzafuula.”

41 Yesu atayandikila mzinda wa Yerusalemu, anauyang’ana n’kuyamba kuulilila, 42 amvekele: “Ndipo iwe, ndithu iweyo ukanazindikila lelo zinthu zokhudza mtendele—koma tsopano zabisika kwa iwe kuti usazione. 43 Cifukwa masiku adzakufikila pamene adani ako adzamanga mpanda wamitengo yosongoka n’kukuzungulila ndi kukutsekela* mbali zonse. 44 Iwo adzakuponya pansi pamodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwamba pa unzake mwa iwe, cifukwa sunazindikile kuti nthawi yokuyendela yafika.”

45 Kenako, Yesu analowa m’kacisi ndipo anayamba kupitikitsila panja anthu omwe anali kugulitsa zinthu. 46 Anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphelelamo,’ koma inu mwaisandutsa phanga la acifwamba.”

47 Iye anali kuwaphunzitsa m’kacisi tsiku lililonse. Koma ansembe aakulu, alembi, komanso atsogoleli a anthu, anali kufunitsitsa kumupha. 48 Koma sanapeze njila iliyonse yocitila zimenezi, cifukwa anthu ambili anali kumuunjilila kuti amumvetsele, ndipo sanali kusiyana naye.

20 Tsiku lina Yesu akuphunzitsa anthu m’kacisi ndi kulengeza uthenga wabwino, ansembe aakulu, alembi pamodzi ndi akulu anabwela, 2 ndipo anamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi ulamulilo wocita zimenezi munautenga kuti? Nanga ndani anakupatsani ulamulilo umenewu?” 3 Iye anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani funso, ndipo mundiyankhe: 4 Kodi ubatizo wa Yohane unacokela kumwamba kapena kwa anthu?” 5 Pamenepo iwo anayamba kukambilana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unacokela kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’cifukwa ciyani simunamukhulupilile?’ 6 Komanso sitingakambe kuti, ‘Unacokela kwa anthu,’ cifukwa onse angatiponye miyala, popeza iwo amakhulupilila kuti Yohane anali mneneli.” 7 Conco iwo anayankha kuti sadziwa kumene unacokela. 8 Yesu anati: “Inenso sindikuuzani kumene ndinatenga ulamulilo wocita zimenezi.”

9 Ndiyeno iye anayamba kuuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wampesa, kenako anausiya m’manja mwa alimi n’kupita ku dziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali. 10 Nyengo yokolola itakwana, iye anatuma kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso za m’munda wampesawo. Koma alimiwo anam’menya ndi kumubweza cimanjamanja. 11 Iye anatumanso kapolo wina. Koma nayenso anamumenya ndi kumucita zacipongwe,* ndipo anamubweza cimanjamanja. 12 Ngakhale n’telo, iye anatumanso wacitatu. Koma nayenso anamuvulaza ndi kumuthamangitsa. 13 Mwinimunda wa mpesa uja ataona izi anati, ‘Ndiye ndicite ciyani pamenepa? Cabwino, nditumiza mwana wanga wokondeka. Mosakayikila iwo adzamulemekeza.’ 14 Alimiwo atamuona mwanayo anayamba kukambilana kuti, ‘Eya! uyu ndiye wolandila colowa. Tiyeni timuphe kuti colowaci cikhale cathu.’ 15 Conco iwo anamutulutsila kunja kwa munda wampesawo ndi kumupha. Ndiye kodi mwinimundayo adzawacita ciyani alimiwo? 16 Adzabwela n’kuwapha alimiwo, ndipo adzapeleka mundawo kwa ena.”

Anthuwo atamva zimenezi anati: “Izi siziyenela kucitika!” 17 Koma iye anawayang’anitsitsa n’kunena kuti: “Kodi Malemba amatanthauzanji ponena kuti: ‘Mwala umene omanga anaukana wakhala mwala wapakona wofunika kwambili’?* 18 Aliyense wogwela pa mwalawo adzaphwanyika. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwele udzamupelelatu.”

19 Ndiyeno alembi ndi ansembe aakulu, anadziwa kuti Yesu ponena fanizo limeneli anali kukamba za iwo. Conco anafuna kumugwila nthawi yomweyo koma anaopa anthu. 20 Ndiyeno iwo atayang’anitsitsa mmene iye anali kucitila zinthu, mwakabisila analemba ganyu akazitape kuti akadzipange kukhala olungama n’colinga coti akamutape m’kamwa. Iwo anacita izi kuti akamupeleke ku boma komanso kwa bwanamkubwa. 21 Conco anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tidziwa kuti zimene mumakamba ndi kuphunzitsa n’zolondola, ndipo mulibe tsankho. Mumaphunzitsa njila ya Mulungu m’coonadi: 22 Kodi n’kololeka* kuti ife tizipeleka misonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 23 Koma iye atazindikila ukambelembele wawo anawauza kuti: 24 “Ndionetseni khobili la dinari. Kodi cithunzi ndi mawu omwe ali pamenepo ndi za ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” 25 Iye anawauza kuti: “Conco, pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara koma za Mulungu kwa Mulungu.” 26 Iwo analephela kumutapa m’kamwa pa zimene ananena pamaso pa anthu, koma anadabwa ndi yankho lake, ndipo anangokhala cete.

27 Komabe, Asaduki ena amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwela n’kumufunsa kuti: 28 “Mphunzitsi, Mose anatilembela kuti, ‘Ngati mwamuna wamwalila n’kusiya mkazi, koma sanabeleke naye mwana, m’bale wake wa mwamunayo ayenela kukwatila mkazi wamasiyeyo ndi kumubelekela ana m’bale wake uja.’ 29 Tsopano panali amuna 7 apacibale. Woyamba anakwatila mkazi, koma anamwalila asanabeleke naye mwana. 30 Zinacitika cimodzimodzi kwa waciwili. 31 Kenako wacitatu anamukwatila. Zinacitikanso cimodzimodzi ngakhale kwa onse 7, onse anamwalila osabeleka naye ana. 32 Pamapeto pake mkazi uja nayenso anamwalila. 33 Malinga ndi mmene zinakhalilamu, pamene akufa adzauka, kodi mkaziyo adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatilapo?”

34 Yesu anawauza kuti: “Ana a m’nthawi* ino amakwatila ndi kukwatiwa. 35 Koma amene aonedwa kuti ndi oyenelela kudzapeza moyo m’nthawi ikubwelayo n’kudzaukitsidwa kucokela kwa akufa, sadzakwatila kapena kukwatiwa. 36 Ndiponso iwo sadzafanso, cifukwa adzakhala monga angelo. Ndipo iwo ndi ana a Mulungu pokhala ana a kuuka kwa akufa. 37 Koma zakuti akufa amauka, ngakhale Mose anafotokoza m’nkhani yokhudza citsamba caminga, pamene anakamba kuti Yehova ‘ndi Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki, komanso Mulungu wa Yakobo.’ 38 Iye si Mulungu wa akufa ayi, koma wa anthu amoyo, pakuti kwa iye onse ndi amoyo.”* 39 Poyankha, ena mwa alembiwo anati: “Mphunzitsi, mwakamba bwino.” 40 Iwo anakamba izi cifukwa sanalimbenso mtima kuti amufunse funso lina.

41 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani anthu amakamba kuti Khristu ndi mwana wa Davide? 42 Cifukwa Davide iyemwini, m’buku la Masalimo ananena kuti, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43 kufikila n’taika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’ 44 Davide anamuchula kuti Ambuye, ndiye akhala bwanji mwana wake?”

45 Kenako anthu onse akumvetsela, iye anauza ophunzila ake kuti: 46 “Samalani ndi alembi amene amakonda kumayendayenda atavala mikanjo, amenenso amakonda kupatsidwa moni m’misika. Iwo amakondanso kukhala pa mipando yakutsogolo* m’masunagoge, komanso pa malo olemekezeka kwambili pa cakudya camadzulo. 47 Iwo amalandanso cuma ca akazi* amasiye, komanso amapeleka mapemphelo ataliatali pofuna kudzionetsela.* Amenewa adzalandila cilango cowawa kwambili.”*

21 Tsopano Yesu atakweza maso ake, anaona anthu olemela akuponya mphatso zawo m’zoponyamo zopeleka.* 2 Kenako anaona mkazi wamasiye wosauka akuponyamo tumakobili tuwili tocepa mphamvu kwambili.* 3 Kenako anati: “Ndithu ndikukuuzani, mayi wamasiye wosaukayu waponyamo zambili kuposa onse. 4 Pakuti onsewa aponyamo mphatso zimene atapapo pa zoculuka zimene ali nazo. Koma mayiyu, ngakhale kuti ndi wosauka, wapeleka zonse zimene anali nazo, zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”

5 Pambuyo pake, pamene anthu ena anali kukambilana zokhudza kacisi, mmene anamukongoletsela ndi miyala yokongola komanso zinthu zopelekedwa kwa Mulungu, 6 iye anati: “Kunena za zinthu izi zomwe mukuona palipano, masiku adzafika pamene sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.” 7 Kenako anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti makamaka, nanga cizindikilo cakuti zinthu zimenezi zili pafupi kucitika cidzakhala ciyani?” 8 Iye anati: “Samalani kuti asadzakusoceletseni, pakuti ambili adzabwela m’dzina langa n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine.’ Adzanenanso kuti, ‘Nthawi ija ili pafupi.’ Musakawatsatile. 9 Komanso mukadzamva za nkhondo ndiponso zacipolowe,* musadzacite mantha. Pakuti zimenezi ziyenela kucitika coyamba, koma mapeto sadzafika nthawi yomweyo.”

10 Kenako anawauza kuti: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. 11 Kudzakhala zivomezi zamphamvu, ndipo kumalo osiyanasiyana kudzakhala njala ndi milili. Ndipo kudzaoneka zinthu zocititsa mantha, komanso kumwamba kudzaoneka zizindikilo zodabwitsa.

12 “Koma zinthu zonsezi zisanacitike, anthu adzakugwilani n’kukuzunzani, ndipo adzakupelekani kumasunagoge komanso ku ndende. Adzakupelekani kwa mafumu ndi kwa abwanamkubwa cifukwa ca dzina langa. 13 Zimenezi zidzakupatsani mwayi wocitila umboni. 14 Conco tsimikizani m’mitima yanu kuti musayeseze pasadakhale mmene mukadzitetezele. 15 Pakuti ine ndidzakuuzani mawu amene mudzakamba, ndi kukupatsani nzelu zimene onse okutsutsani sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa. 16 Komanso ngakhale makolo anu, abale anu, acibale anu ndi anzanu adzakupelekani, ndipo iwo adzapha ena a inu. 17 Ndiponso anthu onse adzakudani cifukwa ca dzina langa. 18 Koma ngakhale tsitsi limodzi la m’mutu mwanu silidzawonongeka. 19 Mukadzapilila mudzasunga miyoyo yanu.*

20 “Koma mukadzaona kuti Yerusalemu wazungulilidwa ndi magulu ankhondo, mukadziwe kuti ciwonongeko cake cayandikila. 21 Pamenepo, amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawila ku mapili, ndipo amene adzakhale mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Komanso amene adzakhale m’madela a kumidzi asadzalowemo, 22 cifukwa amenewa adzakhala masiku opeleka ciweluzo,* kuti zinthu zonse zimene zinalembedwa zikwanilitsidwe. 23 Tsoka kwa akazi apathupi komanso oyamwitsa m’masiku amenewo! Cifukwa padzakhala mavuto aakulu padzikoli, komanso mkwiyo udzakhala pa anthu awa. 24 Iwo adzaphedwa ndi lupanga, ndipo adzatengedwa ukapolo n’kupita nawo ku mitundu ina yonse. Anthu a mitundu* ina adzapondaponda Yerusalemu mpaka nthawi zoikika za anthu a mitundu* inayo zitakwana.

25 “Komanso padzakhala zizindikilo pa dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi. Anthu padziko lapansi pano adzakhala m’masautso aakulu, ndipo adzathedwa nzelu cifukwa ca mkokomo wa nyanja ndi kuwinduka kwake. 26 Anthu adzakomoka cifukwa ca mantha komanso cifukwa coyembekezela zinthu zimene zidzacitikila dziko lapansi kumene kuli anthu. Pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 27 Ndiyeno iwo adzaona Mwana wa munthu akubwela mu mtambo, ali ndi mphamvu komanso ulemelelo waukulu. 28 Koma zinthu zimenezi zikadzayamba kucitika, mukaime cilili ndi kutukula mitu yanu, cifukwa cipulumutso canu cayandikila.”

29 Iye atakamba zimenezi, anawauza fanizo kuti: “Yang’anani mtengo wamkuyu ndi mitengo ina yonse. 30 Mukaona kuti mitengoyo yayamba kuphuka, mumadziwa kuti dzinja layandikila. 31 Mofananamo, inunso mukadzaona zinthu zimenezi zikucitika, mukadziwe kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. 32 Ndithu ndikukuuzani, m’badwo uwu sudzatha wonse mpaka zinthu zonsezi zitacitika. 33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mawu anga sadzacoka ayi.

34 “Koma samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambili, kumwa kwambili, komanso nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikileni modzidzimutsa 35 monga msampha. Pakuti tsikulo lidzafikila onse okhala pa dziko lapansi. 36 Conco khalanibe maso, ndipo muzipemphela mopembedzela, kuti mukathe kuthawa zinthu zonsezi zimene ziyenela kucitika, komanso kuti mukathe kuimilila pamaso pa Mwana wa munthu.”

37 Masana, iye anali kuphunzitsa m’kacisi, koma usiku anali kutuluka mu mzinda n’kukagona ku phili lochedwa Phili la Maolivi. 38 Ndipo anthu onse anali kubwela kukacisi m’mamawa kudzamumvetsela.

22 Tsopano Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa cimenenso cimachedwa Pasika, cinali citayandikila. 2 Ndiyeno ansembe aakulu ndi alembi anali kufunafuna njila yabwino yomuphela Yesu, cifukwa anali kuopa anthu. 3 Kenako Satana analowa mwa Yudasi wochedwa Isikariyoti, amene anali mmodzi wa atumwi 12 aja. 4 Ndipo anapita kukakambilana ndi ansembe aakulu komanso akapitawo a pakacisi za mmene angamupelekele kwa iwo. 5 Iwo anakondwela ndi zimenezi, ndipo anagwilizana kuti amupatse ndalama zasiliva. 6 Cotelo iye anavomela, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino woti amupeleke kwa iwo popanda khamu la anthu pafupi.

7 Tsopano tsiku la Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa linafika, tsiku limene nsembe ya Pasika inali kuyenela kupelekedwa. 8 Conco Yesu anatuma Petulo ndi Yohane n’kuwauza kuti: “Pitani mukakonze Pasika kuti tidye.” 9 Iwo anamufunsa kuti: “Mufuna tikakonzele kuti?” 10 Iye anawauza kuti: “Mukakalowa mumzinda, mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi adzakumana nanu. Mukamutsatile m’nyumba imene akalowe. 11 Ndipo mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi akuti kwa inu: “Kodi cipinda ca alendo cili kuti, cimene ndingadyelemo Pasika pamodzi ndi ophunzila anga?”’ 12 Munthuyo adzakuonetsani cipinda cacikulu cam’mwamba cokonzedwa bwino. Mukakonzele mmenemo.” 13 Conco ophunzilawo anapita, ndipo zinacitikadi mmene Yesu anawauzila. Iwo anakonza zonse zofunikila za Pasika.

14 Cotelo nthawi itakwana, iye anakhala pa thebulo pamodzi ndi atumwi. 15 Kenako anawauza kuti: “Ndakhala ndikulakalaka kwambili kudya Pasika uyu pamodzi nanu ndisanayambe kuzunzika. 16 Pakuti ndikukuuzani, sindidzadyanso Pasika uyu kufikila colinga cake citakwanilitsidwa mu Ufumu wa Mulungu.” 17 Ndiyeno atalandila kapu, anayamika n’kunena kuti: “Aneni, ndipo imwani mopatsilana. 18 Pakuti ndikukuuzani kuti, kuyambila tsopano, sindidzamwanso cakumwa cocokela ku mphesa kufikila Ufumu wa Mulungu utabwela.”

19 Komanso, anatenga mtanda wa mkate n’kuyamika, ndipo anaunyemanyema n’kuupeleka kwa iwo. Kenako anati: “Mkate uwu ukuimila thupi langa limene lidzapelekedwa kaamba ka inu. Muzicita zimenezi pondikumbukila.” 20 Anacitanso cimodzimodzi ndi kapu pambuyo pa cakudya ca madzulo. Iye anati: “Kapu iyi ikuimila cipangano catsopano pa maziko a magazi anga amene akhetsedwe kaamba ka inu.

21 “Koma taonani! Wondipeleka uja ali nane pathebulo pano. 22 Pakuti ndithudi, Mwana wa munthu akupita mogwilizana ndi zimene zinanenedwelatu. Koma tsoka kwa munthu amene akumupeleka!” 23 Conco iwo anayamba kukambilana zakuti ndani pakati pawo amene afuna kucita zimenezi.

24 Komanso, iwo anayamba kukangana kwambili zakuti ndani pakati pawo amene anali kuonedwa kuti ndi wamkulu kwambili. 25 Koma iye anawauza kuti: “Mafumu a mitundu ina amapondeleza anthu awo, ndipo amene ali ndi ulamulilo pa anthu, amadziwika kuti ndi anthu amene amacitila ena zabwino. 26 Inu musakhale otelo. Koma wamkulu kwambili pakati panu, akhale ngati wamng’ono kwambili, komanso amene akutsogolela akhale ngati wotumikila. 27 Kodi wamkulu ndani, amene akudya pathebulo kapena amene akutumikila? Kodi si uja amene akudya pathebulo? Koma ine ndili pakati panu monga wotumikila.

28 “Inu mwakhalabe nane m’mayeselo anga. 29 Ndipo ine ndikucita nanu cipangano, monga mmene Atate wanga anacitila cipangano ca ufumu ndi ine, 30 kuti mukadye ndi kumwa pathebulo mu Ufumu wanga, komanso kuti mukakhale pa mipando yacifumu n’kuweluza mafuko 12 a Isiraeli.

31 “Simoni, Simoni, taona! Satana akufuna kuti akupepeteni nonsenu monga tiligu. 32 Koma ine ndakupemphelela mocondelela kuti cikhulupililo cako cisathe. Conco ukabwelela, ukalimbikitse abale ako.” 33 Kenako iye anauza Yesu kuti: “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu kundende komanso kufa nanu.” 34 Koma iye anati: “Ndikukuuza Petulo, tambala asanalile lelo, iwe undikana katatu kuti sundidziwa.”

35 Iye anawauzanso kuti: “Pamene ndinakutumani popanda kunyamula cikwama ca ndalama, cola ca zakudya, komanso nsapato, simunasowe kalikonse, si conco?” Iwo anayankha kuti: “Inde!” 36 Ndiyeno anawauza kuti: “Koma tsopano amene ali ndi cikwama ca ndalama acitenge, atengenso cola ca zakudya, ndipo amene alibe lupanga, agulitse covala cake cakunja n’kugula lupanga. 37 Pakuti ndikukuuzani kuti zimene zinalembedwa ziyenela kukwanilitsidwa mwa ine, zakuti, ‘Anaikidwa pa gulu la anthu osamvela malamulo.’ Cifukwa izi zikukwanilitsidwa pa ine.” 38 Ndiyeno iwo anati: “Ambuye, onani! Tili ndi malupanga awili.” Iye anawauza kuti: “Amenewa ndi okwanila.”

39 Atacoka kumeneko, iye mwacizolowezi cake anapita ku Phili la Maolivi, ndipo ophunzila ake nawonso anamutsatila. 40 Atafika kumeneko anawauza kuti: “Pitilizani kupemphela kuti musalowe m’mayeselo.” 41 Ndipo iye anacoka pamene panali ophunzilawo, n’kupita capatali, ngati pomwe mwala ungagwele munthu atauponya. Kumeneko anagwada pansi n’kuyamba kupemphela, 42 kuti: “Atate, ngati mufuna, ndicotseleni kapu iyi. Koma lolani kuti cifunilo canu cicitike, osati canga.” 43 Kenako, mngelo wocokela kumwamba anaonekela kwa iye, ndipo anamulimbikitsa. 44 Koma iye anavutika kwambili mumtima, moti anapitiliza kupemphela mocokela pansi pa mtima, ndipo thukuta lake linayamba kuoneka ngati madontho a magazi amene akugwela pansi. 45 Atatsiliza kupemphela, ananyamuka n’kupita pamene panali ophunzila ake, ndipo anawapeza akugona, atafooka ndi cisoni. 46 Iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukugona? Ukani, ndipo pitilizani kupemphela kuti musalowe m’mayeselo.”

47 Ali mkati molankhula, kunabwela khamu la anthu. Anthuwo anali ndi munthu wochedwa Yudasi, mmodzi wa atumwi 12 aja, ndipo iye ndiye anali kuwatsogolela. Ndiyeno Yudasi anapita pamene panali Yesu kuti amupsompsone. 48 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Yudasi, ukupeleka Mwana wa munthu mwa kumupsompsona?” 49 Amene anali pafupi ndi Yesu ataona zimene zinali kucitika, anati: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?” 50 Mmodzi wa iwo anatemadi kapolo wa mkulu wa ansembe, mpaka kumudula khutu la kudzanja lamanja. 51 Koma Yesu anayankha kuti: “Musacite zimenezi.” Kenako anagwila khutu lija n’kumucilitsa. 52 Ndiyeno Yesu anafunsa ansembe aakulu, akapitawo a pakacisi komanso akulu amene anabwela kudzamugwila kuti: “N’cifukwa ciyani mwabwela mutanyamula malupanga ndi nkholi ngati kuti mukubwela kudzagwila wacifwamba? 53 Pamene ndinali kukhala nanu m’kacisi tsiku lililonse simunandigwile. Koma ino ndi nthawi yanu komanso ya ulamulilo wa anthu amene ali mumdima.”

54 Ndiyeno anamugwila n’kupita naye. Kenako anamupeleka m’nyumba ya mkulu wa ansembe, koma Petulo anali kuwatsatila capatali. 55 Iwo anayatsa moto mkati mwa bwalo ndipo onse anakhala pansi. Nayenso Petulo anakhala pansi pakati pawo. 56 Koma mtsikana wina wanchito atamuona atakhala pafupi ndi moto wowala, anamuyang’anitsitsa n’kunena kuti: “Awanso anali naye limodzi.” 57 Koma iye anakana kuti: “Mtsikana iwe, munthu ameneyo ine sindimudziwa.” 58 Patapita kanthawi kocepa, munthu wina anamuona ndipo anati: “Inunso ndinu mmodzi wa iwo.” Koma Petulo anati: “Mwamuna iwe, sindine ayi.” 59 Ndiyeno patapita pafupifupi ola limodzi, munthu winanso anayamba kukamba motsimikiza kuti: “Mosakayikila, munthu ameneyu analinso naye limodzi, cifukwa ndi Mgalileya!” 60 Koma Petulo anati: “Mwamuna iwe, zimene ukamba ine sindizidziwa.” Nthawi yomweyo, ali mkati molankhula tambala analila. 61 Pamenepo Ambuye anaceuka ndi kuyang’ana Petulo, ndipo Petulo anakumbukila mawu amene Ambuye anamuuza akuti: “Tambala asanalile lelo, iwe undikana katatu.” 62 Pamenepo anatuluka panja n’kuyamba kulila mwacisoni kwambili.

63 Ndiyeno anthu amene anagwila Yesu aja, anayamba kumucita zacipongwe ndi kumumenya. 64 Kenako iwo anamuphimba kumaso n’kumamufunsa kuti: “Lotela! Wakumenya ndani?” 65 Iwo anakamba zinthu zina zambili zomunyoza.

66 Ndiyeno kutaca, bungwe la akulu la anthu, pamodzi ndi ansembe aakulu komanso alembi, anasonkhana pamodzi, ndipo anapita naye mu holo yawo ya Khoti Yaikulu ya Ayuda* n’kunena kuti: 67 “Tiuze ngati ndiwe Khristu.” Koma iye anawauza kuti: “Ngakhale n’takuuzani, simungakhulupilile ayi. 68 Komanso ndikakufunsani funso, simungandiyankhe. 69 Koma kuyambila tsopano mpaka m’tsogolo, Mwana wa munthu adzakhala kudzanja lamanja lamphamvu la Mulungu.” 70 Atamva zimenezi, onse anati: “Ndiye kodi ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anawayankha kuti: “Inuyo mwanena nokha kuti ndine Mwana wa Mulungu.” 71 Iwo anati: “Kodi n’kufunilanji umboni wina? Cifukwa apa tadzimvela tokha kucokela pakamwa pake.”

23 Conco gulu lonselo linanyamuka pamodzi n’kupita naye kwa Pilato. 2 Kenako anayamba kumuneneza kuti: “Tapeza munthu uyu akupandutsa mtundu wathu, akuletsa anthu kupeleka misonkho kwa Kaisara, ndipo akunena kuti, iye ndi Khristu mfumu.” 3 Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha.” 4 Kenako Pilato anauza ansembe aakulu ndi khamulo kuti: “Munthuyu sindikumupeza ndi mlandu ulionse.” 5 Koma iwo anaumilila kuti: “Munthu ameneyu akusokoneza anthu mwa kuphunzitsa mu Yudeya monse, kuyambila ku Galileya mpaka kuno.” 6 Pilato atamva zimenezo, anafunsa ngati munthuyo anali Mgalileya. 7 Atazindikila kuti iye wacokela m’cigawo colamulidwa ndi Herode, anamutumiza kwa Herode, amenenso anali ku Yerusalemu pa masiku amenewo.

8 Herode ataona Yesu anakondwela kwambili. Kwa nthawi ndithu, anali kufunitsitsa kumuona cifukwa anamva zambili za iye, ndipo anali kuyembekezela kuti Yesu amuonetse cizindikilo cinacake. 9 Conco anayamba kumufunsa mafunso ambili, koma Yesu sanamuyankhe ciliconse. 10 Komabe, ansembe aakulu ndi alembi anali kungonyamukanyamuka n’kumamuneneza mwaukali. 11 Ndiyeno Herode pamodzi ndi asilikali ake, anamunyoza. Ndipo anamucita zacipongwe mwa kumuveka covala cabwino kwambili. Kenako anamubweza kwa Pilato. 12 Patsikuli, Herode ndi Pilato anakhala mabwenzi, koma kumbuyo konseko anali kudana kwambili.

13 Kenako, Pilato anasonkhanitsa ansembe aakulu, olamulila, komanso anthu 14 n’kuwauza kuti: “Mwabweletsa munthu uyu kwa ine, ndipo mwamupatsa mlandu wakuti amatuntha anthu kuukila boma. Onani! Munthuyu ndamufunsa pamaso panu, koma sin’namupeze ndi mlandu ulionse pa zimene mukumuneneza. 15 Nayenso Herode sanamupeze ndi mlandu, ndiye cifukwa cake wamutumizanso kwa ife. Kukamba zoona, munthu ameneyu sanacite ciliconse coyenela cilango ca imfa. 16 Conco, ndidzangomukwapula ndi kumumasula.” 17* —— 18 Koma khamulo linafuula kuti: “Anyongedwe ndithu munthu ameneyu,* ndipo mutimasulile Baraba!” 19 (Munthu ameneyu anaikidwa m’ndende cifukwa ca kuukila boma kumene kunacitika mu mzindawo, komanso cifukwa ca kupha anthu.) 20 Pilato anakambanso nawo kaciwili, cifukwa anali kufuna kumumasula Yesu. 21 Anthuwo anayamba kufuula mwamphamvu kuti: “Apacikidwe! Apacikidwe ndithu!” 22 Anakamba nawo kacitatu kuti: “Cifukwa ciyani? Walakwanji? Ine sindinamupeze ndi mlandu ulionse woyenela cilango ca imfa. Conco, ndidzangomukwapula ndi kumumasula.” 23 Atamva zimenezi, iwo anamuumiliza mokweza mawu kuti Yesu aphedwe.* Iwo anakuwa mwamphamvu cakuti Pilato anangololela. 24 Conco, Pilato anapeleka cigamulo kuti zimene anthuwo anali kufuna zicitike. 25 Iye anawamasulila munthu amene iwo anali kufuna, amene anali ataponyedwa m’ndende cifukwa coukila boma, komanso kupha anthu. Koma anapeleka Yesu m’manja mwawo kuti amucite zimene anali kufuna.

26 Tsopano pamene anali kupita naye, anagwila Simoni wa ku Kurene amene anali kucokela kudela la kumidzi, ndipo iwo anamunyamulitsa mtengo wozunzikilapo,* n’kumulamula kuti azilondola Yesu. 27 Khamu la anthu linali kumulondola, kuphatikizapo azimayi amene cifukwa ca cisoni anali kungodziguguda pacifuwa ndi kumulila. 28 Yesu anaceukila azimayiwo n’kuwauza kuti: “Inu ana aakazi a Yerusalemu, lekani kundilila. M’malo mwake, dzilileni nokha komanso lilani ana anu. 29 Pakuti masiku akubwela pamene anthu adzanena kuti, ‘Odala ndi akazi osabeleka, akazi amene alibe ana, komanso amene sanayamwitsepo!’ 30 Ndiyeno iwo adzayamba kuuza mapili kuti, ‘Tigweleni!’ Komanso adzauza mapili ang’onoang’ono kuti, ‘Tifoceleni!’ 31 Ngati akucita izi mtengo ukali wauwisi, n’ciyani cimene cidzacitika mtengowo ukadzauma?”

32 Amuna awili amene anali zigawenga, nawonso anatengedwa kuti akaphedwe pamodzi ndi Yesu. 33 Ndiyeno atafika pamalo ochedwa Cibade, anamukhomelela pa mtengo pamodzi ndi zigawenga zija, wina anamucipacika ku dzanja lake lamanja, ndipo wina kumanzele kwake. 34 Koma Yesu anali kukamba kuti: “Atate, akhululukileni, pakuti sadziwa zimene akucita.” Iwo anacita maele kuti agawane zovala zake. 35 Anthuwo anangoimilila n’kuyamba kuonelela zimene zinali kucitika. Koma olamulila anali kumunyodola ndi kunena kuti: “Anali kupulumutsa ena, mulekeni adzipulumutse yekha ngati iye alidi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.” 36 Ngakhale asilikali anali kumunyodola. Anali kubwela ndi kumupatsa vinyo wowawasa 37 n’kukamba kuti: “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” 38 Pamwamba pake analembapo mawu akuti: “Iyi ndi Mfumu ya Ayuda.”

39 Ndiyeno mmodzi wa zigawenga zimene anamupacika nazo pamodzi, anayamba kukamba mwacipongwe kuti: “Iwe ndiwe Khristu, si conco? Dzipulumutse, ndi kupulumutsanso ife!” 40 Poyankha mnzakeyo anamudzudzula kuti: “Kodi iwe suopa Mulungu poona kuti iwenso walandila cilango monga ca munthu ameneyu? 41 Ife tiyenela kulangidwa conci, cifukwa tikulandila zogwilizana ndi zimene tinacita. Koma munthu uyu sanalakwitse ciliconse.” 42 Kenako anakamba kuti: “Yesu, mukandikumbukile mukadzalowa mu Ufumu wanu.” 43 Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”

44 Apa nthawi inali ca m’ma 12 koloko masana,* koma m’dziko lonselo munagwa mdima mpaka ca m’ma 3 koloko masana,* 45 cifukwa dzuwa linaleka kuwala. Kenako, cinsalu cochinga ca m’nyumba yopatulika cinang’ambika pakati, kucokela pamwamba mpaka pansi. 46 Kenako Yesu anafuula kuti: “Atate, ndisungiza mzimu wanga m’manja mwanu.” Atakamba zimenezi, anatsilizika.* 47 Kapitawo wa asilikali ataona zimene zinacitika, anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Munthuyu analidi wolungama.” 48 Ndiyeno anthu onse amene anasonkhana kumeneko kudzaonelela zimene zinacitika, ataona zimene zinacitikazo, anabwelela kwawo akudziguguda pacifuwa. 49 Ndipo onse amene anali kumudziwa anaimilila capatali. Nawonso azimayi amene anali kumutsatila kucokela ku Galileya analipo, ndipo anaona zimene zinacitikazo.

50 Ndipo panali munthu wina wabwino komanso wolungama dzina lake Yosefe, wa m’Khoti Yaikulu ya Ayuda. 51 (Munthuyu sanaponyeko voti yovomeleza ciwembu cawo ndi zocita zawo.) Iye anali wocokela ku Arimateya, mzinda wa Ayuda, ndipo anali kuyembekezela Ufumu wa Mulungu. 52 Munthu ameneyu anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. 53 Iye anautsitsa n’kuukulunga m’nsalu yabwino kwambili, ndipo anakamuika m’manda* ogobedwa m’thanthwe, mmene simunaikidwepo mtembo uliwonse. 54 Tsopano linali Tsiku la Cikonzekelo, ndipo Sabata linali litatsala pang’ono kuyamba. 55 Koma azimayi amene anabwela naye kucokela ku Galileya anamutsatila, ndipo anawaona mandawo* ndi mmene anaikila mtembo wake. 56 Iwo anabwelela kukakonza zonunkhilitsa ndi mafuta onunkhila. Koma pa tsiku la Sabata anapumula malinga ndi cilamulo.

24 Koma pa tsiku loyamba la mlunguwo, iwo anapita m’mamawa kumandako,* atanyamula zonunkhilitsa zimene anakonza. 2 Koma anapeza kuti cimwala ca pamandawo* cakunkhunizidwila kumbali. 3 Ndipo atalowa m’mandawo sanaupeze mtembo wa Ambuye Yesu. 4 Akudabwa ndi zimenezi, anangoona kuti amuna awili ovala zovala zonyezimila aimilila pafupi nawo. 5 Azimayiwo anacita mantha, ndipo anawelamitsa nkhope zawo pansi. Ndiyeno amunawo anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukufuna munthu wamoyo pakati pa anthu akufa? 6 Iye sali kuno, waukitsidwa. Kumbukilani zimene anakuuzani pamene anali ku Galileya. 7 Anati Mwana wa munthu ayenela kupelekedwa m’manja mwa anthu ocimwa ndi kuphedwa pamtengo, ndipo pa tsiku lacitatu adzauka.” 8 Pamenepo iwo anakumbukila mawu ake, 9 ndipo anacoka kumandako* n’kupita kukafotokoza zinthu zonsezi kwa atumwi 11 aja, komanso kwa ena onse. 10 Azimayiwo anali Mariya Mmagadala, Jowana, komanso Mariya mayi ake a Yakobo. Ndiponso azimayi ena onse amene anali nawo, anali kufotokozela atumwi zinthu zimenezi. 11 Koma zimenezi zinaoneka ngati zacabecabe kwa iwo, ndipo sanawakhulupilile azimayiwo.

12 Koma Petulo ananyamuka n’kuthamangila kumandako,* ndipo atasuzila m’mandamo anangoona nsalu zokha. Conco, anacoka ndi kupita ali wodabwa ndi zimene zinacitika.

13 Koma patsiku limenelo, awili a iwo anali kupita ku mudzi wochedwa Emau, umene unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 11* kucokela ku Yerusalemu. 14 Iwo anali kukambilana zinthu zonsezi zimene zinacitika.

15 Tsopano pamene anali kukambilana zinthu zimenezi, Yesu anafika n’kuyamba kuyenda nawo limodzi. 16 Koma iwo sanathe kumuzindikila. 17 Iye anawafunsa kuti: “Kodi ndi nkhani zotani zimene mukukambilana pamene mukuyenda?” Iwo anangoima cilili akuoneka acisoni. 18 Mmodzi wa iwo dzina lake Keleopa anamuyankha kuti: “Kodi iwe ukukhala wekha mu Yerusalemu monga mlendo,* ndipo sudziwa zimene zacitika mmenemo m’masiku apitawa?” 19 Iye anawafunsa kuti: “Zinthu zotani?” Iwo anamuyankha kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti, amene anali mneneli wamphamvu m’zocita ndi m’mawu pamaso pa Mulungu, komanso pamaso pa anthu onse. 20 Ndiponso zokhudza mmene ansembe athu aakulu ndi olamulila anamupelekela kuti aphedwe, ndi kumukhomelela pamtengo. 21 Koma ife, tinali kuyembekezela kuti munthu uyu ndiye adzapulumutsa Aisiraeli. Inde, ndipo kuwonjezela apo, lelo ndi tsiku lacitatu kucokela pamene zinthuzi zinacitika. 22 Komanso azimayi ena m’gulu lathu atidabwitsa kwambili, cifukwa anapita ku manda* m’mamawa kwambili. 23 Ndipo ataona kuti mtembo wake mulibe m’mandamo, abwelako n’kutifotokozela kuti aona masomphenya a angelo amene awauza kuti Yesu ali moyo. 24 Ndiyeno ena pakati pathu anapita kumandako, ndipo apeza kuti m’mandamo mulibe aliyense mogwilizana ndi zimene azimayiwo anena. Koma iwo sanamuone.”

25 Conco iye anawauza kuti: “Opanda nzelu inu komanso ocedwa* kukhulupilila zonse zimene aneneli ananena! 26 Kodi sikunali koyenela kuti Khristu avutike ndi zinthu zonsezi n’kulowa mu ulemelelo wake?” 27 Ndiyeno anayamba kuwafotokozela zinthu zonse zokhudza iye m’Malemba onse kuyambila zolemba za Mose, komanso za aneneli onse.

28 Ndiyeno iwo anayandikila mudzi umene anali kupitako, ndipo iye anacita monga akufuna kupitilila mudziwo. 29 Koma iwo anamucondelela kuti akhalebe nawo. Anati: “Khalanibe nafe cifukwa kwayamba kuda, ndiponso tsiku latsala pang’ono kutha.” Iye atamva zimenezo analowa m’nyumba n’kukhala nawo. 30 Pamene anali kudya nawo cakudya, anatenga mkate n’kuudalitsa, kenako anaunyemanyema n’kuyamba kuwapatsa. 31 Pamenepo maso awo anatseguka ndipo anamuzindikila, koma Yesu anangozimililika pakati pawo. 32 Iwo anayamba kukambilana kuti: “Kodi si paja mawu ake anatikhudza kwambili mumtima, pamene anali kulankhula nafe mumsewu muja, ndi kutifotokozela Malemba momveka bwino?” 33 Pa ola lomwelo iwo ananyamuka n’kubwelela ku Yerusalemu, ndipo anapeza atumwi 11 aja ndi anthu ena amene anasonkhana nawo pamodzi. 34 Iwo anati: “Kukamba zoona, Ambuye anaukitsidwa kwa akufa, ndipo anaonekela kwa Simoni!” 35 Ndiyeno anafotokoza zimene zinacitika pamsewu komanso mmene anamudziwila pamene ananyemanyema mkate.

36 Ali mkati mokamba zimenezi, Yesu anaimilila pakati pawo ndi kuwauza kuti: “Mtendele ukhale nanu.” 37 Koma cifukwa cakuti iwo anadzidzimuka ndi kucita mantha, anaganiza kuti akuona mzimu. 38 Cotelo iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukuvutika mumtima komanso kukayikila m’mitima yanu? 39 Onani manja ndi mapazi anga kuti mutsimikize kuti ndine. Ndikhudzeni muone, cifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, koma ine monga mukuonela ndili nazo.” 40 Pokamba zimenezi, anawaonetsa manja ndi mapazi ake. 41 Koma popeza iwo sanakhulupililebe cifukwa ca cimwemwe ndi kudabwa, iye anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi cakudya ciliconse?” 42 Conco iwo anamupatsa cidutswa ca nsomba yowocha, 43 ndipo anacitenga n’kudya iwo akuona.

44 Kenako anawauza kuti: “Awa ndi mawu amene ndinakuuzani ndikali nanu akuti, zinthu zonse zokhudza ine zimene zinalembedwa m’Cilamulo ca Mose, m’zolemba za Aneneli, komanso zolembedwa mu Masalimo ziyenela kukwanilitsidwa.” 45 Kenako anatsegulilatu maganizo awo kuti amvetsetse tanthauzo la Malemba. 46 Ndipo anawauza kuti: “Malemba amati Khristu adzavutika, ndipo pa tsiku lacitatu adzauka kwa akufa. 47 Ndipo m’dzina lake, uthenga wakuti anthu afunika kulapa macimo awo kuti akhululukidwe, udzalalikidwa ku mitundu yonse, kuyambila ku Yerusalemu. 48 Inuyo mudzakhala mboni za zinthu zimenezi. 49 Ndipo taonani, ndidzakutumizilani cimene Atate wanga anakulonjezani. Koma inu mukhalebe mumzindawu, kufikila mutalandila mphamvu yocokela kumwamba.”

50 Ndiyeno anawatsogolela mpaka kukafika nawo ku Betaniya, ndipo kumeneko anakweza manja ake n’kuwadalitsa. 51 Pamene anali kuwadalitsa anawasiya, ndipo Mulungu anamutenga ndi kupita naye kumwamba. 52 Ndiyeno anamugwadila* n’kubwelela ku Yerusalemu ali osangalala kwambili. 53 Nthawi zonse iwo anali kukhala m’kacisi kutamanda Mulungu.

Kapena kuti, “timaziona kuti n’zodalilika.”

Kapena kuti, “Malinga ndi mwambo wa ansembe.”

Kapena kuti, “akali m’mimba mwa mayi ake.”

M’cinenelo coyambilila, “akatembenuze mitima ya atate kwa ana.” Izi zitanthauza kuti adzakhala ndi mtima wodzicepetsa.

Kapena kuti, “utumiki wotumikila anthu.”

Kapena kuti, “anamutomela.”

Kapena kuti, “Palibe ciliconse cimene Mulungu wakamba cimene cingalepheleke.”

Kapena kuti, “Moyo wanga ukulemekeza.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “nyanga yacipulumutso.”

Mawu ake enieni, “Mwana wamwamuna aliyense wotsegula mimba.”

M’cinenelo coyambilila, “ndipo kucokela pa unamwali wake.”

Kapena kuti, “anapitiliza kuwagonjela.”

Kutanthauza Herode Antipa.

M’cinenelo coyambilila, “tetaraki,” kutanthauza wolamulila cigawo cimodzi mwa magawo anayi.

Kapena kuti, “njila ya Mulungu ya cipulumutso.”

Kapena kuti, “covala cosinthila.”

Kapena kuti, “Musamatenge kwa anthu.”

Kapena kuti, “Musamalande aliyense zinthu.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amacotsa ku mbewu monga mpunga akapuntha, ndipo amatha kuwauluza.

Kapena kuti, “pamwamba pa mpanda wa.”

Kapena kuti, “anayeletsedwa.”

Kapena kuti, “kumusakasaka.”

Kutanthauza “Nyanja ya Galileya.”

Kapena kuti, “anakhala nawo pathebulo.”

Kapena kuti, “wolemala.”

Kapena kuti, “wolemala.”

Kapena kuti, “kukana.”

Kutanthauza popanda ciwongoladzanja.

Kapena kuti, “kumasulana.”

Kapena kuti, “mudzamasulidwa.”

Kapena kuti, “zovala zabwino kwambili.”

Mawu ake enieni, “pamaso pako.”

Kapena kuti, “malangizo.”

Mawu ake enieni, “ana ake onse.”

Kapena kuti, “akudya pa thebulo.”

Kapena kuti, “aakulu.”

Thanthwe ndi cimwala cacikulu.

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Ma Baibulo ena amati, “Kwa nthawi yaitali, mzimuwo unamugwila.”

M’cinenelo coyambilila, “apulumutsidwa.”

Kapena kuti, “mphamvu ya moyo.”

M’cinenelo coyambilila, ”siliva.”

Kapena kuti, “covala cosinthila.

Ameneyu ndi Herode Antipa.

M’cinenelo coyambilila, “tetaraki,” kutanthauza wolamulila cigawo cimodzi mwa magawo anayi.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

M’cinenelo coyambilila, “mwana wamng’ono uyu.“

M’cinenelo coyambilila, ”Pamene masiku anali kukwana.”

M’cinenelo coyambilila, ”nkhope yake yalunjika ku.”

M’cinenelo coyambilila, “alibe kulikonse kumene angasamile mutu wake.”

Pa nthawiyo, moni wa mwambo unali kuphatikizapo kupsompsonana, kukumbatilana, ndi kukambilana kwa nthawi yaitali.

Kapena kuti, “Hade,” kutanthauza manda a anthu onse.

M’cinenelo coyambilila, ”mawu awo.”

Kapena kuti, “gawo labwino koposa.”

Kapena kuti, “likhale lopatulika; lionedwe kukhala loyela.”

M’cinenelo coyambilila, “ali nafe nkhongole.”

Dzina lina la Satana.

Kapena kuti, “thadza lopimila.”

Kapena kuti, “limaona bwino.”

M’cinenelo coyambilila, “loipa.”

Kutanthauza kusamba m’manja motsatila mwambo.

Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ndiwo zilizonse za ku dimba.”

Kapena kuti, “yabwino kwambili.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “manda aja osaikidwa cizindikilo.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “adzafunidwa kucokela ku m’badwo uwu.”

M’cinenelo coyambilila, “nyumba.”

Kapena kuti, “magazi amenewo adzafunidwa ku mbadwo uwu.”

Kutanthauza mu Ufumu wa kumwamba. Onani Mateyo 23:13.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “amainyalanyaza.”

M’cinenelo coyambilila, “kukuphunzitsani.”

Kapena kuti, “kaduka.”

Kapena kuti, “ndidzauza moyo wanga kuti.”

Kapena kuti, “Moyo uli.”

Kapena kuti, “miyoyo yanu.”

M’cinenelo coyambilila, “ndi mkono umodzi.”

Kucokela ca m’ma 9 koloko usiku mpaka pakati pa usiku.

Kucokela pakati pa usiku mpaka 3 koloko m’matandakuca.

Kapena kuti, “woyang’anila nyumba.”

Kapena kuti, “gulu la anchito ake a pakhomo.”

Kapena kuti, “kucita mogwilizana ndi zimene mbuye wake anali kufuna.”

M’cinenelo coyambilila, “leptoni yothela.”

Kapena kuti, “mzimu wolemalitsa.”

M’cinenelo coyambilila, “miyeso ya seya.” Muyeso umodzi wa seya unali kukwana malita 7.33.

Kapena kuti, “n’zosamveka.”

Kapena kuti, “matenda a edema. Matendawa amabwela cifukwa ca kuculuka kwa madzi m’thupi.”

M’cinenelo coyambilila, “adzadya mkate.”

Kapena kuti, “otsimphina.”

Kapena kuti, “koma sanacepetse cikondi cake pa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “sangalekane nazo.”

Kapena kuti, “azimayi ena amene ndi anzake.”

Kapena kuti, “umoyo wowononga.”

M’cinenelo coyambilila, “ali ndi thanzi labwino.”

M’cinenelo coyambilila, “anadya.”

Mtsuko umodzi unali kukwana malita 22.

Kapena kuti, “miyeso 100 ya kori.” Muyeso umodzi wa kori unali kukwana malita 220.

Kapena kuti, “moganiza bwino; mocenjela.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kutanthauza mwamuna amene wasudzula mkazi wake pa cifukwa cosakhala ciwelewele.

Kutanthauza mkazi amene wasudzulidwa pa cifukwa cosakhala ciwelewele.

Kapena kuti, kunyambita.

M’cinenelo coyambilila, “pacifuwa ca Abulahamu,” kutanthauza malo abwino apadela.

Kapena kuti, “Hade,” kutanthauza manda a anthu onse.

M’cinenelo coyambilila, “ali pacifuwa cake.”

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

Kapena kuti, “n’kumandipumphuntha mpaka kunditsiliza.”

M’cinenelo coyambilila, “cikhulupililoco.”

Kapena kuti, “ndicitileni cifundo.”

Kapena kuti, “panyengo imene ikubwelayo.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ndinalanda mocita kunamizila munthu mlandu.”

Ndalama ya mina ya Cigiriki inali kulemela magalamu 340, ndipo ndalama imodzi ya mina inali kulingana ndi madalakima 100.

M’cinenelo coyambilila, “siliva.”

M’cinenelo coyambilila, “siliva wanga.”

Kapena kuti, “kukuvutitsa.”

Kapena kuti, “ndi kumucita zinthu zomucotsela ulemu.”

M’cinenelo coyambilila, “mutu wa kona.”

Kapena kuti, “n’coyenela.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “m’kaonedwe kake.”

Kapena kuti, “yabwino kwambili.”

M’cinenelo coyambilila, “amadya nyumba za akazi.”

Kapena kuti, “mwaciphamaso.”

Kapena kuti, “colema.”

Kapena kuti, “m’mabokosi a zopeleka.”

M’cinenelo coyambilila, “maleputoni awili.”

Kapena kuti, “zipwilikiti.”

Kapena kuti, “mudzapeza moyo.”

Kapena kuti, “masiku obwezela.”

Kapena kuti, “anthu akunja.”

Kapena kuti, “anthu akunja.”

M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

M’cinenelo coyambilila, “mutengeni mupite naye.”

Kapena kuti, “aphedwe pamtengo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

M’cinenelo coyambilila, “ola la 6.”

M’cinenelo coyambilila, “ola la 9.”

Kapena kuti, “anapuma kothela.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

M’cinenelo coyambila, “masitadiya 60. Sitadiya imodzi inali kukwana mamita 185.”

Ma Baibulo ena amati, “Kodi ndiwe mlendo yekhayo mu Yerusalemu amene sukudziŵa?”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “amtima wocedwa.”

Kapena kuti, “anamuwelamila.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani