Ndandanda ya Mlungu wa December 30
MLUNGU WA DECEMBER 30
Nyimbo 126 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 2 ndime 14-19, ndi bokosi patsamba 25 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Chivumbulutso 15-22 (Mph. 10)
Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 43
Mph. 10: “Athandizeni kuti ‘Akhazikike m’Cikhulupililo.’” Nkhani. Ndiyeno, citani citsanzo cacidule ca mmene tingayambitsile phunzilo pogwilitsila nchito magazini pa Ciŵelu coyamba mu January. Limbikitsani onse kutengako mbali.
Mph. 10: Thandizani Mwana Wanu Kukhala Wofalitsa. Nkhani yozikidwa m’buku la Gulu patsamba 82, ndime 1 ndi 2. Funsani kholo la citsanzo cabwino limene mwana wake ndi wofalitsa wosabatizika. Kodi anathandiza bwanji mwana wake kuti ayenelele kukhala wofalitsa?
Mph. 10: Ndingacitenso Mantha Ndi Ndani? (Aheberi 13:5, 6) NKhani yokambilana yocokela mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2012 masamba 24-25, ndime 10-12. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene aphunzilapo.
Nyimbo 119 ndi Pemphelo