LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 3/1 tsa. 16
  • Kuyankha Mafunso A m’Baibulo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuyankha Mafunso A m’Baibulo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kodi Yesu Adzacita Ciani Mtsogolo?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kodi Nkhondo Zidzatha Bwanji?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2025
  • Kodi Mulungu Adzacita Ciani Kutsogolo?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 3/1 tsa. 16

Kuyankha Mafunso A m’Baibulo

Kodi n’zotheka kukhala ndi boma limodzi padziko lonse?

Anthu a mitundu yonse ogwilizanitsidwa ndi boma limodzi la padziko lonse

Kodi boma la padziko lonse lingagwilizanitse bwanji anthu a mitundu yonse? Yesaya 32:1, 17; 54:13

Ganizilani mmene boma la padziko lonse lingathandizile anthu. Masiku ano anthu ambili akuvutika cifukwa ndi osauka kwambili pamene ena ndi olemela kwambili. Komabe, boma la padziko lonse limene limaganizila anthu likhoza kuonetsetsa kuti anthu onse ali ndi zimene amafunikila. Kodi muona kuti n’zotheka anthu kupanga boma lotelo?—Ŵelengani Yeremiya 10:23.

Kuyambila kale, maboma alephela kusamalila anthu, makamaka osauka. Maboma ena ndi ankhanza. (Mlaliki 4:1; 8:9) Koma Mulungu Wamphamvuyonse walonjeza kuti adzabweletsa boma limene lidzaphwanya maboma onse ndi kuyamba kulamulila. Wolamulila wake adzasamalila bwino anthu.—Ŵelengani Yesaya 11:4; Danieli 2:44.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita ciani?

Yehova Mulungu wasankha Wolamulila wa dziko lonse wabwino kwambili. Wolamulila ameneyu ndi Yesu Mwana wake. (Luka 1:31-33) Pamene anali padziko lapansi, Yesu anali wofunitsitsa kuthandiza anthu. Monga Mfumu, iye adzagwilizanitsa anthu a mitundu yonse ndi kuthetsa mavuto onse a anthu.—Ŵelengani Salimo 72:8, 12-14.

Kodi ndi anthu onse amene amavomeleza Yesu kukhala Wolamulila wao? Iyai. Ngakhale ndi conco, Yehova ndi woleza mtima. (2 Petulo 3:9) Iye akupatsa anthu mwai wovomeleza Yesu kukhala Wolamulila wao. Posacedwapa Yesu adzaononga anthu onse oipa padzikoli ndi kubweletsa mtendele ndi citetezo—Ŵelengani Mika 4:3, 4.

Kuti mudziwe zambili, onani nkhani 8 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Buku limeneli likupezekanso pa www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani