KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO
Kodi ndani adzapita kumwamba, ndipo n’cifukwa ciani?
Anthu mamiliyoni ambili amafuna kupita kumwamba. Yesu anakamba kuti atumwi ake okhulupilika adzapita kukakhala kumwamba. Yesu asanafe, anawalonjeza kuti iye ndi Atate wake wakumwamba adzawakonzela malo.—Ŵelengani Yohane 14:2.
N’cifukwa ciani anthu ena adzaukitsidwa kuti akakhale kumwamba? Kodi io adzapita kukacita ciani kumeneko? Yesu anauza atumwi ake kuti adzakhala mafumu? Iwo adzalamulila dziko lonse lapansi.—Ŵelengani Luka 22:28-30; Chivumbulutso 5:10.
Kodi anthu onse abwino amapita kumwamba?
M’maiko ambili, anthu ocepa cabe ndi amene amalamulila. Popeza kuti Yesu adzaukitsa anthu kuti akakhale kumwamba n’colinga cakuti adzalamulile dziko, tiyenela kukhulupilila kuti ndi anthu ocepa cabe amene adzasankhidwa. (Luka 12:32) Baibo imachula ciŵelengelo ceni-ceni ca anthu amene adzalamulila ndi Yesu.—Ŵelengani Chivumbulutso 14:1.
Anthu amene adzapita kumwamba si ndiwo okha amene adzalandila madalitso. Nzika zokhulupilika za Ufumu wa Yesu zidzasangalala ndi moyo wamuyaya m’paladaiso padziko lapansi. (Yohane 3:16) Anthu ena adzaloŵa m’Paladaiso pambuyo populumuka cionongeko ca dongosolo la zinthu loipali. Koma ena adzaloŵa m’Paladaiso pambuyo pouka kwa akufa.—Ŵelengani Salimo 37:29; Yohane 5:28, 29.
Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 8 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova
Mungatenge buku limeneli pa www.jw.org
[Cithunzi papeji 32]
Yesu anakonza malo kumwamba kuti otsatila ake ena akakhale kumeneko. Kodi mukudziŵa zimene io adzacita kumeneko?