LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 5/13 tsa. 1
  • N’ciani Cimatisonkhezela Kulalikila?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’ciani Cimatisonkhezela Kulalikila?
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • “Uzikonda Mnzako Mmene Umadzikondela Wekha”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kodi ‘Mumakonda Anzanu Mmene Mumadzikondela’?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • “Uzikonda Yehova Mulungu Wako”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • “Mulungu Ndiye Chikondi”
    Imbirani Yehova
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 5/13 tsa. 1

N’ciani Cimatisonkhezela Kulalikila?

1. Kodi cikondi cimagwilizana motani ndi ulaliki wathu?

1 Nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiyo yofunika kwambili imene tingacite masiku ano. Ndithudi, tikamacita nchito imeneyi, timaonetsa kuti timamvela malamulo aŵili aakulu, akuti, tizikonda Yehova ndi anzathu. (Maliko 12:29-31) Cikondi cimatilimbikitsa kuti tikhale atumiki acangu.—1 Yoh. 5:3.

2. Kodi nchito yathu yolalikila imaonetsa bwanji kuti timakonda Yehova?

2 Kukonda Yehova: Kukonda kwathu bwenzi lathu lapamtima, Yehova, kumatilimbikitsa kuti tiziuzako ena za iye. Iye wakhala akunyozedwa ndi Satana kwa zaka pafupi-fupi 6,000. (2 Akor. 4:3, 4) Cifukwa ca zimenezi, anthu amakhulupilila kuti Mulungu amazunza anthu ocimwa m’moto wa helo, ndi kuti iye ndi Utatu, komanso kuti samasamalila anthu. Kaamba ka zimenezi ambili amaganiza kuti kulibe Mulungu. Ndithudi, timafunitsitsa kwambili kuti anthu adziŵe coonadi ponena za Atate wathu wa kumwamba. Mulungu amasangalala kwambili tikamacitila umboni mwakhama, koma Satana amakhumudwa nazo.—Miy. 27:11; Aheb. 13:15, 16.

3. Kodi ulaliki wathu umasonyeza bwanji kuti timakonda anzathu?

3 Kukonda Anzathu: Nthawi iliyonse tikalalikila munthu, timaonetsa kuti timam’konda. Masiku ano ovuta, anthu afunikila kuti amve uthenga wabwino. Ambili ndi ofanana ndi anthu a ku Nineve m’nthawi ya Yona amene sanali ‘kudziŵa kusiyanitsa dzanja lao lamanja ndi lamanzele.’ (Yona 4:11) Ulaliki wathu umathandiza anthu kuti akhale ndi umoyo wabwino ndi wosangalatsa. (Yes. 48:17-19) Ndipo umawapatsa ciyembekezo. (Aroma 15:4) Iwo “adzapulumuka” ngati amamvela ndi kucita zimene amaphunzila.—Aroma 10:13, 14.

4. Kodi Yehova sadzaiŵala ciani?

4 Ana abwino amaonetsa kuti amakonda makolo ao nthawi zonse osati kokha panyengo zina. Mofananamo, cikondi cathu cacikulu pa Mulungu ndi anzathu cidzatithandiza kulalikila nthawi zonse osati kokha panthawi imene timapita mu utumiki. (Mac. 5:42) Ndithudi, Yehova sadzaiŵala cikondi cathu cimeneci.—Aheb. 6:10.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani