LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 68
  • Anyamata Aŵili Amene Akhalanso Amoyo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anyamata Aŵili Amene Akhalanso Amoyo
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mwana wa Mkazi Wamasiye Aukitsidwa
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Asilikali a Yehova Amoto
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 68

Nkhani 68

Anyamata Aŵili Amene Akhalanso Amoyo

NGATI unafa, ndiyeno waukitsidwa kukhalanso ndi moyo, kodi amai ako angamvele bwanji? Angakondwele kwambili! Koma munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo? Kodi zimenezi zinayamba zacitikapo?

Ona mwamuna, mkazi ndi kamnyamata pacithunzi-thunzi apa. Mwamuna uyu ni mneneli Eliya. Mkaziyu ni wamasiye wa ku mzinda wa Zarefati, ndipo mnyamata ni mwana wake. Tsiku lina mnyamatayu anadwala, ndipo matenda ake anakula kwambili mpaka iye amwalila. Ndiyeno Eliya auza amai ake kuti: ‘Mubweletseni kuno mwana wanu.’

Eliya atenga mwanayo ndi kupita naye kucipinda capamwamba ndipo amugoneka pabedi. Ndiyeno apemphela kuti: ‘O Yehova, cititsani mnyamata uyu kuti akhalenso ndi moyo.’ Pamenepo mnyamatayo ayamba kupuma! Ndiyeno Eliya abwelela naye, ndi kuuza amai ake kuti: ‘Taonani, mwana wanu ali moyo!’ N’cifukwa cake amai ake ni okondwela kwambili.

Mneneli wina wofunika kwambili wa Yehova ni Elisa. Nchito yake ni yothandiza Eliya. Koma m’kupita kwa nthawi, Yehova agwilitsilanso nchito Elisa kucita zozizwitsa. Tsiku lina Elisa anapita ku mzinda wa Sunemu. Kumeneko anapezako mkazi amene anamukomela mtima kwambili. Nthawi ina mkazi ameneyu anabala mwana mwamuna.

Pamene mwanayu akula, tsiku lina anayenda kukagwila nchito pamodzi ndi atate ake kumunda. Mwadzidzidzi mwanayo afuula kuti: ‘Mutu wanga uŵaŵa!’ Pamene anayenda naye kunyumba, mwanayu anamwalila. Amai ake anamva cisoni kwambili! Ndipo nthawi imeneyo anayenda kukaitana Elisa.

Pamene Elisa afika, atenga mwana wakufa uja ndi kuloŵa naye mu cipinda. Iye apemphela kwa Yehova, pamene aŵelamila pathupi la mwanayo. Sipanapite nthawi yaitali, thupi la mwanayo liyamba kufunda, ndipo ayetsemula nthawi zokwanila 7. Amai ake akondwela kwambili pamene aloŵa mu cipindamo ndi kupeza kuti mwana wao ali moyo!

Pali anthu ambili-mbili amene anamwalila. Ndipo zimenezi zapangitsa mabanja ndi mabwenzi ao kukhala acisoni kwambili. Tilibe mphamvu youkitsa akufa. Koma Yehova ali nayo. Nthawi ina tidzaphunzila mmene Yehova adzaukitsila mamiliyoni ambili a anthu akufa kuti akakhalenso ndi moyo.

1 Mafumu 17:8-24; 2 Mafumu 4:8-37.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani