LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp19 na. 2 tsa. 3
  • Pamene Umoyo Wafika Posapililika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pamene Umoyo Wafika Posapililika
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Umoyo Ukafika Poti Simungathenso Kupilila
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Munthu Wokondedwa Akamwalila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Tsoka Likagwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Inde, Moyo Ukali na Phindu kwa Imwe!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
wp19 na. 2 tsa. 3
Alila kunchito

Pamene Umoyo Wafika Posapililika

UMOYO umakhala wokondweletsa kwambili ngati zonse ziyenda bwino. Nanga bwanji ngati umoyo wafika posapililika?

Mwacitsanzo, Sallya wa ku America, katundu wake wambili unawongedwa na cimphepo ca camkuntho cochedwa hurricane. Iye anafotokoza kuti: “N’nali kuona kuti siningakwanitse kupilila vuto limeneli.”

Nanga bwanji munthu amene mumam’konda akamwalila? Janice wa ku Australia anakamba kuti: “Ana anga aŵili aamuna atamwalila, ninamva kupweteka kwambili mumtima. N’nalibe na mphamvu ndipo n’nathedwa nzelu. N’nacondelela Mulungu kuti: ‘Conde, siningakwanitse kupilila, vuto ili lanikulila msinkhu! Lekani kuti nife cabe. Sinifuna kuti maŵa nikakhalenso na moyo.’”

Koma kwa Daniel, cinamuŵaŵa kwambili atadziŵa kuti mkazi wake sanali kuyenda bwino. Iye anati: “Pamene mkazi wanga anaulula kuti anali kucita zaciwelewele, zinali monga kuti wanilasa na mpeni kumtima. Ndipo kwa miyezi ingapo, nthawi zambili n’nali kumva kupweteka kumeneku.”

Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda idzafotokoza mmene moyo ungakhalile waphindu ngakhale pamene

  • Tsoka lakugwelani

  • Munthu amene mumam’konda akamwalila

  • Mnzanu wa m’cikwati sayenda bwino

  • Mwadwala matenda aakulu

  • Mwafika pakuti simufunanso kukhala na moyo

Koma coyamba, kodi tingapilile motani tsoka likatigwela?

a Maina ena m’nkhanizi asinthidwa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani