Ndandanda ya Mlungu wa April 22
MLUNGU WA APRIL 22
Nyimbo 85 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 22 ndime 1 mpaka 6 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Luka 18-21 (Mph. 10)
Na. 1: Luka 18:18-34 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Zidzathekadi Kuti Anthu a Mitundu Yonse Adzagwilizane Monga Abale ndi Alongo?—rs tsa. 238 ndime 1-tsa. 239 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Kufatsa N’kutani, N’cifukwa Ciani Khalidwe Limeneli Lili Lofunika Ndipo Tingatani Kuti Tikhale Nalo?—Zef. 2:2, 3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 120
Mph. 10: “Zimene Mungacite kuti Lipoti Likhale Lolondola.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu yocokela m’buku la Gulu, patsamba 85 ndime 1 mpaka 87 ndime 1. Mukambe nkhaniyi malinga ndi zosoŵa za mpingo, ndipo unikani kufunika kopeleka lipoti lolondola. Yamikilani abale kaamba ka khama lao muulaliki.
Mph. 20: Gwilitsilani Nchito Baibo Mwaluso Muulaliki. Nkhani yokambilana yocokela mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2010, masamba 13 ndi 14 ndime 14 mpaka 17. Pokambilana ndime 15, mukhale ndi citsanzo coonetsa wofalitsa akugwilitsila nchito Baibo mwaluso muulaliki.
Nyimbo 121 ndi Pemphelo