LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 July masa. 12-16
  • “Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • YEHOVA—“AMATITONTHOZA M’NJILA ILIYONSE”
  • YESU—“MKULU WA ANSEMBE WACIFUNDO”
  • MALEMBA AMATILIMBIKITSA
  • MPINGO UMATITONTHOZA KWAMBILI
  • PITILIZANI KUTONTHOZA ENA
  • Kupilila Cisoni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Mmene Mulungu Amatitonthozela
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Yehova ni “Mulungu Amene Amatitonthoza M’njila Iliyonse”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Kulimbikitsa Amene Anacitilidwapo Zolaula
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 July masa. 12-16
Anthu ali kucipatala ndipo akulila

“Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”

“Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.” —1 ATES. 5:11.

NYIMBO: 121, 75

KODI MUKUMBUKILA?

  • Kodi Yehova amapeleka bwanji citonthozo?

  • Ni malemba ati amene angatonthoze anthu ofedwa?

  • Kodi mpingo ungatonthoze bwanji anthu amene ali na cisoni?

1, 2. N’cifukwa ciani tifunika kukambilana mmene tingatonthozele ofedwa? (Onani pikica pamwambapa.)

“MWANA wathu wamwamuna atamwalila, tinavutika na cisoni pafupi-fupi kwa caka cathunthu,” anatelo Susi. Mkhristu winanso anakamba kuti pamene mkazi wake anamwalila mwadzidzidzi, anamvela “ululu wosaneneka.” N’zomvetsa cisoni kuti anthu ambili akuvutika na cisoni cotele. Ambili amene anafedwa mumpingo wacikhristu sanali kuyembekezela kuti okondedwa awo angafe Aramagedo ikalibe kufika. Mwina imwe munataikilidwa wokondedwa wanu, kapena mudziŵako munthu wina amene anafedwa. Ngati n’conco, mungafunse kuti, ‘N’ciani cingathandize anthu ofedwa kupilila?’

2 Anthu ena amakamba kuti cisoni cimasila cokha m’kupita kwa nthawi. Koma kodi n’zoona kuti nthawi payokha ingathetse cisoni? Mayi wina wamasiye anati, “Niona kuti cimene cimathandiza kuti cisoni cithe ndi zimene munthu amacita osati nthawi cabe.” Mwacitsanzo, cilonda cimapola m’kupita kwa nthawi ngati tiikapo mwankhwala na kucisamalila. N’cimodzimodzi ndi cisoni. M’kupita kwa nthawi cimatha, koma timafunika kucitapo kanthu. N’ciani maka-maka cimene cingathandize ofedwa kuthetsa cisoni?

YEHOVA—“AMATITONTHOZA M’NJILA ILIYONSE”

3, 4. Tingatsimikize bwanji kuti Yehova amadziŵa kuti munthu wofedwa afunika citonthozo?

3 Yehova, Atate wathu wacifundo wakumwamba, ndiye gwelo lalikulu la citonthozo. (Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Iye, amene ni wacifundo kwambili kuposa aliyense, anauza anthu ake kuti: “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.”—Yes. 51:12; Sal. 119:50, 52, 76.

4 Atate wathu wacifundo cacikulu anavutikapo na cisoni cifukwa ca imfa ya okondedwa ake monga Abulahamu, Isaki, Yakobo, Mose, ndi Mfumu Davide. (Num. 12:6-8; Mat. 22:31, 32; Mac. 13:22) Mau a Mulungu amakamba kuti Yehova amacita kulaka-laka nthawi pamene adzaukitsa akufa. (Yobu 14:14, 15) Anthuwo akadzaukitsidwa, adzakhala osangalala ndi athanzi. Komanso, kumbukilani kuti Mwana wokondeka wa Mulungu, amene anali kusangalala naye kwambili, anafa imfa yoŵaŵa. (Miy. 8:22, 30) Sitingakwanitse kufotokoza mmene Yehova cinamuwaŵila panthawiyo.—Yoh. 5:20; 10:17.

5, 6. Kodi Yehova angatitonthoze bwanji?

5 Ngati tafedwa, tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzatithandiza. Conco, tizikhala womasuka kupemphela kwa Mulungu ndi kum’fotokozela zonse zokhudza cisoni cimene tili naco. N’zolimbikitsa ngako kudziŵa kuti Yehova amamvetsetsa mmene timvelela, ndipo amatipatsa citonthozo cofunikila. Koma kodi amacita bwanji zimenezi?

6 Njila imodzi imene Mulungu amatitonthozela ni kupitila mwa “mzimu woyela.” (Mac. 9:31) Mzimu woyela, umene ni mphamvu ya Mulungu yogwila nchito, ungathe kutitonthoza kwambili. Yesu analonjeza kuti Atate wathu wakumwamba ni wokonzeka ‘kupeleka mzimu woyela kwa amene akum’pempha.’ (Luka 11:13) Susi, amene tam’gwila mau poyamba, anati: “Nthawi zambili tinali kugwada na kucondelela Yehova kuti atitonthoze. Nthawi zonse tikacita zimenezi, mtendele wa Mulungu unali kuteteza mitima yathu na maganizo athu.”—Ŵelengani Afilipi 4:6, 7.

YESU—“MKULU WA ANSEMBE WACIFUNDO”

7, 8. N’cifukwa ciani tingakhale na cikhulupililo cakuti Yesu adzatitonthoza?

7 Zimene Yesu, Mwana wacifundo wa Mulungu anakamba na kucita pamene anali padziko lapansi, zinaonetsa bwino cifundo cimene Yehova ali naco. (Yoh. 5:19) Yesu anatumiwa padziko kuti akatonthoze “anthu osweka mtima” ndi “onse olila.” (Yes. 61:1, 2; Luka 4:17-21) Conco, iye anali munthu wacifundo cacikulu, anali kumvetsetsa mavuto amene anthu anali kukumana nawo, ndipo anali wofunitsitsa kuwathandiza.—Aheb. 2:17.

8 Pamene Yesu anali wacicepele, mwacionekele anavutikapo na cisoni cifukwa ca imfa ya acibululu kapena mabwenzi ake. Mwacitsanzo, cioneka kuti Yosefe, atate ake a Yesu omulela, anafa iye akali wacicepele.a Ziyenela kuti zinali zovuta kwa Yesu wacifundoyo, amene mwina anali na zaka 20 kapena kucepelapo, kupilila imfa ya atate ake. Ayenelanso kuti anavutika kwambili poona cisoni cimene amayi ake, azilongosi ake, ndi abale ake anali naco.

9. Pamene Lazaro anafa, kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali ndi cisoni?

9 Pa utumiki wake, Yesu anaonetsa kuti anali wozindikila ndi wacifundo. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika pamene mnzake wapamtima Lazaro anamwalila. Ngakhale kuti Yesu anali kudziŵa kuti adzaukitsa Lazaro, anakhudzidwa kwambili ataona cisoni cimene Mariya na Marita anali naco. Iye anamva cisoni kwambili cakuti anafika pogwetsa misozi.—Yoh. 11:33-36.

10. N’cifukwa ciani tingakhale na cikhulupililo cakuti Yesu amatimvela cifundo masiku ano?

10 Kodi cifundo cimene Yesu anaonetsa ndi citonthozo cimene anapeleka, zingatilimbikitse bwanji masiku ano? Malemba amatitsimikizila kuti “Yesu Khristu ali cimodzimodzi dzulo ndi lelo, ndiponso mpaka muyaya.” (Aheb. 13:8) Popeza kuti “Mtumiki Wamkulu wa moyo” amadziŵa mmene cisoni cimaŵaŵila, “amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.” (Mac. 3:15; Aheb. 2:10, 18) Conco, tingakhale na cikhulupililo cakuti ngakhale lomba, Khristu amakhudzidwa na mavuto amene timakumana nawo, amamvetsetsa cisoni cimene timakhala naco, ndipo amatipatsa citonthozo “pa nthawi imene tikufunika thandizo.”—Ŵelengani Aheberi 4:15, 16.

MALEMBA AMATILIMBIKITSA

11. Ni malemba ati amene amakutonthozani ngako inuyo?

11 Lemba limene limakamba za cisoni cacikulu cimene Yesu anamvela pamene Lazaro anamwalila, ni lotonthoza kwambili, ndipo n’limodzi cabe mwa malemba ambili-mbili olimbikitsa opezeka m’Mau a Mulungu. N’cifukwa cake Baibo imati, “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa ciyembekezo cifukwa malembawa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.” (Aroma 15:4) Ngati munafedwa, mungapeze citonthozo pa malemba monga awa:

  • “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Sal. 34:18, 19.

  • “Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mau anu [Yehova] otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”—Sal. 94:19.

  • “Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ndipo amatilimbikitsa m’njila yosalephela ndiponso anatipatsa ciyembekezo cabwino, mwa kukoma mtima kwakukulu, alimbikitse mitima yanu.”—2 Ates. 2:16, 17.b

MPINGO UMATITONTHOZA KWAMBILI

12. Kodi cinthu cimodzi cofunika cimene tingacite potonthoza ena n’citi?

12 Njila ina imene anthu ofedwa angapezele citonthozo ni kupitila mumpingo wacikhristu. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:11.) Kodi anthu amene ali na “mtima wosweka” mungawatonthoze bwanji ndi kuwalimbikitsa? (Miy. 17:22) Kumbukilani kuti pali “nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) Mlongo wina wamasiye, dzina lake Dalene anati: “Anthu amene afedwa amafuna kufotokoza maganizo awo ndi mmene amvelela. Conco, cinthu cofunika kwambili cimene mungacite kwa wofedwa ndi kumumvetsela popanda kum’dula mau.” Junia, amene m’bale wake anadzipha, anakamba kuti: “Ngakhale kuti simungamvetsetse zonse zokhudza cisoni cimene munthu wofedwa ali naco, cofunika ngako ni nkhawa imene mwamuonetsa mwa kuyesetsa kumumvetsela.”

13. N’ciani cimene tifunika kukumbukila pankhani ya kumva cisoni?

13 Tifunikanso kukumbukila kuti anthu amakhudzika mtima ndi kuonetsa cisoni m’njila zosiyana-siyana. Nthawi zina, munthu angakhale na cisoni cacikulu, koma osakwanitsa kufotokoza mmene akumvelela. Mau a Mulungu amati: “Mtima umadziŵa kuŵaŵa kwa moyo wa munthu, ndipo mlendo sangaloŵelele pamene mtimawo ukusangalala.” (Miy. 14:10) Ngakhale munthu atafotokoza mmene amvelela, nthawi zina zimakhalabe zovuta kumumvetsetsa.

14. Kodi anthu amene afedwa tingawatonthoze bwanji?

14 M’pomveka kuti nthawi zina munthu amasoŵa cokamba kwa munthu amene ali na cisoni cacikulu. Ngakhale n’conco, Baibo imakamba kuti “lilime la anthu anzelu limacilitsa.” (Miy. 12:18) Pofuna kutonthoza ena, ambili apeza mfundo zolimbikitsa m’kabuku kakuti, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.c Komabe, nthawi zambili cimene cimakhala cothandiza kwambili ndi ‘kulila ndi anthu amene akulila.’ (Aroma 12:15) Gaby, amene mwamuna wake anamwalila, anati: “Kulila n’kumene kumanitonthoza. N’cifukwa cake nimalimbikitsidwa ngati anzanga akulila nane. Panthawiyi, nimatonthozedwa poona kuti anzanga nawonso ali na cisoni.”

15. Kodi tingapeleke bwanji citonthozo ngati taona kuti n’zovuta kukamba na munthu pamaso-m’pamaso? (Onaninso bokosi yakuti “Mau Otsitsimula ndi Otonthoza.”)

15 Ngati mwaona kuti n’zovuta kuuza munthu mau om’tonthoza pamaso-m’pamaso, mungam’patse khadi ya uthenga wacitonthozo, kumulembela meseji pafoni kapena pa kompyuta, kapena kumulembela kalata. Polemba, mungagwile mau lemba linalake lolimbikitsa, kuchula khalidwe lina labwino la womwalilayo, kapena kufotokoza zinthu zina zokondweletsa zimene munali kucitila pamodzi ndi womwalilayo. Junia anati: “Nikalandila meseji yonilimbikitsa kapena ngati Mkhristu waniitana kuti nikaceze kwawo, nimalimbikitsidwa ngako. Zimenezi zimanicititsa kuona kuti ena amanikonda ndi kuniganizila.”

16. N’ciani cina cimene cimathandiza kwambili potonthoza ena?

16 Kupemphela pamodzi na Mkhristu wofedwa ndiponso kumupemphelela n’zofunika kwambili. N’zoona kuti, cifukwa ca cisoni, zingakhale zovuta kufotokoza bwino-bwino maganizo anu popemphela. Komabe, kupemphela naye mocokela pansi pamtima kungamutonthoze kwambili, ngakhale m’takhala kuti mukulila ndipo mau anu sakumveka bwino. Dalene anati: “Nthawi zina alongo akabwela kudzaniona, nimawapempha kuti anipemphelele. Poyamba kupemphela, nthawi zambili amakamba movutikila, koma posakhalitsa mau awo amayamba kumveka amphamvu ndi acidalilo, ndipo pemphelo limene amapeleka limakhala locokela pansi pamtima. Cikhulupililo canga cimalimba kwambili nikaganizila cikondi cawo, nkhawa imene amanionetsa, ndi cikhulupililo cawo.”

PITILIZANI KUTONTHOZA ENA

17-19. N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kutonthoza ena?

17 Kutalika kwa nthawi imene anthu ofedwa amakhala na cisoni kumasiyana-siyana. Conco, muzilimbikitsa wofedwa osati cabe panthawi ya malilo pamene mabwenzi ndi acibululu ambili alipo, koma ngakhale kwa miyezi ingapo pambuyo pakuti ena abwelela ku zocita zawo za tsiku na tsiku. Baibo imati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Akhristu afunika kupitiliza kutonthoza mnzawo wofedwa mpaka pamene iye adzakwanitsa kupilila payekha.—Ŵelengani 1 Atesalonika 3:7.

18 Kumbukilani kuti pali zinthu zina zimene zingadzutse cisoni ca munthu. Zinthu zimenezi ni monga zocitika zapadela, nyimbo zinazake, masinapu, ngakhale fungo la zinazake, mau, kapena nyengo inayake m’caka. Ngati munthu anafedwa mnzake wam’cikwati, amavutika kwambili na cisoni nthawi yoyamba pamene acita yekha zinthu zimene anazoloŵela kucita ndi mnzakeyo. Zinthu zimenezi ndi monga kupezeka pa misonkhano ikulu-ikulu kapena pa Cikumbutso. M’bale wina anati: “Mkazi wanga atamwalila, n’nadziŵa kuti tsiku lokumbukila cikwati cathu likadzafika nidzavutika kwambili ndi cisoni, ndipo zinalidi zovuta. Koma abale na alongo ena, amene nanzanga anakonza zakuti tidzakhale na maceza n’colinga cakuti patsikulo nisadzakhale nekha.”

19 Komabe, musaiŵale kuti ofedwa amafunika citonthozo nthawi zonse, osati cabe pa nthawi ya zocitika zapadela. Junia anati: “Nthawi zambili, kukhala na maceza ndi kupeleka thandizo kwa munthu pamene kulibe zocitika zapadela kumakhala kothandiza kwambili. Kucita zinthu mwanjila imeneyi n’kopindulitsa ndiponso kumatonthoza kwambili.” N’zoona kuti sitingathetse cisoni conse cimene munthu amakhala naco ngati wokondedwa wake wamwalila. Koma tingathe kum’tonthoza mwa kuyesetsa kumuthandiza m’njila zosiyana-siyana. (1 Yoh. 3:18) Gaby anati: “Niyamikila ngako Yehova cifukwa ca akulu acikondi amene anali nane pa nthawi yonse imene n’nali kuvutika. Ananicititsa kuona kuti Yehova amanikonda.”

20. Kodi malonjezo a Yehova amatitonthoza bwanji?

20 N’zolimbikitsa ngako kudziŵa kuti Yehova, Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, adzathetsa cisoni conse. Adzacita zimenezi pamene “onse ali m’manda acikumbutso adzamva mau ake [a Yesu] ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Mulungu walonjeza kuti “adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.” (Yes. 25:8) Panthawiyo, m’malo ‘molila ndi anthu amene akulila,’ tidzayamba ‘kusangalala ndi anthu amene akusangalala.’—Aroma 12:15.

a Yosefe amachulidwa kotsiliza m’Malemba pamene Yesu anali na zaka 12. Pamene Yesu anacita cozizwitsa cake coyamba, cimene ndi kusandutsa madzi kukhala vinyo, Yosefe sachulidwako. Iye sachulidwakonso ngakhale pa zocitika zina za pambuyo pake. Panthawi imene Yesu anali pamtengo wozunzikilapo, anapatsa mtumwi Yohane udindo wosamalila Mariya. Yosefe akanakhala kuti anali moyo, Yesu sakanacita zimenezi.—Yoh. 19:26, 27.

b Malemba ena amene amatonthoza anthu ambili ndi Salimo 20:1, 2; 31:7; 38:8, 9, 15; 55:22; 121:1, 2; Yesaya 57:15; 66:13; Afilipi 4:13; na 1 Petulo 5:7.

c Onani nkhani yakuti “Muzitonthoza Anthu Amene Aferedwa, Ngati Mmene Yesu Anachitira,” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2010.

Munthu akulemba mau olimbikitsa a m’Baibo pa khadi

“Mau Otsitsimula ndi Otonthoza”

Izi n’zimene ena amalemba potonthoza anzawo ofedwa:

  • “Sitidziŵa cimene tingakambe, koma timakukondani kwambili. Ife sitingadziŵe bwino-bwino mmene mumvelela, koma Yehova adziŵa ndipo adzapitiliza kukulimbikitsani. Tidzapitiliza kukupemphelelani.”

  • “Yehova akulimbitseni panthawi yovuta kwambili imeneyi.”

  • “Dziŵani kuti Mulungu akum’kumbukila wokondedwa wanu. Iye sadzamuiŵala ngakhale pang’ono ndipo adzamuukitsa.”

  • “Mulungu sanaiŵale nchito za cikhulupililo za wokondedwa wanu, ndipo adzamuukitsa m’Paradaiso. Akadzaukitsidwa, sadzakumananso na mdani wotsiliza, imfa.”

  • “Sitingakwanitse kufotokoza mmene cimaŵaŵila ngati munthu amene tinali kum’konda wamwalila. Koma tiyembekezela mwacidwi nthawi pamene Atate wathu wakumwamba adzaukitsa wokondedwa wanu. Panthawiyo, tidzakhala na cisangalalo cosaneneka.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani