Mau a Mulungu ndi Opindulitsa pa Kuphunzitsa
1. Kodi mutu wa msonkhano wa dela wa caka cautumiki ca 2014 ndi wotani? Ndipo ndi funso liti limene lidzayankhidwa pa msonkhano?
1 ‘Mlangizi wathu Wamkulu,’ Yehova, ndiye mphunzitsi wabwino kwambili kuposa wina aliyense. (Yes. 30:20, 21) Koma kodi Yehova amatilangiza bwanji? Iye watipatsa buku lofunika kwambili limene ndi Mau ake ouzilidwa, Baibo. Kodi ziphunzitso za Mulungu zingatithandize bwanji ku thupi, m’maganizo, ndi kuuzimu? Yankho la funso limeneli lidzayankhidwa pa msonkhano wa dela wa caka cautumiki ca 2014. Mutu wa msonkhano ndi wakuti “Mau a Mulungu ndi Opindulitsa pa Kuphunzitsa,” wacokela pa lemba la 2 Timoteyo 3:16.
2. Kodi mfundo zazikulu zidzaonekela pa mayankho a mafunso ati?
2 Pezani Mfundo Zazikulu Izi: Mayankho a mafunso otsatilawa adzaonetsa mfundo zazikulu za msonkhano:
• Kodi ziphunzitso za Mulungu zimakhudza bwanji umoyo wathu? (Yes. 48:17, 18)
• Ngati tifuna kusintha zinthu paumoyo wathu kuti titumikile Yehova mu utumiki wa nthawi zonse, kodi tingakhale otsimikiza mtima kuti tidzapeza ciani? (Mal. 3:10)
• Kodi tiyenela kucita bwanji tikapeza ‘ziphunzitso zacilendo’? (Aheb. 13:9)
• Kodi tingatsanzile bwanji “kaphunzitsidwe” ka Yesu? (Mat. 7:28, 29)
• N’cifukwa ciani aphunzitsi a mumpingo ayenela kuziphunzitsa okha? (Aroma 2:21)
• Kodi Mau a Mulungu ndi opindulitsa pa ciani? (2 Tim. 3:16)
• Kodi anthu amakhudzidwa bwanji ndi ‘kugwedezeka’ kwa amitundu? (Hag. 2:6, 7)
• Kodi Yehova ndi wotsimikiza mtima za ciani ponena za ife? (Aef. 5:1)
• N’cifukwa ciani tiyenela kucita khama kuti tikhale m’ziphunzitso za Yehova? (Luka 13:24)
3. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti tikapezeke ndi kumvetsela mwachelu pulogalamu ya panthawi yake imeneyi?
3 Kumayambililo kwa 2 Timoteyo caputala 3, Paulo asanalembe mau pamene pacokela mutu wa msonkhano, iye anachula za nthawi zovuta zimene zidzakhalako m’masiku otsiliza. Analemba kuti: “Anthu oipa ndi onyenga adzaipila-ipilabe. Iwo azidzasoceletsa ena ndiponso azidzasoceletsedwa.” (2 Tim. 3:13) Kuti tisasoceletsedwe, n’kofunika kwambili kuti tizimvetsela ndi kugwilitsila nchito ziphunzitso za Mulungu. Conco, tiyeni tonse tikapezeke ndi kumvetsela mwachelu pulogalamu ya panthawi yake imeneyi.