KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Yesu adzacita ciani mtsogolo?
M’caka ca 33 C.E.,Yesu anaphedwa, ndipo anaukitsidwa ndi kupita kumwamba. Pambuyo pake, iye anaikidwa kukhala Mfumu. (Danieli 7:13, 14) Pokhala Mfumu, Yesu mtsogolo adzabweletsa mtendele padziko lapansi ndi kucotsapo njala.—Ŵelengani Salimo 72:7, 8, 13.
Pokhala Mfumu, Yesu adzacotsa kusalungama konse padziko lapansi
Monga Wolamulila wa anthu, Yesu adzacita zinthu zabwino zambili. Adzagwilitsila nchito mphamvu zimene Atate wake anam’patsa kubwezeletsa anthu ku ungwilo. Anthu adzasangalala ndi moyo padziko lapansi ndipo sadzakalamba ndi kufa.—Ŵelengani Yohane 5:26-29; 1 Akorinto 15:25, 26.
Kodi Yesu akucita ciani tsopano?
Yesu tsopano akutsogolela nchito yolalikila ya otsatila ake oona. Iwo amacezela anthu ndi kuwaonetsa zimene Baibulo limanena zokhudza Ufumu wa Mulungu. Yesu anakamba kuti adzapitiliza kucilikiza ophunzila ake mpaka pamene Ufumu wa Mulungu udzacotsapo maboma a anthu.—Ŵelengani Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Mogwilitsila nchito mpingo woona wacikristu, Yesu akuthandiza anthu kukhala ndi umoyo wabwino. Adzapitilizabe kuwatsogolela mpaka pa cionongeko ca dongosolo ili la zinthu ndi kuwaloŵetsa m’dziko latsopano.—Ŵelengani 2 Petulo 3:7, 13; Chivumbulutso 7:17.