Ndandanda ya Mlungu wa May 5
MLUNGU WA MAY 5
Nyimbo 33 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 8 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo Ekisodo 23-26 (Mph. 10 )
Na. 1: Ekisodo 25:1-22 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: M’Baibulo Palibe Pamene Panalembedwa kuti Adamu Ankasunga Sabata —rs p. 346 ¶4–p. 347 ¶2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Kukhulupilila Mizimu N’kutani? (bh tsa.100-103 ndime 10-13)
Msonkhano wa nchito:
Nyimbo 117
Mph. 10: Gaŵilani Magazini M’mwezi wa May. Kukambilana. Yambani ndi citsanzo coonetsa mmene mungagaŵilile magazini pogwilitsila nchito maulaliki aŵili acitsanzo amene ali patsamba lino. Ndiyeno kambilananinso maulaliki amenewa. Malizani mwa kulimbikitsa onse kuti azidziŵa bwino magazini iliyonse ndipo azigaŵila ena mosangalala.
Mph. 10: Zosoŵa za pa pampingo.
Mph. 10: Kodi tinacita zotani? Kukambilana. Pemphani omvela kuti afotokoze mapindu ndiponso zocitika za mu ulaliki zosangalatsa pa nkhani yakuti “Kuonjezela Luso Lathu mu Ulaliki—Kukhala Wofalitsa Wothandiza.”
Nyimbo 103 ndi Pemphelo