Uthenga Wabwino wa Anthu Onse
Kuuka kwa Yesu kunapangitsa ophunzila ake kukhala ndi cikhulupililo colimba ndi kuti azicita zinthu mwakhama. Mtumwi Paulo anali ndi khama kwambili ndipo anayenda-yenda ku madela a ku Asia Minor ndi ku Mediterranean. Iye anali kukhazikitsa mipingo ndi kulimbikitsa Akristu kuti asatengele makhalidwe oipa ndiponso kuti asagonje ndi cizunzo. Ngakhale kuti panali mavuto amenewa, anthu ambili anakhala Akristu.
Paulo anaikidwa m’ndende. Koma ngakhale kuti anali m’ndende, iye analemba makalata olimbikitsa ndi kulangiza mipingo yacikristu. Iye anacenjeza Akristu za vuto lalikulu la mpatuko. Motsogoleledwa ndi mzimu woyela wa Mulungu, Paulo anakambilatu kuti pakati pao padzafika “mimbulu yopondeleza” imene idzayamba kulankhula “zinthu zopotoka” ndi ‘kupatutsa ophunzila aziwatsatila.’—Machitidwe 20:29, 30.
Pofika kumapeto kwa nthawi ya atumwi, mpatuko unayamba. Nthawi imeneyo, Yesu anapatsa mtumwi Yohane masomphenya a zinthu zamtsogolo. Monga mmene Yohane analembela, otsutsa ndi aphunzitsi onama sangalepheletse Mulungu kukwanilitsa cifunilo cake coyambilila cokhudza dziko lapansi ndi anthu. Anthu a “fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse” adzamva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 14:6) Dziko lapansi lidzakhala paladaiso, ndipo aliyense amene amafuna kucita cifunilo ca Mulungu ali ndi mwai wodzakhala mmenemo.
Kodi umenewu si “uthenga wabwino” kwa inu? Ngati ndi conco, phunzilani zambili zokhudza uthenga wa Mulungu kwa anthu umene uli m’Baibo, ndi mmene mungapindulile ndi uthenga umenewo pa nthawi ino ndi mtsogolo.
Mungaŵelenge Baibo pa Webusaiti ya www.jw.org. Pa Webusaiti imeneyi, mungaŵelengenso kabuku kakuti Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? ndi kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. Palinso buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, ndi mabuku ena amene amafotokoza cifukwa cake tingakhulupilile Baibo ndiponso mmene tingagwilitsilile nchito malangizo ake othandiza m’banja ndi pa umoyo wathu. Kapena funsani mmodzi wa Mboni za Yehova kuti mudziŵe zambili.
—Yazikidwa pa Machitidwe, Aefeso, Afilipi, Akolose, Filimoni, 1 Yohane, Chivumbulutso.