“Tiyeni Nthawi Zonse Tizitamanda Mulungu. Tizicita Zimenezi Monga Nsembe Imene Tikupeleka kwa Mulungu”
1. Kodi Akristu oyambilila anali kuiona bwanji misonkhano ya mpingo?
1 Zimene Paulo anakamba zokhudza misonkhano palemba la 1 Akorinto 14:26-33, zimatithandiza kudziŵa mmene misonkhano inali kucitikila m’nthawi ya atumwi. Pofotokoza mavesi amenewa, katswili wina wa Baibo analemba kuti: “N’zocititsa cidwi kuti pa misonkhano ya Chalichi coyambilila, pafupi-fupi aliyense akamapita ku misonkhano anali kudziŵa kuti ali ndi mwai ndiponso udindo wocitapo cinacake. Palibe amene anali kubwela kudzangomvetsela. Aliyense anali kubwela osati kudzangolandila koma kuti nayenso adzapeleke cinacake.” Akristu oyambilila anali kuona misonkhano ya mpingo kukhala mwai woonetsa cikhulupililo cao.—Aroma 10:10.
2. (a) Kodi n’ciani cimathandizila kuti misonkhano yathu izikhala yolimbikitsa? Ndipo n’cifukwa ciani zimenezi zimathandiza? (b) Kodi n’ciani cingatithandize kuti tizipeleka mayankho ogwila mtima pamisonkhano?
2 Kulengeza cikhulupililo cathu pa misonkhano kumathandizila kwambili kuti ‘timange mpingo.’ Inunso mungavomeleze kuti ngakhale kuti takhala tikupezeka pa misonkhano kwa zaka zambili, timasangalalabe ndi ndemanga zimene abale ndi alongo amapeleka. Timakhudzidwa ndi mayankho ogwila mtima a acikulile, ndi okhulupilila anzathu; timalimbikitsidwa ngati mkulu wacikondi wapeleka yankho logwila mtima; ndipo timasangalala ngati kamwana kapeleka yankho locokela mumtima loonetsa kuti kamakonda Yehova kwambili. N’zoonekelatu kuti ngati tonsefe tiyankhapo, timathandiza kuti misonkhano yacikristu izikhala yolimbikitsa.
3. (a) Kodi tingaphunzilepo ciani pa citsanzo ca Mose ndi Yeremiya? (b) N’cifukwa ciani mungakhale ndi cidalilo cakuti Mulungu adzakuthandizani kuti muziyankhapo pamisonkhano?
3 Komabe, anthu amantha ndi amanyazi amavutika kwambili kuyankhapo. Ngati inu mumamva conco, musaganize kuti ndinu nokha. Ngakhale atumiki a Mulungu okhulupilika monga Mose ndi Yeremiya ananena kuti analibe luso lolankhula pagulu. (Eks. 4:10; Yer. 1:6) Yehova anawathandiza atumiki akale amenewo kumtanda poyela, inunso adzakuthandizani kupeleka nsembe zomtamanda. (Ŵelengani Aheberi 13:15.) Kodi muyenela kucita ciani kuti Yehova akuthandizeni kuthetsa mantha poyankhapo? Coyamba, muzikonzekela bwino misonkhano. Ndiyeno, musanapite ku Nyumba ya Ufumu, pemphelani kwa Yehova ndi kumuuza mwacindunji kuti akuthandizeni kuyankhapo. (Afil. 4:6) Mungakhale ndi cidalilo cakuti adzayankha pemphelo lanu cifukwa zimene mupempha ndi ‘zogwilizana ndi cifunilo cake.’—1 Yoh. 5:14; Miy. 15:29.