Ndandanda ya Mlungu wa December 23
MLUNGU WA DECEMBER 23
Nyimbo 127 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 2 ndime 7-13, ndi bokosi patsamba 20 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Chivumbulutso 7–14 (Mph. 10)
Na. 1: Chivumbulutso 9:1-21 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Akristu Angasonyeze Bwanji Kuti Ndi Oceleza?—Aheb. 13:2 (Mph. 5)
Na. 3: Akristu a mu Cipembedzo Coona Amakondana Komanso Sakhala Mbali ya Dziko—rs tsa. 90 ndime 2-3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 124
Mph. 10: Cogaŵila mu January ndi February. Nkhani yokambilana. Kambilanani buku limene mudzagaŵila, ndipo khalani ndi zitsanzo ziŵili zosonyeza mmene mungagaŵilile bukulo.
Mph. 10: Acinyamata, Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza Paholide? Nkhani. Fotokozani mwacidule ndime 1 patsamba 113 m’buku la Gulu. Chulani ziyeneletso za upainiya wothandiza. Ndiyeno funsani wofalitsa mmodzi kapena aŵili amene anacitako upainiya wothandiza pamene anali paholide. Limbikitsani acinyamata kuti akaciteko upainiya wothandiza akatsekela sukulu.
Mph. 10: Tiphunzilapo Ciani. Makambilano ocokela mu Nsanja ya Mlonda ya October 15, 2013, patsamba 20. Pemphani wofalitsa mmodzi kapena aŵili kuti afotokoze mwacidule mmene akhalila acipambano pa mavuto a tsiku ndi tsiku
Nyimbo 46 ndi Pemphelo