Ndandanda ya Mlungu wa May 20
MLUNGU WA MAY 20
Nyimbo 70 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 23 ndime 9-15 ndi mabokosi pa masamba 184 ndi 186 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Yohane 8–11 (Mph. 10)
Na. 1: Yohane 8:12-30 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Tingatani Kuti Tisanyengedwe Ndi Anthu Ophunzitsa Zonama?—Aroma 16:17; 2 Yoh. 9-11 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi N’cifukwa Ciani Mulungu Sanangolamula Kuti Onse Amene Azimumvela Adzakhala ndi Moyo Kosatha?—rs tsa. 123 ndime 2-tsa. 124 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 96
Mph. 10: Njila Zoonjezela Utumiki Wanu—Gawo 3. Nkhani yokambilana yocokela m’buku la Gulu, tsamba 116, ndime 1, mpaka tsamba 117, ndime 1. Mwacidule funsani wofalitsa amene athandizila kagulu komanga manyumba a Ufumu. Kodi wapindula bwanji ndi mwai wa utumiki umenewu? Fotokozani kuti abale ndi alongo amene amaitanidwa kuti athandizile nchito yomanga imeneyi, ayenela kukhala obatizika komanso ovomelezedwa ndi bungwe la akulu. Angakhale ndi luso kapena sangakhale nalo. Aja amene afuna kukagwila nchito imeneyi ayenela kusaina fomu ya Kingdom Hall Volunteer Worker Questionnaire kucokela kwa akulu a pampingo.
Mph. 10: Yehova Amatithandiza kuti Tikwanilitse Utumiki Wathu. (Eks. 4:10-12; Afil. 4:13) Kukambitsilana kocokela mu Yearbook ya 2013, tsamba 101, ndime 3, ndi tsamba 111, ndime 3 mpaka tsamba 112 ndime 2. Funsani omvela kuti afotokoze mmene apindulila ndi nkhani za mu Yearbook.
Mph. 10: “Ndani Angacite Nazo Cidwi Izi?” Mafunso ndi mayankho. Pemphani gulu kuti lichule malo a zamalonda ndi mabungwe aboma amene apezeka m’gawo la mpingo amene angacite cidwi maka-maka pankhani inayake yopezeka m’magazini athu.
Nyimbo 92 ndi Pemphelo