Ndandanda ya Mlungu wa August 12
MLUNGU WA AUGUST 12
Nyimbo 112 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 27 ndime 10 mpaka 18 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Aroma 5 mpaka 8 (Mph. 10)
Na. 1: Aroma 6:21–7:12 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: N’cifukwa Ciani Akristu ena Amapita Kumwamba Kukakhala Ndi Kristu?—rs tsa. 217 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa Ciani Kukonda Kwambili Zinthu Zakuthupi Kuposa Zinthu Zauzimu Kumabweletsa Mavuto?—Mat. 6:33; 1 Tim. 6:10 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 37
Mph. 10: “Mau a Mulungu ndi Opindulitsa pa Kuphunzitsa.” Mafunso ndi mayankho. Muchule deti la msonkhano wa dela ngati likudziŵika.
Mph. 10: Kodi Autilaini Ingatithandize Bwanji mu Utumiki. Nkhani yokambilana yocokela m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 167, ndime 1, mpaka tsamba 168, ndime 1. Pogwilitsila nchito cofalitsa cimene tidzagaŵila mweziwo, mukhale ndi citsanzo ca wofalitsa akamba yekha asanapite mu utumiki, akuyesa kukumbukila mfundo zazikulu za autilaini yake imene anakonzekela ya mu utumiki.
Mph. 10: Tiphunzilapo Ciani? Ŵelengani Machitidwe 8:26-31 ndipo kambilanani mmene lembali lingatithandizile mu utumiki.
Nyimbo 61 ndi Pemphelo