Ndandanda ya Mlungu wa December 16
MLUNGU WA DECEMBER 16
Nyimbo 116 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 2 ndime 1-6, ndi chati patsamba 19 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Chivumbulutso 1-6 (Mph. 10)
Na. 1: Chivumbulutso 3:14–4:8 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cipembedzo Coona Sicicita Zinthu Mwamwambo—rs tsa. 90 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Yesu Anapatsa Bwanji Citsanzo Ophunzila Ake?—Yohane 13:15 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 44
Mph. 10: Kodi Tinacita Zotani? Nkhani yokambilana yokambidwa ndi woyang’anila nchito. Chulani ku mpingo mbali ya gawo imene munakwanitsa kulalikila pa nthawi ya kampeni yogaŵila Tumapepala Twauthenga Na. 38. Pemphani omvela kuti afotokoze mmene anapindulila ndi kampeni imeneyi ndipo achule zocitika zocititsa cidwi.
Mph. 10: Acinyamata Tamandani Yehova. (Sal. 148:12, 13) Funsani acinyamata aŵili kapena atatu acitsanzo cabwino. Kodi amakuma ndi mavuto otani kusukulu cifukwa ca cikhulupililo cao? Nanga makolo ao ndi anthu ena awathandiza motani kuti apilile ziyeso zimenezo? N’ciani cawathandiza kuti azilankhula za cikhulupililo cao molimba mtima? Apempheni kuti afotokoze zocitikazo.
Mph. 10: “Tiyeni Nthawi Zonse Tizitamanda Mulungu. Tizicita Zimenezi Monga Nsembe Imene Tikupeleka kwa Mulungu.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 75 ndi Pemphelo