Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa April 28, 2014.
Kodi n’ciani cinathandiza Yosefe kupewa kucita cisembwele ndi mkazi wa Potifala? (Gen. 39:7-12) [Mar. 3, w13 2/15 tsa. 4 ndime 6; w07 10/15 tsa. 23 ndime 16]
Kodi Yosefe ndi citsanzo cabwino motani kwa anthu amene amacitilidwa mosalungama ndi amene amavutika? (Gen. 41:14, 39, 40) [Mar. 10, w04 1/15 tsa. 29 ndime 6; w04 6/1 tsa. 20 ndime 4]
Kodi Yosefe anasonyeza cifundo abale ake pa zifukwa ziti? [Mar. 17, w99 1/1 tsa. 30 ndime 6-7]
Kodi fuko la Benjamini linakwanilitsa bwanji ulosi wa pa Genesis 49:27 m’kupita kwa nthawi? [Mar. 24, w12 1/1 tsa. 29, bokosi]
Kodi lemba la Ekisodo 3:7-10 litiphunzitsa ciani ponena za Yehova? [Mar. 31, w09 3/1 tsa. 15 ndime 3-6]
Kodi Yehova anacita zinthu ziti mogwilizana ndi tanthauzo limodzi la dzina lake m’nthawi ya Mose? (Eks. 3:14, 15) [Mar. 31, w13 3/15 mas. 25-26 ndime 5-6]
Malinga ndi Ekisodo 7:1, kodi Mose anakhala bwanji ngati “Mulungu kwa Farao”? [Apr. 7, w04 3/15 tsa. 25 ndime 7]
Ngakhale kuti Aisiraeli anaona mphamvu za Yehova zopulumutsa ku Iguputo, kodi io anaonetsa mtima wotani pambuyo pake? Nanga ife tiphunzilapo ciani? (Eks. 14:30, 31) [Apr. 14, w12 3/15 mas. 26-27 ndime 8-10]
N’cifukwa ciani mau akuti “ndanyamula inu monga pa mapiko a ciombankhanga” ndi oyenelela ponena za mmene Yehova anacitila ndi mtundu waung’ono wa Aisiraeli? (Eks. 19:4) [Apr. 28, w96 6/15 tsa. 10 ndime 5–tsa. 11 ndime 2]
Kodi zitanthauza ciani kuti Yehova ‘amalanga ana cifukwa ca atate ao’? (Eks. 20:5) [Apr. 28, w04 3/15 tsa. 27 ndime 1]