N’cifukwa Ciani Tifunika Kutamanda Yehova?
“Tamandani Ya . . . pakuti kuimbila Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino.”—SAL. 147:1.
1-3. (a) Kodi lemba la Salimo 147 liyenela kuti linalembedwa liti? (b) Nanga kuphunzila za lemba limeneli kungatithandize bwanji?
MUNTHU akagwila bwino nchito imene wapatsidwa, kapena akacita zinthu zoonetsa khalidwe linalake losililika, amafunika kutamandidwa. Ngati munthu amatamandidwa, kuli bwanji Yehova Mulungu? Tifunika kumutamanda cifukwa ali na mphamvu zosayelekezeka, zimene zimaonekela m’zinthu zodabwitsa zimene analenga. Afunikanso kutamandidwa cifukwa ca cikondi cake kwa anthu, cimene anacionetsa mwa kutumiza Mwana wake monga nsembe ya dipo.
2 Wolemba Salimo 147 anasonkhezeleka kutamanda Yehova. Kuwonjezela apo, analimbikitsa ena kutamanda Mulungu pamodzi naye.—Ŵelengani Salimo 147:1, 7, 12.
3 Sitidziŵa amene analemba salimo limeneli, koma cioneka kuti iye anakhalako panthawi imene Yehova anabwezeletsa Aisiraeli ku Yerusalemu kucoka ku ukapolo ku Babulo. (Sal. 147:2) Wamasalimoyu ataona kuti anthu a Mulungu abwelela ku malo awo olambilila, analimbikitsidwa kutamanda Yehova. Koma anachulanso zifukwa zina zotamandila Mulungu. N’zifukwa ziti zimene anachula? Nanga imwe muli na zifukwa zanji ‘zotamandila’ Yehova pa umoyo wanu?—Sal. 147:1.
YEHOVA AMACILITSA ANTHU OSWEKA MTIMA
4. Pamene Mfumu Koresi anamasula Aisiraeli mu ukapolo, kodi iwo ayenela kuti anamvela bwanji? Nanga n’cifukwa ciani anamvela conco?
4 Ganizilani mmene Aisiraeli anamvelela pamene anali mu ukapolo ku Babulo. Anthu amene anawagwila ukapolo anali kuwatonza. Anali kuwauza kuti: “Tiimbileni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni.” Panthawiyo, Yerusalemu, amene anali kuwapangitsa kukondwela kwambili mwa Yehova, anali atawonongedwa. (Sal. 137:1-3, 6) Ayuda sanali kufuna kuimba. Iwo anali osweka mtima, ndipo anafunika kutonthozedwa. Koma mogwilizana ndi mau ake aulosi, Mulungu anapulumutsa Aisiraeli kupitila mwa Koresi, mfumu ya Perisiya. Iye anagonjetsa Babulo ndi kupeleka cilengezo cakuti: “Yehova . . . wandituma kuti ndim’mangile nyumba ku Yerusalemu . . . Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikila, Yehova Mulungu wake akhale naye. Conco apite.” (2 Mbiri 36:23) Izi ziyenela kuti zinawalimbikitsa kwambili Aisiraeli amene anali kukhala ku Babulo.
5. Kodi wamasalimo anakamba ciani coonetsa kuti Yehova ali na mphamvu zocilitsa?
5 Yehova sanatonthoze cabe Aisiraeli monga mtundu, koma anatonthozanso Mwiisiraeli aliyense payekha. Ni mmenenso amacitila masiku ano. Ponena za Mulungu, wamasalimo analemba kuti: “Iye amacilitsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Sal. 147:3) Ndithudi, Yehova amasamalila anthu amene akumana ndi mavuto. Amawathandiza mwakuthupi ndi kuwalimbikitsa. Tikakhala na nkhawa, Yehova ni wokonzeka kutitonthoza ndi kutitsitsimula. (Sal. 34:18; Yes. 57:15) Iye amatipatsa nzelu ndi mphamvu zotithandiza kupilila mavuto aliwonse amene tingakumane nawo.—Yak. 1:5.
6. Kodi kuganizila zimene wamasalimo anakamba pa Salimo 147:4 kungatipindulitse bwanji? (Onani pikica kuciyambi.)
6 Pambuyo pake, wamasalimo anayamba kukamba za kumwamba. Iye anakamba kuti Yehova “amawelenga nyenyezi zonse, ndipo zonsezo amazichula mayina ake.” (Sal. 147:4) N’cifukwa ciani iye anayamba kukamba za nyenyezi zakumwamba? Ganizilani izi: Panthawiyo wamasalimo anali kuziona nyenyezi, koma sanali kudziŵa kuti zilipo zingati. Masiku ano, anthu amakwanitsa kuona nyenyezi zambili-mbili kuposa kale. Anthu ena amakamba kuti mumlalang’amba wathu, wochedwa Milky Way, muli nyenyezi mabiliyoni ambili. Ndipo cioneka kuti mumlengalenga muli milalang’amba mathililiyoni ambili. Zoonadi, kwa ise anthu, nyenyezi n’zosaŵelengeka. Koma Mlengi amachula nyenyezi iliyonse ndi dzina lake. Izi zitanthauza kuti Yehova amaona nyenyezi iliyonse kukhala yapadela. (1 Akor. 15:41) Nanga kodi iye amawaona bwanji anthu padziko lapansi? Popeza kuti nthawi zonse Mulungu amatha kudziŵa pamene nyenyezi iliyonse ili, inunso amakudziŵani bwino panokha. Amadziŵa bwino-bwino pamene muli, mmene mumvelela, ndi zimene mufunikila panthawi iliyonse.
7, 8. (a) Kodi Yehova amaganizila ciani populumutsa anthu ake pa mayeselo? (b) Fotokozani citsanzo coonetsa kuti Yehova amacita zinthu mokoma mtima kwambili pothandiza anthu opanda ungwilo.
7 Yehova amakukondani inu panokha, komanso ali na cifundo ndi mphamvu moti angathe kukuthandizani pa mavuto anu. (Ŵelengani Salimo 147:5.) Nthawi zina, mungaone kuti mavuto amene mwakumana nawo ni aakulu kwambili cakuti simungakwanitse kuwapilila. Mulungu amadziŵa kufooka kwathu; “amakumbukila kuti ndife fumbi.” (Sal. 103:14) Cifukwa copanda ungwilo, tingacite colakwa mobweleza-bweleza. Cimatiŵaŵa kwambili tikakamba mau oipa cifukwa cokangiwa kulamulila lilime lathu. Cimatiŵaŵanso tikagonja ku zizoloŵezi zoipa zathupi, kapenanso tikalephela kuthetsa nsanje. Koma Yehova salakwitsa ciliconse. Ngakhale n’conco, iye amatidziŵa bwino ndipo amatimvetsetsa kwambili.—Yes. 40:28.
8 Mwina inu munaonapo mmene Yehova anakupulumutsilani na dzanja lake lamphamvu pamene munakumana ndi ciyeso. (Yes. 41:10, 13) Mwacitsanzo, mlongo Kyoko amene ni mpainiya, zinam’fooketsa kwambili atamusinthila ku gawo lina latsopano. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anali kumvetsetsa mavuto ake? Kumeneko, Kyoko anapeza anthu ambili amene anali kumumvetsetsa ndi kumuganizila. Iye anaona monga kuti Yehova akumuuza kuti: “Nimakukonda, osati cabe cifukwa ndiwe mpainiya, komanso cifukwa ndiwe mwana wanga, ndipo unadzipeleka kwa ine. Nifuna kuti uzisangalala pa umoyo wako cifukwa ndiwe Mboni yanga.” Nanga bwanji imwe? Ni zinthu ziti zimene Wamphamvuyonse wakucitilani zoonetsa kuti “nzelu zake zilibe malile”?
YEHOVA AMATIPATSA ZIMENE TIMAFUNIKILA
9, 10. Kodi thandizo lalikulu limene Yehova amatipatsa ni liti? Fotokozani citsanzo.
9 Nthawi zina, tingasoŵe zinthu zakuthupi zofunikila pa umoyo. Mwacitsanzo, mungakhale na nkhawa kuti mudzasoŵa cakudya. Koma kumbukilani kuti Yehova analenga dziko m’njila yakuti lizikhala ndi cakudya cokwanila, cimene ngakhale ana a makwangwala amalilila. (Ŵelengani Salimo 147:8, 9.) Popeza Yehova amadyetsa ngakhale makwangwala, mufunika kukhala na cikhulupililo cakuti adzakupatsani zofunikila pa moyo wanu.—Sal. 37:25.
10 Cofunika kwambili kuposa zonse n’cakuti Yehova amatisamalila mwauzimu. Amatipatsa ‘mtendele wake umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.’ (Afil. 4:6, 7) Mwacitsanzo, ganizilani za Mutsuo ndi mkazi wake. Iwo anaona kuti Yehova anawathandiza kwambili panthawi ya cigumula ca madzi cochedwa tsunami cimene cinacitika mu 2011 ku Japan. Panthawiyo, iwo anacita kukwela kumtenje kuti apulumuke cigumulaco. Ngakhale n’conco, zinthu zonse zimene anali nazo zinawonongeka. Iwo anakhala mumdima usiku wonse m’cipinda capamwamba ca nyumba yawo, imene inali itagumuka-gumuka. M’cipindaco munalinso mozizila. Kutaca, anayamba kusakila zofalitsa zimene zikanawalimbikitsa mwauzimu. Iwo anangopezako Buku Lapacaka la 2006. Mutsuo anacita cidwi ngako atangoona mutu wina m’bukulo wakuti “Zigumula za Madzi Zoopsa Kwambili Zimene Zinacitikapo.” Nkhaniyo inali kukamba za civomezi capamadzi cimene cinacitika ku Sumatra mu 2004, cimene cinalengetsa zigumula zamadzi zoopsa m’mbili yonse ya anthu. Mutsuo na mkazi wake anali kulila pamene anali kuŵelenga nkhaniyo. Iwo anaona kuti Mulungu anawasamalila mwacikondi mwa kuwapatsa cilimbikitso cauzimu pa nthawi yake. Yehova anawasamalilanso mwakuthupi. Abale awo auzimu anawapatsa zakudya na zovala. Koma cimene cinawalimbikitsa kwambili n’cakuti abale oimilako gulu la Mulungu anabwela kudzayendela mpingo wawo. Mutsuo anati: “N’naona kuti Yehova anali pafupi na aliyense wa ife ndi kuti anali kutisamalila. Tinalimbikitsidwa ngako!” Izi zionetsa kuti njila yaikulu imene Mulungu amatithandizila ndi kutipatsa zosoŵa zauzimu, koma amatipatsanso zosoŵa zakuthupi.
MMENE TIMAPINDULILA NA MPHAMVU ZOPULUMUTSA ZA MULUNGU
11. Kodi tifunika kucita ciani kuti Mulungu azitithandiza?
11 Nthawi zonse, Yehova amakhala wokonzeka ‘kuthandiza anthu ofatsa.’ (Sal. 147:6a) Koma kodi tingacite ciani kuti iye azitithandiza? Tifunika kukhala naye pa ubale wolimba. Kuti izi zitheke, tifunika kukhala ofatsa. (Zef. 2:3) Anthu ofatsa amayembekezela Mulungu kuti ndiye adzathetsa zinthu zonse zoipa zimene zicitika ndi mavuto amene akumana nawo. Anthu aconco, Yehova amawakonda kwambili.
12, 13. (a) Kodi tifunika kupewa ciani kuti Mulungu azitithandiza? (b) Ni anthu ati amene Yehova amakondwela nawo?
12 Mosiyana ndi ofatsa, “anthu oipa [Mulungu] amawagwetsela pansi.” (Sal. 147:6b) Mau amenewa ni amphamvu kwambili. Conco, kuti tipindule ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova ndi kupewa mkwiyo wake, tifunika kudana ndi zimene iye amadana nazo. (Sal. 97:10) Mwacitsanzo, tifunika kudana ndi ciwelewele. Izi zitanthauza kuti tifunika kupewelatu ciliconse cimene cingatigwetsele m’chimo limeneli, monga kuonelela zamalisece. (Sal. 119:37; Mat. 5:28) Kupewa kucita zimenezi kungakhale kovuta. Koma tifunika kuyesetsabe kuti Yehova atidalitse.
13 Kuti tipambane pa nkhondo yathu yauzimu, sitifunika kudzidalila, koma tifunika kudalila Yehova. Iye sangakondwele ngati tiyesa kudzipulumutsa tekha ndi “mphamvu za hatchi,” kapena kuti kudalila zinthu zimene anthu a m’dzikoli amadalila. Sitifunikanso kudalila “liwilo la miyendo ya munthu.” Izi zitanthauza kuti sitifunika kudzidalila kapena kudalila anthu ena kuti atipulumutse. (Sal. 147:10) M’malomwake, tifunika kucondelela Yehova kupitila m’pemphelo kuti atithandize. Mosiyana ndi alangizi a anthu, iye salema na kumvetsela mapemphelo athu, ngakhale titamupempha mobweleza-bweleza kuti atithandize. Malemba amati: “Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa, amene amayembekezela kukoma mtima kwake kosatha.” (Sal. 147:11) Conco, tifunika kukhala na cidalilo cakuti cifukwa ca kukoma mtima kwake kosatha, iye sadzatitaya ndipo adzatithandiza kugonjetsa zilakolako zoipa.
14. Kodi wamasalimo anali kukhulupilila ciani cimene cinamulimbikitsa?
14 Yehova amatitsimikizila kuti adzatithandiza pa nthawi imene takumana ndi mavuto. Pokamba za kubwezeletsa Yerusalemu, wamasalimo anaimba nyimbo yotamanda Yehova. Iye anati: “Walimbitsa mipilingidzo ya zipata zako. Wadalitsa ana ako amene ali mwa iwe. Iye akukhazikitsa mtendele m’dziko lako.” (Sal. 147:13, 14) Wamasalimoyu ayenela kuti analimbikitsidwa ngako pamene anadziŵa kuti Mulungu adzalimbitsa zipata za mzinda wa Yerusalemu kuti ateteze olambila ake.
Kodi Mau a Mulungu angatithandize bwanji ngati tili na nkhawa kwambili cifukwa ca mavuto? (Onani palagilafu 15-17)
15-17. (a) Kodi nthawi zina tingamvele bwanji cifukwa ca mavuto amene timakumana nawo? Nanga Yehova amatithandiza bwanji na Mau ake? (b) Fotokozani citsanzo coonetsa kuti ‘mau a Mulugnu amathamanga kwambili.’
15 Nthawi zina, mungakumane ndi mavuto amene angacititse kuti mukhale na nkhawa kwambili. Koma Yehova angakupatseni nzelu kuti muthe kupilila. Wamasalimo anakamba kuti Mulungu “amatumiza mau ake padziko lapansi, ndipo mau akewo amathamanga kwambili.” Anakambanso kuti Yehova ‘amapeleka cipale cofewa, amamwaza mame oundana, ndi kuponya pansi madzi oundana.’ Ndiyeno, anafunsa kuti: “Ndani angaime m’cisanu cake?” Iye anapitiliza kuti, Yehova “amatumiza mau ake ndi kusungunula madzi oundanawo.” (Sal. 147:15-18) Inde, Mulungu wathu wanzelu zopanda malile ndi wamphamvuyonse, amene amalamulila “cipale cofewa” ndi “madzi oundana” kapena kuti matalala, angatithandize kupilila mavuto aliwonse amene tingakumane nawo.
16 Masiku ano, Yehova amatitsogolela kupitila m’Mau ake, Baibo. Ndipo “mau akewo amathamanga kwambili” m’lingalilo lakuti nthawi zonse Mulungu amatipatsa mwamsanga malangizo amene timafunikila. Ganizilani mmene timapindulila cifukwa ca kuŵelenga Baibo, kuphunzila zofalitsa za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” kutamba TV yathu yochedwa JW Broadcasting, ndi kuyanjana ndi Akhristu anzathu. Timapindulanso kwambili na webusaiti yathu ya jw.org, komanso malangizo amene akulu amatipatsa. (Mat. 24:45) Kodi inu panokha mwaona kuti Yehova amakupatsani malangizo mwamsanga?
17 Simone anadzionela yekha kuti Mau a Mulungu ni amphamvu. Iye anali kudziona ngati wosafunika, moti nthawi zina anali kuona kuti Mulungu sangamukonde. Koma akakhala na nkhawa kwambili, anali kupemphela kaŵili-kaŵili, kupempha Yehova kuti amuthandize. Analinso kuphunzila Baibo payekha mwakhama. Iye anati: “Nimaona kuti Yehova amanipatsa mphamvu na kunitsogolela nthawi zonse.” Zimenezi zamuthandiza kuti asamadzione ngati wosafunika.
18. N’cifukwa ciani mumaona kuti Mulungu amakukondani? Ni zifukwa ziti zimene inu muli nazo zofuulila kuti “Tamandani Ya”?
18 Wamasalimo anadziŵa kuti Mulungu anali kuwakonda anthu ake a m’nthawi yakale. Iwo anali mtundu wokhawo umene Mulungu anaupatsa ‘mau ake, malangizo ake ndi zigamulo zake.’ (Ŵelengani Salimo 147:19, 20.) Ifenso ndife odala masiku ano cifukwa ndise cabe amene timadziŵika na dzina la Mulungu. Tili pa ubale wabwino na Yehova cifukwa tinamudziŵa ndipo timatsatila Mau ake pa umoyo wathu. Molingana ndi wolemba Salimo 147, kodi si zoona kuti tili na zifukwa zambili zofuulila kuti “Tamandani Ya!” ndi kulimbikitsakonso ena kucita zimenezi?