LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp19 na. 2 masa. 4-5
  • Tsoka Likagwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tsoka Likagwa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUDZIŴA COONADI CA M’BAIBO KUMAPANGITSA MOYO KUKHALA WAPHINDU
  • Kodi Ndimwe Wokonzeka?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Tulilani Yehova Nkhawa Zanu Zonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Mmene Tingathanilane Nazo Nkhawa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Thandizani Ena Kupilila pa Nthawi Zovuta
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
wp19 na. 2 masa. 4-5
Anthu aŵili ali pakati panyumba imene yawonongedwa

Tsoka Likagwa

Andrew wa ku Sierra Leone anati: “Nzelu zinathelatu. Kuundumuka kwa nthaka kucokela m’phili, na kusefukila kwa madzi kunawononga katundu wathu wonse.”

David wa ku Virgin Islands anati: “Cimphepo camkuntho citapita tinabwelela kunyumba. Koma sitinapeze ciliconse, moti tinalibiletu n’cokamba. Mwana wanga wamkazi anangogwada pansi n’kuyamba kulila.”

NGATI tsoka linakugwelamponi, ndiye kuti mungamvetse mmene ena anamvelela tsoka litaŵagwela. Iwo amakhala odabwa kwambili, sakhulupilila, amavutika maganizo, nkhawa, komanso kucita mantha. Ambili amene anapulumuka tsoka, amavutika maganizo komanso kulefuka. Ndipo amakhala alibe cifuno copitiliza kukhala na moyo.

Ngati zinthu zanu zonse zinawonongeka pa tsoka, mwina mungaone kuti umoyo wafika posapililika. Mungayambe kuona kuti moyo wanu ulibe phindu. Komabe, Baibo imafotokoza kuti moyo wanu ni wofunika, ndipo mungakhale na zifukwa zabwino zoyembekezela tsogolo labwino.

KUDZIŴA COONADI CA M’BAIBO KUMAPANGITSA MOYO KUKHALA WAPHINDU

Mlaliki 7:8 imati: “Mapeto a cinthu amakhala bwino kuposa ciyambi cake.” Tsoka likangocitika kumene, zingaoneke monga kuti umoyo wanu sudzakhalanso bwino. Koma mukalimbikila kukonzanso zinthu pang’ono-pang’ono, umoyo wanu udzakhalanso bwino.

Baibo imakambilatu za nthawi pamene ‘sikudzamvekanso kulila kokweza mawu kapena kulila kwacisoni.’ (Yesaya 65:19) Izi zidzacitika dziko lapansi likadzakonzedwa kukhala paradaiso mu Ufumu wa Mulungu. (Salimo 37:11, 29) Masoka adzakhala zinthu zakale. Zinthu zonse zotivutitsa maganizo, komanso zotibweletsela cisoni zidzafafanizika m’maganizo mwathu kwamuyaya. Izi zidzacitikadi, cifukwa Mulungu Wamphamvuzonse anatilonjeza kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso ndipo sizidzabwelanso mumtima.”—Yesaya 65:17.

Tangoganizilani cabe, Mlengi wathu wakonza zakuti ‘mukhale ndi ciyembekezo, komanso tsogolo labwino.’ Ndithudi, udzakhala umoyo wabwino kwambili mu ulamulilo wangwilo wa Mulungu. (Yeremiya 29:11) Kodi kudziŵa zimenezi kungakuthandizeni kuona moyo wanu kukhala wofunika? Sally, amene tam’chula m’nkhani yoyamba, anati: “Kuganizila zinthu zosangalatsa zimene Ufumu wa Mulungu udzaticitila kutsogolo, kungakuthandizeni kuiŵala mavuto akumbuyo, na kupilila amene mukukumana nawo pali pano.”

Kodi na imwe simungakonde kuphunzila zambili zimene Ufumu wa Mulungu udzacitila anthu posacedwa? Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuona kuti, mosasamala kanthu za tsoka limene linakucitikilani, moyo wanu ni wofunika ngakhale pali pano, pamene mukuyembekezela mwacidwi tsogolo lopanda tsoka lililonse. Ndipo Baibo ili na malangizo amene angakuthandizeni kupilila zovuta zimene tsoka linakubweletselani. Onani zitsanzo zocepa cabe pa peji yotsatila.

Mavesi a m’Baibo Amene Angakuthandizeni

Muzigona mokwanila.

“Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.

Akatswili amati tsoka likacitika, “munthu amalephela kugona bwino. . . Izi zimawonjezela vuto la kupsinjika maganizo.” Conco, n’cinthu canzelu kuti muzigona mokwanila.

Uzankoni ena mmene mumvelela.

“Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauwelamitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa”—Miyambo 12:25.

Mungauzeko wa m’banja mwanu mmene mumvelela, kapena mnzanu wodalilika. Iwo adzakumvetselani mokoma mtima. Komanso adzakulimbikitsani na kukupatsani thandizo lofunikila.a

Ganizilani za madalitso akutsogolo.

“Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezela mogwilizana ndi lonjezo lake [Mulungu], ndipo mmenemo mudzakhala cilungamo.”—2 Petulo 3:13.

a Munthu amene wavutika maganizo, kapena kukhala na nkhawa kwa nthawi yaitali, angafunikile kukaonana na dokotala.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani