Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuonetsa Anthu Cidwi
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Yesu anali kuganizila munthu aliyense payekha ndipo anali kuonetsa cikondi anthuwo. Mwacitsanzo, pa cocitika cina iye anazindikila kuti munthu amene anali wogontha akanacita manyazi kumucilitsila pa gulu la anthu. Conco pomucilitsa, iye anatenga munthuyo n’kucoka naye pa khamu la anthu ndi kupita naye pambali. (Maliko 7:31-35) Yesu anaganizilanso ophunzila ake mwa kupewa kuwaphunzitsa zinthu zambili pa nthawi imodzi, podziŵa kuti sakanazimvetsa. (Yoh. 16:12) Yesu amaonetsabe anthu cidwi ngakhale pamene ali pa udindo wake kumwamba. (2 Tim. 4:17) Monga otsatila a Kristu, tifunika kutengela citsanzo cake. (1 Pet. 2:21; 1 Yoh. 3:16, 18) Kuonjezela apo, ulaliki wathu ungakhale wogwila mtima ngati tionetsa cidwi mwininyumba mwa kuyesetsa kudziŵa mmene zinthu zilili kwa iye, zimene amakonda ndiponso zimene zimamudetsa nkhawa. Iye akazindikila kuti tikucita zinthu momuganizila, angamvetsele zimene tikulankhula naye. Koma tikamacita ngati tabwela kudzamuuza cabe uthenga kapena kumusiila cofalitsa, munthuyo sangamvetsele.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Yesezani kucita izi pa nthawi ya kulambila kwa pabanja. Mungacite citsanzo ca mmene wofalitsa angasinthile ulaliki kuti ugwilizane ndi zimene mwininyumba wanena.
Pa misonkhano ina yokonzekela ulaliki wakumunda, m’bale amene akutsogolela angakambe njila za mmene tingaonetsele ena cidwi.