Mankhwala Amene Adzathetselatu Tsankho
Anthu mamiliyoni aseŵenzetsa mfundo zimene zafotokozedwa m’nkhani zapita, ndipo zawathandiza kwambili kuthetsa tsankho mu mtima mwawo. Koma kukamba zoona, mwa mphamvu zathu sitingakwanitse kuthetselatu tsankho. Kodi izi zitanthauza kuti tsankho silikatha mpaka kale-kale?
Boma Labwino Koposa
Maboma a anthu alephela kuthetsa tsankho. Koma kodi zimenezi zitanthauza kuti palibe boma limene lingakwanitse kuthetsa tsankho?
Kuti boma likwanitse kuthetsa tsankho, lingafunike:
1. Kulimbikitsa anthu kusintha maganizo awo komanso mmene amaonela anthu ena.
2. Kuthetsa zinthu zopanda cilungamo zimene zimasonkhezela tsankho pakati pa anthu.
3. Kukhala na olamulila acilungamo amene alibiletu tsankho.
4. Kugwilizanitsa anthu a mitundu yonse.
Baibo imatitsimikizila kuti Mulungu anapanga boma laconco. Limachedwa “Ufumu wa Mulungu.”—Luka 4:43.
Onani zimene boma limenelo lidzacitila nzika zake:
1. Lidzapeleka Maphunzilo Abwino Kwambili
“Anthu okhala panthaka ya dzikolo adzaphunzila cilungamo.”—YESAYA 26:9.
“Nchito ya cilungamo ceni-ceni idzakhala mtendele, ndipo zocita za cilungamo ceni-ceni zidzakhala bata ndi mtendele mpaka kale-kale.”—YESAYA 32:17.
Kodi malembawa atanthauza ciani? Ufumu wa Mulungu udzaphunzitsa anthu kucita zabwino. Anthu akadziŵa coyenela na cosayenela, colungama na cosalungama, amasintha mmene amaonela wina na mnzake. Aliyense adzadziŵa kuti ayenela kukonda anthu a mitundu yonse.
2. Lidzathetsa Zinthu Zopanda Cilungamo
Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale zopweteka. Zakalezo zapita.”—CHIVUMBULUTSO 21:4.
Kodi lembali litanthauza ciani? Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse obwela cifukwa ca zinthu zopanda cilungamo zimene anthu amacita. Anthu sadzakhalanso pa udani cifukwa ca zinthu zopanda cilungamo zimene ena anawacitila.
3. Mtsogoleli Wake Adzakhala Wacilungamo
“Sadzaweluza potengela zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengela zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweluza mwacilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.”—YESAYA 11:3, 4.
Kodi lembali litanthauza ciani? Yesu Khristu, Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, adzalamulila dziko lapansi mwacilungamo komanso mopanda tsankho. Yesu sakonda mtundu wina kuposa unzake, ndipo adzaonetsetsa kuti anthu onse padziko lapansi akutsatila malamulo ake olungama.
4. Lidzagwilizanitsa Anthu Onse
Ufumu wa Mulungu umaphunzitsa anthu kuti akhale “ndi maganizo amodzi, ndi cikondi cofanana. [Akhalenso] ogwilizana mu mzimu umodzi ndi mtima umodzi.”—AFILIPI 2:2.
Kodi lembali litanthauza ciani? Mgwilizano umene nzika za Ufumu wa Mulungu zidzakhala nawo udzakhala weni-weni. Adzakhala ‘ogwilizana ndi mtima umodzi’ cifukwa adzakhala okondana na mtima wonse.