Ndandanda ya Mlungu wa August 19
MLUNGU WA AUGUST 19
Nyimbo 51 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 27 ndime 19 mpaka 26 ndi mabokosi pa tsamba 212, 214, ndi 217 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Aroma 9 mpaka 12 (Mph. 10)
Na. 1: Aroma 9:19 mpaka 33 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Ngati Wina Wanena Kuti, ‘Kodi Mumakhulupilila Kuti Akristu Okhulupilika Adzatengedwa Ndi Matupi ao N’kukakumana Ndi Ambuye M’mlengalenga?’—rs tsa. 217 ndime 5-tsa. 218 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibo Limapeleka Zifukwa Ziti Zimene Sitiyenela Kuopa Anthu?—Luka 12:4-12 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 113
Mph. 10: “Mau a Mulungu ndi Amphamvu.” Mafunso ndi mayankho. Chulani deti la msonkhano wa tsiku limodzi ngati ndi lodziŵika.
Mph. 10: Mmene Tingayankhile Anthu Amene Sakufuna Kumvetsela. Nkhani yokambilana. Yokambidwa ndi woyang’anila nchito. Chulani zinthu ziŵili kapena zitatu zimene mumakumana nazo mu gawo lanu za anthu amene safuna kumvetsela koma sizipezeka m’buku la Kukambitsilana. Pemphani omvela kuti ayankhe mmene angacitile. Citani citsanzo cimodzi mwacidule.
Mph. 10: Lalikilani Molimba Mtima. (Machitidwe 4:29) Nkhani yokambilana yocokela m’buku Lapacaka, tsamba 49, ndime 1 mpaka 6, ndi tsamba 69, ndime 1 mpaka 6. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene aphunzila.
Nyimbo 92 ndi Pemphelo