Tidzagaŵila Kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38 mu November
1. Kodi ndi mafunso ati amene anthu amafunsa ponena za akufa? Nanga mafunso amenewa adzayankhidwa bwanji mu November?
1 Imfa ndi mdani wa anthu onse, mosasamala kanthu za zimene amakhulupilila. (1 Akor. 15:26) Ambili amafuna kudziŵa kumene akufa ali ndipo ngati adzawaonanso. Conco, kwa mwezi wathunthu mipingo yonse padziko lapansi idzagaŵila kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38, kakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo? Nchito yapadela imeneyi idzayamba pa November 1. Pambuyo pake kapepala ka Uthenga Wabwino Na. 38 kazigaŵilidwa mu ulaliki mofanana ndi tumapepala tonse.
2. Kodi kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38 kanapangidwa m’njila yotani?
2 Mmene Kanapangidwila: Kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38 kanapangidwa m’njila yakuti kazipindika kuti mutu wokopa cidwi ndi mau akuti “Kodi mungayankhe kuti . . . inde? iyai? kapena?” azionekela patsamba loyamba la kapepala. Woŵelenga akatsegula kapepala kameneka, adzaona zimene Baibo imanena poyankha funso limene lili pa mutu wa kapepalaka. Adzaonanso mmene angapindulile ndi malonjezo a m’Baibo, komanso zifukwa zimene ayenela kudalila Baibo. Patsamba lothela la kapepala kameneka, pali funso lofunika kuti woŵelenga aliganizilepo ndi lom’pempha kuphunzila zoonjezeleka.
3. Kodi tidzagaŵila bwanji kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38?
3 Mmene Tidzagaŵilila Kapepalaka: Nchito yapadela yogaŵila kapepalaka idzacitika mofanana ndi mmene timacitila poitanila anthu ku Cikumbutso ndi msonkhano wacigawo. Akulu adzapeleka malangizo ofotokoza mmene mpingo ungafolele gawo lao, mogwilizana ndi kalata imene analandila pa April 1, 2013. Mpingo umene uli ndi gawo laling’ono, ungadzipeleke kuti uthandize mpingo wapafupi umene uli ndi gawo lalikulu. Potenga tumapepala twa Uthenga wa Ufumu Na. 38, kumbukilani kutenga cabe tumene mungathe kugaŵila mlungu umenewo. Pa nyengo yogwila nchito yapadela imeneyi tingagaŵile tumapepala kwa anthu pocita ulaliki wapoyela pambuyo pakuti tamaliza nyumba zonse m’gawo lathu. Ngati mwamaliza kugaŵila tumapepala tonse mwezi usanathe, mungagaŵile cofalitsa ca mwezi umenewo. Pa Ciŵelu coyamba, tidzangocita nchito yapadela m’malo moyambitsa maphunzilo a Baibo. Ngati n’kotheka, kumapeto kwa mlungu tizigaŵilanso magazini. Kodi mukukonza zinthu zina kuti mukatengeko mbali mokwanila m’nchito yapadela imeneyi?