Ndandanda ya Mlungu wa May 13
MLUNGU WA MAY 13
Nyimbo 4 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 23 ndime 1-8 ndi bokosi patsamba 180 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Yohane 5–7 (Mph. 10)
Na. 1: Yohane 6:22-40 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi N’cifukwa Ciani Zinali Zoyenela Kuti Dipo Lipelekedwe M’njila Imene Linapelekedwela?—rs tsa. 122 ndime 6–tsa. 123 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingatsatile Bwanji Mfundo Yopezeka pa Numeri 15:37-40? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 126
Mph. 10: Zogaŵila za mu May ndi June. Nkhani. Mwacidule fotokozani cifukwa cake tumapepala tumenetu tudzakopa cidwi ca anthu a m’gawo lanu. Citani citsanzo cosonyeza mmene mungagaŵile kapepala kamodzi kapena tuŵili pocita ulaliki wa nyumba ndi nyumba.
Mph. 10: Tiphunzilapo Ciani? Kukambilana. Ŵelengani Mateyu 5:11, 12 ndi Mateyu 11:16-19 ndipo kambilanani mmene malembawa angatithandizile mu utumiki.
Mph. 10: “N’ciani Cimatisonkhezela Kulalikila?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 91 ndi Pemphelo