Kodi Ndinu Wokonzeka Kusintha?
1. Pamene dzikoli lisintha, kodi ndi kusintha kotani kumene tiyenela kupanga?
1 Pa lemba la 1 Akorinto 7:31, Baibo imayelekezela dziko ndi bwalo locitilapo seŵelo, limene anthu a m’seŵelo amasintha-sintha. Pamene dzikoli lisintha ifenso tifunika nthawi ndi nthawi kusintha njila zimene timagwilitsila nchito polalikila, ndandanda yathu ndi mmene timalalikilila. Kodi ndinu wokonzeka kusintha?
2. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala okonzeka kusintha kuti tiyendele pamodzi ndi gulu la Yehova?
2 Njila Zogwilitsila Nchito Polalikila: Mpingo Wacikristu wakhala ukusintha nthawi zonse. Pamene Yesu anatumiza ophunzila ake nthawi yoyamba, anawauza kuti asatenge thumba la cakudya kapena zikwama zao za ndalama. (Mat. 10:9, 10) Koma pambuyo pake anasintha malangizo awa pofuna kukonzekeletsa ophunzila ake kaamba ka mavuto amene anadzakumana nao mtsogolo, komanso kukula kwa nchito yolalikila kumene kunafika m’madela ena. (Luka 22:36) Kwa zaka zoposa 100, gulu la Yehova lagwilitsila nchito njila zosiyana-siyana polalikila. Mwacitsanzo lagwilitsila nchito zinthu monga, makadi aumboni, kuulutsa mau pawailesi ndi galimoto zokhala ndi zokuzila mau malinga ndi mmene zinalili zofunikila panthawiyo. Masiku ano, popeza kuti anthu m’madela ambili sapezeka panyumba, takhala tikulimbikitsidwa kwambili kulalikila kumene kumapezeka anthu kapena kucita ulaliki wamwai m’malo molalikila nyumba ndi nyumba. Takhala tikulimbikitsidwanso kucita ulaliki wa kunyumba ndi nyumba kumadzulo ngati nthawi ya masana anthu amakhala kunchito. Pamene galeta lakumwamba la Yehova likusintha njila yake, kodi inu mumayendela nalo pamodzi?—Ezek. 1:20, 21.
3. Kodi kukhala wokonzeka kusintha muulaliki kumatithandiza bwanji kukhala wogwila mtima m’gawo lathu?
3 Ulaliki Wanu: Kodi anthu a m’gawo lanu akuda nkhawa ndi ciani? Kodi akuda nkhawa ndi ndalama, banja, kapena nkhondo? N’kofunika kuti tizidziŵa mavuto ndi mikhalidwe imene yafala m’gawo lathu kuti tizikonzekela ulaliki umene uli woyenelela. (1 Akor. 9:20-23) Pamene anthu atiuza nkhawa zao, sitiyenela kuyankha mwamwambo ndi kupitiliza kukamba ulaliki umene takonzekela. Koma kungakhale bwino kusintha ulaliki wathu mogwilizana ndi nkhawa zao.
4. N’cifukwa ciani tiyenela kusintha mwamsanga?
4 Posacedwapa “zocitika” za padzikoli zidzatha, ndipo cisautso cacikulu cidzayamba. Komanso “nthawi yotsalayi yafupika.” (1 Akor. 7:29) Conco, n’kofunika kwambili kuti tizisintha mwamsanga, n’colinga cakuti ticite zambili m’nthawi yocepa yotsalayi!