Ndandanda ya Mlungu wa June 24
MLUNGU WA JUNE 24
Nyimbo 123 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 25 ndime 1 mpaka 7, bokosi pa tsamba 199 ndi 200 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Machitidwe 8 mpaka 10 (Mph. 10)
Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 93
Mph. 10: “Kambilanani Nkhani Imodzi, koma Gaŵilani Magazini Onse Aŵili.” Nkhani. Pambuyo pankhani, onetsani mmene mungayambitsile phunzilo pa Ciŵelu coyamba mu July, mwa kugwilitsila nchito ulaliki wacitsanzo amene ali patsamba 4.
Mph. 10: Nchito Yathu Sidzapita Pacabe. (Aheb. 6:10) Nkhani yokambilana yocokela mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2012, masamba 8-9. Pemphani omvela kuti akambepo zimene aphunzila.
Mph. 10: Zogaŵila za mu July ndi August. Nkhani. Mwacidule kambilanani nkhani zimene zipezeka m’kabuku kamene mudzagaŵila. Citani citsanzo coonetsa mmene mungagaŵilile tumabuku tuŵili. Citsanzo cimodzi cikhale ca mmene mungagaŵilile kabuku ka Uthenga Wabwino, mwa kugwilitsila nchito maulaliki acitsanzo ali patsamba 4 kapena opezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2013.
Nyimbo 129 ndi Pemphelo