Mau Oyamba
Muganiza Bwanji?
Ngati Baibulo si buku locokela kwa Mulungu, kodi Mulungu akanaiteteza kuti anthu asaiwononge?
Baibulo imakamba yokha kuti: “Udzu wobiliŵilawo wauma. Maluŵawo afota. Koma mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”—Yesaya 40:8.
Nkhani za m’magazini ino zifotokoza nkhani yocititsa cidwi ya mmene Baibulo yapulumukila.